Kusamalira Mkwiyo—Wanu ndi wa Ena
TIKUKHALA mu chitaganya choyedzamira ku mkwiyo. Kuchuluka kwa magalimoto pa msewu, mikhalidwe yowombana ndi yomasinthasintha, kusamvana, kusayeruzika, kapena zokwiyitsa zina za tsiku ndi tsiku za moyo zimapangitsa kupsyinjika kokulira. Kupsyinjika kuli kokhoza kuwunjikika, ndipo chifupifupi aliyense ali ndi mlingo wake womalizira. Chotero, tiyenera kuphunzira kukhala omasuka. Tingalowe mu tsiku lirilonse ndi kawonedwe kabwino—kusonyeza kuleza mtima, kulekerera, ndi khalidwe labwino. Ambiri a ife tiri ndi mabanja amene amatikonda. Akristu alinso ndi Akristu anzawo omvera mu mpingo, ndipo pamwamba pa zonse, iwo ali ndi Mbusa wachikondi, Yehova Mulungu. Chotero, palibe chifukwa chakukhala ndi mantha a magwero ofala a mkwiyo: kudzimva kukhala wosungulumwa, wotayidwa.—Masalmo 23:1-6; Ahebri 13:5, 6.
Ngati, ngakhale kuli tero, timva mkwiyo kapena tiyenera kuyang’anizana ndi mkwiyo wa munthu wina, tiyenera kuusamalira iwo bwino lomwe kotero kuti tisunge chimwemwe chathu ndi kukhala kwathu bwino. Motani? Baibulo limatiuza ife: “Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mudzi.” (Miyambo 16:32) Mmalo mwakukhala ofulumira kulingalira kusonyeza mkwiyo, tiyenera kulingalira zotulukapo zothekera za kachitidwe kathu. Kuwerenga kufika ku khumi kungatipewetse ife kuchita chinachake chimene tidzadandaula pambuyo pake.—Miyambo 14:17.
Ngati takwiya ndipo sitikudziwa nchifukwa ninji, modzichepetsa ndi mowona mtima tiyenera kupempha kaamba ka thandizo. Kuwauza ena, makamaka awo amene amatikonda ife, mantha athu kapena kufunika kwathu kwathandizo sichiri chofooka; iri njira yanzeru ndi kulimba mtima. Kenaka tingafike pamuzu wa vutolo. Baibulo limati: “Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.”—Miyambo 15:22.
Kuyesera kumvetsetsa zifukwa zimene ena amachitira mnjira imene iwo amachitira kudzatithandiza ife kuletsa kachitidwe kathu ka malingaliro. Mkuwonjezerapo, ngati tiyankha munthu wokwiya, “ndikumvetsetsa chifukwa chimene wakwiyira,” iye mwamsanga angathetse mkwiyo wake. Baibulo limapereka uphungu: “Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.”—Miyambo 19:11.
Ngati ife mosalingalira tikhumudwitsa wina, timafunikira kumupepesa iye. Mwachitsanzo, ngati wina wake aponda pachala chanu cha kumwendo, mungayedzamire ku kukhala wokwiya. Koma pamene iye apepesa, mkwiyo wanu umazimiririka. Chala chanu chingakhale chikupwetekabe, koma ulemerero wanu walemekezedwa. Mofananamo, makhalidwe abwino kumbali yathu, limodzi ndi ulemu wanthawi zonse ndi khalidwe laumoyo wabwino, lingasungunule chidani ndi kusunga ulemu kulinga kwa ife mu maunansi athu ndi akazi athu, ana, mabwenzi, ndi ziwalo za mpingo Wachikristu.—Miyambo 16:24; Akolose 4:6; 1 Petro 3:8.
Mkuchita ndi mikhalidwe imene imatipangitsa ife kudzimva wokwiya, chimathandiza kudziwa mmene tingalankhulire ponena za mkwiyo wathu popanda kukhumudwitsa munthu wina. Pali kusiyana kotheratu pakati pa kuyambitsa ndewu ndi mawu (“Chitsiru iwe!” kapena, “Ndidzakuwomba mbama pa mphuno!”) ndi kusimba mkwiyo wa wina (“Ndakhumudwitsidwa kwambiri” kapena, “Ndikudzimva wopwetekedwa”). Kuyambitsa ndewu mwa mawu kawirikawiri kumalephera chifukwa chakuti kumayambitsa munthu winayo kubwezera, pamene kusimba mmene akudzimverera sikuli kuputa kwenikweni, ndipo munthu winayo angafulumizidwe kupanga masinthidwe. Monga mmene Baibulo likunenera: “Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mawu owawitsa aputa msunamo. Munthu wozaza aputa makani; koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.”—Miyambo15:1, 18.
Mkwiyo Wolungama
Kwa ambiri a ife chiri chachibadwa kudzimva kukhala okwiya nthawi ndi nthawi. Baibulo limanena kuti ngakhale Yehova amamva mkwiyo. (Zefaniya 2:2, 3; 3:8) Chotero sichiri chodabwitsa kuti munthu, wopangidwa mu chifaniziro Chake, ayenera kukumana ndi malingaliro ofananawo. (Genesis 1:26) Chotero, kudzimva kwa mkwiyo sikuli chimo mwa iko kokha.
Komabe, pamene Yehova wakwiya, nthawi zonse chimakhala ndi chifukwa choyenera: Maprinsipulo olungama anyalanyazidwa. Ndipo kuyankha kwake nthatwi zonse kumakhala kolungama ndipo kumasamaliridwa mwangwiro. Ndi anthu opanda ungwiro chiri chosiyanako. Kawirikawiri timakwiya chifukwa chakuti kunyada kwathu kwapwetekedwa kapena chifukwa cha zofooka zina za anthu. Chotero pafunikira chisamaliro mnjira imene timasamalira mkwiyo wathu. Monga mmene mtumwi Paulo anachenjezera: “Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire, ndiponso musampatse malo Mdyerekezi.” (Aefeso 4:26, 27) Inde, Satana angatenge mwawi wa mkwiyo wathu wosalamuliridwa. Mchenicheni, “zopsya mtima” ziri pakati pa “ntchito zathupi” zimene zimam’letsa munthu kulowa mu Ufumu wa Mulungu.—Agalatiya 5:19-21.
Chimenecho ndi chifukwa chake wophunzira Yakobo anapereka uphungu: “Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale. . . wodekha pa kupsya mtima. Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.” (Yakobo 1:19, 20) Ngakhale ngati mkwiyo wathu uli wolungamitsika, kupanda ungwiro kungatitsogoze ife kuchita m’njira yosalamulirika, njira yolakwa. Chotero, tiyenera nthawi zonse kutsogozedwa ndi prinsipulo ili: “Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; ‘pakuti kwalembedwa, kubwezera kuli kwanga, ine ndidzabwezera, ati [Yehova, NW]’“ (Aroma 12:19) Kumbukirani, kachiwirinso, kuti monga anthu opanda ungwiro, tingakhale olakwa. Chotero, icho chiri cholakwika kuweruza ena mwamsanga mu dzina la kuvutika mtima kolungama.—Yakobo 2:13; 4:11, 12; 5:9.
Malinga ndi Malemba, tikukhala mu nthawi za mapeto. Mu masiku ano otsiriza, amitundu anakwiya” kukwiyira Ufumu wa Mulungu, ndipo Mdyerekezi ali “ndi udani waukulu, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.” (Chivumbulutso 11:17, 18; 12:10-12) Chotero, kukhala kwathu molingana ndi Mawu a Mulungu liri chinjirizo limodzi lokha lenileni kwa ife. (Masalmo 119:105) Mwamsanga Mulungu adzapereka chiweruzo pakati pa amitundu ndipo chisalungamo chonse chidzachotsedwa padziko lapansi. (Yesaya 35:10; 65:23; Mika 4:3, 4) Panthawi ino, tifunikira kukhala otsimikizira kusatsanzira njira za dziko la mkwiyoli. Kuletsa mkwiyo wathu moyenerera kudzatithandiza kusunga chikondi cha m’banja, umodzi wa Chikristu, ndi mtendere waumwini ndi chimwemwe. Ndipo chofunika koposa, chidzatithandiza ife kupitiriza kusangalala ndi chiyanjo cha Yehova Mulungu ndi madalitso ake.—Masalmo 119:165.