Mverani Atsogoleri
“Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera.”—AHEBRI 13:17.
1. Kodi ndimotani mmene timapindulira kuchokera ku ntchito ya oyang’anira Achikristu?
YEHOVA wapereka oyang’anira kaamba ka gulu lake “mu nthaŵi [ino] ya mapeto.” (Danieli 12:4) Iwo amatsogolera m’kusamalira onga nkhosa, ndipo kuyang’anira kwawo kuli kotsitsimula. (Yesaya 32:1, 2) Ndiponso, uyang’aniro wachikondi wochitidwa ndi akulu amene amachitira nkhosa za Mulungu mokoma mtima umatumikira monga chinjirizo kwa Satana ndi dongosolo lazinthu loipa iri.—Machitidwe 20:28-30; 1 Petro 5:8; 1 Yohane 5:19.
2. Kodi ndimotani mmene ena anawonera mtumwi Paulo, koma kodi ndi mkhalidwe wotani kulinga kwa akulu womwe uli woyenerera?
2 Koma kodi mumawawona motani akulu? Kodi mumati mu mtima mwanu: ‘Sindidzapitanso kwa mkulu wina yense mu mpingo uno ngati ndiri ndi vuto, chifukwa chakuti ndiribe chidaliro mwa aliyense wa iwo’? Ngati mumamva motero, kodi mungakhale mukukuza ndi malovu kupanda ungwiro kwawo? Mu Korinto wakale, ena ananena za mtumwi Paulo kuti: “Akalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma mawonekedwe a thupi lake ngofoka, ndi mawu ake ngachabe.” Komabe, Mulungu anagawira Paulo ku utumiki ndi kumgwiritsira ntchito monga “mtumwi kwa amitundu.” (2 Akorinto 10:10; Aroma 11:13; 1 Timoteo 1:12) Pamenepa, kukuyembekezeredwa, kuti mulingalire mofanana kwambiri ndi mlongo wina amene ananena kuti: “Tiri ndi bungwe la akulu labwino koposa m’dziko. Iwo anali pompano kudzathandiza pamene anafunika.”
Kodi Nkuwamvereranji?
3. Ngati Ambuye ati akhale ndi mzimu umene tisonyeza, kodi ndimotani mmene tiyenera kuwonera abusa aang’ono Achikristu?
3 Popeza abusa aang’ono Achikristu aperekedwa ndi Mbusa Wamkulu, Yehova Mulungu, kodi muganiza kuti iye afuna kuti tiwawone motani? Ndithudi, Mulungu amatiyembekezera ife kutsatira malangizo ochokera m’Baibulo olandiridwa kudzera mwa oyang’anira achikondi otsogoleredwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Pamenepo ‘Ambuye adzakhala ndi mzimu umene tisonyeza,’ tidzakhala ndi mtendere, ndipo tidzalimbikitsidwa mwauzimu.—2 Timoteo 4:22; yerekezani ndi Machitidwe 9:31; 15:23-32.
4. Kodi ndimotani mmene ife tingagwiritsirire ntchito kwa ife eni Ahebri 13:7?
4 Paulo anadandaulira kuti: “Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mawu a Mulungu; ndipo poyang’anira chitsimikiziro cha mayendedwe awo mutsanze chikhulupiriro chawo.” (Ahebri 13:7) Pakati pa Akristu oyambirira, choyamba atumwi anatsogolera. Lerolino, tingamvere awo opanga Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehava, oyang’anira ena odzozedwa, ndi amuna a “khamu lalikulu” otsogolera pakati pathu. (Chibvumbulutso 7:9) Ngakhale kuti sitikufulumizidwa kutsanzira kamvekedwe ka liwu lawo, kaimidwe ka thupi, kapena zizoloŵezi zina zaumunthu, tiyenera kukhoza kupangitsa mkhalidwe wathu kukhala wabwinopo mwa kutsanzira chikhulupiriro chawo.
5. Pa dziko lapansi lerolino, kodi ndikwandani kumene thayo lokulira la kusamalira mpingo Wachikristu laikiziridwako, ndipo kodi nchiyani chimene iwo ali oyenerera?
5 Padziko lapansi lerolino, thayo lalikulu la kusamaliridwa kwa zosoŵa zathu zauzimu laikiziridwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Woimira wake Bungwe Lolamulira limatsogolera ndi kugwirizanitsa ntchito yolalikira Ufumu ya padziko lonse. (Mateyu 24:14, 45-47) Makamaka akulu oikidwa ndi mzimu amenewa awonedwa monga olamulira auzimu, chifukwa chakuti Ahebri 13:7 angatembenuzidwe motere: “Kumbukirani okulamulirani . . . ” (Kingdom Interlinear) Pokhala ndi mipingo yoposa 60,000 ndi olengeza Ufumu oposa 3,500,000, akulu 12 opanga Bungwe Lolamulira ali ndi ‘zambiri zochita m’ntchito ya Ambuye.’ (1 Akorinto 15:58) Chifukwa cha ntchito yawo yopatsidwa ndi Mulungu, iwo amayenerera kugwirizanika kwathu kotheratu, monga momwedi bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba linachirikizidwira ndi Akristu oyambirira.—Machitidwe 15:1, 2.
6. Kodi ndi zinthu zina ziti zochitidwa ndi akulu zopindulitsa anthu a Yehova?
6 Oyang’anira aikidwa ndi mzimu kusamalira zosoŵa zauzimu za mpingo. (Machitidwe 20:28) Iwo amatsimikizira kuti uthenga wa Ufumu ukulalikidwa m’gawo la mpingo wa mmalowo. Amuna oyeneretsedwa Mwamalemba amenewa amaperekanso chitsogozo chauzimu mu mkhalidwe wachikondi. Iwo amalangiza, kutonthoza, ndi kuchitira umboni kwa abale awo auzimu ndi alongo, kumlingo umene amenewa angapitirizebe kuyenda moyenerera Mulungu. (1 Atesalonika 2:7, 8, 11, 12) Ngakhale pamene wina atenga njira yolakwa asanazindikire, amuna amenewa amafunafuna kumkonzanso “mu mzimu wachifatso.”—Agalatiya 6:1.
7. Kodi ndi uphungu wotani umene Paulo anapereka pa Ahebri 13:17?
7 Mitima yathu imafulumizidwa kuchita mogwirizana ndi oyang’anira a chikondi oterowo. Zimenezi ziri zoyenerera, popeza kuti Paulo analemba kuti: “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.” (Ahebri 13:17) Kodi tikaumva kukhala ukutanthauzanji uphungu umenewu?
8, 9. (a) Mogwirizana ndi Ahebri 13:17, kodi nchifukwa ninji tifunikira kukhala omvera kwa awo otsogolera? (b) Kodi kumvera kwathu ndi kugonjera zingakhale ndi ziyambukiro zabwino zotani?
8 Paulo akutidandaulira kumvera otilamulira mwauzimu. Tiyenera kukhala “ogonjera,” kulepa kwa abusa aang’ono amenewa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ‘iwo akuyang’anira miyoyo yathu,’ kapena miyoyo yoperekedwa kwa Mulungu. Ndipo kodi iwo “akuyang’anira” motani? Pano pa mawu olongosola chochitika cha nthaŵi yomweyo cha mneni Wachigriki a·gru·pneʹo kwenikweni amatanthauza kuti akulu “amasiya kugona.” Izi zimatikumbutsa ife za mbusa wokhala yekha amene amasiya kugona kuti achinjirize nkhosa zake ku maupandu a nthaŵi ya usiku. Nthaŵi zina akulu amathera masiku osagona ali m’mapemphero osonyeza nkhaŵa kaamba ka gulu la Mulungu kapena m’kupereka chithandizo chauzimu kwa okhulupirira anzawo. Tiyenera kuyamikira kwambiri chotani nanga utumiki wawo wokhulupirika! Ndithudi, sitifuna kukhala ofanana ndi “anthu osapembedza” a m’tsiku la Yuda amene ‘anapeputsa ufumu, nachitira mwano maulemerero,’ akulu Achikristu odzozedwa okhala ndi ulemerero woperekedwa ndi Mulungu, kapena ulemu, woikidwa pa iwo.—Yuda 3, 4, 8.
9 Yehova akakwiya ngati tikalephera kukhala omvera ndi ogonjera kwa oyang’anira Achikristu. Zimenezi zikatsimikiziranso kukhala zothodwetsa kwa iwo ndipo zikativulaza mwauzimu. Ngati tinali osagwirizanika, akulu angasamalire mathayo awo mwachisoni, mwinamwake mu mkhalidwe wokhumudwa umene ungatulukepo kutayika kwa chimwemwe m’ntchito zathu Zachikristu. Koma kumvera kwathu ndi kugonjera zimapititsa patsogolo mkhalidwe waumulungu ndi kulimbitsa chikhulupiriro chathu. ‘Ambuye amakhala ndi mzimu umene timasonyeza,’ ndipo chimwemwe chimasefukira mu mkhalidwe woterowo wa kugwirizanika, mtendere, ndi umodzi.—2 Timoteo 4:22; Salmo 133:1.
10. Mogwirizana ndi 1 Timoteo 5:17, kodi nchifukwa ninji otsogolera m’njira yabwino amayenerera ulemu?
10 Kukhala kwathu omvera ndi ogonjera kwa akulu a mumpingo sikumatanthauza kuti ndife okondweretsa anthu. Zimenezo zikakhala zosagwirizana ndi malemba, popeza kuti akapolo Achikristu a m’zaka za zana loyamba anawuzidwa kumvera ambuye awo, “wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuwopa [Yehova, NW].” (Akolose 3:22; Aefeso 6:5, 6) Oyang’anira amene ‘amayang’anira m’njira yabwino ndi kugwira ntchito zolimba m’kulankhula ndi kuphunzitsa’ amayenerera ulemu kwakukulukulu chifukwa chakuti chiphunzitso chawo chiri chozikidwa pa Mawu a Mulungu. Monga momwe Paulo analembera: “Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akuchititsa m’mawu ndi m’chiphunzitso. Pakuti malembo ati, usapunamiza ng’ombe yopuntha tirigu. Ndipo, wogwira ntchito ayenera kulipira kwake.”—1 Timoteo 5:17, 18.
11. Kodi “ulemu wowirikiza” umabwera motani kwa mkulu, koma kodi iye ayenera kupeŵa chiyani?
11 Mawu a Paulo ogwidwa mawu kumenewo amasonyeza kuti chithandizo cha zinthu zakuthupi chingaperekedwe moyenerera kwa awo oyang’anira zabwino zauzimu za ena. Komabe, zimenezi sizitanthauza kuti akulu ayenera kulanda malipiro, ndipo ndithudi “ulemu wowirikiza” suli chinthu chofunsiridwa ndi mkulu. Uwo ungachokere ku ziŵalo za mpingo mosaupempha, komatu iye safunikira konse kugwiritsira ntchito thayo lake kupeza ulamuliro kapena chuma chakuthupi. Iye sayenera kufunafuna ulemerero wa iyemwini kapena kuyanjana kwakukulukulu ndi anthu olemera kwambiri kuti apeze phindu la zinthu zakuthupi ndi kunyalanyaza ena. (Miyambo 25:27; 29:23; Yuda 16) M’malomwake, woyang’anira ayenera kuŵeta gulu la Mulungu ‘mofunitsitsa, osati kaamba ka chikondi cha phindu lonyansa, koma mofunitsitsa.’—1 Petro 5:2.
12. Kodi ndi kukumbukira yani kuti tidzathandizidwa kumvera awo otsogolera pakati pathu?
12 Tidzathandizidwa kumvera ndi kulemekeza otsogolerawo ngati tikumbukira kuti Mulungu iyemwini ndiye wapereka akuluwo. (Aefeso 4:7-13) Popeza amuna amenewa ali oikidwa ndi mzimu ndipo gulu la Mulungu liri ndi malo ofunika m’miyoyo ya Mboni za Yehova, ndithudi timafuna kusonyeza chiyamikiro chathu ndi ulemu kaamba ka makonzedwe a teokratiki. Ndiponso, tingathandize atsopano kukulitsa mkhalidwe umenewu ngati tikhazikitsa chitsanzo chabwino cha kumvera ndi kugonjera otsogolera pakati pathu.
Kodi Nkuyamikiriranji Utumiki Wawo?
13. (a) Kodi ndi malingaliro osiyana ati a uyang’aniro amene ali m’dziko ndi m’gulu la Mulungu? (b) Kodi tiri ndi zifukwa zabwino ziti za kukhalira ndi chidaliro mwa amuna otsogolera pakati pathu? (c) M’malo mokulitsa kupanda ungwiro kwa akulu ogwira ntchito zolimba, kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita?
13 M’dziko, muli chikhoterero cha kukana kutsogoleredwa. Monga momwe mphunzitsi wina ananenera: “Mlingo womakwerakwera wa maphunziro wawongolera maluso kotero kuti otsatira akhala osuliza kwambiri kwakuti amakhala pafupifupi osatheka kuwatsogolera.” Komatu mzimu wa kudzigangira suli wofunga m’gulu la Mulungu, ndipo tiri ndi zifukwa zabwino za kukhalira ndi chidaliro mwa amuna otsogolera pakati pathu. Mwachitsanzo, awo okha ofikitsa ziyeneretso Zamalemba amaikidwa kukhala akulu. (1 Timoteo 3:1-7) Iwo amaphunzitsidwa kukhala achifundo, achikondi, ndi othandiza, komabe a nkhokera m’kuchirikiza miyezo yolungama ya Yehova. Akulu amamamatira ku chowonadi Chamalemba, ‘kugwiririra zolimba ku mawu a chikhulupiriro, kuti akhale okhoza kulangiza ndi chiphunzitso cha moyo.’ (Tito 1:5-9) Ndithudi, sitiyenera kukulitsa kupanda ungwiro kwawo kwaumunthu, popeza kuti tonsefe ndife opanda ungwiro. (1 Mafumu 8:46; Aroma 5:12) M’malo mwa kudziwona kukhala ogwiritsidwa mwala ndi zofooka zawo ndi kuwona uphungu wawo mopepuka, tiyeni tiyamikire ndi kulandira chitsogozo chozikidwa m’Baibulo cha akulu monga chochokera kwa Mulungu.
14. Mogwirizana ndi 1 Timoteo 1:12, kodi mkulu ayenera kuwona motani utumiki wogawiridwa kwa iye?
14 Paulo, mwamuna woyamikira, ananena kuti: “Ndimyamika iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Kristu Yesu, Ambuye wathu, kuti anandiyesa wokhulupirika, nandiika kuutumiki.” (1 Timoteo 1:12) Utumiki umenewo, kapena udindo, unaphatikizapo ntchito yolalikira ndi kutumikiridwa kwa okhulupirira anzake. Ngakhale kuti woyang’anira ali ndi gawo loperekedwa ndi mzimu woyera la kutumikira monga mbusa, limeneli silifunikira kumpangitsa iye kudziwona kukhala wapamwamba kuposa ena, popeza kuti iyemwini ali mbali ya gulu la Mulungu longa nkhosa. (1 Petro 5:4) M’malomwake, iye ayenera kuyamikira kuti Mutu wa mpingo, Yesu Kristu, anamuŵerengera iye kukhala woyenerera kutumikira ziŵalo za gulu ndi kuti Mulungu anamuyeneretsa iye mwa kumpatsa mlingo wa chidziŵitso, nzeru, ndi luntha. (2 Akorinto 3:5) Popeza kuti mkulu ali ndi chifukwa cha kukhalira woyamikira kaamba ka mwaŵi wake woperekedwa ndi Mulungu, ziŵalo zina za mpingo ziyenera kuyamikira uminisitala umenewu, kapena utumiki.
15. Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la uphungu wa Paulo pa 1 Atesalonika 5:12, 13?
15 Mboni za Yehova ziri zoyamikira kaamba ka gulu limene Mulungu wapanga m’masiku otsiriza ano, ndipo chiyamikiro chimenecho chimatisonkhezera kulemekeza akulu. Tiyenera kukhala achimwemwe kugwirizana kotheratu ndi makonzedwe amene iwo amapanga kutipindulitsa. Paulo ananena kuti: “Koma, abale, tikupemphani, dziŵani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhale akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirireni inu; ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yawo.” (1 Atesalonika 5:12, 13) Kugwiritsira ntchito uphungu umenewu kumabweretsa chimwemwe ndi dalitso la Yehova.
Fulumirani Kugwiritsira Ntchito Uphungu
16, 17. Kodi ndi uphungu wotani umene akulu angapereke ponena za ukwati, ndipo kodi kuutsatira kungatulutsenji?
16 Paulo anadandaulira Tito ‘kulangiza ndi kudzudzula ndi ulamuliro wonse.’ (Tito 2:15) Mofananamo, oimira a Mulungu lerolino amatitsogoza ku malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo ndi malamulo. Pali zifukwa zabwino za kulandirira malangizo obwerezedwabwerezedwa a kugwiritsira ntchito uphungu ndi malangizo a gulu la Yehova ndi akulu oikidwa.
17 Mwachitsanzo: Akulu angadandaulire Mkristu wina uphungu wa Baibulo wa kukwatira “kokha mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39; Deuteronomo 7:3, 4) Iwo anganene kuti kukwatira munthu wosabatizidwa kungatsogolere ku mavuto okulira, monga momwedi Mfumu Solomo anachimwira kwambiri mwa kutenga akazi akunja, omwe anakhotereretsa mtima wake ku milungu yonyenga ndi kupatuka kwa Yehova. (1 Mafumu 11:1-6) Akulu angalongosolenso kuti Ezara anachititsa amuna Achiyuda kuleka akazi awo achikunja, ndipo Nehemiya ananena kuti awo okwatira osakhulupirira anali ‘kuchita cholakwa chachikulu mwa kuchita mosakhulupirika kutsutsana ndi Mulungu.’ (Nehemiya 13:23-27; Ezara 10:10-14; onani Nsanja ya Olonda, (Chingelezi) March 15, 1982, tsamba 31; November 15, 1986, masamba 26-30.) Madalitso ndi chikhutiritso zochokera m’kukondweretsa Yehova zimakhalapo mwa kugwiritsira ntchito uphungu woterowo Wamalemba woperekedwa ndi akulu achikondi.
18. Polingalira zimene Paulo analemba pa 1 Akorinto 5:9-13, kodi ndimotani mmene tiyenera kuchitira ngati chiŵalo cha banja chachotsedwa?
18 Kulinso koyenerera kulemekeza zosankha zachiweruzo za akulu. Paulo anauza Akristu m’Korinto kuti “musayanjana naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere iai.” Iwo anafunikira ‘kuchotsa woipayo pakati pawo.’ (1 Akorinto 5:9-13) Koma kodi mukachita motani ngati mmodzi wa achibale anu anachotsedwa? Pamene kuli kwakuti pangafunikire kuwonana kochepa kusamalira nkhani za banja, mayanjano onse auzimu ndi wachibale wochotsedwayo akafunikira kudulidwa. (Wonani Nsanja ya Olonda, April 15, 1988, masamba 26-31.) Ndithudi, kukhulupirika kwa Mulungu ndi gulu lake kuyenera kutisonkhezera kulemekeza zosankha zachiweruzo za oyang’anira.
19. Kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita ngati akulu akutisonyeza kuti tikupita m’njira yolakwika mwauzimu?
19 Sikuli kosavuta kukhalabe panjira yopapatiza yomka ku moyo. Kuti titero, tifunikira kutsatira malangizo operekedwa m’Mawu a Mulungu ndi a oikiziridwa mathayo a kuŵeta m’gulu lake. (Mateyu 7:13, 14) Ngati tinali kuyenda kuchokera ku mzinda wina kumka ku unzake pa galimoto ndipo tinatembenukira m’njira yolakwika, tidzafunikira kuchitapo kanthu kuwongolera njira yathu. Apo phuluzi, sitingafike konse kumene tikupita. Mofananamo, ngati akulu akutisonyeza kuti tasokera mwauzimu, mwinamwake mwa kupalana ubwenzi ndi wosakhulupirira, tifunikira kugwiritsa ntchito msanga uphungu wawo Wamalemba. Imeneyi ingakhale njira imodzi ya kusonyezera kuti ife kwenikweni “timakhulupirira Yehova.”—Miyambo 3:5, 6.
Ulemu Ngakhale m’Zinthu Zazing’ono
20. Kodi ndi mwa kudzifunsa mafunso otani kumene kungatithandize kusoyeza ulemu malangizo a akulu ngakhale m’nkhani zochepera?
20 Tifunikira kusonyeza ulemu ku malangizo a akulu ngakhale m’nkhani zazing’ono. Chotero tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimagwirizanika ngati akulu atipempha kuchezera odwala kapena kuphunzitsa atsopano mu uminisitala wakumunda? Kodi ndimalandira mosaŵiringula magawo pamisonkhano ndi kuwakonzekera iwo bwino lomwe? Kodi ndimalandira pamene akulu apereka malangizo okhudza kusunga mipando pa misonkhano, mkhalidwe wathu wa kavalidwe, ndi zina zotero? Kodi ndimagwirizanika pamene atipempha kuthandiza m’kuyeretsa Nyumba Yaufumu, kuchitira ripoti utumiki wathu wa kumunda mofulumira, kapena kufika pa misonkhano m’nthaŵi?’
21. Kodi kusonyeza kwathu ulemu kwa akulu kungatikumbutse mawu ati a Yesu?
21 Oyang’anira a mipingo amayamikira kugwirizanika kwathu, ndipo pamakhala zotulukapo zambiri zabwino. Kwenikweni, kukhala kwathu aulemu ndi ogwirizanika ngakhale m’nkhani zazing’ono kungatikumbutsedi mawu a Yesu akuti: ‘Wokhulupirika m’chaching’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu.’ (Luka 16:10) Ndithudi, timafuna kulingaliridwa kukhala okhulupirika.
Pitirizanibe Kulabadira Uyang’aniro Wachikondi
22. Kodi ndi ati amene ali ena a mapindu otuluka kuchokera mu uyang’aniro wachikondi wa kapolo wokhulupirika ndi akulu ampingo?
22 Mapindu ochokera mu uyang’aniro wachikondi wa kapolo wokhulupirika ndi akulu ampingo umatsimikizira kuti madalitso olemerera a Yehova ali pa gulu lake lapadziko lapansi. Ndiponso, malangizo aluso operekedwa ndi akulu amagwirizanitsa maluso awo ndipo amapititsa patsogolo umodzi pakati pathu. Amatulukiranso m’kuyesayesa kogwirizana ndi kwachipambano kupititsa patsogolo zabwino za Ufumu. Ndithudi, chotulukapo chimodzi chabwino cha kulabadira kwathu koyamikira uyang’aniro wa otsogolera chiri chakuti Mulungu amadalitsa ntchito yathu yolalikira ndi yopanga ophunzira. (Mateyu 28:19, 20) Kugwirizanika kwathu ndi akulu kukutikonzekeretsanso moyo wosatha m’dongosolo latsopano la zinthu.
23. Mogwirizana ndi 1 Yohane 5:3, kodi nchiyani chimene tiyenera kusonkhezeredwa kuchita?
23 Popeza timamkonda Yehova, kummvera sikuli ntchito yosasangalatsa. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.” (1 Yohane 5:3) Akristu okhulupirika amamvera mosangalala malamulo a Yehova ndipo amasonkhezeredwa kuchita mogwirizana ndi awo amene waikizirako uyang’aniro wampingo. Tiri oyamikira chotani nanga kukhala m’gulu la Mulungu ndi kukhala ndi “mphatso mwa amuna” zoterozo! (Aefeso 4:8) Pamenepa, tiri ndi chidaliro chotheratu chakuti Mulungu akutsogoza anthu ake, tikhaletu omvera nthaŵi zonse kwa okhala ndi mwaŵi wa kutsogolera pakati pa Mboni za Yehova.
Kodi Nziti Zimene Ziri Ndemanga Zanu?
◻ Kodi nkukhaliranji omvera kwa otsogolera pakati pathu?
◻ Kodi ndimkhalidwe wotani umene tiyenera kukhala nawo kulinga ku utumiki woperekedwa ndi akulu ogwira ntchito zolimba?
◻ Kodi nkukhaliranji ofulumira kugwiritsira ntchito uphungu woperekedwa ndi akulu?
◻ Kodi ndi mapindu otani amene amachokera m’kulabadira kwathu koyamikira uyang’aniro wachikondi?
[Mawu Otsindika patsamba 24]
Kodi mumachita mogwirizana ndi akulu mwa kulandira magawo a pa misonkhano, mwa kuthandiza kuyeretsa Nyumba Yaufumu, mwa kuchitira ripoti mofulumira ntchito yanu ya utumiki wa kumunda, ndi m’njira zina?
[Chithunzi patsamba 23]
Paulo anali wosangalala kulalikira mbiri yabwino ndi kutumikira okhulupirira anzake. Monga mkulu, kodi muli woyamikira mwaŵi wanu wopatsidwa ndi Mulungu wa utumiki?