Kodi Mulungu Amakuona Motani Kulambira kwa Dziko Lachikristu?
“SI YENSE wakunena kwa ine, Ambuye, Ambuye, adzaloŵa mu ufumu wakumwamba,” anatero Yesu Kristu, “koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wakumwamba. Ambiri adzati kwa ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi . . . [sitina]chita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziŵani inu nthaŵi zonse; chokani kwa ine, inu akuchita kusayeruzika.”—Mateyu 7:21-23.
Kupyolera m’Mawu ake opatulika, Baibulo Loyera, Mulungu wamveketsa bwino chimene chili chifuniro chake. Kodi matchalitchi a Dziko Lachikristu akuchita chifuniro cha Mulungu? Kapena kodi ali amene Yesu anatcha “akuchita kusayeruzika”?
Kukhetsa Mwazi
Usiku imfa ya Mbuye wake isanachitike, Petro anatsala pang’ono kuyambitsa nkhondo ndi gulu la asilikali amene anatumidwa kudzagwira Yesu. (Yohane 18:3, 10) Koma Yesu anabwezeretsa bata nachenjeza Petro kuti: “Onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” (Mateyu 26:52) Chenjezo lomveka limeneli labwerezedwa pa Chivumbulutso 13:10. Kodi matchalitchi a Dziko Lachikristu alilabadira? Kapena kodi alinso ndi thayo la nkhondo zimene zikuchitika m’madera osiyanasiyana a dziko lapansi?
M’Nkhondo Yadziko II, Asebiya ndi Akroati zikwi mazana ambiri anaphedwa m’dzina la chipembedzo. “Ku Croatia,” ikutero The New Encyclopædia Britannica, “boma la komweko lachifasisti linaika lamulo la ‘kuyeretsa mtundu’ kumene kunaposa ndi machitachita a Anazi. . . . Panalengezedwa kuti limodzi la magawo atatu a Asebiya lidzapitikitsidwa m’dzikolo, limodzi la magawo atatu lidzatembenuzidwa kukhala Aroma Katolika, ndipo limodzi la magawo atatu lidzafafanizidwa. . . . Kuvomereza machitachita ameneŵa kwa atsogoleri achipembedzo achikatolika kunasokoneza kwambiri maunansi a tchalitchi ndi boma pambuyo pa nkhondo.” Anthu osaŵerengeka anakakamizidwa kusankhapo kukhala Akatolika kapena kufa; ena zikwi zambiri sanapatsidwe ndi mpata wakusankha. Midzi yathunthu—amuna, akazi, ndi ana—anakakamizidwa kuloŵa m’matchalitchi awo a Orthodox ndi kuphedwa. Nanga bwanji za magulu a nkhondo otsutsa achikomyunizimu? Kodi nawonso anachirikizidwa ndi chipembedzo?
“Ansembe ena anatengamo mbali m’nkhondo kumbali ya magulu a nkhondo oukira boma,” likutero buku lakuti History of Yugoslavia. “Magulu a nkhondo a Zigaŵenga anaphatikizapo ndi ansembe a matchalitchi onse aŵiri cha Serbian Orthodox ndi cha Roma Katolika,” likutero buku lakuti Yugoslavia and the New Communism. Mikangano ya zipembedzo ikupitiriza kusonkhezera nkhondo kumaiko a Balkan.
Ndipo bwanji za ku Rwanda? Mlembi wamkulu wa Catholic Institute for International Relations, Ian Linden, analankhula mawu otsatirawa ovomereza m’magazini a The Month: “Kufufuza kochitidwa ndi African Rights ku London kumasonyeza chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri za atsogoleri a Tchalitchi cha Katolika, Angilikani ndi Baptist amene aimbidwa mlandu wa kunyalanyaza kapena kuchirikiza mbanda za asilikali. . . . Palibiretu chikayikiro chakuti Akristu ambiri omveka okhala m’madera oyang’aniridwa ndi ansembe anachitako mbandazo.” Nzachisoni kuti kumenyana kwa otchedwa Akristu kukusakazabe chigawo chapakati pa Afirika.
Dama ndi Chigololo
Malinga ndi Mawu a Mulungu, pali malo amodzi okha olemekezeka amene kugonana kuyenera kuchitikiramo, ndipo amenewo ndiwo muukwati. “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse,” limatero Baibulo, “ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.” (Ahebri 13:4) Kodi atsogoleri a matchalitchi akuchirikiza chiphunzitso cha Mulungu chimenechi?
Mu 1989 Tchalitchi cha Angilikani ku Australia chinatulutsa chikalata chonena za kugonana chimene chinanena kuti kugonana ukwati usanakhale sikulakwa ngati aŵiriwo amvana. Posachedwapa, mtsogoleri wa Tchalitchi cha Angilikani ku Scotland anati: “Tchalitchi sichiyenera kukaniza kugonana kuti ndi tchimo ndi kuti kuli kosayenera. Tchalitchi chiyenera kuzindikira kuti chigololo chimachititsidwa ndi chibadwa chathu.”
Ku South Africa atsogoleri achipembedzo ambiri alankhula mwamphamvu kuchirikiza mathanyula. Mwachitsanzo, mu 1990 magazini a ku South Africa akuti You anagwira mawu mtumiki womveka wa Angilikani yemwe anati: “Malemba samagwira ntchito kosatha. . . . Ndikhulupirira kuti maganizo a tchalitchi ndi malamulo ake kulinga kwa anthu amathanyula adzasintha.”—Siyanitsani ndi Aroma 1:26, 27.
Malinga ndi 1994 Britannica Book of the Year, nkhani ya kugonana yakhala yaikulu m’matchalitchi a America, makamaka nkhani zonga “kuika amathanyula amuna ndi akazi kukhala atumiki, kumvetsa kwa chipembedzo zoyenera za amathanyula, kudalitsa ‘maukwati a amathanyula,’ ndi kulola kapena kukaniza moyo wa amathanyula.” Matchalitchi ambiri aakulu amalekerera atsogoleri achipembedzo amene amachita mkupiti wofuna ufulu wokulirapo wa kugonana. Malinga ndi 1995 Britannica Book of the Year, mabishopu 55 a Episkopo anasaina chikalata “chovomereza kuti kuika amathanyula kukhala atumiki kuli bwino limodzi ndi machitachita awo.”
Atsogoleri ena achipembedzo amachirikiza mathanyula, akumati Yesu sanaletse. Koma kodi ndi mmenedi zilili? Yesu Kristu anati Mawu a Mulungu ndi choonadi. (Yohane 17:17) Zimenezo zikutanthauza kuti iye anachirikiza lingaliro la Mulungu pa mathanyula lofotokozedwa pa Levitiko 18:22, pomwe pamati: “Usamagonana ndi mwamuna, monga amagonana ndi mkazi; chonyansa ichi.” Ndiponso, Yesu anatchula dama ndi chigololo pamodzi ndi “zoipa izi zonse [zimene] zituluka mkati, nizidetsa munthu.” (Marko 7:21-23) Liwu lachigiriki la dama limaphatikizapo zambiri kuposa lija la chigololo. Limanena za kugonana kwamtundu uliwonse kunja kwa ukwati walamulo, kuphatikizapo mathanyula. (Yuda 7) Yesu Kristu anachenjezanso otsatira ake kusalola mphunzitsi yemwe amati ndi Mkristu koma amaluluza kuwopsa kwa dama.—Chivumbulutso 1:1; 2:14, 20.
Pamene atsogoleri achipembedzo achita mkupiti wakuti amathanyula amuna ndi akazi aikidwe kukhala atumiki, kodi zimenezi zimawakhudza motani anthu a m’matchalitchi mwawo makamaka achichepere? Kodi sizimawasonkhezera kuchita kugonana kunja kwa ukwati? Mosiyana ndi zimenezo, Mawu a Mulungu amauza Akristu ‘kuthaŵa dama.’ (1 Akorinto 6:18) Ngati wokhulupirira wagwera m’tchimo lotero, amapatsidwa chithandizo chachikondi ndi cholinga chakuti munthuyo apezenso chiyanjo cha Mulungu. (Yakobo 5:16, 19, 20) Bwanji ngati akana chithandizo chotero? Baibulo limati ngati otero salapa, “sadzaloŵa ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:9, 10.
“Akuletsa Ukwati”
Chifukwa cha “[kuchuluka kwa, NW] madama,” Baibulo limati “nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.” (1 Akorinto 7:2, 9) Mosasamala kanthu za uphungu umenewu wanzeru, ambiri mwa atsogoleri achipembedzo amafunikira kukhala mbeta, ndiye kuti, osakwatira. “Lumbiro la umbeta silimasweka,” akutero Nino Lo Bello m’buku lake lakuti The Vatican Papers, “ngati wansembe, mmonke kapena mvirigo wagonana ndi wina. . . . Chikhululukiro pa kugonana chingapezeke mwa kulankhula moona mtima poulula, pamene kuli kwakuti ukwati wa wansembe aliyense Tchalitchi sichingauzindikire konse.” Kodi chiphunzitso chimenechi chabala zipatso zabwino kapena zoipa?—Mateyu 7:15-19.
Mosakayikira, ansembe ambiri ali ndi moyo wa makhalidwe oyera, koma ochuluka alibe. Malinga ndi 1992 Britannica Book of the Year, “zinamveka kuti Tchalitchi cha Roma Katolika chinalipira $300 miliyoni kuthetsa milandu ya atsogoleri achipembedzo ogona ena.” Pambuyo pake, kope lake la mu 1994 linati: “Imfa za atsogoleri achipembedzo ambiri chifukwa cha AIDS zinasonyeza poyera kuti panali ansembe amathanyula ndi umboni wakuti panali amathanyula . . . ochuluka olembedwa unsembe.” Nchifukwa chake Baibulo limati ‘kuletsa ukwati’ ndi ‘chiphunzitso cha ziŵanda.’ (1 Timoteo 4:1-3) “Malinga ndi olemba mbiri ena,” akulemba motero Peter de Rosa m’buku lake lakuti Vicars of Christ, “[umbeta wa ansembe] mwinamwake wawononga kwambiri makhalidwe Kumadzulo kuposa china chilichonse, ngakhale uhule. . . . [Uwo] kambiri wakhala chodetsa dzina la Chikristu. . . . Nthaŵi zonse umbeta wokakamiza wachititsa chinyengo pakati pa atsogoleri achipembedzo. . . . Wansembe akhoza kuchimwa nthaŵi chikwi koma lamulo la tchalitchi silimamlola kukwatira nkamodzi komwe.”
Polingalira mmene Mulungu anaonera kulambira Baala, nkwapafupi kuzindikira mmene akuonera matchalitchi ogaŵanika a Dziko Lachikristu. Buku lomaliza la Baibulo limaphatikiza pamodzi mitundu yonse ya kulambira konyenga mwa kuitcha dzina la “Babulo Wamkulu, amayi wa achigololo ndi wa zonyansitsa za dziko.” “Momwemo,” Baibulo limawonjezera, “munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.”—Chivumbulutso 17:5; 18:24.
Chifukwa chake, Mulungu akufulumiza onse amene afuna kukhala olambira ake oona kuti: “Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake. . . . Miliri yake idzadza m’tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo udzapserera ndi moto; chifukwa [Yehova, NW] Mulungu woweruza ndiye wolimba.”—Chivumbulutso 18:4, 8.
Tsopano pakubuka funso lakuti: Kodi munthu atatuluka m’chipembedzo chonyenga ayenera kupita kuti? Kodi ndi kulambira kwamtundu wotani kumene Mulungu amavomereza?
[Bokosi/Chithunzi patsamba 5]
Kupembedza Mafano
Kulambira Baala kunaphatikizapo kugwiritsira ntchito mafano. Aisrayeli anayesa kusanganiza kulambira kwa Yehova ndi kuja kwa Baala. Anabweretsa ndi mafano m’kachisi wa Yehova. Lingaliro la Mulungu pa mafano linasonyezedwa bwino pamene anadzetsa chiwonongeko pa Yerusalemu ndi kachisi wake.
Matchalitchi ambiri a Dziko Lachikristu ali odzala ndi mafano, akhale mtanda, zithunzi, kapena zifanizo za Mariya. Ndiponso, ambiri opita kutchalitchi amaphunzitsidwa kuŵerama, kugwada, kapena kupanga chizindikiro cha mtanda pamaso pa mafano ameneŵa. Mosiyana ndi zimenezo, Akristu oona amalamulidwa ‘kuthaŵa kupembedza mafano.’ (1 Akorinto 10:14) Samayesa kulambira Mulungu mothandizidwa ndi zinthu zooneka.—Yohane 4:24.
[Mawu a Chithunzi]
Musée du Louvre, Paris
[Bokosi patsamba 7]
“Mtsogoleri wa Tchalitchi Ayenera kukhala Wopanda Mlandu”
MAWU ameneŵa atengedwa pa Tito 1:7, malinga ndi Today’s English Version. King James Version imati: “Bishopu ayenera kukhala wopanda chilema.” Liwulo “bishopu” limachokera ku liwu lachigiriki lotanthauza “woyang’anira.” Chotero amuna amene amaikidwa kutsogolera mpingo woona wachikristu ayenera kukwaniritsa miyezo yaikulu ya Baibulo. Ngati satero, ayenera kuchotsedwa pamalo awo auyang’aniro pakuti sakhalanso “zitsanzo za gululo.” (1 Petro 5:2, 3) Kodi matchalitchi a Dziko Lachikristu amachiona mwamphamvu motani chofunika chimenechi?
M’buku lake lakuti I Care About Your Marriage, Dr. Everett Worthington akutchula kufufuza kumene kunachitidwa pa apasitala 100 m’boma la Virginia, U.S.A. Oposa 40 peresenti anavomereza kuti anachita khalidwe lina lake lodzutsa chilakolako cha kugonana ndi wina amene sanali mnzawo wa muukwati. Ambiri mwa iwo anachita chigololo.
“Pazaka khumi zapitazi,” ikutero Christianity Today, “tchalitchi chagwedezeka mobwerezabwereza ndi kuululika kwa khalidwe loipa limene ena a atsogoleri ake olemekezeka anachita.” Nkhani yakuti “Chifukwa Chake Apasitala Achigololo Sayenera Kubwezeretsedwa” inatsutsa chizoloŵezi cha Dziko Lachikristu cha kubwezeretsa msanga atsogoleri a tchalitchi pamalo awo oyamba pambuyo poti “apezeka ndi tchimo lachigololo.”