-
Tizikhala Osiyana ndi Anthu a M’dzikoliNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2018 | January
-
-
9. N’chiyani chingathandize ana kuti azimvera makolo awo?
9 Ana angapewe kutengera khalidwe la kusamvera akamaganizira zinthu zabwino zimene makolo awo awachitira. Angachitenso bwino kukumbukira kuti Mulungu, yemwe ndi Atate wa tonsefe, amatilamula kuti tikhale omvera. Ana akamalankhula zinthu zabwino zokhudza makolo awo, angathandize ana anzawo kuti azilemekezanso makolo awo. Koma ana akaona kuti makolo awo sakuwakonda kwenikweni zingakhale zovuta kuti aziwamvera kuchokera pansi pa mtima. Mosiyana ndi zimenezi, ana akaona kuti makolo awo amawakonda ndi mtima wonse, amafuna kuchita zinthu zowasangalatsa ngakhale zitakhala zovuta kwambiri kwa anawo. Mnyamata wina dzina lake Austin ananena kuti: “Nthawi zambiri ndinkafuna kuchita zosiyana ndi zimene makolo anga ankafuna. Koma iwo ankaika malamulo omveka, ankafotokoza chifukwa chimene akuikira malamulowo komanso ankakambirana nane momasuka. Izi zinandithandiza kuti ndiziwamvera. Ndinkaona kuti amandikonda ndipo zimenezi zinandithandiza kuti ndiziyesetsa kuwasangalatsa.”
10, 11. (a) Kodi ndi makhalidwe oipa ati amene anthu osakonda anzawo amasonyeza? (b) Kodi Akhristu oona amasonyeza chikondi kwa ndani?
10 Paulo anatchula makhalidwe ena oipa amene anthu amasonyeza chifukwa chosakonda anzawo. Iye atatchula anthu “osamvera makolo” anatchula anthu osayamika, ndipo m’pomveka chifukwa anthu otere sayamikira zinthu zabwino zimene ena awachitira. Ananena kuti anthu adzakhala osakhulupirika komanso osafuna kugwirizana ndi anzawo. Ananenanso kuti anthu adzakhala achiwembu komanso onyoza, omwe amanena zinthu zonyoza anzawo ngakhalenso Mulungu. Anatinso anthu adzakhala onenera anzawo zoipa, kapena kuti anthu amene amafalitsa miseche n’cholinga choti awononge mbiri ya anthu ena.a
-
-
Tizikhala Osiyana ndi Anthu a M’dzikoliNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2018 | January
-
-
a Mawu achigiriki amene anamasuliridwa kuti “wonenera anzawo zoipa” ndi di·aʹbo·los, ndipo m’Baibulo mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za Satana, yemwe amanenera Mulungu zoipa.
-