Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 3/15 tsamba 12-17
  • Kupatulidwa ndi Ufulu wa Kusankha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupatulidwa ndi Ufulu wa Kusankha
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupatulidwira kwa “Mulungu wa Israyeli”
  • Kudzipatulira kwa “Israyeli wa Mulungu”
  • Kugwiritsira Ntchito Mwanzeru Ufulu Wopatsidwa ndi Mulungu
  • Kusankha Kukhala Kapolo wa Ndani?
  • Kuphunzira Mmene Tingadzipindulitsire
  • Anabadwira mu Mtundu Wosankhika wa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kodi Mukuchita Mogwirizana ndi Kudzipatulira Kwanu?
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kuchita Mogwirizana ndi Kudzipatulira Kwathu “Tsiku ndi Tsiku”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • N’chifukwa Chiyani Muyenera Kudzipereka kwa Yehova?
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 3/15 tsamba 12-17

Kupatulidwa ndi Ufulu wa Kusankha

“Kristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu.”​—AGALATIYA 5:1.

1. Kodi mawu achihebri ndi achigiriki otembenuzidwa kuti “kupatulira,” “kupatula,” kapena “kupereka” kwenikweni amagwiritsiridwa ntchito kutanthauzanji?

OLEMBA Baibulo anagwiritsira ntchito mawu angapo achihebri ndi achigiriki popereka lingaliro la kupatulidwa, kapena kusankhidwa, ncholinga cha kuchita chifuno chopatulika. M’mabaibulo achicheŵa mawu ameneŵa atembenuzidwa kuti “kupatulira,” “kupatula,” kapena “kupereka.” Nthaŵi zina mawu ameneŵa amagwiritsiridwa ntchito mogwirizana ndi zimango​—makamaka kachisi wa Mulungu mu Yerusalemu wakale ndi kulambira kumene kunali kuchitikira mmenemo. Mawu ameneŵa sagwiritsiridwa ntchito kwenikweni m’nkhani wamba.

Kupatulidwira kwa “Mulungu wa Israyeli”

2. Kodi nchifukwa ninji Yehova moyenerera anatchedwa “Mulungu wa Israyeli”?

2 Mu 1513 B.C.E., Mulungu analanditsa Aisrayeli mu ukapolo ku Igupto. Patangopita nthaŵi yochepa, iye anawapatula kuti akhale anthu ake apadera, kuwaloŵetsa mu unansi wa pangano ndi iyemwini. Anawauza kuti: “Tsopano, ngati mudzamvera mawu anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa chapadera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa.” (Eksodo 19:5; Salmo 135:4) Atasankha Aisrayeli akuthupi kukhala chuma chake chapadera, moyenerera Yehova anatchedwa “Mulungu wa Israyeli.”​—Yoswa 24:23.

3. Kodi nchifukwa ninji Yehova sanasonyeze kukondera pamene anasankha Aisrayeli kukhala anthu ake?

3 Pamene anasankha Aisrayeli kukhala anthu ake opatulidwa, Yehova sanasonyeze kukondera, chifukwa chakuti iye anakondanso anthu amene sanali Aisrayeli. Iye anauza anthu ake kuti: “Mlendo akagonera m’dziko mwanu, musamamsautsa. Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m’dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m’dziko la Aigupto; ine ndine Yehova Mulungu wanu.” (Levitiko 19:33, 34) Patapita zaka mazana ambiri, kaimidwe ka Mulungu kanagogomezeredwa kwambiri ndi mtumwi Petro, amene anatsimikizira kuti: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”​—Machitidwe 10:34, 35.

4. Kodi unansi wa pakati pa Mulungu ndi Israyeli unadalira pa chiyani, ndipo kodi Aisrayeli anakhala mogwirizana ndi zimenezo?

4 Onaninso kuti kukhala anthu opatulidwa a Mulungu kunadalira pa zochita zawo. Nthaŵi yokhayo imene anatsatira mawu a Mulungu mosamalitsa ndi kusunga pangano lake ndiyo nthaŵi imene iwo anali “chuma [chake] chapadera.” Mwachisoni, Aisrayeliwo analephera kukwaniritsa zofunika zimenezi. Atakana Mesiya wotumizidwa ndi Mulungu m’zaka za zana loyamba C.E., iwo anataya mwaŵi wawo umenewo. Yehova sanalinso “Mulungu wa Israyeli.” Ndipo Aisrayeli sanalinso anthu opatulidwa a Mulungu.​—Yerekezerani ndi Mateyu 23:23.

Kudzipatulira kwa “Israyeli wa Mulungu”

5, 6. (a) Kodi Yesu anatanthauzanji pamene ananena mawu aulosi olembedwa pa Mateyu 21:42, 43? (b) Kodi “Israyeli wa Mulungu” anakhalapo liti ndipo anakhalapo motani?

5 Kodi zimenezi zinatanthauza kuti tsopano Yehova sadzakhalanso ndi anthu opatulidwa? Ayi. Pogwira mawu a wamasalmo, Yesu Kristu ananeneratu kuti: “Kodi simunaŵerenga konse m’malembo, mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangondya: ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m’maso mwathu? Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.”​—Mateyu 21:42, 43.

6 “Anthu akupatsa zipatso zake” anapezeka kuti ndiwo mpingo wachikristu. Pamene anali padziko lapansi, Yesu anasankha anthu oyambirira odzakhala mamembala ake. Koma patsiku la Pentekoste wa 33 C.E., anali Yehova Mulungu iyemwini amene anakhazikitsa mpingo wachikristu mwa kuthira mzimu wake woyera pa mamembala ake oyamba, okwanira 120. (Machitidwe 1:15; 2:1-4) Monga momwe mtumwi Petro analembera pambuyo pake, mpingo wongokhazikitsidwa kumenewu unakhala “mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake.” Osankhidwira chiyani? Kuti ‘akalalikire zoposazo za Iye amene anawaitana atuluke mumdima, naloŵe kuunika kwake kodabwitsa.’ (1 Petro 2:9) Otsatira a Kristu, odzozedwa ndi mzimu wa Mulungu, tsopano anakhala mtundu wopatulidwa, “Israyeli wa Mulungu.”​—Agalatiya 6:16.

7. Kodi mamembala a Israyeli wa Mulungu anayembekezera kukhala ndi chiyani, ndipo kodi iwo anauzidwa kupeŵanji?

7 Ngakhale kuti mamembala a mumtundu wopatulika anali “anthu a mwini wake,” iwo sanafunikire kukhala akapolo. Mosiyana ndi zimenezo, iwo anali kudzakhala ndi ufulu wokulirapo kusiyana ndi umene mtundu wa Israyeli wakuthupi unali nawo. Yesu analonjeza mamembala oyembekezera kukhala mtundu watsopano umenewu kuti: “Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Mtumwi Paulo anafotokoza kuti Akristu anamasulidwa ku zofunika za m’pangano la Chilamulo. Iye anafotokoza zimenezi kwa okhulupirira anzake a ku Galatiya kuti: “Kristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chirimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.”​—Agalatiya 5:1.

8. Kodi makonzedwe achikristu amapereka motani ufulu wokulirapo kusiyana ndi umene unali m’chipangano cha Chilamulo?

8 Mosiyana ndi Israyeli wakale wakuthupi, kufikira lerolino Israyeli wa Mulungu wakhala akutsatira mosamalitsa zofunika zilizonse zokhudza kudzipatulira kwake. Zimenezi siziyenera kutidabwitsa chifukwa chakuti mamembala ake anasankha kumvera mwaufulu. Pamene kuli kwakuti mamembala a Israyeli wakuthupi anali kupatulidwa mwachibadwa, mamembala a Israyeli wa Mulungu anakhala mamembala ake mwa kusankha. Choncho makonzedwe achikristu anakhala osiyana ndi pangano la Chilamulo lachiyuda, limene linali kungopatula anthu osawalola kaye kuti akhale ndi ufulu wa kusankha.

9, 10. (a) Kodi Yeremiya anasonyeza motani kuti nkhani ya kupatulidwa inali kudzasintha? (b) Kodi nchifukwa ninji munganene kuti si Akristu onse odzipatulira lerolino amene ali mamembala a Israyeli wa Mulungu?

9 Mneneri Yeremiya ananeneratu za kusintha kwa nkhani ya kupatulidwa pamene analemba kuti: “Taonani, masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda; si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo awo tsiku lija ndinawagwira manja kuwatulutsa m’dziko la Aigupto; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyawo, ati Yehova. Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israyeli atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa mkati mwawo, ndipo m’mtima mwawo ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, nadzakhala iwo anthu anga.”​—Yeremiya 31:31-33.

10 Popeza kuti ali ndi chilamulo cha Mulungu “mkati mwawo,” cholembedwa “m’mtima mwawo,” kunena kwake titero, mamembala a Israyeli wa Mulungu amasonkhezeredwa kukhala mogwirizana ndi kudzipatulira kwawo. Kusonkhezeredwa kwawo kuli ndi mphamvu yaikulu kuposa ya Aisrayeli akuthupi, amene anali kupatulidwa mwachibadwa, osati mwa kusankha. Lerolino, kusonkhezeredwa kwamphamvu kuti achite chifuniro cha Mulungu, monga momwe Israyeli wa Mulungu akuchitira, kukuchitikanso pakati pa olambira anzawo oposa mamiliyoni asanu padziko lonse lapansi. Nawonso apatulira miyoyo yawo kwa Yehova Mulungu kuti achite chifuniro chake. Ngakhale kuti anthu ameneŵa alibe chiyembekezo cha moyo wakumwamba monga chomwe chili ndi awo amene amapanga Israyeli wa Mulungu, iwo amasangalala ndi chiyembekezo cha kukhala kosatha padziko lapansi mu ulamuliro wa Ufumu wakumwamba wa Mulungu. Iwo amasonyeza kuyamikira kwawo Israyeli wauzimu mwa kuchirikiza mokangalika mamembala ake ochepa otsalira padziko lapansi kukwaniritsa ntchito yawo ya ‘kulalikira zoposazo za Iye amene anawaitana atuluke mumdima, naloŵe kuunika kwake kodabwitsa.’

Kugwiritsira Ntchito Mwanzeru Ufulu Wopatsidwa ndi Mulungu

11. Kodi munthu analengedwa ndi ufulu wotani, ndipo kodi uyenera kugwiritsiridwa ntchito motani?

11 Mulungu analenga anthu kuti azikonda ufulu. Iye anawapatsa ufulu wa kusankha. Mwamuna ndi mkazi wake oyamba anagwiritsira ntchito ufulu wawo wa kusankha. Komabe, iwo anasankha mopanda nzeru ndiponso mopanda chikondi ndipo kusankha kumeneko kunadzetsa mavuto kwa onse aŵiriwo ndiponso kwa mbadwa zawo. Ngakhale zili motero, zimenezi zikusonyeza bwino lomwe kuti Yehova sakakamiza zolengedwa zake zanzeru kuti zisankhe kuchita zinthu zosemphana ndi chikumbumtima chawo kapena zokhumba zawo. Ndipo popeza kuti “Mulungu akonda wopereka mokondwerera,” kudzipatulira kokha kumene kuli kovomerezeka kwa iye ndiko kudzipatulira kozikidwa pa chikondi, kopangidwa modzifunira ndiponso mokondwera, kozikidwa pa ufulu wa kusankha. (2 Akorinto 9:7) Kudzipatulira kwa mtundu wina uliwonse wosemphana ndi zimenezi nkosaloledwa.

12, 13. Kodi nchifukwa ninji Timoteo ali chitsanzo cha ana ophunzitsidwa bwino, ndipo kodi chitsanzo chake chapangitsa achinyamata ambiri kuchitanji?

12 Pozindikira kwambiri chofunika chimenechi, Mboni za Yehova zimalimbikitsa kuti munthu ayenera kudzipatulira yekha kwa Mulungu, koma sayesa mpang’ono pomwe kukakamiza munthu aliyense kuti adzipatulire, ndipo sakakamiza ngakhale ana awo. Mosiyana ndi matchalitchi ambiri, Mboni sizibatiza ana awo akali akhanda, monga kuti nzotheka kuwakakamiza kuti adzipatulire popanda kudzisankhira iwo eni. Mnyamatayo Timoteo ndiye chitsanzo cha m’Malemba choyenera kuchitsanzira. Monga munthu wamkulu, iye anauzidwa ndi mtumwi Paulo kuti: “Ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziŵa amene adakuphunzitsa; ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziŵa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Kristu Yesu.”​—2 Timoteo 3:14, 15.

13 Nzosangalatsa kudziŵa kuti Timoteo anadziŵa malemba opatulika chifukwa chakuti anaphunzitsidwa kuyambira ukhanda wake. Iye anatsimikizika mtima​—osati kukakamizidwa​—nakhulupirira ziphunzitso zachikristu zimene anaphunzitsidwa ndi amayi ake ndi agogo ake aakazi. (2 Timoteo 1:5) Chotsatirapo chake, Timoteo anazindikira kuti nkwanzeru kukhala wotsatira Kristu ndipo chotero anapanga chosankha chaumwini cha kudzipatulira kwachikristu. M’nthaŵi zamakono, anyamata ndi atsikana zikwi makumi ambiri amene makolo awo ndi Mboni za Yehova atsanzira chitsanzo chimenechi. (Salmo 110:3) Ena sanatero. Chili chosankha chaumwini.

Kusankha Kukhala Kapolo wa Ndani?

14. Kodi Aroma 6:16 amatiuzanji ponena za ufulu wotheratu?

14 Palibe munthu amene ali ndi ufulu wotheratu wochita chilichonse chimene angafune. Ufulu wa aliyense umatsekerezedwa ndi malamulo achilengedwe, monga lamulo la gravity (mphamvu yokoka), limene silinganyalanyazidwe mwa njira iliyonse. Tikanenanso zauzimu, palibe munthu amene ali ndi ufulu wotheratu wochita chilichonse chimene angafune. Paulo analingalira kuti: “Kodi simudziŵa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo?”​—Aroma 6:16.

15. (a) Kodi anthu amadzimva motani akalingalira za kukhala akapolo, koma kodi ambiri pomalizira pake amachitanji? (b) Kodi ndi mafunso oyenerera ati amene tingadzifunse?

15 Lingaliro la kukhala kapolo wa munthu wina limakhala losasangalatsa kwa anthu ambiri. Komabe, m’dziko lamakono ndithudi anthu ambiri amalola kuchitiridwa zinthu zina kapena kusonkhezeredwa m’njira zambiri zosazindikirika msanga zimene pomalizira pake zimawapangitsa kuchita mosadzifunira zinthu zimene ena akufuna kuti iwo achite. Mwachitsanzo, osatsa malonda ndi opanga zosangulutsa amakakamiza anthu kuti azichita zinthu zofanana mwa kuwakhazikitsira zinthu zoti azitsanzira. Mabungwe andale ndi achipembedzo amapangitsa kuti anthu azichirikiza malingaliro ndi zofuna zawo, ndipo nthaŵi zambiri sachita zimenezo pogwiritsira ntchito mfundo zokhutiritsa, koma nthaŵi zambiri amawapempha kuti akhale ochirimika ndi okhulupirika. Popeza kuti Paulo anati ‘ndife akapolo a amene timvera,’ aliyense wa ife angachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndine kapolo wa ndani? Kodi ndani amene amalamulira kwambiri malingaliro ndi njira yanga ya moyo? Kodi ndi atsogoleri achipembedzo, atsogoleri andale, anthu achuma, kapena anthu ochita zinthu zosangulutsa? Kodi ndimamvera ndani​—Mulungu kapena anthu?’

16. Kodi Akristu ali akapolo a Mulungu m’lingaliro lotani, ndipo kodi kaonedwe koyenerera nkotani kokhudza ukapolo umenewo?

16 Akristu amaona kuti kumvera Mulungu sikutanthauza kuti akusokoneza ufulu wawo. Iwo amagwiritsira ntchito ufulu wawo mofunitsitsa monga momwe anachitira Wopereka Chitsanzo wawo, Yesu Kristu, ndipo zofuna ndi zosankha zawo zimakhala zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. (Yohane 5:30; 6:38) Amakulitsa “mtima wa Kristu,” ndipo amamumvera kwambiri monga Mutu wa mpingo. (1 Akorinto 2:14-16; Akolose 1:15-18) Zimenezi zili zofanana ndi mkazi amene amakwatiwa ndi kugwirizana mofunitsitsa ndi mwamuna wake wokondedwa. Kunena zoona, gulu la Akristu odzozedwa limafanizidwa ndi namwali wokhulupirika amene anatomeredwa ndi Kristu.​—2 Akorinto 11:2; Aefeso 5:23, 24; Chivumbulutso 19:7, 8.

17. Kodi Mboni zonse za Yehova zinasankha kukhala ayani?

17 Aliyense wa Mboni za Yehova, kaya ali ndi chiyembekezo cha kumwamba kapena cha padziko lapansi, anadzipatulira yekha kwa Mulungu kuti achite chifuniro chake ndi kumumvera monga Wolamulira. Aliyense wa Mboni anadzisankhira yekha kuti adzipatulire ndi kukhala kapolo wa Mulungu m’malo mokhala kapolo wa anthu. Zimenezi zili zogwirizana ndi uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: “Munagulidwa ndi mtengo wake; musakhale akapolo a anthu.”​—1 Akorinto 7:23.

Kuphunzira Mmene Tingadzipindulitsire

18. Kodi ndi liti pamene munthu woyembekezera kukhala Mboni amayenera kubatizidwa?

18 Munthu asanayenerere kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova, iye amafunikira kukwaniritsa ziyeneretso za m’Malemba. Akulu amapenda mosamalitsa kuti aone ngati munthu wofuna kukhala Mboni akumvetsetsadi tanthauzo la kudzipatulira kwachikristu. Kodi iye akufunadi kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova? Kodi ali wofunitsitsa kukhala mogwirizana ndi zofunika zake? Ngati sakutero, ndiye kuti sali woyenerera kubatizidwa.

19. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kusuliza munthu amene walingalira zokhala mtumiki wodzipatulira wa Mulungu?

19 Komabe, ngati munthu akwaniritsa zofunika zonse, kodi angasulizidwe bwanji chifukwa cha kupanga chosankha chake chodzifunira kuti azisonkhezeredwa ndi Mulungu ndiponso ndi Mawu Ake ouziridwa? Kodi nkosaloledwa kwenikweni kuti munthu asankhe kusonkhezeredwa ndi Mulungu m’malo mosonkhezeredwa ndi anthu? Kapena kodi zimenezi nzosapindulitsa kwenikweni? Mboni za Yehova sizilingalira motero. Iwo amavomereza ndi mtima wonse mawu a Mulungu olembedwa ndi Yesaya akuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.”​—Yesaya 48:17.

20. Kodi anthu amamasulidwa motani ndi choonadi cha Baibulo?

20 Choonadi cha Baibulo chimamasula anthu kuti asamakhulupirire ziphunzitso za zipembedzo zonyenga, monga chiphunzitso cha kuzunzidwa kosatha m’helo wamoto. (Mlaliki 9:5, 10) M’malo mwake, chimadzaza mitima yawo ndi chiyamikiro chifukwa cha chiyembekezo choona cha akufa​—kuukitsidwa kumene kudzachitika pamaziko a nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. (Mateyu 20:28; Machitidwe 24:15; Aroma 6:23) Choonadi cha Baibulo chimamasula anthu ku kukhumudwa kumene kumachitika chifukwa cha kudalira malonjezo a atsogoleri andale amene nthaŵi zambiri amagwiritsa mwala. M’malo mwake, chimapangitsa mitima yawo kusefukira ndi chimwemwe pozindikira kuti Ufumu wa Yehova wayamba kale kulamulira kumwamba ndipo posachedwapa udzalamulira padziko lonse lapansi. Choonadi cha Baibulo chimamasula anthu ku machitachita amene salemekeza Mulungu, ngakhale kuti amaoneka ngati osangalatsa thupi lopanda ungwiroli, ndiponso amene amadzetsa mavuto aakulu chifukwa cha maubwenzi osweka, matenda, ndi imfa za achinyamata. Kunena mwachidule, kukhala kapolo wa Mulungu nkopindulitsa kwambiri kusiyana ndi kukhala kapolo wa anthu. Kunena zoona, kudzipatulira kwa Mulungu nkopindulitsa “tsopano nthaŵi ino, . . . ndipo nthaŵi ilinkudza, moyo wosatha.”​—Marko 10:29, 30.

21. Kodi Mboni za Yehova zimakuona motani kudzipatulira kwa Mulungu, ndipo kodi iwo amafunitsitsa kuchitanji?

21 Mboni za Yehova lerolino sali anthu opatulidwa mwachibadwa monga momwe analili Aisrayeli akale. Mboni zili mumpingo wa Akristu odzipatulira. Mboni iliyonse yobatizidwa yatero chifukwa chakuti ili ndi ufulu wake wa kusankha kuti idzipatulire. Ndithudi, Mboni za Yehova zimaona kuti kudzipatulira kumawapangitsa kukhala paunansi wathithithi ndi Mulungu umene amausonyeza mwa kumtumikira kwawo mofunitsitsa. Iwo amafunitsitsa kusungabe unansi wosangalatsa umenewu, kugwiritsitsa kwamuyaya ufulu umene Yesu Kristu anawasandutsira mfulu.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi nchifukwa ninji Mulungu sanasonyeze kukondera pamene anasankha Aisrayeli kuti akhale “chuma [chake] chapadera”?

◻ Kodi nchifukwa ninji munganene kuti kudzipatulira kwachikristu sikutanthauza kutaya ufulu?

◻ Kodi kudzipatulira kwa Yehova Mulungu kuli ndi mapindu otani?

◻ Kodi nchifukwa ninji kuli bwino kukhala mtumiki wa Yehova kusiyana ndi kukhala kapolo wa anthu?

[Chithunzi patsamba 15]

Mu Israyeli wakale, kupatulidwira kwa Mulungu kunali kuchitika mwachibadwa

[Chithunzi patsamba 16]

Kudzipatulira kwachikristu kumachitika mwa kusankha

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena