Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mungapirire Kufika Kuchimaliziro
    Nsanja ya Olonda—1999 | October 1
    • 10 Mumpikisano wothamangira moyo umene Akristu aloŵamo, kodi oonerera ndani? Atalongosola mboni za Yehova za m’nthaŵi yoyambirira kusanakhale Chikristu, monga momwe zilili mu chaputala 11 cha Ahebri, Paulo analemba kuti: “Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, . . . tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.” (Ahebri 12:1) Pogwiritsa ntchito phiphiritso la mtambo, Paulo sanagwiritse ntchito mawu achigiriki otanthauza mtambo weniweni wokhala ndi ukulu ndi malire oonekera bwino iyayi. M’malo mwake, iye anagwiritsa ntchito mawu amene malinga ndi kunena kwa mkonzi wa dikishonale W. E. Vine “amatanthauza chigulu cha zinthu chooneka ngati mtambo kuthambo, chosadziŵika bwino ukulu wake.” Ndithudi, Paulo anali kuganizira za khamu lalikulu la mboni​—mboni zambirimbiri moti zinali ngati mtambo.

      11, 12. (a) Kodi mboni zomwe zinaliko kusanakhale Chikristu zingatichemerere motani, titero kunena kwake, kuti tipitirize kuthamanga ndi chipiriro? (b) Kodi tingapindule kwambiri motani ndi ‘mtambo waukulu wa mboni’?

      11 Kodi mboni zomwe zinaliko kusanakhale Chikristu zingakhale oonerera enieni amakono? Kutalitali. Onse anagona mu imfa, kuyembekeza chiukiriro. Komabe, iwowo anathamanga mwachipambano pamene anali amoyo, ndipo zitsanzo zawo n’zamoyobe m’masamba a m’Baibulo. Pamene tiphunzira Malemba, tingawakumbukire bwino lomwe anthu okhulupirika ameneŵa ndipo angatichemerere, titero kunena kwake, kuti tithamange kufika kuchimaliziro.​—Aroma 15:4.a

      12 Mwachitsanzo, ngati mwayi wakudziko winawake watiika pachiyeso, kodi kusinkhasinkha za mmene Mose anakanira ulemerero wa Igupto sikungatilimbikitse kukhalabe panjira yabwino? Ngati takumana ndi chiyeso choŵaŵa, kukumbukira chiyeso chachikulu chimene Abrahamu anakumana nacho pamene anapemphedwa kupereka mwana wake Isake nsembe kudzatilimbikitsadi kuti tisatope pampikisano wathu wa chikhulupiriro. Chisonkhezero chimene ‘mtambo waukulu’ wa mboni umatipatsa m’njira imeneyo chimadalira pa mmene timazionera bwino mbonizo ndi maso athu a kuzindikira.

      13. Kodi ndi motani mmene Mboni za Yehova zamakono zingatipatsire nyonga pampikisano wothamangira moyo?

      13 Tazingidwanso ndi Mboni za Yehova zambiri zedi m’nthaŵi zamakonozi. Akristu odzozedwa limodzinso ndi amuna ndi akazi a mu “khamu lalikulu” ameneŵa apereka zitsanzo zachikhulupiriro zokongola kwabasi! (Chivumbulutso 7:9) Nthaŵi ndi nthaŵi tingaŵerenge nkhani zosimba za moyo wawo m’magazini ino ndi m’zofalitsa zina za Watch Tower.b Pamene tisinkhasinkha za chikhulupiriro chawo, timalimbikitsidwa kuti tipirire mpaka kuchimaliziro. Ndipo n’zosangalatsatu kwambiri kuchirikizidwa ndi mabwenzi apamtima ndi achibale athu amenenso akutumikira Yehova mokhulupirika! Inde, tili ndi anthu ambiri amene angatipatse nyonga pampikisano wothamangira moyo.

      Thamangani Paliŵiro Labwino

      14, 15. (a) N’chifukwa chiyani kuthamanga paliŵiro labwino kuli kofunika kwa ife? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kuika zolinga zathu mofatsa?

      14 Pothamanga mtunda wautali, wothamangayo ayenera kuyamba ndi liŵiro labwino. “Kungoyamba ndi liŵiro la mtondo wadooka kungakupangitseni kuti mulephere,” inatero magazini yotchedwa New York Runner. “Chimene chingachitike n’chakuti mungavutike kwadzaoneni kuti mumalize makilomita angapo omalizira mwinanso mutha kungolephereratu.” Winawake wochita nawo mpikisano wothamanga pa mtunda wautali anakumbukira kuti: “Wochititsa msonkhano umene ndinakapezekapo pokonzekera mpikisanowu anachenjeza mosapita m’mbali kuti: ‘Musalimbane ndi othamanga a liŵiro la mtima bi. Thamangani paliŵiro lanu. Apo ayi mudzatopa ndipo mwina mungalephere kumaliza.’ Kulabadira malangizo ameneŵa kunandithandiza kumaliza mtunda wonse.”

      15 Pampikisano wothamangira moyo, atumiki a Mulungu ayenera kuyesetsa mwamphamvu. (Luka 13:24) Komabe, wophunzira Yakobo analemba kuti: “Nzeru zochokera Kumwamba [ndi] . . . zofatsa.” (Yakobo 3:17, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Pamene kuli kwakuti zitsanzo zabwino za ena zingatilimbikitse kuchita zambiri, kufatsa kudzatithandiza kuika zolinga zofikirika malinga ndi zimene tingathe kuchita ndiponso mkhalidwe wathu. Malemba amatikumbutsa kuti: “Yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina. Pakuti yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.”​—Agalatiya 6:4, 5.

      16. Kodi kudzichepetsa kumatithandiza motani kuthamanga paliŵiro labwino?

      16 Pa Mika 6:8, tikufunsidwapo funso lofika pamtima ili: “Yehova afunanji nawe koma . . . kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?” Kudzichepetsa kumaphatikizapo kuzindikira zinthu zimene sitingathe kuchita. Kodi thanzi lovuta kapena ukalamba zatipangitsa kuti tisamathe kuchita zinthu zina muutumiki wa Mulungu? Tisakhumudwe. Yehova amalandira zoyesayesa zathu ndi kudzimana kwathu ‘monga momwe tili nazo, si monga tilibe.’​—2 Akorinto 8:12; yerekezani ndi Luka 21:1-4.

  • Mungapirire Kufika Kuchimaliziro
    Nsanja ya Olonda—1999 | October 1
    • Pamene Chimaliziro Chikuyandikira

      20. Kodi mpikisano wothamangira moyo ungakhale wovuta motani pamene ukuyandikira mapeto ake?

      20 Mumpikisano wothamangira moyo, tifunikira kulimbana ndi mdani wathu wamkulu, Satana Mdyerekezi. Pamene tikuyandikira chimaliziro, akuyesetsa mwamphamphu kutipinga kapena kutipangitsa kuti tichepetse liŵiro. (Chivumbulutso 12:12, 17) Ndipo n’zovuta kupitirizabe kukhala olengeza Ufumu okhulupirika ndi odzipatulira chifukwa cha nkhondo, njala, miliri, ndi mavuto ena onse amene ali chizindikiro cha “nthaŵi ya chimaliziro.” (Danieli 12:4; Mateyu 24:3-14; Luka 21:11; 2 Timoteo 3:1-5) Komanso, chimaliziro chingaoneke ngati kuti chili kutali kwambiri kusiyana ndi mmene tinkaganizira, makamaka ngati tinaloŵa mumpikisanowu zaka zambirimbiri kalelo. Komabe, Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti chimalizirocho chidzafika. Yehova akuti sichidzazengereza. Chimalizirocho chili pafupi kwenikweni.​—Habakuku 2:3; 2 Petro 3:9, 10.

      21. (a) Kodi n’chiyani chidzatilimbitsa pamene tipiritizabe kuthamanga mumpikisano wothamangira moyo? (b) Kodi tiyenera kutsimikiza mtima ponena za chiyani pamene chimaliziro chiyandikira?

      21 Ndiye kuti ngati tikufuna kupambana pampikisano wothamangira moyo, tiyenera kupeza mphamvu pachakudya chauzimu chimene Yehova wapereka mwachikondi. Tifunikiranso chilimbikitso chonse chimene tingapeze mwa kuyanjana ndi okhulupirira anzathu nthaŵi zonse, amenenso akuthamanga mumpikisanowu. Ngakhale chizunzo choopsa ndi zochitika zotigwera zitapangitsa kuthamanga kwathu kukhala kovuta kwambiri, tingapirire kufika kuchimaliziro chifukwa chakuti Yehova amapereka “ukulu woposa wamphamvu.” (2 Akorinto 4:7) N’zolimbikitsatu kwambiri kudziŵa kuti Yehova akufuna kuti timalize makani a liŵiro ameneŵa mwachipambano! Motsimikizadi mtima, “tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira,” tikudziŵa pansi pa mtima kuti “panyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.”​—Ahebri 12:1; Agalatiya 6:9.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena