Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Zopakapaka Ndingazigwiritsire Ntchito Bwino Motani?
“KODI ukufuna kudzola zopakapaka pang’ono?” Nina anadabwitsidwa kumva amake akumufunsa funso limeneli. Zaka ziŵiri kuchiyambiyambi, anali anakaniridwa kupatsidwa chilolezo kuti adzole zopakapaka. Koma pachochitika chapaderachi, paphwando lachikwati limene anati akapezekeko, amake anasankhapo kuti inali nthaŵi kwa Nina kuphunzira luso la akazili la kudzola zopakapaka. “Ndinanyumwa pang’ono,” akukumbukira tero Nina. “Sindinadziŵe kuzipaka bwino. Chotero Amayi anandipaka lipstick (zopaka m’milomo) pang’ono ndi blush (zofiiritsa masaya).”
Mwinamwake makolo anu amalingalira mofananamo kuti kukakhala koyenerera kwa inu kudzola zopakapaka.a Zitagwiritsiridwa bwino—ndipo mwachikatikati—zopakapaka zingakongoletse mawonekedwe a munthu. Komabe, zitagwiritsiridwa ntchito molakwika, zimakhala ndi chiyambukiro chosiyana kwenikweni. “Asungwana ena amadzola zopakapaka ndipo zimawoneka bwino,” anatero mnyamata wina wa zaka zapakati pa 13 ndi 19. “Koma asungwana ena amadzimatika zopakazo mopambanitsa, ndipo zimawapangitsa kuwoneka ngati chinyawu.”
“Atadzola mtundu wotuŵa, ndipo ngotuŵadi mbuu,” akuwonjezera tero msungwana wina wa zaka zapakati pa 13 ndi 19, “umangowapangitsa kuwoneka ngati choseketsa!” Kodi mungagwiritsire ntchito motani zopakapaka m’njira imene idzakongoletsa—osati kuipitsa—kawonekedwe kanu?
Zitsogozo Zochokera m’Mawu a Mulungu
Mafuta odzipaka siatsopano. M’mabwinja a Israyeli munapezedwa mbale kapena zotengera zobisika zimene modabwitsa zinatumikira chifuno chamakonochi. Izi “zinagwiritsiridwa ntchito kukometsera nkhope” za akazi Achiisrayeli. Mogwirizana ndi The Biblical Archaeologist, February 1955, “kugwiritsira ntchito . . . mafuta odzipaka kunali kofala” ngakhale m’nthaŵi za Baibulo.—Ezekieli 23:40.
Lerolino, indasitale ya mafuta odzipaka imawononga madola mamiliyoni zikwi ziŵiri pachaka ikusatsa malonda mu United States mokha. Mwakugwiritsira ntchito zitsanzo zokongola kwenikweni, iwo amapititsa patsogolo “uchiphadzuwa” wamakono, kuyambira pa “wachibadwa” kunka ku wongokometsera. “Chiphadzuwa” uyu, amatero, angakhale inu mutangogula mafuta odzipaka opangidwira chifunochi. Komabe, asungwana oŵerengeka amafikapo pakuwoneka mofanana ndi zitsanzo za fashonizo. Ndipo ngakhale atatero, “uchiphadzuwa” watsopanowu ungakhale wachabechabe botolo loyambirira la lipstick lisanathe.
Baibulo limakuthandizani kupewa kulamulidwa ndi mphepo yamafashoni. Ilo limati: ‘Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano; koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chiri chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.’ (Aroma 12:2) M’nthaŵi za Baibulo, akazi ena Achikristu angakhale anakhoterera kuvala zovala zokhumbiza ena ndi masitayelo atsitsi onkitsa amene anali ofala nthaŵiyo. Koma mtumwi Paulo analangiza kuti: ‘Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi chikatikati, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali.’—1 Timoteo 2:9.
Uphungu wa Paulo sumaletsa kuti muwoneke wokongola. Umangotanthauza kuti mawonekedwe anu ayenera kukhala “oyenera,” kapena abwino, osati okhumbiza ena; achikatikati ndi anzeru, osati opambanitsa kapena achikale. Liwu Lachigiriki kaamba ka “chikatikati” liri ndi tanthauzo la ‘kulemekeza malingaliro a ena,’ ndipo inu muyeneradi kulemekeza malingaliro a makolo anu. Chotero tiyeni tiwone mmene ichi chingagwirizanirane ndi kudzola zopakapaka.
Musanadzole Zopakapaka
Popeza kuti zopakapaka nzolinganizidwira kukongoletsa mawonekedwe anu, osati kupanga chinyawu kapena chinyengo, nkwanzeru choyamba kusamalira mawonekedwe anu achibadwa ndi umoyo wanu wonse. Chotero kukhala ndi kadyedwe kabwino ndikupuma mokwanira ndikuchita maseŵera mokhazikika kungachite zambiri kuwonjezera kukongola kwanu kuposa zimene zopakazopaka zirizonse zingachite.
Katswiri wa kukongola kwathupi Jane Parks-McKay akusonkhezera asungwana achichepere mowonjezereka “kuyamba ndi zoyambirira—zotchedwa, kusamalira khungu kokhazikika. . . . Anthu ambiri amakhoterera kunyalanyaza khungu lawo . . . [ndipo pambuyo pake] amaphimba khungu lawo losakongolalo ndi mafuta odzipaka akumayembekezera kuti izi zidzawakongoletsa.”
Zopakapaka zimagwira bwino pakhungu losamaliridwa bwino. Bukhu lakuti A Lifetime of Beauty likulongosola kuti: “Kuyeretsa khungu nkofanana ndi kukonzekera khoma popaka utoto watsopano: mosasamala kanthu ndi kukongola kwa mtundu, utoto wopakidwa udzawoneka wokakala ngati muli dothi ndi malo osasalala mkatimo. Khungu losasamalidwa bwino lidzawoneka loipa ndi lokakala.”
Chotero katswiri wa zopakapaka anauza Galamukani! kuti: “Mmawa, msungwana angasambe nkhope yake ndi choyeretsera nkhope chabwino. Pambuyo pake angadzole mafuta a kumaso ndi mafuta abwino ochepetsa thukuta.”
Kusanthula Zosowa Zanu
Tsopano, yang’anani bwino nkhope pa kalilole wanu ndikusanthula zabwino ndi zoipa. Kodi munafupidwa ndi maso owala, mawonekedwe osalala bwino, kapena khungu laumoyo, ngakhale lofewa bwino? Pamenepo mudzafunikira zopakapaka zochepa kapena ngakhale kusazichita. Komabe, mwinamwake khungu lanu nlamafuta kwambiri (ofala pamsinkhu waunamwali) ndi zipupu. Kapena mungakhale ndi zinthu zina zakumaso (monga ngati mafupa anu a m’masaya) zimene mukufuna kuzisamalira. Kugwiritsira ntchito bwino zopakapaka mwinamwake kungathe kuthandiza.
M’nthaŵi za Baibulo akazi ena anadzipaka utoto wakuda mwachinyengo kuti ‘akulitse maso.’ (Yeremiya 4:30) Lerolino, zopaka m’zikope, mapensulo opakila nsidze, ndi mafuta opakila nsidze amagwiritsiridwa ntchito kaamba ka chifuno chofananachi. Mafuta odzola ndi akhungu angasalalitse khungu lokakala. Zofiiritsa masaya zingakometsere mafupa anu a m’masaya.
Bwanji ngati mufunikira thandizo posankha kapena kudzola zopakapaka? Pali mabuku opezeka mmalaibulale apoyera omwe angathandize. Koma mungafunikirenso kufunsa amanu kapena bwenzi lachikulire. Msungwana wa zaka zapakati pa 13 ndi 19 wotchedwa Tina akukumbukira izi: “Amayi anapita nane kukagula ndipo anafunsa wogulitsa zopakapaka kundisankhira mitundu imene ndikayenera kudzola.” Akatswiri a kukongola kwakhungu m’masitolo otchuka angapereke uphungu wa mitundu imene ingayenderane bwino ndi khungu lanu ndi mmene zopakapaka zingadzoledwere bwino. Koma popeza kuti ntchito yawo njokugulitsani zinthu, samalirani kuti simukugula zinthu zimene simufunikira. Ndipo chifukwa cha kufunikira kwa mayendedwe anu Achikristu, mudzafuna kutsimikizira kuti simukugula mitundu imene ingagwire ntchito bwino m’maphwando amadzulo koma imene ingakhale yosayenerera ku machitachita a kusukulu kapena Achikristu.
Uphungu wa Zopakapaka
Masitayelo a zopakapaka amasiyanasiyana dziko ndi dziko. Koma malamulo achisawawa ochepera awa anganenedwe:
Lingalirani Khungu Lanu. Popeza kuti achichepere ambiri ali ndi khungu lamafuta ambiri, inu mwachidziŵikire mudzafunikira kumamatira ku zopakapaka zamadzi okhaokha, zopanda mafuta. Izi zimawonekera pang’ono, chotero mudzawonekera okhala ndi zopakapaka pang’ono. Ambiri amalingaliranso kuti zopakapaka zamafuta zimawonjezera zipupu.
Ŵerengani Mapepala Amalangizo. Yerekezerani zosanganiza zokhala ndi mtengo wotsika ndi zamtengo wokwera. Mwinamwake kusiyana kwenikweni kokha ndimtengo ndi zoikidwamo. Kuŵerenga mapepala amalangizo nkofunika mwapadera ngati mumadwala ndi zopakapaka.
Gwiritsirani Ntchito Zowunikira Zowalitsa. Ngati kuwala nkosakwanira, inu mungadzole zopakapaka zambiri. Popeza kuti zopakapaka zogwiritsiridwa ntchito ndi kuwala kwa gulobo ya fluorescent kungakhale koipa m’kuwala kwadzuwa, yesani kudzola zopakapaka zanu pafupi ndi zenera kotero kuti muwone mmene zikuwonekera m’kuwala kwachibadwa.
Gwiritsirani Ntchito Zopakapaka Mwachikatikati. Kupambanitsa ngakhale chinthu chabwino kungakhale kovulaza. (Yerekezerani ndi Miyambo 24:13; 25:27.) Ngati nkhope yanu nthaŵi zonse imawonetseratu kuti mwadzola “zopakapaka!” ndiko kuti mukudzola mopambanitsa kapena mukudzola mitundu yamphamvu kwambiri. Zopakapaka zimene zimachitidwa mopambanitsa zimaipitsa mawonekedwe anu ndipo zingaperekedi chithunzi cholakwika cha mayendedwe anu. (Yerekezerani ndi Ezekieli 23:36-42.) Chotero mamatirani ku zopaka zabwino, osati zopambanitsa. Zoloŵerani njira za kugwiritsira ntchito zopakapaka kotero kuti zofiiritsa masaya sizikuwoneka ngati mzera wopakidwa utoto wodutsa pankhope yanu kapena zopaka m’zikope sizikukupangitsa kuwoneka ngati nyani.
Samabani Nkhope Yanu Mosamalitsa. Bukhu lotchedwa A Lifetime of Beauty likuti: “Musapite kukagona usiku popanda kuchotsa zopakapaka zonse . . . Chizoloŵezi cha kugona ndi zotsala zakuda, ndi utoto wokangamila pankhope panu kudzapangitsa nkhope yanu kuwoneka yopanda udongo ndi yoipa.” Katswiri wina wa khungu ananenadi kuti “munthu amaika moyo pangozi ya kuyambukiridwa ndikuyabwidwa ngati alephera kuyeretsa zopakapaka zonse asanapite kukagona usiku uliwonse.” Gwiritsirani ntchito sopo yotsukira zopakapaka, monga ngati yathovu, kuyeretsa nkhope yanu.
Miyambo 31:30 ikuti: “Kukongola kungonyenga,” ndipo ngakhale zopakapaka zoikidwa mosamalitsa sizingabise kaimidwe koipa kapena umbuli wamaganizo. Baibulo likutikumbutsa kuti: “Kukongola kwanu sikufunikira kuchokera ku zokometsera zakunja . . . Mmalo mwake, kuyenera kukhala kwamkati mwanu, kukongola kosatha kwa mzimu wachete ndi wabata, womwe uli wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu.”—1 Petro 3:3, 4, New International Version.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Kodi Makolo Anga Adzandilola Liti Kudzikometsera?” yopezeka m’kope la Galamukani! la June 8, 1990.
[Bokosi patsamba 20]
Ngozi za Zopakapaka
Wochenjeza ogula Elaine Brumberg akusimba kuti: “Kusang’anizidwa kwa mankhwala opaka ambiri nkokhoza kubowola khungu ndikulowa m’thupi.” Zosang’aniza zina zofala zogwiritsiridwa ntchito nzokaikiridwa kukhala ndi zodzetsa kansa.
Zosanganiza zina (kaŵirikaŵiri zonunkhira ndi zosungitsa) zadziŵika kuchititsa matenda a kuyabwa ndi kuyetsemula. Zowona, zopangidwa zina zanenedwa kukhala zosadzetsa ziyambukiro kapena “zosanthulidwa ziyambukiro.” Koma mmene inu mudzachitira ndi chopangidwacho kungatsimikiziridwe mwa kuŵerenga ndi kusanthula kapepala ka malangizo basi.
Ngozi ina yofalikira njoyambukiridwa ndi tizilombo. Zopaka m’nsidze zingakhale mbuna yobalira tizilombo tating’ono tonka pamenepo kuchokera m’zikope kapena kuchokera m’zala kudzera mkamtengo kopakira zopaka m’nsidze. Ichi chingapangitse diso kuyambukiridwa ndi matenda ngati zopakidwazo ziloledwa kukhudza diso. Kuipitsa kulidi vuto m’zoyesera za m’masitolo mmene anthu ambirimbiri amagwiragwira ndi zala zawo. Chotero akatswiri ena amayamikira kuti mupewe kugwiritsira ntchito zoyesera za m’masitolo pankhope panu.
[Chithunzi patsamba 18]
Mayi wanu angathe kukuphunzitsani luso la kudzola zopakapaka