-
Kodi Baibulo Ndi Mawu a Mulungudi?Nsanja ya Olonda—2010 | March 1
-
-
“Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu, kulangiza m’chilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera mokwanira, wokonzeka bwino lomwe kuchita ntchito iliyonse yabwino.”—2 TIMOTEYO 3:16, 17.
MAWU a mtumwi Paulo amenewa ndi okhudza mtima kwambiri ndipo akusonyeza kuti Baibulo ndi buku lothandiza kwabasi. Kwenikweni, Paulo ankanena za mbali ya Baibulo imene inalipo pa nthawiyo, yomwe nthawi zina anthu amangoitcha kuti Chipangano Chakale. Komabe mawu a Paulowa akugwiranso ntchito pa mabuku onse 66 amene ali m’Baibulo, kuphatikizapo mabuku amene analembedwa ndi ophunzira a Yesu okhulupirika m’nthawi ya atumwi.
Kodi inunso mumaona kuti Baibulo ndi lofunika kwambiri ngati mmene Paulo ankalionera? Kodi mumakhulupirira kuti amene analemba Baibulo anauziridwadi ndi Mulungu? Akhristu am’nthawi ya atumwi ankakhulupirira zimenezi monganso mmene amachitira Akhristu masiku ano. Mwachitsanzo, m’zaka za m’ma 1300, mtsogoleri wina wa chipembedzo wa ku England, dzina lake John Wycliffe, ankaona kuti Baibulo ndi “buku la choonadi chokhachokha.” Buku lina lomasulira mawu a m’Baibulo linathirira ndemanga pa mawu a Paulo ali pamwambawo. Bukuli linanena kuti mfundo yoti Mulungu “anauzira Baibulo ikutsimikizira kuti zonse zimene Baibulo limanena ndi zoona.”—The New Bible Dictionary.
-
-
Baibulo Ndi Mawu Ouziridwadi ndi MulunguNsanja ya Olonda—2010 | March 1
-
-
KODI mtumwi Paulo ankatanthauza chiyani kwenikweni ponena kuti Baibulo ‘analiuzira ndi Mulungu’? (2 Timoteyo 3:16) Iye ankatanthauza kuti Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera potsogolera anthu amene analemba Baibulo kuti alembe zinthu zokhazo zimene Mulunguyo ankafuna.
-