Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 5/1 tsamba 7
  • Chowonadi cha Baibulo “Chimapereka Mphamvu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chowonadi cha Baibulo “Chimapereka Mphamvu”
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchitira Umboni Kubala Zipatso Panyumba ndi Kusukulu
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Mphamvu ya Kusintha ya Mawu a Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1996
  • ‘Mawu a Mulungu Ndi Amphamvu’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Nsanja ya Olonda—1988
w88 5/1 tsamba 7

Ripoti la Olengeza Ufumu

Chowonadi cha Baibulo “Chimapereka Mphamvu”

DZIKO lino limawononga nthaŵi yochulukira ndi ndalama kuyesera kulamulira zochita za anthu oipa. Malamulo akuperekedwa molimbana ndi upandu wonga ngati kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka, kuba, ndi kupha koma malamulo amenewa sakupanga anthu oipa kukhala abwino. Kumbali ina, Mawu a Mulungu, Baibulo, ali ndi mphamvu yosintha, ndipo anthu omwe amagwiritsira ntchito malamulowo ndi maprinsipulo amakhala owongoka, owona mtima, ndi anthu oleza mtima.​—Aroma 12:2.

◻ Mwachitsanzo, Mboni ziŵiri mu Australia zinapanga ulendo wobwereza kwa achichepere osiyanasiyana, amuna osalembedwa ntchito. Pamene zinalowa m’nyumba imene amunawo anali, iwo anafika m’chipinda cha mdima, chodzala ndi utsi. Munali zidutswa za chamba pa tebulo ndi zokoloweka zazikulu zoika m’makoma. Kumbali kwa chipindacho kunali chokuzira mawu chachikulu cha gitala ya magetsi. Icho chinali chipinda chosoŵerera cha gulu la oimba nyimbo za rock. Iwo anali okhoza kuyamba phunziro la Baibulo ndi atatu a amunawo omwe anali pachibale mwa kuthupi. Zaka zingapo poyambirira amayi awo ankaphunzira Baibulo ndi Mboni, ndipo ndi thandizo la bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, iwo anaphunzitsa anyamatawo ponena za lonjezo la Mulungu la paradaiso ya mtsogolo. Kenaka banjalo linasamuka, ndipo phunzirolo linalekedwa. Tsopano, ndi chikondi chawo kaamba ka chowonadi chitakhalitsidwanso chatsopano, iwo mwamsanga anagwirizana m’phunziro lawo ndi mabwenzi aŵiri.

Mkati mwa miyezi itatu, mmodzi wa iwo ankachitira umboni, ndipo mwezi umodzi pambuyo pake anagwirizana ndi ena aŵiriwo. Iwo analeka gululo, ndipo mkati mwa miyezi inayi, atatu onsewo ankatengamo phande m’ntchito ya kulengeza. Panthaŵiyo, amayi awo, mbale wawo wachichepere, ndi mlongo wawo wachikulire wokwatiwa anayamba kuphunzira Baibulo. Mwamsanga pambuyo pake bwenzi lina linafunsa kaamba ka phunziro la Baibulo. Chinali chisangalalo chotani nanga kuwona asanu onsewo akubatizidwa pa tsiku limodzi pa msonkhano wadera! Aŵiri enawo akugwirira ntchito kulinga ku ubatizo, pamene kuli kwakuti amayi ndi mwana wamkazi akupitirizabe kupanga kupita patsogolo kwabwino. Ndithudi, Mawu a Mulungu amapereka mphamvu.

◻ Mwamuna wina mu Argentina anali ndi wolembedwa ntchito yemwe anali waulesi ndi wabodza ndipo anali ndi ngongole zambiri kwa iye. Tsiku lina wogwira ntchitoyo anasowa. Kenaka, zaka zingapo pambuyo pake, m’khwalala pafupi ndi nyumba yake mwamunayo anakumana ndi wolembedwa ntchito wake wakaleyo. Wolembedwa ntchito wakaleyo anampatsa moni iye, akumanena kuti: “Ndinali kupita kunyumba kwanu kukalipira ndalama zomwe ndiri nazo m’ngongole kwa inu. Si izi ndalama zanu. Zikomo kwambiri, ndipo chonde ndikhululukireni pa kusazibwezera izo mwamsanga.” Atadabwitsidwa, mwamunayo anamfunsa iye chifukwa chimene anachitira chimenechi. Iye anayankha kuti: “Ndikuphunzira Baibulo tsopano, ndipo ndiri mmodzi wa Mboni za Yehova. Baibulo limanena kuti sitifunikira kukhala ndi ngongole iriyonse kuposa chikondi. Chimenecho ndicho chifukwa chake ndabwezera zimene ziri zanu.” Mwamunayo anafunsa kuti: “Kodi ndi mphamvu yotani imene Baibulo iri nayo kuti itulutse masinthidwe oterowo mwa munthu?” Phunziro la Baibulo linayambidwa ndi iye, ndipo tsopano iye nayenso akuphunzira chowonadi, zonsezo chifukwa cha kusintha kokulira kumene chowonadi cha Baibulo chinapanga mu Wolembedwa ntchito wake woyambirira.

Anthu owona mtima ambiri mu Argentina akulandira chowonadi chosintha maganizo cha Baibulo ndi kusintha njira yawo ya moyo, monga mmene chokumana nacho chotsatira chikusonyezera.

◻ “Tsiku lina pamene tinagogoda pa chitseko pamene tinali mu utumiki,” inasimba tero Mboni ina, “tinamva kufuula kukumadza kuchokera mkati mwa nyumba. M’kuyankha ku kugogoda kwathu, mwamuna wina anatuluka​—alidi wokwiya, kwenikweni. Tinayamba kulongosola chifuno cha kuchezera kwathu, koma iye anawopsyeza kutithamangitsa pamalo ake. Tinapitirizabe kulankhula mofatsa ndi moleza mtima. Pang’ono ndi pang’ono iye anasintha. Tikumadziŵa chimenechi, tinalongosola kwa iye zochulukira ponena za zifuno zodabwitsa za Yehova kaamba ka mtundu wa anthu. Atakondweretsedwa ndi ichi, mwamunayo anatidabwitsa ife mwakunena kuti: ‘Mulungu wakutumizani inu pano.’ Iye kenaka anatiitana ife kulowa m’nyumba. Mmenemo, wodzipanikiza pa ngodya, anali ‘mkazi’ wake ndi ana, akumalira. Kenaka iye anaululula kuti: ‘Pamene munadza, ndinali pafupi kupha banja langa ndi inemwini. Ndiri wodera nkhaŵa! Ndinataya ntchito yanga, ndipo tsopano adzatipitikitsa ife m’nyumba muno, ndipo ndiri ndi ngongole zambiri zofunikira kulipira.’”

Chokumana nacho chimenechi chinali ndi mapeto achimwemwe. Mlongo wina anapeza ntchito kaamba ka mwamunayo, ndipo anapezanso nyumba ina. Iye ndi “mkazi” wake anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anakwatirana pambuyo pa kukhala pamodzi kwa zaka 15.

Chowonadi cha Baibulo “chimapereka mphamvu” monga mmene zokumana nazo zimenezi zasonyezera, ndipo chingachite chimenecho kaamba ka aliyense yemwe ali ndi mtima wofatsa yemwe adzaphunzira ndi kuligwiritsira ntchito.

[Mawu Otsindika patsamba 7]

“Mawu a Mulungu ngamoyo ndipo amapereka mphamvu.”​—AHEBRI 4:12

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena