Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Enoke Wopanda Mantha Zivute Zitani
    Nsanja ya Olonda—1997 | January 15
    • Mulungu Anamtenga Enoke​—Motani?

      Yehova sanalole Satana kapena atumiki ake apadziko lapansi kupha Enoke. M’malo mwake, nkhani youziridwayo imati: “Mulungu anamtenga.” (Genesis 5:24) Mtumwi Paulo akufotokoza nkhaniyo motere: “Ndi chikhulupiriro Enoke anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeka, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu.”​—Ahebri 11:5.

      Kodi ndi motani mmene Enoke ‘anatengedwera kuti angaone imfa’? Kapena monga momwe matembenuzidwe a R. A. Knox amanenera, kodi ndi motani mmene Enoke “anatengedwera popanda kukumana ndi imfa”? Mulungu anauthetsa moyo wa Enoke mwa mtendere, akumpeŵetsa zoŵaŵa za imfa kaya mwa matenda kapena mwa chiwawa kwa adani ake. Inde, Yehova anafupikitsa moyo wa Enoke pa usinkhu wa zaka 365​—ali wachichepere ndithu poyerekezera ndi ena a m’nthaŵi yake.

      Kodi ndi motani mmene Enoke ‘anachitidwira umboni kuti anakondweretsa Mulungu’? Unali umboni wotani womwe anali nawo? Kuchita ngati Mulungu anamgoneka Enoke tulo, monga mmene mtumwi Paulo “anakwatulidwa” kapena kutengedwa, mwachionekere akumaona masomphenya a paradaiso wauzimu wamtsogolo wa mpingo wachikristu. (2 Akorinto 12:3, 4) Umboni wakuti Enoke anali kukondweretsa Mulungu ungakhale utaphatikizapo zideruderu zamasomphenya a paradaiso wapadziko lapansi mtsogolomu mmene onse okhala ndi moyo adzachirikiza ulamuliro wa Mulungu. Kapena kunali pamene Enoke anali chipenyere masomphenya osangalatsa ameneŵa pamene Mulungu anamtenga mu imfa yopanda ululu kuti agone kufikira tsiku lachiukiriro chake. Kukuoneka kuti monga momwe zinachitikira kwa Mose, Yehova anachotsa thupi la Enoke, pakuti “sanapezeka.”​—Ahebri 11:5; Deuteronomo 34:5, 6; Yuda 9.

  • Enoke Wopanda Mantha Zivute Zitani
    Nsanja ya Olonda—1997 | January 15
    • Kodi Enoke Anapita Kumwamba?

      “Ndi chikhulupiriro Enoke anatengedwa kuti angaone imfa.” Potembenuza chigawo chimenechi cha Ahebri 11:​5, ma Baibulo ena amasonyeza kuti Enoke sanafe kwenikweni. Mwa chitsanzo, A new Translation of the Bible, la James Moffat, limati: “Kunali mwa chikhulupiriro mmene Enoke anatengedwera kumwamba kotero kuti sanafe konse.”

      Komabe, zaka 3,000 pambuyo pa tsiku la Enoke, Yesu Kristu anati: “Kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu.” (Yohane 3:13) The New English Bible limati: “Palibe aliyense anakwerapo kumwamba kusiyapo iye amene anatsika kumwamba, Mwana wa Munthuyo.” Pamene Yesu ananena mawu amenewo, ngakhale iye anali asanakwere kumwamba.​—Yerekezerani ndi Luka 7:28.

      Mtumwi Paulo anatero kuti Enoke ndi ena amene ali mtambo waukulu wa mboni zoyambirira Chikristu chisanakhale ‘onse anamwalira’ ndipo “sanalandira lonjezanolo.” (Ahebri 11:​13, 39) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti anthu onse, kuphatikizapo Enoke, analandira choloŵa chauchimo kuchokera kwa Adamu. (Salmo 51:5; Aroma 5:12) Njira yokha yachipulumutso ndiyo kupyolera mwa nsembe ya dipo ya Kristu Yesu. (Machitidwe 4:12; 1 Yohane 2:​1, 2) M’tsiku la Enoke dipo limenelo linali lisanalipiridwe. Chotero, Enoke sanapite kumwamba, koma ali chigonere mtulo taimfa kudikira chiukiriro padziko lapansi.​—Yohane 5:​28, 29.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena