Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Mwalowa mu Mpumulo wa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2011 | July 15
    • “Mawu a Mulungu Ndi Amoyo”

      20. Kodi tingamve lemba la Aheberi 4:12 m’njira ziwiri ziti? (Onani mawu a m’munsi.)

      20 Pamene Paulo ankalemba kuti “mawu a Mulungu ndi amoyo,” kwenikweni sanali kunena za Baibulo, lomwe ndi Mawu ouziridwa a Mulungu.c Mavesi ena m’chaputalachi amasonyeza kuti ankanena za malonjezo a Mulungu. Paulo ankatanthauza kuti Mulungu saiwala lonjezo lake. Yehova ananena zimenezi kudzera mwa mneneri Yesaya pamene anati: “Mawu otuluka pakamwa panga . . . sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake, koma . . . adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.” (Yes. 55:11) Choncho tiyenera kukhala oleza mtima ngati tikuona kuti Mulungu sakukwaniritsa malonjezo ake pa nthawi imene ifeyo timafuna. Yehova “akugwirabe ntchito” kuti akwaniritse bwinobwino cholinga chake.​—Yoh. 5:17.

      21. Kodi lemba la Aheberi 4:12 lingalimbikitse bwanji Akhristu achikulire okhulupirika a “khamu lalikulu”?

      21 Akhristu achikulire a “khamu lalikulu” amene ndi okhulupirika atumikira Yehova kwa zaka zambiri. (Chiv. 7:9) Ambiri sankaganiza kuti adzakalamba dziko loipali lilipobe. Ngakhale zili choncho, iwo akuyesetsabe kutumikira Yehova. (Sal. 92:14) Iwo amadziwa kuti mawu a Mulungu ndi amoyo ndipo malonjezo a Yehova adzakwaniritsidwa. Mulungu amaona kuti cholinga chake n’chofunika kwambiri choncho amasangalala akamaona kuti ifenso timaona kuti cholinga chakechi n’chofunika. Palibe chimene chingalepheretse Yehova kukwaniritsa cholinga chake pa tsiku lake la 7 lomwe ndi la mpumulo. Iye amadziwanso kuti, monga gulu, anthu ake azichita zinthu mogwirizana ndi cholinga chakechi. Kodi inuyo mwalowa mu mpumulo wa Mulungu?

  • Kodi Mwalowa mu Mpumulo wa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2011 | July 15
    • c Masiku ano, Mulungu amatilankhula kudzera m’Mawu ake Baibulo, lomwe lili ndi mphamvu zotithandiza kusintha moyo wathu. Choncho tingati mawu a Paulo a pa Aheberi 4:12 amanenanso za Baibulo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena