Olengeza Ufumu Akusimba
“Chita Ntchito ya Mlaliki”
KODI kukhala mlaliki kumatanthauzanji? Liwulo latembenuzidwa kuchokera ku liwu la Chingelezi evangelizer, lotengedwa ku liwu la Chigiriki lakuti eu·ag·ge·li·stesʹ, limene lili logwirizana kwambiri ndi liwu lakuti eu·ag·geʹli·on, lotanthauza “uthenga wabwino.” Motero, mlaliki ndiye wolengeza uthenga wabwino.
Akristu oona onse ali alaliki a uthenga wabwino chifukwa chakuti amalengeza uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu. Moyenerera, mtumwi Paulo analimbikitsa Timoteo “[ku]chita ntchito ya mlaliki wa uthenga wabwino.” Timoteo sanayenere kupeputsa ntchito imeneyi. Paulo anamlimbikitsa ‘kukhala maso m’zonse’ ndi ‘kukwaniritsa utumiki wake.’—2 Timoteo 4:5.
Monga alaliki a uthenga wabwino ifenso sitimapeputsa utumiki wathu ndipo ‘timakhala maso m’zonse,’ kapena timakhala atcheru kuuza ena za uthenga wabwino pa mpata uliwonse. M’njira imeneyo ambiri adziŵa Yehova ndi malonjezo ake pambuyo poti afikiridwa ndi Mboni za Yehova m’mikhalidwe ya mwamwaŵi. Zimenezo nzimene zinachitika kwa Seymore, mwamuna wa ku Barbados.
Seymore anali mphunzitsi wa pasukulu ya boma. Charles, mphunzitsi wa maola ochepa pasukulu imodzimodziyo ndi amene anali mmodzi wa Mboni za Yehova, anali mlaliki wauthenga wabwino watcheru. Iye anali mtumiki wanthaŵi yonse, kapena mpainiya, ndipo anagwiritsira ntchito mpata uliwonse kuuza ena za uthenga wabwino. Kunali kupyolera mwa ulaliki wamwamwaŵi wa Charles kuti Seymore anamva uthenga wa Ufumu kwa nthaŵi yoyamba.
Posapita nthaŵi Seymore nayenso anali wofunitsitsa kugaŵana choonadi cha m’Baibulo ndi ambiri monga momwe akanathera. Motero anayamba makambitsirano amwamwaŵi ndi anthu pamalo ake a ntchito, makamaka ophunzira ake. Ngakhale kuti m’maiko ena chipembedzo sichimaloledwa pasukulu za boma, mwamuna ameneyu anapatsidwa ntchito ya kuphuzitsa zachipembedzo ndi makhalidwe abwino. Koma tsopano malingaliro a Seymore akale pa nkhani zimenezi anali ataloŵedwa m’malo ndi chidziŵitso chake chatsopano cha Baibulo chimene anali atapeza kumene. Panthaŵi za kupuma, anali kulankhula ndi ophunzira ake ponena za malonjezo a Mulungu a dziko latsopano ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.
Kodi anawo anatani? Ambiri anasonyeza chikondwerero chenicheni cha uthenga wabwino wa Ufumu wa Yehova. Ndiyeno Seymore anayamba kuchititsa maphunziro a Baibulo 13 pakati pa ophunzira ake. Chikondwerero chawo chinali chachikulu kwakuti analinganiza kuphunzira Baibulo kaŵiri pamlungu. M’kupita kwa nthaŵi ambiri a iwo anayamba kufika pamisonkhano Yachikristu pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya kumaloko. Pakali pano asanu ndi anayi a iwo akhala Mboni za Yehova zodzipatulira ndi zobatizidwa. Ponena za Seymore, iye tsopano akuchita utumiki wake mokwanira mwa kutumikira monga mpainiya wokhazikika ndi mkulu mumpingo wina wa Mboni za Yehova ku Barbados.
Ichi nchitsanzo chimodzi chabe cha mmene Mboni za Yehova padziko lonse lapansi ‘zimachitira ntchito ya mlaliki wa uthenga wabwino,’ nthaŵi zina mwa kukhala ndi phande mu ulaliki wamwamwaŵi. Iwo amatsatira uphungu wa Baibulo wopezeka pa Akolose 4:5, 6, umene umati: “Muyendere mu nzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthaŵi ingatayike. Mawu anu akhale m’chisomo, okoleretsa, kuti mukadziŵe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.”