-
Kodi Mumatsatira “Njira Yopambana” ya Chikondi?Nsanja ya Olonda—2009 | July 15
-
-
Zimakhala zosangalatsa kwambiri kukhala m’banja logwirizana ndiponso lokondana kwambiri. Mawu a Chigiriki akuti stor·geʹ nthawi zambiri ankagwiritsidwa ntchito pofotokoza chikondi chimene anthu a banja limodzi amasonyezana mwachibadwa. Akhristu amayesetsa kusonyeza chikondi kwa anthu a m’banja lawo. Paulo analosera kuti m’masiku otsiriza, anthu adzakhala “opanda chikondi chachibadwa.”b—2 Tim. 3:1, 3.
N’zomvetsa chisoni kuti masiku ano anthu m’banja alibe chikondi chachibadwa. N’chifukwa chiyani amayi ambiri oyembekezera amachotsa mimba? N’chifukwa chiyani mabanja ambiri safuna kusamalira makolo awo okalamba? N’chifukwa chiyani chiwerengero cha anthu osudzulana chikukwera? Chifukwa chake n’chakuti anthu alibe chikondi chachibadwa.
-
-
Kodi Mumatsatira “Njira Yopambana” ya Chikondi?Nsanja ya Olonda—2009 | July 15
-
-
b Mawu akuti “opanda chikondi chachibadwa” amasuliridwa kuchokera ku mawu akuti aʹstor·goi. Mawuwa achokera ku mawu akuti stor·geʹ, koma ali ndi mphatikira kutsogolo a-, wotanthauza “opanda.”—Onaninso Aroma 1:31.
-