Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Tsanzirani Chikhulupiriro cha Mose
    Nsanja ya Olonda—2014 | April 15
    • 1, 2. (a) Kodi Mose ali ndi zaka 40 anasankha kuchita chiyani? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) N’chifukwa chiyani Mose anasankha kuvutikira limodzi ndi anthu a Mulungu?

      MOSE analeredwa m’banja lachifumu ndipo ankadziwa zinthu zabwino zimene zinali ku Iguputo. Iye ankaona nyumba zikuluzikulu za anthu olemera komanso “anaphunzira nzeru zonse za Aiguputo” monga luso losiyanasiyana, masamu ndi maphunziro ena a sayansi. (Mac. 7:22) Iye akanatha kukhala ndi chuma, udindo komanso zinthu zina zimene Aiguputo ena sakanazipeza.

      2 Koma ali ndi zaka 40, Mose anachita zinthu zimene zinadabwitsa kwambiri banja lachifumu limene linkamulera. Iye anasankha kuchoka m’banja lachifumu. Kodi anangokhala ngati munthu wamba wa ku Iguputo? Ayi. Iye anasankha kukhala ndi anthu a mtundu wake amene anali akapolo. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Mose anali ndi chikhulupiriro. (Werengani Aheberi 11:24-26.) Chifukwa cha chikhulupiriro, Mose sankangoona zinthu zooneka. Iye ankakhulupirira Yehova “Wosaonekayo” ndipo ankadziwa kuti malonjezo ake onse adzakwaniritsidwa.—Aheb. 11:27.

  • Tsanzirani Chikhulupiriro cha Mose
    Nsanja ya Olonda—2014 | April 15
    • 4. Kodi Mose anazindikira chiyani zokhudza ‘zosangalatsa zauchimo’?

      4 Chifukwa cha chikhulupiriro, Mose anazindikira kuti ‘zinthu zosangalatsa zauchimo’ ndi zosakhalitsa. Koma anthu ena akanatha kuganiza kuti ngakhale kuti Aiguputo ankalambira mafano komanso kukhulupirira mizimu, ulamuliro wawo unali wamphamvu padziko lonse pamene anthu a Mulungu anali akapolo. Koma Mose ankadziwa kuti Mulungu angasinthe zinthu. Ngakhale kuti anthu ochita zofuna zawo ankaoneka kuti zinthu zikuwayendera, Mose ankadziwa kuti anthu oipa alibe tsogolo. Choncho iye sanakopeke ndi “zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo.”

      5. N’chiyani chingatithandize kukana “zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo”?

      5 Kodi mungakane bwanji “zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo”? Musaiwale kuti zosangalatsa zauchimo ndi zakanthawi. Chikhulupiriro chanu chingakuthandizeni kuona kuti “dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake.” (1 Yoh. 2:15-17) Muziganizira zimene zidzachitikire anthu osalapa. Iwo ali “pamalo oterera . . . kuti awonongeke.” (Sal. 73:18, 19) Tikamayesedwa kuti tichite zoipa, tiyenera kudzifunsa kuti, ‘kodi ndikufuna kuti tsogolo langa lidzakhale lotani?’

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena