Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Zovala Zolembedwa Dzina la Ozipanga Kodi Nzanga?
“ZOVALA zimasonyeza mtundu wa munthu. . . . Nthaŵi zonse zovala ndizo chizindikiro cha zimene muli.” Ndimo mmene ananenera Barbara Dickstein, katswiri wa zovala pamyuziyamu ina yaikulu koposa. “Zimasimba mkhalidwe wanu, mbali yanu m’moyo, malo anu m’chitaganya,” iye anawonjezera motero. Pamenepo, mposadabwitsa kwambiri, kuti zovala nzofunika kwa anthu ambiri—ndi msampha pakati pa achichepere ena.
Komabe, kwa achichepere ambiri, nkhaŵa ya zovala imapambana pakukhala wofuna masitayelo chabe. Ambiri amaderanso nkhaŵa ndi dzina la opanga ake. Kwenikweni chinthu chirichonse chimene amagula—kuyambira pamatenesi kufikira pamagalasi a mmaso—ziyenera kukhala ndi chizindikiro chotchukacho cha ozipanga. Mwachitsanzo, kupenda kwa m’magazini a Seventeen kunavumbula kuti 90 peresenti ya asungwana achichepere amalingalira kuti dzina la opanga nlofunika pamene tikugula zovala za maseŵera.
Polingalira za kuchirikiza kwamphamvu kumene ofalitsa nkhani apereka pa zovala zolembedwa dzina la opanga m’zaka zaposachedwapa, zimenezi siziyenera kutidabwitsa. Kupyolera mwa kusatsa malonda kwa pa TV, kusatsa malonda kwa m’magazini ndi nyuzipepala, zikwangwani zosatsira malonda, ndi akanema, ogula zinthu akukopedwa ndi manenanena a opanga zovala. Cholinga ndicho kugonetsa anthu tulo kuti akhulupirire kuti chizindikiro cha opanga chiri ndi mphamvu ya kusanduliza chovalacho—ndi wochivala. Popanda chizindikiro cha opanga, majini amangokhala mathalauza wamba basi. Koma akakhala ndi chizindikiro cha wopanga, pomwepo majiniwo amakhala chinsinsi cha kutchuka, chikondwerero, ndi chikondi!
Kukopa kwa Chizindikiro
“Kodi dzina liri nchiyani?” anafunsa motero wotenga mbali wina m’limodzi la maseŵero a Shakespeare. Ponena za zovala, maina angakhale ofunika kwambiri. Bukhu lina lophunzitsa akatswiri ogulitsa akatundu linati: “Makasitomala ambiri amafunitsitsa kulipira mitengo yokwererapo chifukwa cha maina a zovala . . . ndi maina a opanga ake. Maina a zovala zambiri ali ndi mbiri ya muyezo wapamwamba wa sitayelo, mawonekedwe, kulimba, ndi mpangidwe. Kaŵirikaŵiri zovala zolembedwa dzina la ozipanga zimapereka mawonekedwe apadera.” (Know Your Merchandise, lolembedwa ndi Wingate, Gillespie, ndi Barry) Mofananamo, nkhani ya mu The New York Times Magazine imanena kuti “ukatswiri ndi kaombedwe m’zovala zodula kwambiri kaŵirikaŵiri ngwosiyana kwambiri” ndi wa m’zovala zotchipha. Motero zovala zolembedwa dzina la ozipanga zimakhala zolimbirapo ndipo zimawonekera bwino koposa zovala zotchipha.
Chikhalirechobe, kwa achichepere ambiri zizindikiro za opanga zovala siziri kwenikweni zizindikiro za kulimba kwake koma ziri zizindikiro za mkhalidwe wa munthu m’chitaganya—mabaji a ulemu. Monga momwe Sam wa zaka 17 akunenera kuti, “ngati ulibe, ndiwe wotsalira!”
Mphamvu ya Chitsenderezo cha Anzanu
Pamenepo, mposadabwitsa kuti wachichepere wina wotchedwa Casey akuti: “Pali chitsenderezo chachikulu cha kuvala zovala zolembedwa dzina la ozipanga.” Tennile wa zaka 14 akuwonjezera kuti: “Nthaŵi zonse aliyense amakufunsa kuti, ‘Kodi swetala yakoyo, jekete, kapena jini iri ndi dzina lanji?’” Malinga nkunena kwa wachichepere wina, chitsenderezo chingakhale chachikulu kwambiri kwakuti ngati sugwirizana nawo, “anthu adzakusinjirira ndi kukunena, kuti umavala nsapato zopanda maina kapena kuti umagula zinthu pakaunjika.”
Zowonadi, kufuna kufanana ndi ena ndi kuvomerezedwa nkwachibadwa. Andy wa zaka khumi ndi zisanu akuti: “Palibe munthu amene amafuna kukhala wotsalira ndi kukhala mbuli.” Koma kodi muyenera kufika pati kuti mugwirizane nawo? Joe wa zaka khumi ndi zinayi akuvomereza kuti: “Nthaŵi zina umagula zovala zimene sufuna—kungoti ugwirizane nawo chabe.”
Koma kodi kumakhala kwanzeru kulola ena kukupangirani zosankha, kukuchotserani ulemu wanu, kapena kukuthupsani kuti muwononge zokonda zanu, miyezo, kapena kulingalira kwanu kozoloŵereka? Aroma 6:16 amati: “Kodi simudziŵa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye?” Kodi ndani amene amafuna kukhala kapolo wa munthu wina? Komatu zimenezo ndizo zimene mumakhala pamene mulola anzanu kukusankhirani zimene mumavala, kapena ngati mudzilola kutengekatengeka ndi masitayelo kapena mafashoni.—Yerekezerani ndi Aefeso 4:14.
Kupeza Lingaliro la Baibulo
Kodi mungaphunzire motani kudziganizira? Khalani ozoloŵerana ndi malamulo a makhalidwe abwino a Mawu a Mulungu. Pamene kuganiza kwanu kuli kogwirizanitsidwa ndi Baibulo, mumakhala wosayedzamira kwambiri pakulamuliridwa kapena kunyengedwa ndi ena. (Miyambo 1:4) Zowona, Baibulo siliri bukhu la mafashoni. Koma liri ndi malamulo a makhalidwe abwino amene angakuthandizeni kusankha zimene mungavale. Mwachitsanzo, lingalirani mawu a mtumwi Paulo pa 1 Timoteo 2:9. Iye analangiza Akristu pamenepo ‘kudziveka ndi chovala choyenera, ndi kudzichepetsa ndi kulama maganizo, osati ndi . . . chovala chamtengo wokwera.’
Ndithudi Paulo sanali kunena kuti muyenera kuvala monga mphaŵi kapena kuvala zovala zimene ziri za sitayelo yachikale kwambiri momvetsa manyazi. Yesu Kristu mwiniyo mwachiwonekere anali ndi chovala chokwera mtengo. (Yohane 19:23, 24) Mmalomwake, Paulo anali kuchenjeza Akristu kusaika chisamaliro chonkitsa pa iwo eni cha momwe amavalira. Kugula chovala chifukwa cha kulimba kwake, kukongola, kapena ubwino wake nkomveka. Koma kuvala chovala chokhala ndi chizindikiro cha ochipanga kokha kuti ‘mudziwonetsere’ kapena ‘kusonkhezera mpikisano’ nkwadyera ndi kodzitamandira. (1 Yohane 2:16; Agalatiya 5:26) Mungachititse chidwi anthu ochepa nzeru oŵerengeka, komanso mungayambitse nsanje, kaduka, ndi mkwiyo mwa ena.
Paulo anauza Akristu kusonyeza kulama maganizo, kapena kulingalira bwino, ponena za mmene amavalira. Kumbali zina, kuvala zovala zolembedwa dzina la ozipanga ndiko chinthu chaupandu. Mwachitsanzo, Michael Thomas wa zaka khumi ndi zisanu, anaphedwa chifukwa cha kuvala nsapato za maseŵera othamanga zolembedwa dzina la ozipanga zogudwa U.S.$100. Wachichepere wina ankafuna nsapatozo. The New York Times inasimba kuti m’masukulu ambiri a m’mizinda mu United States, kuvala zinthu zodula zolembedwa dzina la ozipanga “kungayambitsedi ndewu ndipo ngakhale kuphana.” Motero wachichepere wina Katherine anati: “Kusasonkhezeredwa ndi anzanga m’njira imene ndimavalira ndakupeza kukhala tchinjirizo. Apo phuluzi, ndingadzutse maganizo osayenera mwa ena kulinga kwa ine mwini.”
Ndithudi, siachichepere onse amene angathe kugula zovala zolembedwa dzina la ozipanga. Ngati muli mumkhalidwe wotero, simungachitire mwina koma kuphunzira kukhala ‘wokhutira ndi chakudya ndi chovala’—ngakhale ngati chovalacho sichiri sitayelo yamakono kapena chopambana. (1 Timoteo 6:8) Mmalo mwa kuyamba kuchita nsanje, imene iri yowononga, yesani kuchita zimene mungathe mumkhalidwe wanu. (Tito 3:3) Zovala zanu zingakhale ziribe chizindikiro chapamwamba, komatu zingakhale zaudongo, zoyera, ndi zolemekezeka.
Kugula Mosamala
Zimene mumavala siziri kwenikweni zofunika ngati mtundu wa munthu amene inu muli. (1 Petro 3:3, 4) Komabe, uliwonse umene uli mkhalidwe wanu, kuli kwanzeru kuvala moyenerera kaamba ka chochitika chirichonse. Monga Mkristu, mulinso ndi thayo la kuvala mwanjira imene imayenera mminisitala wachichepere.—2 Akorinto 6:3.
Ubwino wake, kudekha Kwachikristu sikumatanthauza kwenikweni kuti muyenera kukhala wopanda sitayelo. Wachichepere wina Tamaria akufotokoza bwino lomwe pamene akuti: “Palibe cholakwika ndi kuvala chovala cha sitayelo—malinga ngati sunkitsa.” Ndiponso palibe cholakwika chirichonse ndi kuvala chovala chapamwamba. Kwenikweni, malinga nkunena kwa bukhu lotchedwa Dressing Smart, lolembedwa ndi Pamela Redmond Satran, akatswiri “amalangiza kugula zovala zabwino kopambana zimene mungathe ndipo amagogomezera pakulimba kwake koposa kuchuluka kwake.” Bukhu la Know Your Merchandise nalonso limapereka chilangizo ichi: “Wadirobu yaing’ono ya zovala zolimba, zosankhidwa mosamalitsa njabwino kwambiri koposa wadirobu yaikulu ya zovala zosalimba ndi zimene zingakhale m’fashoni kwanthaŵi yaifupi.”
Zimenezi zingakufunikiritseni kukhala wogula zovala mwanzeru—monga ‘mkazi wokhoza’ wofotokozedwa m’Baibulo pa Miyambo 31:10, 14, 18. Ankapita “kutali” ‘kukagula mosamala.’ Ndipo nanunso mungaphunzire ‘kudzigulira mosamala.’ Kope la magazini a Ladies’ Home Journal linaperekera lingaliro kuti: “Funsani ngati pali mtengo wa selo—ngakhale kumasitolo aakulu. . . . Fufuzani muli kunyumba. Pendani mitengo kumasitolo angapo.” Mwina mungaphunzire mmene mungakambirane mitengo ndi anthu ogulitsa, makamaka kumasitolo aang’ono.
Komabe, magazini a Consumer Reports amatikumbutsa kuti, “mtengo ndi mawonekedwe sindizo zitsogozo zopanda zolakwa ponena za kulimba kwa chovala.” Ndithudi, ofufuza ake amapeza kuti zovala zina zimene ziri zosadula zinali pafupifupi zofanana kulimba kwake ndi zovala zolembedwa dzina la ozipanga zodula. Bukhulo Dressing Smart limati: “Nthaŵi zina, zovala zimakhala zodula kokha chifukwa cha sitayelo yake, dzina la ozipanga, kapena kuyesa anthu ngati angagule.” Nthaŵi zina zizindikiro za opanga zovala zimaikidwa pazinthu zosalimba. Ndipo ngakhale ngati chizindikiro chake chiri chenicheni, kusaombeka bwino kwa nsalu kufakitale kungachitike.
Chotero musapusitsidwe ndi zizindikiro kapena mitengo. Samalani. (Miyambo 14:15) Pendani mosamala chovalacho—nsalu yake, mapangidwe ake, masokedwe, ndi zina zotero. Kodi chikuima bwino? Kodi pali mpendero wokwanira woti nkuwonjezeretsa chovalacho? Kodi pali zizindikiro zapadera za kulimba kwake, monga ngati nsalu yake yamkati ndi choimitsira kolala? Bwanji za tsatanetsatane wake, monga ngati misoko ndi kugwirizana kwa maluŵa kapena zithunzithunzi za nsaluyo?
Mwa kukhala wochenjera ndi wanzeru, mungapeŵe msampha wa chizindikiro cha opanga zovala kukukolani kupanga chosankha choipa. Mungathe kuvala bwino, popanda kuvala monkitsa.
[Mawu Otsindika patsamba 22]
Jini yokhala ndi chizindikiro cha opanga, mwamsanga imakhala chinsinsi cha kutchuka, chisangalalo, ndi chikondi!
[Chithunzi patsamba 23]
Musapusitsidwe ndi chizindikiro. Pendani mosamala chovala chirichonse musanachigule