Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 11/15 tsamba 19-23
  • “Woyang’anira Ayenera Kukhala . . . Wodziletsa”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Woyang’anira Ayenera Kukhala . . . Wodziletsa”
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kudziletsa​—Chiyeneretso cha Akulu
  • Pochita ndi Ena
  • Kudziletsa Pamisonkhano ya Akulu ndi Milandu Yachiweruzo
  • Kudziletsa ndi Osiyana Nawo Chiŵalo
  • Kudziletsa m’Mbali Zina
  • Kukulitsa Chipatso cha Kudziletsa
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kudziletsa—Kodi Nchifukwa Ninji Kuli Kofunika Motero?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Khalani Wodziletsa Kuti Mudzalandire Mphoto!
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Wonjezerani Kudziletsa pa Chizindikiritso Chanu
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 11/15 tsamba 19-23

“Woyang’anira Ayenera Kukhala . . . Wodziletsa”

“Woyang’anira ayenera kukhala . . . wodziletsa.”​—TITO 1:7, 8.

1, 2. Kodi nchitsanzo chakudziletsa chotani chimene William wa ku Orange anapereka, ndipo ndi zotulukapo zopindulitsa zotani?

MBIRI yakale imapereka chitsanzo chabwino koposa chokhudza kuletsa maganizo. Chapakati pa zaka za zana la 16, William wa ku Orange, kalonga wachichepere wochokera ku Netherlands anali paulendo wosaka ndi Mfumu Henry II wa ku Falansa. Mfumuyo inaululira William pulani imene iye ndi mfumu ya ku Spanya anapanga yakupululutsa Aprotesitanti onse m’Falansa ndi mu Netherlands​—kwenikwenidi, m’Chikristu Chadziko chonse. Mfumu Henry analingalira kuti William wachichepereyo anali Mkatolika wodzipereka monga iyemwini ndipo chotero anafotokoza tsatanetsatane yense wa chiwembucho. Zimene William anamva zinamchititsa mantha kwambiri chifukwa chakuti mabwenzi ake ambiri apamtima anali Aprotesitanti, koma sanasonyeze mmene anamverera; m’malomwake, anasonyeza chikondwerero chachikulu m’tsatanetsatane yense amene mfumuyo inampatsa.

2 Komabe, mwamsanga pamene William anali wokhoza kutero, anayambitsa mapulani amene akalepheretsa chiwembucho, ndipo ichi chinatsogolera ku kuwonjoledwa kotheratu kwa Netherlands kuchoka muulamuliro Wachikatolika wa Spanya. Chifukwa chakuti William anali wokhoza kusonyeza kudziletsa pamene anamva kwanthaŵi yoyamba za chiwembucho, iye anadzadziŵika monga “William Wachete.” William wa ku Orange anali wachipambano kwenikweni kwakuti tikuuzidwa kuti: “Iye anali woyambitsa weniweni wa ufulu ndi ukulu wa lipabuliki la Netherlands.”

3. Kodi ndani amene amapindula pamene akulu Achikristu asonyeza kudziletsa?

3 Chifukwa cha kudziletsa kwake, William Wachete anapindulitsa kwakukulu ponse paŵiri iyemwini ndi anthu ake. M’njira yofananayo, chipatso cha mzimu woyera cha kudziletsa chiyenera kusonyezedwa lerolino ndi akulu Achikristu, kapena oyang’anira. (Agalatiya 5:22, 23) Mwakusonyeza mkhalidwe umenewu, iwo amapindulitsa ponse paŵiri iwo eni ndi mipingo. Kumbali ina, kulephera kwawo kusonyeza kudziletsa kungavulaze kotheratu.

Kudziletsa​—Chiyeneretso cha Akulu

4. Kodi ndiuphungu uti wa mtumwi Paulo umene umagogomezera kufunika kwa akulu kusonyeza kudziletsa?

4 Paulo, yemwe analinso mkulu, anazindikira kufunika kwa kudziletsa. Pamene analangiza akulu omwe anadza kwa iye kuchokera ku Efeso, anawauza kuti: “Mudzipenyerere nokha ndi gulu lonse.” Pakati pa zinthu zina, kudzipenyerera okha kunaphatikizapo kufunika kwa kusonyeza kudziletsa, kuyang’anira khalidwe lawo. Pomulembera Timoteo, Paulo anapanga mfundo imodzimodziyo, akumati: ‘Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho.’ Uphungu woterowo unasonyeza kuzindikira kwa Paulo chikhoterero chachibadwa cha anthu ena chakukhala odera nkhaŵa ndi kuuza ena mmalo mochita zinthuzo iwo eni. Chotero, iye anagogomezera poyamba kufunika kwakudziyang’anira okha.​—Machitidwe 20:28, NW; 1 Timoteo 4:16.

5. Kodi akulu Achikristu amaikidwa motani, ndipo kodi ziyeneretso zawo zinalembedwa pati m’Malemba?

5 M’zaka zonsezi, mbali Yamalemba ya akulu yakhala ikumvekera bwino pang’onopang’ono. Lerolino, tikuwona kuti ukulu ndiudindo woikidwa. Akulu amaikidwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova kapena oimira ake achindunji. Bungwe limenelo, nalonso, limaimira “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Ziyeneretso zokhalira woyang’anira Wachikristu, kapena mkulu, zaperekedwa choyamba ndi mtumwi Paulo pa 1 Timoteo 3:1-7 ndi Tito 1:5-9.

6, 7. Kodi nziyineretso zachindunji ziti za akulu zimene zimafunikira kudziletsa?

6 Paulo akufotokoza pa 1 Timoteo 3:2, 3 kuti woyang’anira ayenera kukhala wodekha m’zizoloŵezi. Ichi ndi kufunika kwa mkulu kukhala wolongosoka kumafunikira kusonyeza kudziletsa. Munthu woyenerera kukhala woyang’anira sayenera kukhala wandewu ndipo samakhala wokangana. Ziyeneretso zimenezi zimafunikiranso kuti mkulu akhale wodziletsa. Ndiponso, kuti mkulu asakhale woledzera, womwetsa vinyo, ayenera kusonyeza kudziletsa.​—Onaninso mawu am’tsinde a 1 Timoteo 3:2, 3, NW.

7 Pa Tito 1:7, 8, Paulo analongosola mwachindunji kuti woyang’anira ayenera kukhala wodziletsa. Komabe, onani kuti ndi zingati za ziyeneretso zina zimene zandandalitsidwa m’mavesi ameneŵa zimene zimaphatikizapo kudziletsa. Mwachitsanzo, woyang’anira ayenera kukhala wopanda chinenezo, inde, wopanda chifukwa. Ndithudi, mkulu sangafikiritse ziyeneretso zimenezo pokhapo ngati asonyeza kudziletsa.

Pochita ndi Ena

8. Kodi ndimikhalidwe iti yofunikira kwa akulu popereka uphungu imene imasonyeza kufunika kwa kudziletsa?

8 Ndiyenonso, woyang’anira ayenera kukhala woleza mtima ndi wopirira pochita ndi okhulupirira anzake, ndipo ichi chimafunikira kudziletsa. Mwachitsanzo, pa Agalatiya 6:1, timaŵerenga kuti: ‘Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu [makamaka akulu], mubweze wotereyo mumzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.’ Kusonyeza mzimu wachifatso kumafunikira kudziletsa. M’nkhani yoteroyo, kudziletsa kumaphatikizaponso kudzipenyerera wekha. Mofananamo, pamene mkulu waitanidwa ndi munthu wopsinjika kudzathandiza, kudziletsa kumakhala kofunika kwambiri. Mosasamala kanthu za zimene mkuluyo angaganizire za munthuyo, iye ayenera kukhala wokoma mtima, woleza mtima, ndi womvetsetsa. M’malo mofulumira kupereka uphungu, mkuluyo ayenera kukhala wofunitsitsa kumvetsera ndi kulola munthuyo kutulutsa zakukhosi kuwonetsetsa zomwe zikuwonekera kumvuta.

9. Kodi akulu ayenera kukhala ndi uphungu uti m’malingaliro pamene akuchita ndi abale ovutitsidwa maganizo?

9 Makamaka pochita ndi anthu ovutitsidwa maganizo ndipamene uphungu uwu wa pa Yakobo 1:19 umakhala woyenerera: ‘Mudziŵa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.’ Inde, makamaka pamene akuyang’anizana ndi mayankho okwiya kapena aukali mpamene mkulu ayenera kukhala wosamala kusayankha mofananamo. Kumatenga kudziletsa kusayankha mawu aukali ndi mawu aukali, ‘kusabwezera choipa chosinthana ndi choipa.’ (Aroma 12:17) Kuyankha m’mkhalidwe wofananawo kumangoipitsa nkhaniyo. Chotero panonso Mawu a Mulungu amapereka uphungu wabwino kwa akulu, kuwakumbutsa kuti “mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo.”​—Miyambo 15:1.

Kudziletsa Pamisonkhano ya Akulu ndi Milandu Yachiweruzo

10, 11. Kodi nchiyani chimene chinachitikapo pamisonkhano ya akulu, kusonyeza kufunika kwa kudziletsa pazochitika zoterozo?

10 Mbali ina imene oyang’anira Achikristu amafunikira kukhala osamala kusonyeza kudziletsa ndiyo pamisonkhano ya akulu. Kulankhula mwabata chifukwa cha chowonadi ndi chilungamo nthaŵi zina kumafunikira kudziletsa kwakukulu. Kumafunikiranso kudziletsa kupeŵa kuyesayesa kulamulira kukambitsirana. Pamene mkulu ali ndi chikhoterero choterocho, kukakhala kukoma mtima ngati mkulu wina ampatsa uphungu.​—Yerekezerani ndi 3 Yohane 9.

11 Ndiyenonso, pamisonkhano ya akulu, mkulu wowona mtima mopambanitsa angatengeke maganizo, ngakhale kulankhula mokweza mawu. Ha, kachitidwe koteroko kamasonyeza motani nanga kusoŵeka kwa kudziletsa! Iwo mosakaikira ali kudzigonjetsa. Kumbali ina, kuukulu umene munthu amataya kudziletsa kwake, kuukulu umenewo amafooketsa nkhani yake mwakulola malingaliro kuphimba kulingalira kwanzeru. Kumbali ina, kuukulu umene munthu amasonkhezeredwa mwamalingaliro, amakwiyitsa kapena kuyambanitsa akulu anzake. Ndiponso, pokhapo ngati akulu ali osamala, kusiyana kwakukulu kwa malingaliro kungapangitse magawano pakati pawo. Ichi chimavulaza iwo limodzi ndi mpingo.​—Yerekezerani ndi Machitidwe 15:36-40.

12. Kodi akulu ayenera kukhala osamala kusonyeza kudziletsa pochita ndi mikhalidwe yotani?

12 Kudziletsa kumafunikiranso kwambiri kwa akulu kuti apeŵe kukhala atsankho kapena kugwiritsira ntchito moipa ulamuliro wawo. Kuli kokhweka kugonjera ku chiyeso, kulola zolingalira zopanda ungwiro zaumunthu kuyambukira zimene munthu amanena kapena kuchita! Kaŵirikaŵiri, akulu alephera kuchita molunjika pamene mmodzi wa ana awo kapena wachibale wina anapezedwa ndi liŵongo lakuchita choipa. M’zochitika zoterozo kumafunikira kudziletsa kuti asalole maunansi akuthupi kutsekereza kachitidwe kolungama.​—Deuteronomo 10:17.

13. Kodi nchifukwa ninji kudziletsa kuli kofunika kwa akulu makamaka pamilandu yachiweruzo?

13 Mkhalidwe wina umene kudziletsa kuli kofunika koposa ndiwo pamene pali mlandu wachiweruzo. Akulu ayenera kusonyeza kudziletsa kwakukulu kotero kuti sakusonkhezeredwa mosayenerera ndi malingaliro. Iwo sayenera kupatutsidwa mopepuka ndi misozi. Panthaŵi imodzimodziyo, mkulu ayenera kukhala wosamala kusataya mtima pamene kukangana kubuka ndipo anganyozedwe, monga mmene zingakhalire pochita ndi ampatuko. Panopa mawu a Paulo ali oyenerera kwambiri: ‘Kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndewu, komatu akhale [wodekha, NW] pa onse.’ Kumafunikira kudziletsa kuti mukhale wodekha pansi pa chitsenderezo. Paulo akupitiriza kusonyeza kuti “kapolo wa Ambuye” ayenera kukhala ‘wodziŵa kuphunzitsa, woleza, wolangiza iwo akutsutsana mofatsa.’ Kusonyeza kufatsa ndikudziletsa pamene mukuchita ndi chitsutso kumafunikira kudziletsa kwakukulu.​—2 Timoteo 2:24, 25.

Kudziletsa ndi Osiyana Nawo Chiŵalo

14. Kodi ndiuphungu wabwino uti umene akulu ayenera kulabadira m’zochita zawo ndi osiyana nawo chiŵalo?

14 Akulu ayenera kukhala amaso kwenikweni kusonyeza kudziletsa pamene achita ndi osiyana nawo chiŵalo. Sikuli koyenera kuti mkulu apange ulendo waubusa kwa mlongo ali yekha. Mkuluyo ayenera kutsagana ndi mkulu wina kapena mtumiki wotumikira. Mwachidziŵikire akumazindikira vutoli, Paulo analangiza mkulu Timoteo kuti: ‘Udandaulire . . . akazi aakulu ngati amayi; akazi aang’ono ngati alongo, m’kuyera mtima konse.’ (1 Timoteo 5:1, 2) Akulu ena awonedwa kuti amaika manja awo pa mlongo molingana ndi kagwiridwe ka tate. Koma angakhale akudzinyenga okha, popeza kuti kagwiridwe koteroko kangasonkhezeredwe ndi mphamvu ya kukondana m’malo mwa chikondi chaubale Chachikristu chenicheni.​—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 7:1.

15. Kodi ndimotani mmene chochitika china chimagogomezera chitonzo chimene chingakhale padzina la Yehova pamene mkulu sasonyeza kudziletsa?

15 Pakhala chivulazo chachikulu chotani nanga chifukwa chakuti akulu ena sanasonyeze kudziletsa m’zochita zawo ndi alongo mumpingo! Zaka zingapo zapitazo, mkulu anachotsedwa chifukwa chakuti anachita chigololo ndi mlongo Wachikristu yemwe mwamuna wake sanali Mboni. Pausiku wakulengezedwa kwa kuchotsedwa kwa yemwe kale anali mkuluyo, mwamuna wokwiyitsidwayo analoŵa m’Nyumba Yaufumu ali ndi mfuti nawombera pa anthu aŵiri aliŵongowo. Palibe aliyense wa iwo amene anaphedwa, ndipo analandidwa mfutiyo panthaŵi yomweyo, koma tsiku lotsatira nyuzipepala yaikulu inawonetsa patsamba lake loyamba nkhani ya ‘kuwomberana patchalitchi.’ Ha, kusadziletsa kwa mkulu ameneyo kunabweretsa chitonzo chotani nanga pa mpingo ndi padzina la Yehova!

Kudziletsa m’Mbali Zina

16. Kodi nchifukwa ninji akulu ayenera kukhala osamala kusonyeza kudziletsa pamene akupereka nkhani zapoyera?

16 Kudziletsa kumafunikiranso pamene mkulu apereka nkhani yapoyera. Mlankhuli wapoyera ayenera kukhala chitsanzo cha chidaliro ndi kulinganizika. Ena amayesayesa kusangalatsa amvetseri awo ndi ndemanga zongofuna kuwaseketsa. Uku ndikugonjera ku chiyeso cha kukondweretsa omvetsera. Ndithudi, kugonjera chiyeso kulikonse kuli kusoŵeka kwa kudziletsa. Kunganenedwe kuti kudya nthaŵi popereka nkhani kumasonyezanso kusoŵeka kwa kudziletsa, limodzinso ndi kusakonzekera bwino.

17, 18. Kodi kudziletsa kumachita mbali yanji m’kulinganiza mathayo osiyanasiyana a mkulu?

17 Mkulu aliyense wogwira ntchito zolimba ayenera kuchifikira chitokoso chakulinganiza zinthu zambiri zofunikira pa nthaŵi ndi nyonga yake. Kumafunikira kudziletsa kuti asapite kumlingo wopambanitsa uliwonse. Akulu ena amakhala odera nkhaŵa mopambanitsa ndi zosoŵa za mpingo kwakuti amanyalanyaza mabanja awo. Mwachitsanzo, pamene mlongo wina anauza mkazi wa mkulu ponena za ulendo waubusa wabwino umene anapanga, mkazi wa mkuluyo anafuula kuti: “Ndikulakalaka kuti akanapanga ulendo waubusa kwa ine nthaŵi ina!”​—1 Timoteo 3:2, 4, 5.

18 Mkulu amafunikiranso kudziletsa kotero kuti alinganize nthaŵi imene amathera pa phunziro laumwini ndi nthaŵi imene amathera muuminisitala wakumunda kapena pamaulendo aubusa. Polingalira za kunyenga kwa mtima wa munthu, kuli kokhweka kwambiri kwa mkulu kuthera nthaŵi yochuluka koposa kuposa mmene ayenera pa zinthu zimene zimamsangalatsa kwambiri. Ngati iye amakonda mabuku, angamathere nthaŵi yochuluka paphunziro laumwini kuposa mmene ayenera kuchitira. Ngati amapeza uminisitala wakunyumba ndi nyumba kukhala wovuta, angapeze chodzikhululukira chounyalanyazira mwakupanga maulendo aubusa.

19. Kodi akulu ali ndithayo lanji limene limagogomezera kufunika kwa kudziletsa?

19 Thayo lakusunga chinsinsi limafunikiranso kuti mkulu akhale wamaso kusonyeza kudziletsa kolimba. Woyenerera panopa uli uphungu uwu: “Osaulula zinsinsi za mwini.” (Miyambo 25:9) Zokumana nazo zimapereka lingaliro lakuti ichi nchimodzi cha ziyeneretso zolakwiridwa kwambiri pakati pa akulu. Ngati mkulu ali ndi mkazi wanzeru ndi wachikondi amene amalankhulana naye bwino, pangakhale chikhoterero cha kukambitsirana kapena kungotchula nkhani zachinsinsi. Komatu izi siziri zoyenera ndiponso kuli kupanda nzeru kwakukulu. Choyamba, kumasonyeza kusoŵeka kwa chidaliro. Abale ndi alongo auzimu amafika kwa akulu ndikuwaululira zinthu chifukwa cha chidaliro chimene alinacho kuti nkhanizo zidzakhala zachinsinsi. Kuuza mkazi wanu nkhani zachinsinsi kuli kulakwa, kupanda nzeru, ndiponso kuli kupanda chikondi chifukwa kumaika mtolo wosayenerera pa iye.​—Miyambo 10:19; 11:13.

20. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwa akulu kusonyeza kudziletsa?

20 Mosakaikira, kudziletsa kuli kofunika koposa, ndipo makamaka kwa akulu! Chifukwa choikiziridwa thayo lakutsogolera pakati pa anthu a Yehova, iwo ali oŵerengeredwa mokulira. Popeza kuti zambiri zaperekedwa kwa iwo, zambiri zidzafunidwa kwa iwo. (Luka 12:48; 16:10; yerekezerani ndi Yakobo 3:1.) Uli mwaŵi ndi thayo la akulu kukhazikitsa chitsanzo chabwino kwa ena. Kuposa zimenezo, akulu oikidwa ali ndiudindo wakuchita zabwino zambiri kapena chivulazo chachikulu kwa ena, kaŵirikaŵiri zikumadalira pakuti kaya iwo amasonyeza kudziletsa kapena ayi. Nkosadabwitsa kuti Paulo anati: “Woyang’anira ayenera kukhala . . . wodziletsa.”

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi nziyeneretso Zamalemba za akulu zotani zimene zimasonyeza kuti ayenera kusonyeza kudziletsa?

◻ Kodi nchifukwa ninji kudziletsa kumafunikira kwa akulu pamene akuchita ndi okhulupirira anzawo?

◻ Kodi ndimotani mmene kudziletsa kuyenera kusonyezedwera pamisonkhano ya akulu?

◻ Kodi nchitokoso chotani chimene chimaperekedwa ndi kufunika kwa kusunga chinsinsi kwa akulu?

[Chithunzi patsamba 20]

Kusonyeza kudziletsa kuli kofunika pamisonkhano ya akulu

[Chithunzi patsamba 23]

Akulu Achikristu ayenera kusonyeza kudziletsa ndi kusunga chinsinsi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena