Chitirani Umboni Yehova Ndipo Musaleme
“Talingilirani iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotere, . . . kuti mungaleme ndi kukomoka m’moyo mwanu.”—AHEBRI 12:3.
1, 2. Kodi ndi chitsimikiziro chokhutiritsa chotani chimene Yesu anapereka kwa ophunzira ake kuti iye anali atawukitsidwa?
“NDAWONA Ambuye.” Ndi mawu ozizwitsa amenewo, Mariya Magadala anabukitsa mbiri ya kuwuka kwa Yesu. (Yohane 20:18) Ichi chinazindikiritsa chiyambi cha masiku 40 odzala ndi zochitika zosangalatsa kwa ophunzira a Kristu, omwe papitapo anamvetsedwa chisoni ndi imfa yake.
2 Yesu sanafune kusiya chikaikiro chirichonse m’maganizo mwa ophunzira ake kuti iye analidi wamoyo. Chotero, monga mmene Luka akusimbira kuti: “Kwa iwonso anadziwonetsera yekha [Yesu] wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, nawonekera kwa iwo masiku makumi anayi.” (Machitidwe 1:3) M’chenicheni, pa nthaŵi ina “anawoneka kwa abale oposa mazana asanu.” (1 Akorinto 15:6) Motsimikizirika, tsopano panalibenso mpata wowonjezereka wa chikaikiro. Yesu anali wamoyo!
3. Kodi ndi mafunso otani onena za Ufumu amene ophunzira a Yesu anamfunsa iye, ndipo kodi nchifukwa ninji yankho lake linawazizwitsa iwo?
3 Pamenepo ophunzira a Yesu anangoganizira za “ufumu wa Mulungu” wa pa dziko lapansi, wobwezeretsedwa kwa Israyeli. (Luka 19:11; 24:21) Chotero iwo anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, kodi nthaŵi ino mubwezera ufumu kwa Israyeli?” Mosakaikira yankho lake linawazizwitsa iwo, popeza anati: “Sikuli kwa inu kudziŵa nthaŵi kapena nyengo, zimene Atate anaziika mu ulamuliro wake wa iye yekha. Komatu mudzalandira mphamvu, mzimu woyera utadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:6-8) Ndi chitokoso chotani nanga chomwe tsopano chinaikidwa pamaso pa ophunzira! Ndipo linali thayo lotani nanga! Kodi ndimotani mmene akakwaniritsira ntchito yoteroyo? Yankho linadza mofulumira mu mkhalidwe wodabwitsa.
Kulandira Chitokosocho
4. Longosolani chomwe chinachitika pa tsiku la Pentekoste.
4 Luka akusimba kuti: “Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pa malo amodzi. Ndipo mwadzidzidzi anamveka mawu ochokera kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene anali kukhalamo. Ndipo anawonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga a moto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekha wayekha. Ndipo anadzazidwa onse ndi mzimu woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga mzimu unawalankhulitsa.” Phokosolo linali lalikulu kwenikweni kotero kuti linakoka chisamaliro cha makamu a Ayuda okhala m’Yerusalemu kaamba ka phwandolo. Iwo anazizwitsidwa kumva ‘ali kulankhula m’malilime awo zazikulu za Mulungu.’—Machitidwe 2:1-11.
5. Kodi ndi ku mlingo wotali kumene kuneneratu kwa Yesu pa Machitidwe 1:8 kunakwaniritsidwa mwamsanga?
5 Petro sanataye nthaŵi iriyonse kupereka nkhani yogalamutsa, akumatsimikizira zikaikiro zonse kuti “Yesu Mnazarayo,” yemwe iwo anapachika, anali “Ambuye” wonenedweratu ndi Davide m’mawu akuti: “[Yehova, NW] anati kwa Mbuye wanga, Khalani kudzanja lamanja langa, kufikira ndikaike adani ako chopondapo mapazi ako.” Atalaswa mumtima, amvetseri a Petro anafunsa kuti: “Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?” M’kuyankha Petro anawachonderera iwo kuti: “Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu m’kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu.” Chotulukapo chake? Zikwi zitatu anabatizidwa! (Machitidwe 2:14-41) Kalekale umboni unali kuperekedwa m’Yerusalemu. Pambuyo pake, unafutukulidwa ku Yudeya yonse, kenaka Samariya, ndipo potsirizira pake “kumalekezero a dziko.” Kufutukuka kwa ntchito yolalikira Ufumu kunali kofulumira kwenikweni kotero kuti podzafika 60 C.E. mtumwi Paulo akakhoza kunena kuti uthenga wabwino ‘unalalikidwa ku cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’—Akolose 1:23.
Kufutukulidwa Kwaufumu ndi Chizunzo
6, 7. (a) Kodi ndimotani mmene kufutukulidwa kwa Ufumu ndi chizunzo cha Akristu zinayendera limodzi mkati mwa zaka za zana loyamba? (b) Kodi ndi kusoŵa kofulumira kotani komwe kunabuka pakati pa Akristu m’Yerusalemu, ndipo kodi ndimotani mmene kusoŵa kumeneku kunakwaniritsidwira?
6 Pasanapite nthaŵi yaitali pambuyo pa Pentekoste wa 33 C.E., ophunzira a Yesu anali ndi chifukwa chokumbukirira mawu ake akuti: “Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandizunza ine, adzakuzunzaninso.” (Yohane 15:20, NW) Atsogoleri Achiyuda anakwiyitsidwa pamene “mawu a Mulungu anakula; ndipo chiŵerengero cha akuphunzira chidachulukatu ku Yerusalemu.” Pa milandu yachinyengo, wophunzira Stefano anaponyedwa miyala ndi kufa. Chimenecho chinawonekera kukhala chizindikiro chimene ambiri ankachiyembekezera, popeza kuti “tsikulo kunayamba kuzunza kwakukulu pa mpingo unali m’Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m’maiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ayi.”—Machitidwe 6:7; 7:58-60; 8:1.
7 Chizunzocho chinazimiririka mwapang’ono. Koma mwamsanga pambuyo pake, Herode Agripa I anapha mtumwi Yakobo. Petro anaikidwa m’ndende koma anamasulidwa ndi mngelo. Pambuyo pake abale m’Yerusalemu anakhala ndi usiwa wakuthupi, ndipo chithandizo chinayenera kutumizidwa kwa iwo ndi akhulupiriri anzawo a kwinakwake. (Machitidwe 9:31; 12:1-11; 1 Akorinto 16:1-3) M’nthaŵi ya kuchezera kwa mtumwi Paulo ku Yerusalemu, chikhulupiriro chopanda maziko chachipembedzo chinawonekera popeza kuti makamu anakweza mawu kuti: “Achoke pa dziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.” (Machitidwe 22:22) Motsimikizirika, Akristu amenewo okhala m’Yerusalemu ndi Yudeya anafunikira chilimbikitso chokulira cha kupitirizabe kuchitira umboni mokhulupirika ponena za Ufumu. Yesu anali atalonjeza ophunzira ake kuti ‘mzimu woyera, umene Atate adzatumiza m’dzina langa,’ ukachita monga ‘mthandizi.’ (Yohane 14:26) Koma kodi ndimotani mmene Atate tsopano akaperekera thandizo lofunika loterolo kapena chitonthozo? Yankho, mwapang’ono, linali kupyolera mwa mtumwi Paulo.
Kalata ya Paulo kwa Ahebri
8. (a) Kodi nchiyani chimene chinafulumiza Paulo kulemba kalata yake kwa Ahebri? (b) Kodi ndi pa mbali iti ya kalata yake pamene tidzalunjikitsa chisamaliro chathu, ndipo nchifukwa ninji?
8 Podzafika 61 C.E., Paulo anali ataikidwa m’ndende mu Roma, koma anadziŵa za chimene chinali kuchitika kwa abale ake m’Yerusalemu. Chotero, pansi pa chitsogozo cha mzimu wa Yehova, iye analemba kalata yake ya panthaŵi yake kwa Ahebri. Iyo iri yodzala ndi kudera nkhaŵa kwachikondi kaamba ka abale ndi alongo ake Achihebri. Paulo anadziŵa chimene iwo anafunikira kuti amangirire chikhulupiriro ndi chidaliro chawo mwa Yehova monga Mthandizi wawo. Pamenepo akakhoza ‘kuthamanga mwachipiriro makaniwo oikidwa pamaso pawo’ ndi kunena modalirika kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga; sindidzawopa. Kodi munthu angandichitenji?” (Ahebri 12:1; 13:6, NW) Ndi pa nsonga imeneyi ya kalata ya Paulo kwa Ahebri (mitu 11-13) pamene tsopano tikufuna kulunjikitsa chisamaliro chathu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mkhalidwe umene Akristu oyambirirawo anakumana nawo uli wofanana ndi umene ukukumanidwa ndi Mboni za Yehova lerolino.
9. Kodi ndi nkhani iti yoyang’anizana ndi Akristu m’zaka za zana loyamba yomwe ikuyang’anizana ndi Akristu lerolino, ndipo kodi ndimotani mokha mmene ingakumanizidwire?
9 M’mbadwo wathu, makamu ayankha mwaubwino ku uthenga wa Ufumu mwa kudzipereka okha kwa Yehova ndi kubatizidwa monga Mboni zake. Komabe, limodzi ndi kufutukuka kwa kulambira kowona kumeneku kwadzanso chizunzo chachiwawa, Akristu ambiri akumatayikiridwadi miyoyo yawo monga mmene anachitira Stefano, Yakobo, ndi mboni zina zokhulupirika za m’zaka za zana loyamba. Chotero, nkhani iri yofanana tsopano monga mmene inaliri pa nthaŵiyo: Kodi ndani yemwe adzakhala wokhoza kuchirimika chiyeso cha umphumphu wawo poyang’anizana ndi chitsutso chomawunjikidwa ku uthenga Waufumu? Ndiponso, kodi ndani yemwe adzakhala wokhoza kuyang’anizana ndi zochitika zowopsya pamene “chisautso chachikulu” chosayerekezeka chibwera mofulumira pa mbadwo wamakono uno? (Mateyu 24:21) Yankho liri lakuti, awo okonzekera “kulimba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro,” awo omwe ali “okhazikika m’chikhulupiriro.” Awa ndi amene potsirizira pake adzakhala okhoza kunena kuti: “Ichi ndi chilako tililaka nacho dziko, ndicho chikhulupiriro chathu.”—1 Timoteo 6:12; 1 Petro 5:9; 1 Yohane 5:4.
Kupindula Kuchokera ku Zitsanzo Zokhulupirika
10. (a) Kodi chikhulupiriro nchiyani? (b) Kodi ndimotani mmene Mulungu anadzimverera ponena za amuna ndi akazi achikhulupiriro a m’nthaŵi zakale?
10 Kodi chikhulupiriro nchiyani? Paulo akuyankha kuti: “Chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka. Pakuti momwemo akulu anachitidwa umboni.” (Ahebri 11:1, 2) Paulo kenaka akuchirikiza kumasulira kwake kwa chikhulupiriro mwa kusonyeza chikhulupiriro chikugwira ntchito. Iye akutenga mfundo zazikulu m’miyoyo ya “amuna akale,” limodzinso ndi akazi onga ngati Sara ndi Rahabi. Ndi cholimbikitsa chotani nanga kupeza kuti “Mulungu sachita manyazi nawo poitanidwa Mulungu wawo”! (Ahebri 11:16) Kodi Mulungu anganene chofananacho kwa ife chifukwa cha chikhulupiriro chathu? Lolani kuti tisamuchititse manyazi pamene tsiku lirilonse likutha.
11. Kodi ndimotani mmene tingapindulire lerolino ku ‘mtambo waukulu wa mboni zotizinga’?
11 Kutsatira cholembedwa cha amuna ndi akazi okhulupirika amenewo, Paulo akunena kuti: “Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chirichonse, ndi chimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.” (Ahebri 12:1) Ngakhale kuti iwo tsopano aligone m’manda, kodi mboni zokhulupirika zachitsanzo chabwino zimenezi ziri zamoyo m’maganizo athu? Kodi mumazidziŵa izo mokwanira limodzi ndi zokumana nazo zawo kotero kuti mungakhoze kuyankha kuti inde? Iyi iri imodzi ya mphotho zochulukira za phunziro la Baibulo lokhazikika, kugwiritsira ntchito maganizo athu onse kukhalitsa ndi moyo zokumana nazo zosangalatsa za “mtambo wa mboni” umenewu. Zowonadi, kuphunzira zitsanzo zawo zokhulupirika kudzatithandiza ife mokulira kulaka kusoŵeka kwa chikhulupiriro kulikonse. Pambuyo pake, ichi chidzatithandiza kupereka umboni wolimba mtima ndi wopanda mantha wa chowonadi pansi pa mikhalidwe iriyonse.—Aroma 15:4.
Musaleme
12. (a) Kodi ndimotani mmene chitsanzo cha Yesu chimatithandizira ife ‘kusalema ndi kukomoka m’moyo mwathu’? (b) Kodi ndi ziti zomwe ziri zitsanzo zamakono za awo osalema?
12 Chitsanzo chathu chachikulu koposa cha chikhulupiriro ndicho Yesu. Paulo akuchonderera kuti: “Tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambirira ndi womalizira wa chikhulupiriro chathu, Yesu. . . . Pakuti talingilirani iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotere, kuti [musaleme] ndi kukomoka m’moyo mwanu.” (Ahebri 12:1-3) Kodi ndi ‘mosamalitsa’ chotani mmene inu mwalingalira chitsanzo cha Yesu? Kodi ‘ndimopenyetsetsa’ chotani mmene inu mwakhala mukumuyang’anira? (1 Petro 2:21) Satana amafuna kuti ife ‘tileme ndi kukomoka m’moyo mwathu.’ Iye amafuna kuti tileke kuchita ntchito ya kuchitira umboni. Kodi ndimotani mmene iye amachitira chimenechi? Nthaŵi zina mwa chitsutso chotheratu kuchokera ku maulamuliro a chipembedzo ndi a dziko, mofanana ndi m’zaka za zana loyamba. Chaka chatha, ntchito yolalikira Ufumu inaikiridwa malire m’maiko 40. Koma kodi chimenechi chinapangitsa abale athu kulema? Ayi! Ntchito yawo yokhulupirika inatulukapo anthu 17,000 ndi owonjezereka akumabatizidwa m’maiko amenewo mu 1988. Kodi ndi chotsitsimula chotani nanga mmene chimenechi chiyenera kukhalira kwa onse okhala m’maiko amene muli ufulu wokulirapo! Lolani kuti tisaleme m’kulalikira mbiri yabwino Yaufumu!
13. (a) Kodi ndi zinthu zamachenjera ziti zimene zingatipangitse kufooka m’ntchito yathu yolalikira? (b) Kodi nchiyani chomwe chinali ‘chimwemwe choikidwa pamaso pa Yesu,’ ndipo kodi ndimotani mmene tingapezere mkhalidwe wachimwemwe wofananawo?
13 Komabe, pali zinthu zina zopambanitsa zomwe zingatipangitse kukhala ofooka. Izi zimaphatikizapo chitsutso m’nyumba yogawanikana, kutsendereza kwa maganizo, mavuto aumoyo, kutsendereza kwa mabwenzi, zokhumudwitsa chifukwa cha kusoŵeka kwa zotulukapo zabwino m’ntchito yathu yolalikira, kapena mwinamwake kudzimva osaleza mtima chifukwa chakuti mapeto a dongosolo iri lazinthu sanadzebe. Chabwino, kodi nchiyani chomwe chinathandiza Yesu kupirira kuvutika kwa maganizo ndi kwakuthupi? Chinali “chimwemwe choikidwacho pamaso pake.” (Ahebri 12:2) Yesu anachirikizidwa ndi chimwemwe cha kusangalatsa mtima wa Atate ake mwa kumulemekeza Iye ndi mwa chiyembekezero cha chimwemwe cha pambuyo pake chomwe iye akakumana nacho m’kupereka madalitso odabwitsa a Ufumu Waumesiya. (Salmo 2:6-8; 40:9, 10; Miyambo 27:11) Kodi tingatsanzire mosamalitsa kwenikweni mkhalidwe wachimwemwe umenewu wa Yesu? Ndipo kumbukirani chitsimikiziro cha Petro pa 1 Petro 5:9: “Zowawa zomwezo ziri m’kukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko.” Kudziŵa kuti Yehova amamvetsetsa, kumva kutentha kwa ubale wa dziko lonse, ndi kuyang’ana pa chimwemwe chomwe chiri kutsogolo kwathu pansi pa ulamuliro wa Ufumu—zonsezi zidzatithandiza ife kusalema m’kutumikira Yehova m’chikhulupiriro ndi m’kulalikira pamene mapeto ali pafupi kwenikweni.
Chifukwa Chimene Yehova Amalangira
14. Kodi ndi mapindu otani amene angatuluke m’ziyeso ndi kuvutika komwe tingafunikire kupirira nako?
14 Paulo tsopano akuwunikira pa chifukwa chimene tifunikira kupirira ziyeso ndi kuvutika. Iye akulingalira kuti tiyang’ane pa zimenezo monga mkhalidwe wa chilango. Paulo akulingalira kuti: “Mwana wanga, usayese chopepuka kulanga kwa [Yehova, NW], kapena usakomoke podzudzulidwa ndi iye; pakuti iye amene [Yehova, NW] amkonda amlanga.” (Ahebri 12:5, 6) Ngakhale Yesu “anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo.” (Ahebri 5:8) Ndithudi, nafenso tifunikira kuphunzira chimvero. Onani ziyambukiro zopindulitsa zolola chilango kutilungamitsa. Paulo anatero kuti: “Chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloŵetsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.” Ndi cholimbikitsa chotani nanga chimenecho!—Ahebri 12:11.
15. Kodi ndimotani mmene tingagwiritsire ntchito uphungu wa Paulo wa ‘kusunga njira za miyendo yathu zolongosoka’?
15 Ngati tilandira “chilango cha Yehova” m’nkhaniyi, tidzasunga mu mtima uphungu wabwino wa Paulo wakuti: “Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi mawondo olobodoka; ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu.” (Ahebri 12:12, 13) Nthaŵi zina chiri chopepuka kupatuka pa ‘njira yopapatiza yotsogolera ku moyo.’ (Mateyu 7:14) Mtumwi Petro ndi ena mu Antiyokeya pa nthaŵi ina anali ndi liŵongo la kuchita chimenechi. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti “sanalikuyenda kowongoka, monga mwa chowonadi cha uthenga wabwino.” (Agalatiya 2:14) Lerolino, tiyenera kupitirizabe kumvetsera kwa Mlangizi wathu Wamkulu, Yehova Mulungu. Tifunikira kugwiritsira ntchito mokwanira zithandizo zoperekedwa kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Ichi chidzatsimikizira ‘njira yowongoka’ kumapazi athu.—Mateyu 24:45-47; Yesaya 30:20, 21.
16. (a) Kodi ndimotani mmene “muzu wina wa kuwawa mtima” ungayambire mu mpingo? (b) Kodi nchifukwa ninji Paulo akugwirizanitsa chisembwere ndi kusoŵeka kwa chiyamikiro cha zinthu zopatulika, ndipo kodi ndimotani mmene tingadzichinjirizire ife eni molimbana ndi ngozi zoterozo?
16 Paulo chotsatira akuchenjeza kuti tiyenera “kuyang’anira kuti pangakhale wina wakupereŵera chisomo cha Mulungu, kuti ungaphuke muzu wina wa kuwawa mtima mungavutike inu, ndipo unyinji angadetsedwe nawo.” (Ahebri 12:15) Kukwiyitsidwa, kusakhutiritsidwa, kufunafuna zolakwa m’njira imene zinthu zikuchitidwira mumpingo kungafanane ndi “muzu wina wa kuwawa mtima” womwe ungafalikire mofulumira ndi kuika paizoni m’malingaliro abwino a ena mu mpingo. Tingapeŵetse malingaliro oipa oterowo mwa kupenyetsetsa pa madalitso osaŵerengeka amene chowonadi chabweretsa m’moyo wathu. (Salmo 40:5) Ngozi ina iri ija ya kukhala ndi zikhoterero za chisembwere kapena ‘kupanda chiyamikiro cha zinthu zopatulika, mofanana ndi Esau.’ (Ahebri 12:16) Paulo akuika pamodzi ngozi ziŵiri zimenezi, popeza kuti chimodzi chingatsogolere ku chinzake mosavuta. Palibe Mkristu amene akufunikira kugonjera ku zikhumbo zadyera zoterozo ngati iye agwiritsira ntchito mawu a Petro akuti: “Ameneyo [Mdyerekezi] mumukanize okhazikika m’chikhulupiriro.”—1 Petro 5:9.
“Zinthu Zosapenyeka”
17. Yerekezani zochitika zowopsya pa Phiri la Sinai ndi zija zokumanizidwa ndi Akristu lerolino.
17 Chikhulupiriro chathu chiri chodalira kwenikweni pa “zinthu zosapenyeka.” (Ahebri 11:1) Zina za zinthu zosapenyeka zimenezi Paulo akupitiriza kuzilankhula pa Ahebri 12:18-27. Iye akulongosola zochitika zowopsya pa Phiri la Sinai pamene Mulungu analankhula mwachindunji kwa Israyeli ndi pamene Mose ananena kuti: “Ndiwopatu ndi kunthunthumira.” Mtumwiyo kenaka akuwonjezera kuti: “Komatu mwayandikira ku Phiri la Ziyoni, ndi mudzi wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba, ndi ku unyinji wochuluka wa angelo, ndi kwa msonkhano wa onse.” M’nkhani ya Aisrayeli akale pa Phiri la Sinai, liwu la Mulungu linagwedeza dziko, anatero Paulo, koma tsopano Iye walonjeza, akumanena kuti: “Kamodzi ndidzagwedeza, si dziko lokha, komanso m’mwamba.” Ngakhale kuti mawu ameneŵa alembedwera choyambirira kwa Akristu odzozedwa, “khamu lalikulu” la nkhosa zina lingawaikenso ku mtima. (Chibvumbulutso 7:9) Kodi inu mumayamikira mokwanira zimene Paulo akunena? Tikuima pamaso pa msonkhano wa makumi a zikwi za angelo. Ndithudi, tikuimanso pamaso pa Yehova. Kudzanja lake lamanja kuli Yesu Kristu. Ndithudi, tiri pamalo owopsya kwenikweni ndipo pansi pa thayo lalikulu kuposa mmene analiri Ahebri akale amenewo pa Phiri la Sinai! Ndipo kumbukirani, kugwedeza kwa nkhondo yomadza ya Armagedo kudzapangitsa miyamba yoipa iripoyi ndi dziko lapansi kuthetsedwa. Lerolino motsimikizirika siiri nthaŵi ya “kunyumwa” kumvetsera ku Mawu a Mulungu ndi kuwalabadira!
18. Kodi ndimotani mokha mmene tingapitirizebe kuchitira umboni Yehova, osalema?
18 Chotero mowonadi, tikukhala m’nthaŵi yowopsya kwenikweni m’mbiri ya anthu. Monga Mboni za Yehova, tatumizidwa ku malekezero a dziko lapansi kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu. Kuti tichite tero, tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chimene sichingagwedezeke, chikhulupiriro chimene sichimalema, chikhulupiriro chimene chimatitheketsa kulandira chilango cha Yehova. Ngati tiri ndi chikhulupiriro choterocho, tidzapezedwa pakati pa awo omwe ‘adzapitirizabe kukhala ndi kukoma mtima kwapadera, mwa kumene tingapatse Mulungu molandirika utumiki wopatulika limodzi ndi mantha ndi chinthenthe chaumulungu.’ (Ahebri 12:28, NW) Inde, ndipo tidzapitirizabe kuchitira umboni Yehova ndipo osalema.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji kalata ya Paulo kwa Ahebri iri yopindulitsa kwa ife?
◻ Kodi ndi nkhani iti imene Akristu ayenera kuyang’anizana nayo lerolino?
◻ Kodi ndimotani mmene tingapindulire kuchokera ku mboni zokhulupirika zakale?
◻ Kodi nchifukwa ninji Yehova amalanga awo amene iye amawakonda?
◻ Kodi nchiyani chimene chiri mfungulo ku kuchitira umboni popanda kulema?