Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 6/1 tsamba 30-31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Yesu Kristu Angatithandizire
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Tiziyamikira Kukoma Mtima Kwakukulu kwa Mulungu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Tinamasulidwa ku Uchimo Chifukwa cha Kukoma Mtima Kwakukulu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Tizilalikira Uthenga wa Kukoma Mtima Kwakukulu kwa Mulungu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 6/1 tsamba 30-31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi ndimotani mmene mapindu a mautumiki a Kristu Yesu monga mkulu wa ansembe, otchulidwa pa Ahebri 4:15, 16, amagwirira ntchito kwa “nkhosa zina” tsopano lino?

Ngakhale kuti ntchito ya Yesu monga Mkulu wa Ansembe ili yofunika kwambiri kwa aja amene adzakhala naye kumwamba, Akristu amene ali ndi ziyembekezo za pa dziko lapansi amapindula ngakhale tsopano ndi mautumiki aunsembe a Yesu.

Kuyambira pa Adamu, anthu anyamula chimtolo cha uchimo. Tili ndi kupanda ungwiro kwacholoŵa, monga momwe analili Aisrayeli. Iwo anayang’ana kwa akulu a ansembe ndi ansembe anzawo otsatizanatsatizana, amene anapereka nsembe za machimo a iwo eni ndiponso a anthu. M’kupita kwa nthaŵi, Yesu anadzozedwa kukhala wansembe “monga mwa chilongosoko cha Melikizedeke.” Ataukitsidwa, Yesu anakaonekera pamaso pa Yehova kukapereka mtengo wa nsembe yake yangwiro yaumunthu.​—Salmo 110:1, 4.

Kodi zimenezi zimatanthauzanji kwa ife lerolino? M’kalata yake kwa Ahebri, Paulo anafotokoza utumiki wa Yesu monga Mkulu wa Ansembe. Pa Ahebri 5:1, timaŵerenga kuti: “Mkulu wa ansembe aliyense, wotengedwa mwa anthu, amaikika chifukwa cha anthu m’zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mitulo, ndiponso nsembe, chifukwa cha machimo.” Ndiyeno, m’vesi 5 ndi 6, Paulo anasonyeza kuti Yesu anakhala mkulu wa ansembe, chinthu chimene chingatipindulitse.

Motani? Paulo analemba kuti: “Angakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuŵaŵa nazo; ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera iye chifukwa cha chipulumutso chosatha.” (Ahebri 5:8 9) Poyamba, vesi limenelo lingatiganizitse za mmene tidzakhoza kupindulira m’dziko latsopano, pamene aja okhulupirika kwa Mulungu ndi Yesu adzachotseredwa mkhalidwe wawo wauchimo ndi kulandira moyo wosatha. Chimenecho ndi chiyembekezo chotsimikizirika, chozikidwa pa mtengo woombola wa nsembe ya Yesu ndi utumiki wake monga Mkulu wa Ansembe.

Koma kwenikweni, tingapindulenso ngakhale panthaŵi ino ndi ntchito yake kapena utumiki wake monga Mkulu wa Ansembe. Mvetserani zimene Ahebri 4:15, 16 amanena: “Sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo. Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthaŵi yakusoŵa.” Kodi “nthaŵi yakusoŵa” imeneyo ndi liti? Ndi pamene tifunikira chifundo ndi chisomo. Tonsefe tiyenera kufuna zimenezi tsopano chifukwa ndife opanda ungwiro.

Ahebri 4:15, 16 akutchula mfundo yakuti Yesu​—yemwe tsopano ndi wansembe kumwamba​—anakhalapo munthu, chotero angakhale wachifundo. Kwa yani? Kwa ife. Liti? Tsopano. Pamene anali munthu, Yesu anakumana ndi zovuta zozoloŵereka kwa anthu. Panthaŵi ina, Yesu anamva njala ndi ludzu. Ndipo ngakhale kuti anali wangwiro, iye anatopa. Zimenezo ziyenera kutitonthoza. Chifukwa? Chifukwa pokhala kuti Yesu anakhala ndi kutopa kwachibadwa, iye amamvetsetsa mmene timamvera kaŵirikaŵiri. Kumbukiraninso kuti Yesu analimbana ndi kukangana kwa nsanje pakati pa atumwi ake. (Marko 9:33-37; Luka 22:24) Inde, anagwiritsidwa mwala. Kodi zimenezo siziyenera kutipatsa chidaliro chakuti amamvetsetsa pamene tagwiritsidwa mwala ndi kukhumudwa? Ziyeneradi kutero.

Pamene mwakhumudwa, kodi mungachite chiyani? Kodi Paulo ananena kuti mungofunikira kudikira kufikira Mkulu wa Ansembe wanu, Yesu, atakuthandizani kukhala wangwiro m’maganizo ndi thupi m’dziko latsopano? Ayi. Paulo anati: “Tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthaŵi yakusoŵa,” ndipo zimenezo zimaphatikizapo nthaŵi ino. Ndiponso, pamene Yesu anali munthu, anazunzika nakumana ndi zovuta, ‘akumayesedwa m’zonse monga ife.’ Chotero pamene tikumana ndi zinthu zotero, iye ali wokonzekera kutithandiza podziŵa zimene zikutichitikira. Kodi zimenezo sizimakukokerani kwa iye?

Tsopano taonani vesi 16. Paulo akuti ife​—ndipotu zimenezi zikuphatikizapo odzozedwa ndi a nkhosa zina​—tingafike kwa Mulungu ndi ufulu wa kulankhula. (Yohane 10:16) Mtumwiyo sanatanthauze kuti tingatchule zilizonse zimene tifuna m’pemphero, ngakhale zokwiyitsa ndi zosafunika. M’malo mwake, anatanthauza kuti tingamfikire Mulungu ngakhale kuti ndife ochimwa, chifukwa cha nsembe ya Yesu ndi ntchito yake monga Mkulu wa Ansembe,.

Njira ina imene ngakhale tsopano tingapindulire ndi mautumiki a Mkulu wathu wa Ansembe, Yesu Kristu, imakhudza machimo athu, kapena zolakwa. Ndithudi, sitiganiza kuti m’dongosolo lilipoli Yesu adzagwiritsira ntchito pa ife mtengo wonse wa nsembe yake. Ngakhale ngati akanatero, sitikanapezabe moyo wosatha. Kodi mukukumbukira nkhani ya pa Luka 5:18-26, yonena za munthu wamanjenje amene kama wake anatsitsidwira pa tsindwi? Yesu anamuuza kuti: “Munthu iwe, machimo ako akhululukidwa.” Zimenezi sizinatanthauze machimo ena akutiakuti amene anachititsa manjenjewo. Ayenera anatanthauza machimo wamba a munthuyo, ndipo ku mlingo winawake anaphatikizapo kupanda ungwiro kwake kwa choloŵa, kumene kumachititsa matenda.

Chifukwa cha nsembe imene anali kudzapereka, Yesu anakhoza kunyamula machimo a munthuyo, monga momwe mbuzi ya Azazeli inanyamulira machimo a Israyeli pa Tsiku Lotetezera. (Levitiko 16:7-10) Komabe, mwamuna wamanjenjeyo anali munthu ndithu. Iye anali kudzalakwanso, ndipo m’kupita kwa nthaŵi anamwalira, mmene zimakhalira kwa ochimwa. (Aroma 5:12; 6:23) Zimene Yesu ananena sizinatanthauze kuti munthuyo anapeza moyo wosatha panthaŵi yomweyo. Koma munthuyo anadalitsidwa ndi chikhululukiro cha machimo kumlingo winawake panthaŵiyo.

Tsopano talingalirani mkhalidwe wathu. Pokhala opanda ungwiro, timalakwa tsiku ndi tsiku. (Yakobo 3:2) Kodi tingachitenji pa zimenezo? Eya, tili ndi Mkulu wa Ansembe wachifundo kumwamba mwa amene tingafikire Yehova m’pemphero. Inde, monga momwe Paulo analembera, tonsefe ‘tingayandikire [ndi ufulu wa kulankhula, NW] mpando wachisomo [wa Mulungu], kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthaŵi yakusoŵa.’ Chotero, onse lerolino amene ali a nkhosa zina akupezadi mapindu abwino koposa a mautumiki a Kristu monga mkulu wa ansembe.

Akristu onse okhala ndi chiyembekezo cha pa dziko lapansi angayang’ane mtsogolo ku mapindu okulirapo m’dziko latsopano limene likuyandikalo. Pamenepo Mkulu wathu wa Ansembe wakumwamba adzagwiritsira ntchito mtengo wonse wa nsembe yake, kudzetsa chikhululukiro chokwana cha machimo. Ndiponso adzawonjezera mapindu mwa kusamalira thanzi lakuthupi ndi lauzimu la anthu. Ndipo Yesu adzafutukula kwambiri maphunziro a anthu a Mulungu pa dziko lapansi, popeza kuphunzitsa Chilamulo kunali thayo lalikulu la ansembe m’Israyeli. (Levitiko 10:8-11; Deuteronomo 24:8; 33:8, 10) Chotero, pamene kuli kwakuti tikupindula ndi mautumiki a Yesu monga wansembe tsopano, pali zambiri zimene zikutiyembekezera!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena