-
Yunike ndi Loisi—Aphunzitsi Opereka Chitsanzo ChabwinoNsanja ya Olonda—1998 | May 15
-
-
Komabe, Yunike sanali yekha amene anali ndi zikhulupirirozo. Zimaonetsa kuti Timoteo anaphunzitsidwa “malembo opatulika” ndi onse aŵiri amayi ake ndi agogo ake aakazi otchedwa Loisi, amene anabala amake.a Mtumwi Paulo analangiza Timoteo kuti: “Ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziŵa amene adakuphunzitsa; ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziŵa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Kristu Yesu.”—2 Timoteo 3:14, 15.
-
-
Yunike ndi Loisi—Aphunzitsi Opereka Chitsanzo ChabwinoNsanja ya Olonda—1998 | May 15
-
-
Timoteo ‘anatsimikizika mtima’ ndi choonadi cha m’Malemba. Malinga nkunena kwa dikishonale ina yachigiriki, mawu amene Paulo anagwiritsira ntchito panopo amatanthauza “kukopeka kwambiri ndi; kukhutiritsidwa ndi” chinachake. Mosakayika konse, panafunikira nthaŵi yaitali ndi khama kuti akhomereze chikhulupiriro chimenecho mumtima mwa Timoteo, zimene zinamthandiza kuti azisinkhasinkha za Mawu a Mulungu ndi kuwakhulupirira. Choncho, mwachionekere, onse aŵiri Yunike ndi Loisi anachita khama pophunzitsa Timoteo za m’Malemba. Ndipo ndi phindu lotani nanga limene akazi aumulungu amenewo anapeza! Ponena za Timoteo, Paulo analemba kuti: “Pokumbukira chikhulupiriro chosanyenga chili mwa iwe, chimene chinayamba kukhala mwa mbuye wako Loisi, ndi mwa mayi wako Yunike, ndipo, ndakopeka mtima, mwa iwenso.”—2 Timoteo 1:5.
-