Anthu “Akumva Zomwezi Tizimva Ife”
IYE anali mfumu ndi mneneri koma analinso atate wachikondi. Mmodzi mwa ana ake atakula anakhala wachabechabe ndi wodzitukumula. Poyesayesa kulanda ufumuwo, mwana ameneyu anayambitsa nkhondo yapachiŵeniŵeni, ncholinga cha kupha atate wake. Koma pankhondo imene inatsatirapo, anali mwana ameneyu amene anaphedwa. Pamene atatewo anazindikira za imfa ya mwanayo, iwo anakwera kuchipinda chosanja nalira kuti: “Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!” (2 Samueli 18:33) Atatewo anali Mfumu Davide. Monga aneneri ena onse a Yehova, iye anali “munthu wakumva zomwezi tizimva ife.”—Yakobo 5:17.
M’nthaŵi za Baibulo amuna ndi akazi amene analankhulira Yehova anali anthu a mikhalidwe yosiyanasiyana ndipo anali anthu wamba. Monga ife, iwo anakumananso ndi mavuto ndipo anali kuphophonya. Kodi ena mwa aneneri ameneŵa ndi ayani, nanga kodi iwo anamva motani zomwezi tizimva ife?
Mose Anachoka pa Kudzidalira Kopambanitsa Nafika pa Kufatsa
Mneneri wodziŵika kwambiri amene anakhalako Chikristu chisanadze anali Mose. Komabe, ngakhale pamene anali ndi zaka 40 zakubadwa, iye anali asanayenererebe kutumikira monga wolankhulira Yehova. Chifukwa chiyani? Pamene abale ake anali kuzunzidwa ndi Farao wa ku Igupto, Mose analeredwera m’banja la Farao ndipo anali “wamphamvu m’mawu ake ndi m’ntchito zake.” Mbiri imasimba kuti: “Anayesa kuti abale ake akazindikira kuti Mulungu alikuwapatsa chipulumutso mwa dzanja lake.” Chifukwa cha kudzidalira kopambanitsa, iye anachinjiriza mwaukali kapolo wachihebri, napha Mwaigupto.—Machitidwe 7:22-25; Eksodo 2:11-14.
Panthaŵiyi Mose anakakamizika kuthaŵa, ndipo anatha zaka 40 zotsatira akugwira ntchito monga mbusa kudziko lakutali la Midyani. (Eksodo 2:15) Pambuyo pake, Mose, amene tsopano anali ndi zaka 80 zakubadwa, anatumidwa ndi Yehova monga mneneri. Koma tsopano Mose sanalinso wodzidalira kopambanitsa. Iye anaona kuti anali wosayenerera nkomwe kuchita zimenezo kotero kuti anakayika zakuti Yehova angamtume monga mneneri, ndipo anagwiritsira ntchito mawu monga akuti, “Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao?” ndiponso anati, ‘Ndikanena chiyani?’ (Eksodo 3:11, 13) Mothandizidwa ndi chilimbikitso ndi chithandizo chachikondi cha Yehova, Mose anakagwira ntchito yakeyo mwachipambano chachikulu.
Kodi inuyo, mofanana ndi Mose, munanenapo kapena kuchitapo zinthu zopanda nzeru chifukwa cha kudzidalira kopambanitsa? Ngati zili choncho, muyenera kulandira maphunziro owonjezereka modzichepetsa. Kapena kodi munadzimvapo kukhala wosayenerera kuchita ntchito zinazake zachikristu? M’malo mokana kuzichita, muyenera kulandira chithandizo choperekedwa ndi Yehova ndi gulu lake. Amene anathandiza Mose angakuthandizeninso.
Eliya Anamva Zomwezi Tizimva Ife Panthaŵi Yopereka Chilango
“Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwa mvula padziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi.” (Yakobo 5:17) Pemphero la Eliya linali logwirizana ndi chifuniro cha Yehova chakuti alange mtundu umene unapandukira Iye. Komabe, Eliya anadziŵa kuti chirala chimene anali kuchipempherera chinali kudzazunza anthu. Israyeli anali kudalira kwambiri ulimi; mame ndi mvula ndizo zimene zinali kusunga moyo wa anthu. Chirala chosatha chikanadzetsa mavuto aakulu. Zomera zikanauma; mbewu zikanalephera kukula. Ziŵeto zogwiritsira ntchito ndiponso zimene anali kudya zikanafa, ndipo mabanja ena akanavutika ndi njala. Kodi ndani amene akanavutika kwambiri? Anthu wamba. Mkazi wamasiye anauza Eliya pambuyo pake kuti anali ndi ufa wodzala dzanja limodzi ndi mafuta pang’ono. Mkaziyo anatsimikiza kuti iye ndi mwana wake mosakayika konse adzafa ndi njala posachedwa. (1 Mafumu 17:12) Kuti Eliya apemphere, iye anali ndi chikhulupiriro cholimba chakuti Yehova adzasamalira atumiki Ake—olemera kapena osauka—amene sanasiye kulambira koona. Monga momwe mbiri yolembedwa imasonyezera, Eliya sanagwiritsidwe mwala.—1 Mafumu 17:13-16; 18:3-5.
Patapita zaka zitatu, pamene Yehova ananena kuti adzagwetsa mvula posachedwa, Eliya anasonyeza kuti anali wofunitsitsa kuti chirala chithe mwa mapemphero ake obwerezabwereza ochokera pansi pa mtima pamene ‘anagwadira pansi, naika nkhope yake pakati pa maondo ake.’ (1 Mafumu 18:42) Iye anauza mnyamata wake mobwerezabwereza kuti: “Kwera kapenyerere kunyanja” pofuna kuti akaone zinthu zosonyeza kuti Yehova anayankha mapemphero ake. (1 Mafumu 18:43) Ndipo ayenera kuti anasangalala chotani nanga pamene pomalizira pake, poyankha mapemphero ake, “m’mwamba munatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zake”!—Yakobo 5:18.
Ngati ndinu kholo kapena mkulu wa mumpingo wachikristu, mungafunikire kulimbana ndi malingaliro opweteka pamene mupereka chilango. Komabe, malingaliro amenewo aumunthu ayenera kuchepetsedwa podziŵa kuti chilango chimakhala chofunikira nthaŵi zina ndiponso podziŵa kuti pamene chiperekedwa mwachikondi, icho ‘chimapereka chipatso cha mtendere, ndicho cha chilungamo.’ (Ahebri 12:11) Zotsatirapo za kumvera malamulo a Yehova nthaŵi zonse zimakhala zosangalatsa. Monga Eliya, tikupemphera kuchokera pansi pa mtima kuti malamulowo atsatiridwe.
Yeremiya Anasonyeza Kulimba Mtima Mosasamala Kanthu za Zokhumudwitsa
Mwa anthu onse amene analemba Baibulo, mwinamwake Yeremiya ndiye amene analemba zambiri ponena za mmene anali kumverera. Monga mnyamata, iye anakayika zovomera kugwira ntchito imene anapatsidwa. (Yeremiya 1:6) Komabe, iye anagwira ntchitoyo molimba mtima nalalikira mawu a Mulungu, koma anayang’anizana ndi chitsutso chachikulu chochokera kwa Aisrayeli anzake—kungoyambira mfumu yake ndi anthu wamba omwe. Chitsutso chimenecho nthaŵi zina chinali kumkwiyitsa ndi kumliritsa misozi. (Yeremiya 9:3; 18:20-23; 20:7-18) Panthaŵi zosiyanasiyana iye anafwambidwa, kumenyedwa, kuikidwa m’goli, kuponyedwa m’ndende, kuopsezedwa ndi imfa, ndi kusiyidwa m’matope kuti afe pansi pa chitsime chopanda madzi. Nthaŵi zina ngakhale uthenga wa Yehova weniweniwo unali wopweteka, monga momwe zikusonyezedwera ndi mawu ake akuti: “Matumbo anga, matumbo anga! ndipoteka pamtima panga penipeni.”—Yeremiya 4:19.
Komatu iye anakondabe mawu a Yehova, nanena: “Mawu anu anakhala kwa ine chikondwerero ndi chisangalalo cha mtima wanga.” (Yeremiya 15:16) Panthaŵi imodzimodziyo, iye analirira Yehova chifukwa cha kukhumudwa nanena: ‘Mwakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera,’ monga madzi a m’dambo limene limaphwa msanga. (Yeremiya 15:18) Komabe, Yehova anazindikira kusweka maganizo kwake ndipo anapitiriza kumchirikiza pofuna kuti akwaniritse ntchito yake.—Yeremiya 15:20; onaninso 20:7-9.
Monga Yeremiya, kodi inu mumakhumudwanso kapena kuyang’anizana ndi chitsutso pamene muchita utumiki wanu? Yang’anani kwa Yehova. Pitirizani kutsatira chitsogozo chake, ndipo Yehova adzakupatsaninso mphotho chifukwa cha zoyesayesa zanu.
Yesu Anali Wakumva Zomwezi Tizimva Ife
Mneneri wamkulu woposa onse amene anakhalako anali Mwana weniweniyo wa Mulungu, Yesu Kristu. Ngakhale kuti anali munthu wangwiro, iye sanabise malingaliro ake. Nthaŵi zambiri timaŵerenga za mmene iye anali kumvera mkati mwake, zimene ziyenera kuti zinaonekera pankhope yake ndi mmene anali kuchitira kwa ena. Nthaŵi zambiri Yesu anali ‘kugwidwa chifundo,’ ndipo anali kugwiritsira ntchito mawu amodzimodziwo pofotokoza za anthu a m’mafanizo ake.—Marko 1:41; 6:34; Luka 10:33.
Iye ayenera kuti anafuula pamene anatulutsa anthu ochita zamalonda ndiponso ziŵeto m’kachisi nanena kuti: “Chotsani izi muno”! (Yohane 2:14-16) Malingaliro a Petro akuti, “Dzichitireni chifundo,” anampangitsa kuti amuyankhe mwaukali kuti, “Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe.”—Mateyu 16:22, 23.
Yesu anali kukonda kwambiri anthu ena amene makamaka anali oyandikana naye kwambiri. Mtumwi Yohane anatchulidwa kuti anali “wophunzira uja amene Yesu anamkonda.” (Yohane 21:7, 20) Ndipo timaŵerenga kuti: “Koma Yesu anakonda Marita, ndi mbale wake, ndi Lazaro.”—Yohane 11:5.
Yesu anali kuswekanso maganizo. Atamva chisoni chachikulu chifukwa cha imfa ya Lazaro, “Yesu analira.” (Yohane 11:32-36) Posonyeza kupwetekedwa mtima chifukwa cha kuperekedwa kwake ndi Yudasi Isikariote, Yesu anagwira mawu odandaula kuchokera m’Masalmo akuti: “Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine chidendene chake.”—Yohane 13:18; Salmo 41:9.
Ngakhale pamene anali kumva ululu waukulu pamtengo, Yesu anasonyeza chifundo chake. Mwachikondi, iye anaika amayi wake m’manja mwa “wophunzira amene anamkonda.” (Yohane 19:26, 27) Pamene anaona kuti mmodzi mwa anthu ochita zoipa amene anapachikidwa naye pamodzi anasonyeza kulapa, Yesu analankhula mwachifundo nati: “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Tingazindikire kuti anamva chisoni kwambiri pamene analira kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?” (Mateyu 27:46) Ndipo mawu ake pakufa akuti, “Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga,” amasonyeza chikondi chake chochokera pansi pa mtima ndi chidaliro chake.—Luka 23:46.
Zimenezi zikutipatsa chitsimikizo chotani nanga! “Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma [Yesu] wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.”—Ahebri 4:15.
Chidaliro cha Yehova
Yehova sanagwiritsidwe mwala konse ndi anthu omlankhulira amene iye anawasankha. Anadziŵa kuti iwo anali okhulupirika kwa iye, ndipo mwachifundo ananyalanyaza zofooka za anthu amene anali opanda ungwiro. Komabe, iye anafunitsitsa kuti iwo akwaniritse ntchito imene anapatsidwa. Mwa chithandizo chake iwo anachita zimenezo.
Moleza mtima tiyeni tizisonyeza chidaliro mwa abale ndi alongo athu okhulupirika. Iwo adzakhalabe opanda ungwiro m’dongosolo lino la zinthu, monga momwe ife tidzakhalira. Komabe, sitiyenera konse kuweruza abale athu kuti ngosayenerera chikondi ndi chisamaliro chathu. Paulo analemba kuti: “Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.”—Aroma 15:1; Akolose 3:13, 14.
Aneneri a Yehova anamvanso zonse zimene tizimva ife. Komabe, anadalira Yehova, ndipo Yehova anawachirikiza. Kuwonjezera pamenepo, Yehova anawapatsa zifukwa zokhalira ndi chimwemwe—chikumbumtima choyera, kuyanjidwa ndi iye, mabwenzi okhulupirika amene anawachirikiza, ndiponso lonjezo la mtsogolo mwachimwemwe. (Ahebri 12:1-3) Ifenso tiyenera kumamatira kwa Yehova ndi chidaliro chonse pamene titsanzira chikhulupiriro cha aneneri akale, anthu “akumva zomwezi tizimva ife.”