Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Muzikhulupirira Yehova Nthawi Zonse
    Nsanja ya Olonda—2015 | April 15
    • 2 Imeneyi ndi nthawi yomwe mtumwi Paulo anamangidwa kachiwiri ku Roma. Kodi zikanatheka kuti Akhristu anzake amupulumutse? Mwina mtumwi Paulo ankaona kuti palibe amene angamuthandize. Mwina n’chifukwa chake analembera Timoteyo kuti: “Pamene ndinali kudziteteza koyamba pa mlandu wanga, palibe amene anakhala kumbali yanga. Onse anandisiya ndekha. Ngakhale zinali choncho, usakhale mlandu kwa iwo.” Komabe iye anazindikira kuti akhoza kupeza thandizo chifukwa analemba kuti: “Koma Ambuye anaima pafupi ndi ine ndi kundipatsa mphamvu.” Yesu ndi amene anapereka mphamvu kwa mtumwiyu. Kodi mtumwi Paulo anathandizidwadi? Iye anati: “Ndinapulumutsidwa m’kamwa mwa mkango.”—2 Tim. 4:16, 17.a

      3 Mtumwi Paulo ankalimbikitsidwa akamakumbukira zimenezi chifukwa ankaona kuti kukhulupirira Yehova kudzamuthandiza kupirira mayesero alionse. N’chifukwa chake anapitiriza kulemba kuti: “Ambuye adzandipulumutsa ku choipa chilichonse.” (2 Tim. 4:18) Apatu zikuonetseratu kuti Paulo anazindikira kuti Yehova ndi Yesu amatithandiza pamene tikuona kuti palibiretu mtengo wogwira.

  • Muzikhulupirira Yehova Nthawi Zonse
    Nsanja ya Olonda—2015 | April 15
    • “M’KAMWA MWA MKANGO”

      10-12. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingasokoneze maganizo a Mkhristu amene akusamalira matenda aakulu? (b) Kodi kukhulupirira Yehova pa nthawi ya mavuto kumalimbitsa bwanji ubwenzi wathu ndi iye? Perekani chitsanzo.

      10 Paulo atakumana ndi mavuto aakulu ankamva ngati ali pafupi kulowa m’kamwa mwa mkango.” Mavuto ena akhoza kukuchititsaninso kumva ngati kuti muli pafupi kulowa mkamwa mwa mkango kapena mungamve kuti mwalowa kale. Pa nthawi ngati imeneyi kukhulupirira Yehova kumakhala kovuta koma kofunika kwambiri. Tiyerekeze kuti mukusamalira wachibale wanu amene akudwala matenda aakulu. Mwina mwapempha Yehova kuti akupatseni nzeru ndiponso mphamvu.b Kodi zikatero mumakhala ndi mtendere mumtima podziwa kuti Yehova akuona zonse ndipo adzakupatsani zonse zofunika kuti mupirire?—Sal. 32:8.

  • Muzikhulupirira Yehova Nthawi Zonse
    Nsanja ya Olonda—2015 | April 15
    • a Mwina mtumwi Paulo anapulumutsidwadi “mkamwa mwa mkango” weniweni kapena ankangophiphiritsa.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena