Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi ‘Mukuona Wosaonekayo’?
    Nsanja ya Olonda—2014 | April 15
    • 10. (a) Kodi Yehova anapereka malangizo otani kwa Aisiraeli m’mwezi wa Nisani mu 1513 B.C.E.? (b) N’chifukwa chiyani Mose anamvera malangizo a Mulungu?

      10 M’mwezi wa Nisani m’chaka cha 1513 B.C.E., Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti akapereke malangizo ovuta kumvetsa kwa Aisiraeli. Malangizo ake anali akuti asankhe nkhosa kapena mbuzi yamphongo yathanzi n’kuipha ndipo magazi akewo awaze pamafelemu a nyumba zawo. (Eks. 12:3-7) Kodi Mose anachita chiyani? Patapita nthawi, mtumwi Paulo analemba zimene anachita. Anati: “Mwa chikhulupiriro, iye anachita pasika ndiponso anawaza magazi pamafelemu a pakhomo, kuti wowonongayo asakhudze ana awo oyamba kubadwa.” (Aheb. 11:28) Mose ankadziwa kuti Yehova ndi wodalirika, ndipo ankakhulupirira malonjezo ake akuti adzapha ana onse oyamba kubadwa a Aiguputo.

      11. N’chifukwa chiyani Mose anachenjeza Aisiraeli?

      11 Zikuoneka kuti ana a Mose anali ku Midiyani, kutali ndi “wowonongayo.”a (Eks. 18:1-6) Koma Mose anamvera Mulungu ndipo anapereka malangizowo kwa Aisiraeli anzakewo kuti ana awo oyamba kubadwa asaphedwe. Mose ankakonda anthu ndipo sankafuna kuti aliyense aphedwe. Baibulo limanena kuti: “Mwamsanga, Mose anaitana akulu onse a Isiraeli ndi kuwauza kuti: ‘Sankhani nkhosa ndi mbuzi . . . muiphere nsembe ya pasika.’”—Eks. 12:21.

      12. Kodi Yehova akufuna kuti tilengeze uthenga wofunika uti?

      12 Motsogoleredwa ndi angelo, anthu a Yehova akulengeza uthenga wofunika kwambiri wakuti: “Opani Mulungu ndi kumupatsa ulemerero, chifukwa ola lakuti apereke chiweruzo lafika. Chotero lambirani Iye amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe amadzi.” (Chiv. 14:7) Ino ndiye nthawi yoti tilengeze uthengawo. Tiyenera kuchenjeza anthu kuti atuluke mu Babulo Wamkulu, kuti ‘asalandire nawo ina ya miliri yake.’ (Chiv. 18:4) A “nkhosa zina” limodzi ndi Akhristu odzozedwa akuchonderera anthu amene atalikirana ndi Mulungu kuti ‘agwirizanenso’ naye.—Yoh. 10:16; 2 Akor. 5:20.

      Mlongoyu akukonzekera kukalalikira ndipo m’maganizo mwake akuona angelo atagwira mphepo zowononga

      Mukamakhulupirira malonjezo a Yehova mudzakhala ofunitsitsa kulengeza uthenga wabwino(Onani ndime 13)

      13. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe ofunitsitsa kulengeza uthenga wabwino?

      13 Sitikukayikira kuti “ola lakuti [Mulungu] apereke chiweruzo” lafika. Tikukhulupiriranso kuti Yehova sakukokomeza potiuza kuti tikufunika kugwira mwamsanga ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu. M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona “angelo anayi ataimirira m’makona anayi a dziko lapansi. Iwo anali atagwira mwamphamvu mphepo zinayi za dziko lapansi.” (Chiv. 7:1) Kodi chikhulupiriro chanu chikukuthandizani kuona kuti angelowo atsala pang’ono kusiya mphepoyo kuti iwononge dzikoli pa chisautso chachikulu? Ngati zili choncho, mudzalengeza uthenga wabwino molimba mtima.

  • Kodi ‘Mukuona Wosaonekayo’?
    Nsanja ya Olonda—2014 | April 15
    • a Zikuoneka kuti Yehova anatumiza angelo kuti akapereke chiweruzo kwa Aiguputo.—Sal. 78:49-51.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena