Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w00 8/15 tsamba 26-29
  • Kodi Ndinu Mkristu ‘Wokhwima Ndithu’?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndinu Mkristu ‘Wokhwima Ndithu’?
  • Nsanja ya Olonda—2000
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “M’chidziŵitso Akulu Misinkhu”
  • Alaliki Komanso Aphunzitsi Achangu
  • Osunga Umphumphu
  • Okhulupirika
  • Kusonyeza Chikondi mwa Machitidwe Anu
  • Kugwiritsa Ntchito Chuma Chathu Kuchirikiza Kulambira Koyera
  • Pitirizani Kutsata Ukulu Msinkhu!
  • ‘Tiyesetse Mwakhama Kuti Tikhale Aakulu Mwauzimu’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Kodi Mukuyesetsa Kukhala Ngati Khristu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • ‘Lolani Kupita Patsogolo Kwanu Kuwonekera’
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Onetsani Kuti Mukupita Patsogolo
    Nsanja ya Olonda—2001
Nsanja ya Olonda—2000
w00 8/15 tsamba 26-29

Kodi Ndinu Mkristu ‘Wokhwima Ndithu’?

“PAMENE ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana.” Analemba choncho mtumwi Paulo. Zoonadi, tonsefe tinakhalako makanda osatha kudzithandiza. Komabe, sitinakhalebe makanda kwa nthaŵi zonse. Paulo ananena kuti: “Tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.”​—1 Akorinto 13:11.

Mofananamo, Akristu onse amayamba monga makanda auzimu. Koma m’kupita kwa nthaŵi, onse ‘angafike ku umodzi umene upezeka pakukhulupirira, ndiponso pakudziŵa Mwana wa Mulungu. Pamenepo adzakhwima ndithu, ndi kufika pamsinkhu wathunthu wa Kristu.’ (Aefeso 4:13, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Pa 1 Akorinto 14:20, tikulangizidwa kuti: “Abale, musakhale ana m’chidziŵitso . . . Koma m’chidziŵitso akulu misinkhu.”

Kukhalapo kwa Akristu akulu msinkhu, okhwima ndithu, ndi dalitso kwa anthu a Mulungu lerolino, makamaka chifukwa chakuti pali atsopano ambiri kwabasi. Akristu okhwima ndithu amalimbitsa mpingo. Amathandiza mpingo uliwonse umene amasonkhana kukhala ndi mzimu wabwino.

Pamene kukula kwakuthupi kumachitika kokha, kukula kwauzimu kumafuna nthaŵi ndi khama. N’zosadabwitsa kuti kale m’nthaŵi ya Paulo, Akristu ena analephera ‘kupitirira kutsata ukulu msinkhu,’ ngakhale kuti anatumikira Mulungu kwa zaka zambiri. (Ahebri 5:12; 6:1) Bwanji inuyo? Kaya mwatumikira Mulungu kwa zaka zambiri kapena kwa nthaŵi yochepa chabe, mungachite bwino kudzipenda nokha moona mtima. (2 Akorinto 13:5) Kodi muli m’gulu la anthu amene angatchedwedi Akristu okhwima, kapena akulu msinkhu? Ngati si choncho, kodi mungakhale bwanji otero?

“M’chidziŵitso Akulu Misinkhu”

Khanda lauzimu, mosavuta ‘limagwedezekagwedezeka, kutengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusokeretsa.’ Choncho Paulo analimbikitsa kuti: “Mwa chikondi tikakule m’zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Kristu.” (Aefeso 4:14, 15) Ndi motani mmene munthu angachitire zimenezo? Ahebri 5:14 amati: “Chakudya chotafuna chili cha anthu akulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloŵeretsa zizindikiritso zawo [“anazoloŵeretsa mphamvu zawo za kuzindikira mwa kuzigwiritsa ntchito,” NW] kusiyanitsa chabwino ndi choipa.”

Onani kuti anthu okhwima ndithu amazoloŵeretsa mphamvu zawo za kuzindikira mwa kuzigwiritsa ntchito potsata mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo. N’zachidziŵikire kuti munthu sangakhwime tsiku limodzi; pamatenga nthaŵi kuti ukule mwauzimu. Ngakhale zili choncho, mungachite zambiri kusonkhezera kukula kwanu kwauzimu ndi phunziro laumwini​—makamaka la zinthu zakuya za Mawu a Mulungu. Posachedwapa Nsanja ya Olonda yafotokoza nkhani zakuya zambiri. Anthu okhwima sapewa nkhanizo chifukwa zili ndi “zina zovuta kuzizindikira.” (2 Petro 3: 16) Koma, amadya​—kudyeratu chakudya cholimbacho!

Alaliki Komanso Aphunzitsi Achangu

Yesu analangiza ophunzira ake kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Kuchita ntchito yolalikira mwachangu kungafulumizenso kukula kwanu kwauzimu. Bwanji osalimbikira kuchitako ntchito imeneyi monga mmene mikhalidwe yanu ingalolere?​—Mateyu 13:23.

Nthaŵi zina, zovuta za moyo zingapangitse kuti kupeza nthaŵi yolalikira kuvute. Komabe, mwa ‘kuyesetsa’ monga mlaliki, mumaonetsa kuti “uthenga wabwino” n’ngwofunika kwambiri kwa inu. (Luka 13:24; Aroma 1:16) Choncho mungaonedwe monga ‘chitsanzo kwa iwo okhulupirira.’​—1 Timoteo 4:12.

Osunga Umphumphu

Kukula mpaka kukhwima kumafunanso kuchita khama posunga umphumphu wanu. Monga mmene zinalembedwera pa Salmo 26:1, Davide analengeza kuti: ‘Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda m’ungwiro [“umphumphu,” NW] wanga.’ Umphumphu ndiwo kukhala wabwino, kapena wokwanira, m’makhalidwe. Komabe, sutanthauza ungwiro. Davide iye mwini anachita machimo ambiri aakulu. Koma chifukwa chakuti anavomereza chidzudzulo n’kusiya njira yake, anasonyeza kuti mtima wake unali nachobe chikondi chenicheni cha Yehova Mulungu. (Salmo 26:2, 3, 6, 8, 11) Umphumphu umaphatikizapo, kudzipereka kwathunthu, kapena kwa mtima wonse. Davide anauza mwana wake Solomo kuti: “Um’dziŵe Mulungu wa atate wako, um’tumikire ndi mtima wangwiro [“wonse,” NW].”​—1 Mbiri 28:9.

Kusunga umphumphu kumaphatikizapo kusakhala “a dziko lapansi,” kusaloŵa m’ndale za mayiko ndi nkhondo zawo. (Yohane 17:16) Muyenera kupeŵa zochita zoipa, monga dama, chigololo, ndi mankhwala osokoneza bongo. (Agalatiya 5:19-21) Komabe, kusunga umphumphu kumatanthauza zambiri, kuposa kungopeŵa zinthu zimenezo. Solomo anachenjeza kuti: “Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa nizioletsa mafuta onunkhira a sing’anga; chomwecho kupusa kwapang’ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu.” (Mlaliki 10:1) Inde, ngakhale “kupusa kwapang’ono,” monga nthabwala zosayenera kapena makhalidwe okopana amuna ndi akazi, zingawononge mbiri ya munthu ‘wotchuka chifukwa cha nzeru.’ (Yobu 31:1) Chifukwa chake, onetsani kukula kwanu mwa kuyesetsa kukhala chitsanzo chabwino m’makhalidwe anu onse, kupeŵa ngakhale “maonekedwe onse a choipa.”​—1 Atesalonika 5:22.

Okhulupirika

Mkristu wokhwima ndithu alinso wokhulupirika. Monga mmene timaŵerengera pa Aefeso 4:24, NW, mtumwi Paulo akuchenjeza Akristu kuti: ‘Muvale umunthu watsopano umene unalengedwa monga mwa chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chenicheni ndi kukhulupirika.’ M’Malemba Achigiriki, liwu la chinenero choyambirira lotembenuzidwa kuti ‘kukhulupirika’ lili ndi lingaliro la chiyero, chilungamo, ndi ulemu. Munthu wokhulupirika n’ngwodzipereka, n’ngwopembedza kwambiri; amakwaniritsa maudindo ake onse kwa Mulungu.

Kodi zina mwa njira zimene mungakhalire wokhulupirika motere n’ziti? Njira ina ingakhale ya kugwirizana ndi akulu a mpingo wanu. (Ahebri 13:17) Pozindikira kuti Kristu ndiye Mutu woikidwa wa mpingo wachikristu, Akristu okhwima amakhulupirika kwa oikidwa kuti ‘aŵete Eklesia wa Mulungu.’ (Machitidwe 20:28) Zingakhale zosayeneratu kutsutsa kapena kunyoza ulamuliro wa akulu oikidwa! Muyeneranso kukhulupirika kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi mabungwe amene akuwagwiritsa ntchito kupereka “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake.” (Mateyu 24:45) Fulumirani kuŵerenga ndi kugwiritsa ntchito chidziŵitso chopezeka mu Nsanja ya Olonda ndi mabuku anzake.

Kusonyeza Chikondi mwa Machitidwe Anu

Paulo analembera Akristu a m’Tesalonika kuti: “Chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake.” (2 Atesalonika 1:3) Kukula m’chikondi ndi mbali yofunika kwambiri pa kukula kwauzimu. Monga mmene zinalembedwera pa Yohane 13:35, Yesu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” Chikondano chaubale choterocho sichidziŵika ndi kungotengeka maganizo. Dikishonale yotchedwa Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words imanena kuti: “Chikondi chingadziŵike ndi zochita zimene chimasonkhezera.” Inde, mumapitiriza kukula msinkhu mwa kuchita ntchito zosonyeza chikondi!

Mwachitsanzo, pa Aroma 15:7, timaŵerenga kuti: “Mulandirane wina ndi mnzake.” Njira imodzi yosonyezera chikondi ndiyo kupereka moni kwa okhulupirira anzathu ndi atsopano pamisonkhano ya mpingo, mwachikondi ndi nsangala! Adziŵeni inu mwininu. ‘Mupenyererenso’ za ena. (Afilipi 2:4) Mwina mungathenso kuitana anthu osiyanasiyana ndi kuwachereza kunyumba kwanu. (Machitidwe 16:14, 15) Nthaŵi zina kupanda ungwiro kwa ena kungayese kuya kwa chikondi chanu. Koma pamene muphunzira ‘kuwalolera mwa chikondi,’ mumasonyeza kuti mukukhwima ndithu.​—Aefeso 4:2.

Kugwiritsa Ntchito Chuma Chathu Kuchirikiza Kulambira Koyera

Kale, si anthu a Mulungu onse amene anakwaniritsa udindo wawo wa kuchirikiza kachisi wa Yehova. Choncho Mulungu anatumiza aneneri, monga Hagai ndi Malaki, kuti asonkhezere anthu Ake pankhani imeneyo. (Hagai 1:2-6; Malaki 3:10) Akristu akulu misinkhu lerolino amagwiritsa ntchito chuma chawo mwachimwemwe kuchirikiza kulambira kwa Yehova. Atsanzireni ameneŵa mwa kutsatira mfundo imene ili pa 1 Akorinto 16:1, 2, nthaŵi zonse ‘kusunga’ chopereka cha mpingo ndi cha ntchito ya padziko lonse ya Mboni za Yehova. Mawu a Mulungu amalonjeza kuti: “Iye wakufesa mooloŵa manja, mooloŵa manjanso adzatuta.”​—2 Akorinto 9:6.

Musachite mphwayi ndi chuma china chimene muli nacho, monga nthaŵi yanu ndi nyonga. Yesani ‘kuombola nthaŵi’ kuchoka pa zinthu zosafunika kwenikweni. (Aefeso 5:15, 16, NW; Afilipi 1: 10) Phunzirani kugwiritsa ntchito bwino kwambiri nthaŵi yanu. Kuteroko kungakutheketseni kugwira nawo ntchito zokonza Nyumba za Ufumu ndi ntchito zina zimene zimachirikiza kulambira Yehova. Kugwiritsa ntchito chuma chanu mwa njira imeneyi kudzapereka umboni wowonjezereka wakuti mukukhala Mkristu wokhwima ndithu.

Pitirizani Kutsata Ukulu Msinkhu!

Amuna ndi akazi amene amakonda kuphunzira ndiponso achidziŵitso, amene ali alaliki achangu, amene umphumphu wawo n’ngwolimba, okhulupirika komanso achikondi, ofunitsitsa kuthandiza kugwira ntchito ndi kupereka chuma pochirikiza ntchito ya Ufumu alidi dalitso lalikulu. Choncho, n’zosadabwitsatu kuti mtumwi Paulo analangiza kuti: “Polekana nawo mawu a chiyambidwe cha Kristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu”!​—Ahebri 6:1.

Kodi ndinu Mkristu wokhwima ndithu? Kapena mwanjira zina, mudakali ngati khanda lauzimu? (Ahebri 5:13) Mulimonse, khalani akhama ndi phunziro laumwini, kulalikira, ndi kusonyeza chikondi kwa abale anu. Landirani uphungu uliwonse ndi mwambo umene anthu akulu misinkhu angakupatseni. (Miyambo 8:33) Nyamulani katundu wanu yense wa udindo wachikristu. Ndi kupita kwa nthaŵi komanso n’kuyesetsa, inunso mungathe ‘kufika ku umodzi umene upezeka pakukhulupirira, ndiponso pakudziŵa Mwana wa Mulungu. Pamenepo mudzakhwima ndithu, ndi kufika pamsinkhu wathunthu wa Kristu.’​—Aefeso 4:13.

[Mawu Otsindika patsamba 27]

Akristu okhwima ndithu amalimbitsa mpingo. Amauthandiza kukhala ndi mzimu wabwino

[Zithunzi patsamba 29]

Anthu akulu misinkhu amathandizira mzimu wa mpingo mwa kukonda ena

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena