-
Kodi Ulosi Umatanthauza Chiyani?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
Kutsogolera maganizo awo. Mulungu ankatsogolera maganizo a aneneri ake kuti iwo azindikire uthenga wake. Izi n’zogwirizana ndi mawu a m’Baibulo akuti: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” Mawu amene anamasuliridwa kuti ‘kuuzira’ akhoza kumasuliridwanso kuti ‘kupumira.’ (2 Timoteyo 3:16; The Emphasised Bible) Choncho zinali ngati Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera, kapena kuti mphamvu imene amagwiritsa ntchito, kuti apumire uthenga wake m’maganizo mwa atumiki ake. Ndiyeno aneneriwo akalandira uthenga wochokera kwa Mulungu, ankasankha mawu abwino oti agwiritse ntchito poulemba.—2 Samueli 23:1, 2.
-
-
Kodi N’chiyani Chingakuthandizeni Kudziwa Bwino Mulungu?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
Zimene Baibulo limanena: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.”—2 Timoteyo 3:16.
Mfundo yake: Mulungu ndi Mlembi wamkulu wa Baibulo. Iye anachititsa kuti anthu alembe maganizo ake m’Baibulo. Pogwiritsa Baibulo, Mulungu watiuza za moyo umene amafuna kuti tikhale nawo. Watiuzanso makhalidwe ake monga chikondi, chilungamo ndi chifundo.—Ekisodo 34:6; Deuteronomo 32:4.
-