Aphunzitseni Kuyambira Ukhanda
KUFUFUZA kwamakono kukusonyeza kuti “miluza imasonyeza ndi thupi lawo kuti imamva mawu.” Ofufuza a pa University of North Carolina “anapeza kuti amayi ataŵerengera ana awo asanabadwe, ana obadwa chatsopanowo anasonyeza kuti anali kumva pamene ndimezo zinaŵerengedwanso,” ikutero Winnipeg Free Press. Pamene akazi okhala ndi pakati aŵerenga momveka, zimenezi zingathandizenso kukhomereza miyezo ya makhalidwe abwino mwa mwana. Baibulo limanena kuti Timoteo ‘anadziŵa malembo opatulika kuyambira ukhanda.’ (2 Timoteo 3:14, 15) Mwachionekere, amake ndi agogo ake aakazi anazindikira kufunika kwa kumphunzitsa kuyambira ukhanda, kumenedi kuyenera kuti kunaphatikizapo kuŵerenga momveka.
Kuŵerenga ndiko “luso la m’moyo lamphamvu koposa limene tili nalo m’chitaganya chathu lerolino,” akutero wolemba Jim Trelease. Maluso a chinenero ndi kudziŵa mawu amawonjezereka ndi kuŵerenga momveka.
Kuli kwanzeru kuyamba kuŵerenga momveka mutangoyamba kulankhula kwa khanda lanu. Ngakhale kuti mwana wanu wosabadwa kapena wongobadwa kumeneyo sadzazindikira zimene mukunena poyamba, ntchitoyo singakhale yachabe polingalira mapindu amene angatulukepo m’kupita kwa nthaŵi. Miyambo 22:6 imati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.”
Kodi ndi chiyani chimene mungaŵerenge chimene chili choyenera ndi chopindulitsa? Ŵerengani Baibulo momveka kwa mwana wanu tsiku lililonse. Ndiponso ŵerengani zofalitsa zoyenera, monga Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo, Buku Langa la Nkhani za Baibulo, Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, ndi nkhani za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
Zoonadi, kudzipereka kwanu m’njira imeneyi kumafuna nthaŵi, koma ndi nthaŵi yotayidwa bwino. Ndi njira yoonekera yosonyeza kuti mumasamala za mwana wanu ndipo mumamkonda.