-
Kodi Baibulo Linaneneratu za Mmene Anthu Adzidzaganizira ndi Kuchitira Zinthu Masiku Ano?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
Mogwirizana ndi ulosiwu, anthu ambiri masiku ano amangoganizira za iwo okha, zimene iwo akufuna, zimene amakonda komanso zimene akuona kuti zingawathandize kuti zinthu ziziwayendera bwino. Makhalidwewa ndi ofala kwambiri ndipo akuchulukirachulukira. Anthu ambiri ndi odzikonda kwambiri moti satha ngakhale pang’ono ‘kukonda zabwino.’ Iwo ndi “osayamika” moti sazindikira kufunika koyamikira zimene ali nazo kapena kuthokoza pa zimene anthu ena amawachitira.—2 Timoteyo 3:2, 3.
-
-
Kodi Baibulo Linaneneratu za Mmene Anthu Adzidzaganizira ndi Kuchitira Zinthu Masiku Ano?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
Kunenera ena zoipa. Anthu “onyoza” komanso “onenera anzawo zoipa” achuluka kwambiri. (2 Timoteyo 3:2, 3) Iwo amanyoza anthu anzawo kapena Mulungu. Amanenanso zabodza zokhudza ena kapena Mulungu.
Kuuma mtima. Anthu ambiri ndi “osakhulupirika,” “osafuna kugwirizana ndi anzawo,” “achiwembu” komanso “osamva za ena.” (2 Timoteyo 3:2-4) Iwo amakana kukambirana ndi ena, kugwirizana ndi anzawo akasemphana maganizo komanso kukwaniritsa zimene anapangana ndi anthu ena.
Chiwawa. Masiku ano, anthu ambiri ndi “oopsa.” Sachedwa kukwiya ndipo nthawi zambiri zimenezi zimachititsa kuti azichita zachipolowe kapena zankhanza.—2 Timoteyo 3:3.
-
-
Kodi Baibulo Linaneneratu za Mmene Anthu Adzidzaganizira ndi Kuchitira Zinthu Masiku Ano?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
Kusakonda achibale. Anthu “osamvera makolo” komanso “osakonda achibale awo” nthawi zambiri sasamalira a m’banja lawo, amawachitira nkhanza komanso zachiwawa.— 2 Timoteyo 3:2, 3.
-