Malangizo Omwe Angatithandize Kulamulira Lilime Lathu
‘KAYA ndimaneneranji zimene zija?’ Kodi munanenapo mawu amenewa? Tonsefe timavutika kulamulira lilime lathu. Baibulo limati tikhoza kuweta pafupifupi nyama iliyonse, “koma lilime, palibe munthu ndi mmodzi yemwe angathe kuliweta.” (Yakobo 3:7, 8) Kodi ndiye kuti tisamayesere n’komwe kulamulira lilime lathu? Ayi. Taganizirani mfundo zina za m’Baibulo zimene zingatithandize kulamulira lilime lathu, lomwe ndi kachiwalo kakang’ono koma kamphamvu kwambiri.
● “Pakachuluka mawu sipalephera kukhala zolakwa, koma wodziwa kulamulira milomo yake amachita zinthu mwanzeru.” (Miyambo 10:19) Tikamalankhula kwambiri, m’pamenenso timatha kunena zinthu zopanda nzeru kapena zimene ena angakhumudwe nazo. Lilime losalamulirika limakhala ngati moto chifukwa limatha kumangofalitsa miseche ndiponso nkhani zabodza zimene zingaike ena m’mavuto. (Yakobo 3:5, 6) Koma ‘tikamalamulira milomo yathu,’ kapena kuti kuganiza kaye tisanalankhule, timadziwa mmene zolankhula zathu zingakhudzire ena. Tikamatero, timadziwika kuti ndife anthu anzeru ndipo ena amatilemekeza komanso amatidalira.
● “Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula, wosafulumira kukwiya.” (Yakobo 1:19) Anthu ena amasangalala tikamamvetsera mwatcheru pamene akulankhula, chifukwa tikatero timasonyeza kuti tili ndi chidwi ndi zimene akunenazo komanso timawalemekeza. Koma bwanji ngati winawake atanena zinazake zopweteka kapena zopsetsa mtima? Ndi bwino kuyesetsa kuti ‘tisafulumire kukwiya’ ndipo tisabwezere. Mwina munthuyo anakhumudwa ndi zinazake ndiponso n’kutheka kuti akhoza kukupepesani pambuyo pake chifukwa cha zimene wanena. Kodi inuyo muli ndi vuto lofulumira kukwiya? Ngati ndi choncho, muyenera kupemphera kwa Mulungu kuti akuthandizeni kudziletsa. Ngati mutamupempha ndi mtima wonse, iye adzakuthandizani.—Luka 11:13.
● “Lilime lofatsa likhoza kuthyola fupa.” (Miyambo 25:15) Anthu ambiri amaganiza kuti munthu ukakhala wofatsa ndiye kuti ndiwe wopusa, koma zimenezi si zoona. Mwachitsanzo, kuyankha mofatsa kumafewetsa anthu a mitima yolimba ngati fupa, amene amatitsutsa chifukwa chokwiya ndi zinazake kapena chifukwa cha tsankho. Kunena zoona, kukhala wofatsa kumavuta kwambiri makamaka munthu akatiputa. Koma muziganizira ubwino wotsatira zimene Baibulo limanena komanso kuipa kozinyalanyaza.
Kunena zoona, mfundo za m’Baibulo ndi “nzeru yochokera kumwamba.” (Yakobo 3:17) Tikagwiritsa ntchito nzeru zimenezi polankhula, mawu athu amakhala aulemu, achikondi ndiponso olimbikitsa. Nthawi zonse amakhala oyenera, ngati “zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.”—Miyambo 25:11.