Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 9/1 tsamba 13-18
  • Chirimikani Molimbana Ndi Machenjera a Satana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chirimikani Molimbana Ndi Machenjera a Satana
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chizindikiritso Chowona cha Satana
  • Machitachita a Satana ochenjera ndi Achinyengo
  • Ndimotani Mmene Tingapewere Satana ndi Kukhalabe Okhulupirika kwa Mulungu?
  • Khalani Maso Satana Akufuna Kukumezani
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Ziwanda Tingalimbane Nazo Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Mdani wa Moyo Wosatha
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Satana
    Galamukani!—2013
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 9/1 tsamba 13-18

Chirimikani Molimbana Ndi Machenjera a Satana

“Tavalani zida zones za Mulungu kuti mukakhoze kuchirimika pokana machenjera [Chigriki, “machitachita achinyengo”] a Mdyerekezi.”​—AEFESO 6:11.

1. Ndi umboni wotani wakuti Satana alipo umene waperekedwa ndi ziyeso za Yesu?

KODI Satana alikodi? Anthu ena amatsutsa kuti m’Baibulo, “Satana” amalozera kokha ku choipa mkati mwa munthu. Iwo amakana kukhalapo kwake monga cholengedwa. Koma kodi nchiyani chimene Malemba amatiuza ife? Mbiri za Uthenga Wabwino wa Mateyu ndi Luka zimasonyeza kuti Kristu Yesu anayesedwa mwachindunji nthaŵi zitatu ndi Satana, ndipo nthaŵi iriyonse Yesu anamkana iye, mwa kugwiritsira ntchito Lemba. Nchifukwa ninji Yesu anamuyankha iye kuchokera ku Malemba a Chihebri? Chifukwa chakuti Satana anabwera kwa iye akumagwiritsira ntchito molakwa Malemba amenewo ndi cholinga chofuna kumpangitsa iye kuchimwa ndi kulephera monga Mwana wa Mulungu, Mbewu yolonjezedwa.​—Mateyu 4:1-11; Luka 4:1-13.

2. Ndimotani mmene timadziŵira kuti Yesu sanangolingalira zokumana nazo zake ndi Satana?

2 Mwachidziŵikire, Yesu, munthu wangwiro, sanangolingalira zokumana nazo zimenezi. (Ahibri 4:15; 7:26) Iye anakumanizana ndi munthu mmodzimodziyo yemwe anali mphamvu kumbuyo kwa chinjoka mu Edeni, yemwe kale anali mbale wake weniweni waungelo yemwe mibadwo ingapo pasadakhale anawukira ndipo tsopano anatuluka kudzazimiriritsa kukwaniritsidwa kwa Genesis 3:15. Satana anafuna kuswa umphumphu wa Mbewu yoonjezedwayo. Pokhala wanzeru ku machitachita ake achinyengo, Yesu mwamphamvu anakana Woyesayo. Nchiyani chomwe chinali chivomerezo cha Satana? “Ndipo Mdyerekezi, mmene adamaliza mayesero onse, analekana naye kufikira nthaŵi ina.” Mwachidziŵikire, Yesu sanaleke mwa iyemwini! Satana, atakwiyitsidwa, anamuleka iye, “ndipo, onani! Angelo anadza namtumikira [Yesu].”​—Luka 4:13; Mateyu 4:11.

3. Nchiyani chimene katswiri mmodzi wa mbiri yakale akunena ponena za kudziŵika kwa kukhalako kwa Mdyerekezi ku Chikristu?

3 Moyenerera, katswiri mmodzi wa mbiri yakale akuchitira ndemanga kuti: “Kukana kukhalapo ndi kufunika kokulira kwa Mdyerekezi mu Chikristu kuli kutsutsana ndi chiphunzitso cha atumwi ndi kukala kwa m’mbiri kwa chiphunzitso cha Chikristu. Popeza kulongosola Chikristu m’mawu ena kuposa awa kuli kopanda tanthauzo, chiri mwanzeru chosagwirizanitsika kulongosola Chikristu chomwe sichiphatikizapo Mdyerekezi. Ngati Mdyerekezi kulibe, chotero Chikristu chakhala chakufa molakwa m’malo a maziko kuyambira pa chiyambi.”a Mapeto amenewa amapereka chitokoso kwa munthu aliyense pa dziko lapansi lerolino. Kodi mukuzindikira kukhalapo kwa mdani wosawoneka yemwe akufuna kukhotetsa ulamuliro wa Mulungu ndi kugwirizana kwa munthu?

Chizindikiritso Chowona cha Satana

4. Ndimotani mmene cholengedwa chauzimu changwiro chinakhalira Satana?

4 Satana ali cholengedwa chauzimu champhamvu, poyambirira wolengedwa ndi Mulungu monga mngelo, mwana wauzimu wokhala ndi kuyenerera m’mabwalo a kumwamba a Yehova. (Yobu 1:6) Ngakhale kuli tero,? Satana anasonyeza kudzifunira kwaufulu m’kutsutsa Mulungu; ndi machenjera iye anatsogoza Hava ndipo, kupyolera mwa iye, Adamu ku kusamvera ndi imfa. (2 Akorinto 11:3) Chotero, iye anakhala Satana, kutanthauza “Mdani”​—wowukira, chiwanda, wakupa anthu, ndi wabodza. (Yohane 8:44) Kali koyenerera chotani nanga kalongosoledwe ka Paulo kakuti “Satana yemwe adziwonetsa ngati mngelo wakuwunika,” pamene m’chenicheni iye ali ‘wolamulira wa mdima uno’! (2 Akorinto 6:14; 11:14; Aefeso 6:12) Mwa kunyenga angelo ena kuti awukire, iye anawatsogoza iwo kuchoka ku kuwunika kwa Mulungu kulowa mu mdima wake. Iye anakhala “wolamulira wa ziwanda.” Yesu anamuzindikiritsanso iye monga “mkulu wa dziko lapansili.” Mwachidziŵikire, ndi cholinga chofuna kukhala wolamulira, iye ayenera kukhalapo monga munthu wauzimu wolengedwa.​—Mateyu 9:34; 12:24-28; Yohane 16:11.

5. Ndimowonekera chotani mmene Satana wazindikiritsidwira m’Malemba Achikristu a Chigriki?

5 Pamene kuli kwakuti Satana satchulidwa kaŵirikaŵiri m’Malemba a Chihebri, iye wavumbulidwa kotheratu m’Malemba Achikristu a Chigriki​—mokulira kotero kuti timakumanizana ndi dzina lakuti Satana nthaŵi 36 ndi liwu lakuti Mdyerekezi, nthaŵi 33. (Onani Comprehensive Concordance of the New World Translation of the Holy Scriptures.) Iye amazindikiritsidwanso pansi pa maina ena ndi maina aulemu. Aŵiri a amenewa anagwiritsiridwa ntchito ndi Yohane pa Chivumbulutso 12:9: “Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, yotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse.”​—Onaninso Mateyu 12:24-27; 2 Akorinto 6:14, 15.

6. Nchiyani chomwe chiri tanthauzo la liwu lakuti “Mdyerekezi”?

6 Pano mu Chivumbulutso pakuwoneka liwu la Chigriki di·aʹbo·los, lotembenuzidwa “Mdyerekezi.” Mogwirizana ndi wophunzira wa Chigriki J. H. Thayer, ilo m’chenicheni limatanthauza kuti “wonenera moipa, wonenera monyenga, woneneza.” (Yerekezani ndi 1 Timoteo 3:11; 2 Timoteo 3:3, Kingdom Interlinear.) W. E. Vine akulongosola Mdyerekezi kukhala “m’dani wotheratu wa Mulungu ndi munthu.”b

7. Nchifukwa ninji Satana angasumike zoyesayesa zake pa anthu a Yehova?

7 Mdani wamkuluyo Sali wosagwira ntchito. (1 Petro 5:8) Mwinamwake chimenecho ndicho chifukwa chake mwambi umanena kuti, “Mdyerekezi amapeza ntchito kaamba ka manja aulesi kuti aichite.” Iye ali pa ulendo wosokeretsa Akristu onse owona. (2 Timoteo 3:12) Ndipo iye angasumike maganizo pa anthu a Yehova kaamba ka chifukwa chimodzi chopepuka​—iye ali nalo kale dziko lonse m’mphamvu yake! (1 Yohane 5:19) Dziko la lerolino liri dziko la Satana. Iye ali wolamulira wake ndi mulungu, kaya anthu amazindikira icho kapena ayi. (Yohane 12:31; 2 Akorinto 4:4) Monga chotulukapo chake, iye adzakhoterera ku machitachita a chinyengo kapena ochenjera kapena malingaliro ndi cholinga chofuna kusokeretsa anthu a Yehova, kaya monga aliyense payekha kapena monga gulu. Tiyeni tisanthule zina za njira zimene amagwiritsira ntchito.​—Marko 4:14, 15; Luka 8:12.

Machitachita a Satana ochenjera ndi Achinyengo

8. Kodi ndi mwaŵi wotani umene Satana angakhale akugwira nawo ntchito m’kutsutsana ndi ife?

8 Satana wakhala ndi nthaŵi yaitali ya kuphunzira malingaliro a anthu, kulinganiza chibadwa cha anthu ndi zophophonya zawo zobadwa nazo ndi zodzitengera. Iye amadziŵa mmene angaseŵerere pa kufooka kwathu ndi kupanda pake kwathu. Tsopano, nchiyani chomwe chiri mkhalidwe ngati mdani wanu adziŵa zofooka zanu ndipo inu mulephera kuzidziŵa izo inu eni? Mwakutero mumakhala osakonzekeretsedwa bwino kudzichinjiriza inu eni, popeza simuzindikira ming’ankha m’chida chanu zauzimu. (1 Akorinto 10:12; Ahebri 12:12, 13) Ali oyenerera chotani nanga mawu a wolemba ndakatulo wa chiScottish: ‘O kukanakhala kwakuti mphamvu ina inatipatsa ife mphatso ya kudziwona ife eni monga mmene ena amatiwonera ife! Iyo ikanatipulumutsa ife ku zophophonya zambiri.’

9. Nchiyani chomwe chingakhale chotulukapo chopanda chimwemwe ngati tilephera kudzisanthula ife eni ndi kusintha?

9 Kodi tiri ofunitsitsa kudziwona ife eni monga mmene ena amatiwonera​—makamaka monga mmene Mululngu kapena Satana angatiwonere ife? Chimenecho chimafunikira kudzisanthula kwaumwini ndi kudziyesa kowona mtima ndi chifuno cha kupanga masinthidwe. Chinyengo chaumwini chiri chopepuka. (Yakobo 1:23, 24) Ndimotani nanga mmene nthaŵi zina timachepetsera kuti tilungamitse njira yathu ya kachitidwe! (Yerekezani 1 Samueli 15:13-15, 20, 21, 24.) Ndipo chiri chopepuka chotani nanga kunena kuti, “Chabwino, mudziŵa, palibe aliyense amene ali wangwiro!” Chimenecho ndicho chokha chimene Satana amadziŵa, ndipo iye amatenga mwaŵi wa kupanda ungwiro kathu. (2 Samueli 11:2-27) Chiri chomvetsa chisoni chotani nanga kufika m’zaka zapakati ndi kufikira pa kuzindikira kuti chifukwa cha njira yolamulira, ndi yopanda ubwenzi, kapena yopanda chifundo imene wina wachitira ndi ena kwa zaka, wakhala wopanda bwenzi; kapena kuzindikira kuti wachita zochepera kwapena osati chirichonse kupangitsa anthu ena kukhala achimwemwe. Ndi machenjera Satana mwinamwake watitsogoza ife kupyolera m’moyo wa kugwiritsira ntchito dyera lathu lachibadwa kutipangitsa khungu. Talephera kugwira zenizeni za maganizo owona a Kristu​—chikondi, kukoma mtima, ndi chifuno.​—1 Yohane 4:8, 11, 20.

10. Ndi mafunso otani amene tingafunse ponena za ife eni, ndipo nchifukwa ninji?

10 Chotero, ndi cholinga chofuna kuthaŵa Satana, tiyenera kudzisanthula ife eni. Kodi muli ndi chofooka chimene Satana angachidyerere kapena akuchidyerera tsopano lino? Kodi muli ndi vuto la malingaliro? Kodi nthaŵi zonse muyenera kukhala woyambirira? Kodi kunyada kuli mphamvu yanu yosonkhezera yobisika? Kodi nsanje, kusirira, kapena chikondi cha ndalama chimasokoneza umunthu wanu? Kodi mumakwiya msanga? Kodi muli ozizira ndi osakhulupirira? Kapena kodi muli ozindikira mopambanitsa pamene mwapatsida malingaliro kapena kusulizidwa? Kodi mumasutsa kapena ngakhale kukana uphungu? Ngati timazidziŵa ife eni, tingawongolere mvuto oterowo, malinga ngati tiri odzichepetsa. Kupanda apo, tikudzisiya ife eni omasuka kwa Satana.​—1 Timoteo 3:6, 7; Ahebri 12:7, 11; 1 Petro 5:6-8.

11. Ndi manjira yamachenjera yotani imene Satana angayesere kupeputsa uzimu wathu?

11 Satana angakaikirenso uzimu wathu m’njira yochenjera, yonyenga. Mwinamwake timakhumudwitsidwa ponena za njira imene zinthu zikuchitidwira mu mpingo kapena m’gulu. Kaŵirikaŵiri sitimakhala ndi nsonga zonse, koma mopepuka timalumphira ku mapeto. Ngati unansi wathu ndi Yehova uli wofooka, chotero uli sitepi lalifupi ku kulingalira koipa ndi zikaikiro ponena za chowonadi. Ena angayang’ane kaamba ka njira yodzilungamitsa iwo eni kuti achoke ku mathayo amene chowonadi chimapereka. Satana kenaka amaika kusakhulupirika ndi chinyengo m’mitima yawo. Mwamsanga iwo amakhala minkhole ya mpatuko, ndipo Satana amakondwera.​—Luka 22:3-6; Yohane 13:2, 27; 2 Yohane 9-11.

12. (a) Ndimotani mmene ena anyengedwera ndi Satana? (b) Ndimotani mmene Satana amatcherera msampha ambiri kulowa mu mkhalidwe wa chisembwere?

12 Ena akodwa ndi Satana osati kokha mwa kuchita chimo lalikulu loyenerera kuchotsedwa koma afikira pa kukhoterera ku kunama ndi chinyengo ndi cholinga chofuna kuyesera kupusitsa akulu mu mpingo. Mofanana ndi Hananiya ndi Safira, iwo amaganiza kuti anganyenge angelo ndi mzimu woyera wa Mulungu. (Machitidwe 5:1-10) Zikwi zambiri m’zaka zaposachedwapa zagwera mu msampha wa Satana wa mkhalidwe wa chisembwere. Mdyerekezi amadziŵa kuti zisonkhezero za mtundu wa anthu za kugonana ziri zamphamvu, ndipo kupyolera m’dongosolo lake la dziko, iye amawunikira, kukhotetsa, ndi kusokoneza mbali ya mkhalidwe wa kugonana. (Numeri 25:1-3) Akristu osakwatira angayesedwe kugwera m’dama kapena kugwiritsira ntchito kwina kolakwa kwa kugonana. (Miyambo 7:6-23) Ngati Akristu okwatira alola maganizo awo ndi mitima kuyendayenda, iwo mopepuka angagwere mu mkhalidwe woipa, kunyenga mkazi kwa amene analumbira kuti adzakhala okhulupirika.​—1 Akorinto 6:18; 7:1-5; Ahebri 13:4.

13. (a) Ndimotani mmene wailesi ya kanema ingawongolere kulingalira kwathu? (b) Ndimotani mmene tingapewere chisonkhezero choterocho?

13 Tikukhala m’dziko limene kunama, kunyenga, ndi mkwiyo wa chiwawa ziri zofala. Satana amagwiritsira ntchito kotheratu dongosolo lowulutsira mawu kuti afalitse mkhalidwe wa maganizo wonyonyotsoka umenewu. Magwero a mawailesi a kanema kapena maprogramu osatsa malonda amasonyeza anthu owoneka okongola okhala mu ukonde wa kunyenga kovomerezedwa. Ngati tilola kulingalira koteroko kutiyambukira ife, mwamsanga tingayambe kugonjera ku machismo “anng’ono,” omwe amakhala mbali yosongoka ya weja kaamba ka “a akulu.” Malingaliro ochenjera a Satana mopepuka amadziloŵetsa iwo eni m’kulingalira kwathu. Ndimotani mmene tingapewere zisonkhezero zoterozo? “Musampatse malo Mdyerekezi,” monga mmene anachenjezera Paulo. Chimenecho chimatanthauzanso kulamulira amene mumamulola m’nyumba yanu kupyolera pa wailesi ya kanema. Kodi sitiyenera kudana ndi kulowerera kwa anthu achiwawa, a makhalidwe a chisembwere, a pakamwa ponunkha omwe amabweretsa kuipitsa nyumba yathu?​—Aefeso 4:23-32.

Ndimotani Mmene Tingapewere Satana ndi Kukhalabe Okhulupirika kwa Mulungu?

14. Ndi chigamulo cha mbali ziŵiri chiti chimene chifunikira ndi cholinga chofuna kupewa Satana, ndipo kodi icho chimafunikiranji?

14 Ndi mdani wamphamvu woteroyo, woposa anthu akumapangira ukali molimbana ndi ife zolengedwa za umunthu zopanda ungwiro, ndimotani mmene tingasungire umphumphu wathu? Mfungulo ikupezeka m’mawu a Yakobo: “Potero, [dzigonjetsereni inu eni NW], kwa Mulungu; koma kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.” (Yakobo 4:7) Dziŵani kuti uphungu wa Yakobo uli wa mbali ziŵiri. Pamene tikukana Mdyerekezi ndi chifuno chake, tiyenera kudzigonjetsera ife eni ku chifuno cha Mulungu. Chimenecho chimaphatikizapo kukonda chifuno cha Mulungu ndi kudana ndi cha Satana. (Aroma 12:9) Chotero, Yakobo akunena kuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m’manja, ochimwa inu, yeretsani mitima, a mitima iŵiri inu.” (Yakobo 4:8) Inde, m’kupewa kwathu Satana, palibe malo kaamba ka kukhala osadzipereka ndi mtima wonse ndi wa mitima iŵiri. Sitingakhoze kuika pa ngozi umphumphu wathu mwa kuwona kuti ndi mwachifupi motani mmene tingabwere ku mzera wa malire kuchokera ku choipa. Tiyenera “kudana ndi choipa.”​—Salmo 97:10.

15. Nchifukwa ninji “zida zonse za Mulungu” ziri zoyenerera? Chitirani chitsanzo.

15 Uphungu wowonekera pa kupewa Satana ukupezeka pa Aefeso mutu 6. Ndimotani mmene Paulo akunenera kuti tingapewere “machenjera,” “makonzedwe,” kapena “njira” za Satana? (Aefeso 6:11, Phillips, New International Version, The Jerusalem Bible) Tavalani zida zonse za Mulungu,” iye akupereka uphungu. Kalongosoledwe kakuti “zida zonse” sikamasiya malo kaamba ka mkhalidwe wosatsimikizirika kulinga ku Chikristu, mofanana ndi mmene msilikali Wachiroma sakanatha kukhala wosatsimikizira pokonzekera kaamba ka nkhondo. Ndimotani mmene msilikali akachitira ngati iye anadzikonzekeretsa iyemwini ndi zida zones kupatulapo chikopa ndi chisoti? Iye akanalingalira kuti, ‘Icho ndithudi chiri chikopa chachikulu, ndipo chisoti chiri cholemera kwambiri. Izo zimalemera mokulira, ndipo sindizifunikira izo kwenikweni.’ Tangoganizirani mkhalidwewo​—msilikali Wachiroma wokonzekeretsedwa kumenya koma alibe zida zake zokulira zodzichinjirizira.​—Aefeso 6:16, 17.

16. (a) Ndimotani mmene tingatsanzirire chitsanzo cha Yesu m’kugwiritsira ntchito “lupanga” lathu? (b) Ndimotani mmene tingadzichinjirizire molimbana ndi “mvi yoyaka moto” ya Satana, ndipo ndi chotulukapo chotani?

16 Tangolingalirani, kachiŵirinso, msilikali wopanda lupanga. “Lupanga la mzimu” liri chochinjirizira chabwino, popeza limagwiritsiridwa ntchito kuchotsera chida chirichonse chimene Satana amabweretsa pa Mkristu. “Lupanga” lathu nthaŵi zonse liyenera kukhala lokonzekera. Chikakhala m’njira imeneyo ngati sitinyalanyaza phunziro lathu la Baibulo laumwini ndi la banja. Koma mwachidziŵikire, “lupanga . . . Mawu a Mulungu” liri chida chathu choyambira. Yesu analigwiritsira ntchito ilo m’njira zonse ziŵiri. (Mateyu 4:6, 7, 10; 22:41-46) Mofananamo ifenso tiyenera kutero. Tiyenera kupitiriza kuzamitsa chiyamikiro chthu cha chowonadi. Sitingasungilire uzimu wathu pa maziko a zimene tinaphunzira miyezi yathu yoyambirira kapena zaka m’chowonadi. Ngati tilephera kukonzanso kukonzanso chatsopano madera auzimu a maganizo athu, masomphenya athu auzimu akakhala ozimiririka. Changu chathu kaamba ka kulambira kowona kwa Yehova chikazimiririka. Tingakhale ofooka mwauzimu. Sitikakhalanso okhoza kupewa kuwukira kwa achibale, mabwenzi, anzathu, ndi ampatuko omwe angawunjike chitonzo pa zikhulupiriro zathu. Koma Mulungu adzatipulumutsa ife kwa Mdyerekezi ndi “mvi yake yoyaka moto” ngati tipitiriza kudzikonzekeretsa ife eni ndi “zida zonse za Mulungu.”​—Yesaya 35:3, 4.

17, 18. Kodi kumenyana kwathu kuli kolimbana ndi ndani, ndipo kodi ndimotani mmene tingapambanire?

17 Inde, Paulo anagogomezera ngozi yokhudzidwa mu nkhondo ya Mkristu pamene analemba kuti: “Pakuti nkhondo yathu si yolimbana ndi adani aumunthu, koma molimbana ndi mphamvu za mlengalenga, molimbana ndi maukulu olamulira dziko la mdima iri, molimbana ndi mphamvu zoposa za umunthu za choipa za kumwamba.” (Aefeso 6:12, The New English Bible) Kodi ndimotani mmene ife anthu ochepa tingapewere ndi kupambana mu nkhondo yosalinganizika yoteroyo? Paulo akumveketsanso nsonga yake: “Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuima chitsutsire kufika tsiku loipa ndipo, mutachita zonse mudzachirimika.” (Aefeso 6:13) Kalongosoledwa ka mfungulo kali: “Ndipo mutachita zonse.” Ichi kachiŵirinso sichimasiya malo kaamba ka Chikristu chosakhala cha mtima umodzi kapena chocheutsidwa.​—1 Yohane 2:15-17.

18 Chotero, lolani kuti tichirimike m’chowonadi, kukonda chilungamo cha Yehova, kulalikira mbiri yabwino ya mtendere, kugwiritsitsa ndi chikhulupiriro champhamvu m’chipulumutso chomwe Yehova akupereka kupyolera mwa Kristu Yesu, pamene tikudalira pa Mawu a Mulungu monga chirikizo lathu lokulira. (Aefeso 6:14-17) Kumbukirani, Mulungu amasamalira kaamba ka ife, ndipo adzatithandiza kupambana mayeso onse ndi zodetsa nkhaŵa zomwe zingabwere m’njira yathu m’dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu la Satana. Lolani kuti tonsefe tilabadire chenjezo lakuti: “Khalani odzisungira, dikirani. Mdani wanu, Mdyerekezi, monga mkango wobuma ayendayenda ndi kufunafuna wina akamulikwire.” Inde, “ameneyo mumukanize wokhazikika m’chikhulupiriro.”​—1 Petro 5:6-9.

19. (a) Ndi makonzedwe owonjezereka ofunikira otani amene tiyenera kugwiritsira ntchito ndi cholinga chofuna kupewa Satana? (b) Nchiyani chomwe kenaka chidzachitika kwa Satana?

19 Lolani kuti tisaiwale kuwonjezera koyenera kwa Paulo ku “zida.” Iye ananena kuti: “Mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthaŵi yonse mwa mzimu. Ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse.” (Aefeso 6:18) Mdani wathu wosawoneka ali wamphamvu kotero kuti tifunikira “pemphero lonse ndi pembedzero.” Ndi owona ndi osinthasintha, chotani nanga, mmene mapemphero athu ayenera kukhalira! Kudalira kwathu kotheratu pa Yehova kuli kofunika koposa ngati tikayenera kupambana nkhondoyo ndi kusungirira umphumphu. Kokha iye angapereke “mphamvu yoposa ya munthu” yomwe idaztitheketsa ife kupewa Mdani wathu wosatopa. Ndi chitonthozo chotani nanga kudziŵa kuti Mdani wathu wamkulu posachedwapa adzatsekeredwa mu phompho ndipo pomalizira kuwonongedwa kotheratu!​—2 Akorinto 4:7; Chivumbulutso 20:1-3, 10.

[Mawu a M’munsi]

a Satan​—The Early Christian Tradition, la Jeffrey Burton Russell, tsamba 25.

b An Expository Dictionary of New Testament Words.

Kodi Mungayankhe?

◻ Ndimotani mmene timadziŵira kuti Satana ali munthu weniweni?

◻ Nchifukwa ninji maina ena ndi maina a ulemu a Satana ali oyenerera?

◻ Ndi kudzisanthula kwaumwini kotani kumene kungatithandize ife kupewa ziwukiro za machenjera za Satana?

◻ Ndi uphungu uti umene udzatithandiza ife kulaka Satana, ndipo nchifukwa ninji?

[Chithunzi patsamba 15]

Njira imodzi yopeŵera chisonkhezero cha Satana iri kukhala opita kunja, othandiza, achikondi

[Chithunzi patsamba 16]

Tiyenera kudzichinjiriza molimbana ndi kukhala monga Hananiya ndi Safira, omwe angonjera kwa Satana

[Chithunzi patsamba 17]

Kuti tipewe mivi ya Satana, sitingasiye mbali iriyonse ya zida zathu zauzimu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena