“Kuyambira Ukhanda Wako Wadziŵa”
MALINGA ndi zimene asayansi apeza posachedwapa, kulankhula ndi makanda kumathandiza kwambiri kakulidwe ka ubongo wawo, kukhazikitsa mphamvu yawo ya kuganiza, kulingalira, ndi kuthetsa mavuto. Zimenezi zimakhala choncho makamaka m’chaka choyambirira cha moyo wa khanda. International Herald Tribune inachita lipoti kuti ofufuza ena tsopano akukhulupirira kuti “chiŵerengero cha mawu amene khanda limamva tsiku lililonse ndicho chochititsa chachikulu koposa cha luntha khandalo likadzakula, chipambano kusukulu ndi chipambano m’moyo.”
Komabe, mawu olankhulidwawo ayenera kuchokera kwa munthu. Zikuoneka kuti wailesi yakanema kapena wailesi wamba singachite zimenezi.
Wasayansi ya minyewa wa pa University of Washington ku Seattle, U.S.A. anati: “Tsopano tikudziŵa kuti minyewa imalunzanitsidwa kuchiyambiyambi cha moyo ndi kuti ubongo wa khanda umakhaladi ukuyembekezera zokumana nazo kuti ulunzanitse minyewayo. Tangodziŵa kumene kuti zimenezi zimachitika kuchiyambi. Mwachitsanzo, makanda adziŵa kamvekedwe ka chinenero chawo pamsinkhu wa miyezi isanu ndi umodzi.”
Zimene apeza zikutsutsa lingaliro lofala lakuti makanda amakhala anzeru ngati angosonyezedwa chikondi chochuluka. Zikusonyezanso ntchito ya makolo pakukula kwa mwana.
Zimenezi zikutikumbutsa mawu a m’kalata youziridwa ya mtumwi Paulo kwa Timoteo akuti: ‘Kuyambira ukhanda wako wadziŵa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso.’ Malembo opatulika, omwe amayi wake ndi agogo ake okhulupirira ankauza Timoteo wakhanda, ayenera kuti anathandiza kwambiri pakukula kwake kukhala mtumiki wachangu kwambiri wa Mulungu.—2 Timoteo 1:5; 3:15.