Jehova Mulungu wa Chifuno
“Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, chotero chidzakhala.”—YESAYA 14:24.
1, 2. Kodi ambiri amanenanji ponena za chifuno cha moyo?
ANTHU kulikonse amafunsa kuti: “Kodi chifuno cha moyo nchiyani?” Mtsogoleri wandale Wakumadzulo ananena kuti: “Anthu ambiri koposa ndi kalelonse akufunsa kuti, ‘Kodi ndife yani? Nanga chifuno chathu nchiyani?’” Pamene nyuzipepala inafunsa achinyamata za chimene chili chifuno cha moyo, mayankho anali akuti: “Kuchita chinthu chilichonse chimene mtima wako ukhumba.” “Kusangalala kotheratu ndi mphindi iliyonse.” “Kumwerekera kotheratu m’zosangalatsa.” “Kukhala ndi ana, kukhala wachimwemwe ndiyeno kufa.” Ochuluka analingalira kuti moyo uno ndiwo wokha umene ulipo. Palibe aliyense amene analankhula za chifuno chokhalitsa cha moyo padziko lapansi.
2 Katswiri Wachikonfyushasi anati: “Tanthauzo lenileni la moyo limapezeka m’kukhalapo kwathu kwanthaŵi zonse, kwaumunthu.” Malinga ndi zimenezi, anthu akapitirizabe kubadwa, kulimbana ndi moyo kwa zaka 70 kapena 80, kenako kufa ndi kusakhalakonso kwamuyaya. Wasayansi yachisinthiko anati: “Tingalakelake yankho ‘lapamwamba’—koma palibe lililonse.” Kwa achisinthiko ameneŵa, moyo ndiwo kulimbana kuti munthuwe upitirize kukhalapo, ndi imfa ikumakhala chimaliziro cha zonse. Nthanthi zoterozo zimapereka lingaliro la moyo wopanda chiyembekezo.
3, 4. Kodi ndimotani mmene mikhalidwe ya dziko imayambukirira mmene ambiri amaonera moyo?
3 Ambiri amakayikira ngati moyo uli ndi chifuno poona kuti kukhalapo kwa anthu kwadzala ndi mavuto osaneneka. M’nthaŵi yathu, pamene munthu ayenera kukhala atafika pachimake pachipambano m’zamaindasitale ndi zasayansi, pafupifupi anthu okwanira mamiliyoni chikwi kuzungulira dziko lonse ali odwala kwakayakaya kapena samadya chakudya chokwanira. Ana mamiliyoni ambiri amafa chaka ndi chaka ndi mavuto ameneŵa. Ndiponso, zaka za zana lino la 20 zakhala ndi imfa za nkhondo zoŵirikiza kanayi kuposa zonse zimene zinachitika m’zaka mazana anayi zapitazo. Upandu, chiwawa, kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala oledzeretsa, kunyonyotsoka kwa mabanja, AIDS ndi matenda ena opatsirana mwa kugonana—ndandanda ya mavutowo ikupitirizabe. Olamulira adziko alibe mankhwala othetsera mavuto ameneŵa.
4 Poona mikhalidwe yoteroyo, munthu wina ananena zimene ambiri amakhulupirira kuti: “Palibe chifuno chokhalira ndi moyo. Ngati zinthu zoipa zonsezi zikuchitika, ndiko kuti moyo sutanthauza kanthu.” Ndipo mwamuna wina wokalamba analemba kuti: “Ndakhala ndikudzifunsa kwa moyo wanga wonse chifukwa chake ndili pano. Ngati pali chifuno chilichonse, ndilibenso nacho kanthu.” Motero, chifukwa chakuti anthu ochuluka samadziŵa chifukwa chake Mulungu akulolera kuvutika, mikhalidwe yadziko yosautsa imawachititsa kukhala opanda chiyembekezo chenicheni cha mtsogolo.
5. Kodi ndimotani mmene zipembedzo za dziko lino zikuwonjezerera chisokonezo pankhani ya chifuno cha moyo?
5 Angakhale atsogoleri achipembedzo ali ogaŵanika, ndi osatsimikiza ponena za chifuno cha moyo. Mbusa wakale wa St. Paul’s Cathedral m’London anati: “Kwa moyo wanga wonse ndakhala ndikumenyera kuti ndipeze chifuno chokhalira ndi moyo. . . . Ndalephera.” Zowona, atsogoleri achipembedzo ambiri amaphunzitsa kuti paimfa anthu abwino amapita kumwamba ndipo oipa amapita kuhelo wamoto kwamuyaya. Koma lingaliro limeneli limasiyabe mtundu wa anthu padziko lapansi ukupitiriza ndi njira yawo yosautsa. Ndipo chikadakhala chifuno cha Mulungu kuti anthu akakhale kumwamba, kodi nchifukwa ninji poyambapo sadawalenga monga zolengedwa zakumwamba, monga momwe analengera angelo, motero akumachinjiriza mavuto ambiri kwa anthu? Choncho, chisokonezo ponena za chifuno cha moyo padziko lapansi kapena kukana kukhulupirira kuti uli ndi chifuno chilichonse nchofala.
Mulungu wa Chifuno
6, 7. Kodi Baibulo limatiuzanji ponena za Mfumu Yachilengedwe Chonse?
6 Komabe, buku lofalitsidwa kopambana m’mbiri yonse, Baibulo Loyera, limatiuza kuti Yehova, Mfumu ya chilengedwe chonse, ali Mulungu wa chifuno. Limatisonyeza kuti iye ali ndi chifuno chofika patali, kwenikweni chokhalitsa, kaamba ka mtundu wa anthu padziko lapansi. Ndipo pamene Yehova wafuna kuchita chinthu, chimachitikadi mosalephera. Monga momwe mvula imameretsera mbewu, akutero Mulungu, “momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m’mene ndinawatumizira.” (Yesaya 55:10, 11) Chilichonse chimene Yehova wanena kuti adzachita, “chotero chidzakhala.”—Yesaya 14:24.
7 Anthufe tikhoza kukhala ndi chidaliro chokwanira chakuti Wamphamvuyonseyo adzasunga malonjezo ake, pakuti Mulungu “sakhoza kunama.” (Tito 1:2; Ahebri 6:18) Pamene iye atiuza kuti adzachita chinthu, mawu ake eniyo ndiwo umboni wakuti chidzachitikadi. Chimakhala monga chachitika kale. Iye akulengeza kuti: “Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina wofana[na] ndi Ine; ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthaŵi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe, ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse; . . . ndanena, ndidzachionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzachichitanso.”—Yesaya 46:9-11.
8. Kodi awo ofuna mowona mtima kupeza Mulungu akhozadi kumpeza?
8 Ndiponso, Yehova ‘safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike pakulapa.’ (2 Petro 3:9) Pachifukwa chimenechi, iye samafuna kuti aliyense akhale wosadziŵa za iye. Mneneri wotchedwa Azariya anati: “Mukamfuna [Mulungu], mudzampeza; koma mukamsiya adzakusiyani.” (2 Mbiri 15:1, 2) Chifukwa chake, awo amene mowona mtima amafuna kudziŵa Mulungu ndi zifuno zake akhozadi kutero ngati ayesetsa mwamphamvu kumfunafuna.
9, 10. (a) Kodi nchiyani chimene chaperekedwa kwa awo ofuna kudziŵa Mulungu? (b) Kodi kufunafuna Mawu a Mulungu kwatikhozetsa kuchitanji?
9 Koma kodi ndikumfunafuna kuti? Kwa awo ofunafunadi Mulungu, iye wapereka mawu ake, Baibulo. Kupyolera mwa mzimu wake woyera, mphamvu yogwira ntchito imodzimodziyo imene anagwiritsira ntchito polenga chilengedwe chonse, Mulungu analangiza amuna okhulupirika kulemba zimene tinafunikira kudziŵa ponena za zifuno zake. Mwachitsanzo, ponena za ulosi wa Baibulo, mtumwi Petro ananena kuti: “Pakuti kalelonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi mzimu woyera, analankhula.” (2 Petro 1:21) Mofananamo, mtumwi Paulo analengeza kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.”—2 Timoteo 3:16, 17; 1 Atesalonika 2:13.
10 Onani kuti Mawu a Mulungu amatikhozetsa kukhala “woyenera, wokonzeka,” osati mwapang’ono koma kwenikweni. Amakhozetsa munthu kukhala wotsimikiza ponena za Mulungu, zifuno zake, ndi zimene amafuna kwa atumiki ake. Buku lolembedwa ndi Mulungu liyeneradi kuchita zimenezo. Ndipo ndiwo magwero okhawo kumene tingafufuze ndi kupezako chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu. (Miyambo 2:1-5; Yohane 17:3) Mwa kuchita zimenezo, sitidzakhalanso “makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa.” (Aefeso 4:13, 14) Wamasalmo anasonyeza lingaliro loyenera pamene anati: “Mawu anu [Mulungu] ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.”—Salmo 119:105.
Zimavumbulidwa Mopitirizabe
11. Kodi ndimotani mmene Yehova wavumbulira zifuniro zake kwa mtundu wa anthu?
11 Pachiyambi penipeni pa banja la anthu, Yehova anavumbula zifuno zake ponena za dziko lapansili ndi anthu okhalapo. (Genesis 1:26-30) Koma pamene makolo athu oyamba anakana ulamuliro wa Mulungu, mtundu wa anthu unagwera mumdima wauzimu ndi imfa. (Aroma 5:12) Komabe, Yehova anadziŵa kuti pakakhala awo omwe akafuna kumtumikira. Chifukwa chake, kwa zaka mazana ambiri, iye wapitiriza kuvumbulira atumiki ake okhulupirika zifuno zake. Pakati pa awo amene analankhulana nawo panali Enoke (Genesis 5:24; Yuda 14, 15), Nowa (Genesis 6:9, 13), Abrahamu (Genesis 12:1-3), ndi Mose (Eksodo 31:18; 34:27, 28). Mneneri wa Mulungu Amosi analemba kuti: “Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.”—Amosi 3:7; Danieli 2:27, 28.
12. Kodi ndimotani mmene Yesu anaunikirira chidziŵitso chowonjezereka pazifuno za Mulungu?
12 Pamene Mwana wa Mulungu Yesu Kristu, anali padziko lapansi pafupifupi zaka 4,000 pambuyo pa chipanduko cha m’Edene, zoloŵetsedwamo zowonjezereka za zifuno za Yehova zinavumbulidwa. Izi zinali choncho makamaka ponena za chifuno cha Mulungu cha kukhazikitsa Ufumu wakumwamba wolamulira dziko lapansi. (Danieli 2:44) Yesu anapanga Ufumu umenewo kukhala mutu wankhani wa kuphunzitsa kwake. (Mateyu 4:17; 6:10) Iye ndi ophunzira ake anaphunzitsa kuti pansi pa Ufumuwo, chifuno choyambirira cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi ndi mtundu wa anthu chikakwaniritsidwa. Dziko lapansi likasandutsidwa paradaiso wokhalamo anthu angwiro, omwe akakhala ndi moyo kosatha. (Salmo 37:29; Mateyu 5:5; Luka 23:43; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:4) Ndiponso, Yesu ndi ophunzira ake anasonyeza zimene zikachitika m’dziko latsopano limenelo mwa zozizwitsa zimene Mulungu anawapatsa mphamvu yoti azichite.—Mateyu 10:1, 8; 15:30, 31; Yohane 11:25-44.
13. Ponena za zochita za Mulungu ndi mtundu wa anthu, kodi ndikusintha kotani kumene kunachitika pa Pentekoste wa 33 C.E.?
13 Pa Pentekoste wa 33 C.E., masiku 50 pambuyo pa kuuka kwa Yesu, mzimu wa Mulungu unatsanuliridwa pampingo wa otsatira a Kristu. Mpingowo unaloŵa m’malo Israyeli wosakhulupirika monga anthu apangano a Yehova. (Mateyu 21:43; 27:51; Machitidwe 2:1-4) Kutsanuliridwa kwa mzimu woyera pachochitikacho kunali umboni wakuti, kuyambira panthaŵiyo kumka mtsogolo, Mulungu akavumbula chowonadi chonena za zifuno zake kudzera mwa kakonzedwe katsopano kameneka. (Aefeso 3:10) Mkati mwa zaka za zana loyamba C.E., kalinganizidwe ka gulu ka mpingo Wachikristu kanakhazikitsidwa.—1 Akorinto 12:27-31; Aefeso 4:11, 12.
14. Kodi ndimotani mmene ofunafuna chowonadi angadziŵire mpingo wowona Wachikristu?
14 Lerolino, ofunafuna chowonadi angadziŵe mpingo wowona Wachikristu mwa kusonyeza kwake kosasintha mkhalidwe wa Mulungu waukulu koposa, chikondi. (1 Yohane 4:8, 16) Indedi, chikondi chaubale ndicho chizindikiro chodziŵira Chikristu chenicheni. Yesu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” “Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu.” (Yohane 13:35; 15:12) Ndipo Yesu anakumbutsa omvetsera ake kuti: “Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulirani inu.” (Yohane 15:14) Chotero atumiki owona a Mulungu ali awo amene amasunga lamulo la chikondi. Iwo samangolankhula ponena za icho, pakuti “chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.”—Yakobo 2:26.
Kuunikiridwa
15. Kodi atumiki a Mulungu angakhale otsimikizira ponena za chiyani?
15 Yesu ananeneratu kuti m’kupita kwanthaŵi, zifuniro za Mulungu zikaunikiridwa mopitirizabe pa mpingo wowona Wachikristu. Iye analonjeza otsatira ake kuti: “Koma nkhosweyo, mzimu woyera, amene Atate adzamtuma m’dzina langa, iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.” (Yohane 14:26) Yesu anatinso: “Onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 28:20) Motero, kuunikiridwa pa chowonadi chonena za Mulungu ndi zifuno zake kukuwonjezereka pakati pa atumiki a Mulungu. Inde, “mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kucha, kumkabe kuŵala kufikira usana woti mbee.”—Miyambo 4:18.
16. Kodi kuunikiridwa kwathu kwauzimu kumatiuzanji ponena za pamene tili m’zifuno za Mulungu?
16 Lerolino, kuunika kwauzimu kumeneko kuli koŵala kuposa ndi kalelonse, pakuti tikukhala m’nthaŵi imene maulosi a Baibulo akukwaniritsidwa kapena kuyandikira kukwaniritsidwa kwawo. Zimenezi zimatisonyeza kuti tikukhala mu “masiku otsiriza” a dongosolo la zinthu loipali. Ino ndiyo nyengo ya nthaŵi yotchedwa “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano”; imene idzatsatiridwa ndi dziko latsopano la Mulungu. (2 Timoteo 3:1-5, 13; Mateyu 24:3-13) Monga momwe Danieli ananeneratu, Ufumu wakumwamba wa Mulungu posachedwapa “udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [omwe alipo tsopano], nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.
17, 18. Kodi ndimaulosi aakulu otani amene tsopano akukwaniritsidwa?
17 Pakati pa maulosi omwe tsopano akukwaniritsidwa pali uja wolembedwa pavesi 14 la Mateyu chaputala 24. Yesu pamenepo anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale umboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” Kuzungulira dziko lonse lapansi, ntchito imeneyo yakulalikira Ufumu ikuchitidwa ndi mamiliyoni a Mboni za Yehova. Ndipo zikwi mazana ambiri za anthu akugwirizana nazo chaka chilichonse. Zimenezi zikugwirizana ndendende ndi ulosi wa pa Yesaya 2:2, 3, umene umanena kuti mu “masiku otsiriza” a dziko loipali, anthu ochokera m’mitundu yambiri adzabwera ku kulambira Yehova kowona, ndipo ‘akawaphunzitsa za njira zake, ndipo akayenda m’mayendedwe ake.’
18 Atsopano ameneŵa akubwera muunyinji “ngati mtambo” kudzalambira Yehova, monga kunanenedweratu pa Yesaya chaputala 60, vesi 8. Isa 60 Vesi 22 limawonjezera kuti: “Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.” Nthaŵi imeneyo, monga momwe umboni ukusonyezera, ndiyo tsopano lino. Ndipo atsopano angakhale ndi chidaliro chakuti poyanjana ndi Mboni za Yehova, iwo adza kudzagwirizana ndi mpingo wowona Wachikristu.
19. Kodi nchifukwa ninji tikunena kuti atsopano amene amayanjana ndi Mboni za Yehova akubwera kumpingo wowona Wachikristu?
19 Kodi nchifukwa ninji tinganene zimenezi motsimikiza? Chifukwa chakuti atsopano ameneŵa, limodzi ndi mamiliyoni omwe ali kale m’gulu la Yehova, apatulira miyoyo yawo kwa Mulungu ndipo akuchita chifuniro chake. Zimenezi zimaphatikizapo kukhala ndi moyo mogwirizana ndi lamulo laumulungu la chikondi. Monga umboni umodzi wa zimenezi, Akristu ameneŵa asula ‘malupanga awo kukhala zolimira, ndi nthungo zawo kukhala anangwape ndipo sakuphunziranso nkhondo.’ (Yesaya 2:4) Mboni za Yehova zonse padziko zachita zimenezi chifukwa chakuti zimasonyeza chikondi. Zimenezi zimatanthauza kuti sanganyamule zida zankhondo ndi kumenyana okhaokha kapena ndi wina aliyense. Mwa zimenezi iwo ali apadera—osiyana ndi zipembedzo zadziko. (Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 3:10-12, 15) Iwo samadziloŵetsa m’machitachita autundu opatulana, chifukwa chakuti amapanga ubale wa dziko lonse womangidwa ndi chikondi, “chomangira cha mtima wamphumphu.”—Akolose 3:14; Mateyu 23:8; 1 Yohane 4:20, 21.
Ochuluka Amasankha Kusadziŵa
20, 21. Kodi nchifukwa ninji anthu ochuluka kwambiri ali mumdima wauzimu? (2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19)
20 Pamene kuunika kwauzimu pakati pa atumiki a Mulungu kukuŵaliraŵalira, anthu ena onse padziko lapansi akuloŵerera mumdima wauzimu wa ndiwe yani. Iwo sakumdziŵa Yehova kapena zifuno zake. Mneneri wa Mulungu analongosola za nthaŵi imeneyi pamene anati: “Pakuti taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu.” (Yesaya 60:2) Zimenezi zili motero chifukwa chakuti iwo sakusonyeza chikondwerero chowona mtima cha kuphunzira za Mulungu, ndipo samasonyezanso ngakhale chikhumbo cha kuyesa kumkondweretsa iye. Yesu anati: “Koma chiweruzo ndi ichi, kuti kuunika kunadza ku dziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zawo zinali zoipa. Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake.”—Yohane 3:19, 20.
21 Anthu oterowo sali ofunitsitsa kudziŵa chifuniro cha Mulungu. M’malo mwake, amasumika miyoyo yawo pakuchita chifuniro chawo. Koma mwa kunyalanyaza chifuniro cha Mulungu, amadziika okha mumkhalidwe wangozi, pakuti Mawu ake amalengeza kuti: “Wopeŵetsa khutu lake kuti asamve chilamulo, ngakhale pemphero lake linyansa.” (Miyambo 28:9) Iwo adzalandira mphotho ya njira imene aisankha. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.”—Agalatiya 6:7.
22. Kodi makamu ofuna kudziŵa Mulungu tsopano akuchitanji?
22 Komabe, pali makamu ambiri amene amafuna kudziŵa chifuniro cha Mulungu, amene mowona mtima amamfunafuna, ndi amene amakopeka ndi iye. “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu,” limatero lemba la Yakobo 4:8. Ponena za oterowo Yesu anati: “Wochita chowonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu.” (Yohane 3:21) Ndipo ndimtsogolo modabwitsa chotani nanga mmene Mulungu walinganizira awo amene alinkudza kukuunika kumeneko! Nkhani yathu yotsatira idzafotokoza ziyembekezo zosangalatsa zimenezo.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ambiri amanenanji ponena za chifuno cha moyo?
◻ Kodi Yehova amadzisonyeza yekha motani kukhala Mulungu wa chifuno?
◻ Kodi ndikuunikiridwa kwakukulu kotani kumene kunachitika m’zaka za zana loyamba C.E.?
◻ Kodi mpingo Wachikristu wowona ungadziŵidwe motani lerolino?