Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 11/1 tsamba 13-18
  • Kukhala m’Dziko Koma Osakhala Mbali Yake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhala m’Dziko Koma Osakhala Mbali Yake
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukula kwa Maulamuliro a Dziko Lonse
  • Ulamuliro Ukudzawo wa Ufumu wa Mulungu
  • Kupeŵa “Chilembo” cha “Chilombo”
  • “Chilombo” ndi “Kaisara”
  • Nzika Zotsatira Chikumbumtima
  • Akristu Osaloŵerera M’zinthu za Dziko M’masiku Otsiriza
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Mulungu ndi Kaisara
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kodi Mukuchirikiza Dziko la Satana, kapena Dongosolo Latsopano la Mulungu?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Dziko
    Kukambitsirana za m’Malemba
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 11/1 tsamba 13-18

Kukhala m’Dziko Koma Osakhala Mbali Yake

“Popeza simuli a dziko lapansi, . . . likudani inu.”​—YOHANE 15:19.

1. Kodi Akristu ali paunansi wotani ndi dziko lapansi, komabe kodi dziko lapansi limawaona motani?

PAUSIKU wake womaliza ndi ophunzira ake, Yesu anawauza kuti: “Simuli a dziko lapansi.” Kodi anali kunena za dziko lapansi liti? Kodi poyamba sananene kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha”? (Yohane 3:16) Ndithudi ophunzira anali mbali ya dziko lapansi limenelo chifukwa chakuti ndiwo anali oyamba kukhulupirira Yesu kuti apeze moyo wosatha. Ndiye nchifukwa ninji Yesu tsopano ananena kuti ophunzira ake anali olekanitsidwa ndi dziko? Ndipo nchifukwa ninji ananenanso kuti: “Popeza simuli a dziko lapansi, . . . chifukwa cha ichi likudani inu”?​—Yohane 15:19.

2, 3. (a) Kodi ndi “dziko lapansi” liti limene Akristu sayenera kukhala mbali yake? (b) Kodi Baibulo limati bwanji ponena za “dziko lapansi” limene Akristu siali mbali yake?

2 Yankho ndilo lakuti Baibulo limagwiritsira ntchito mawuwo “dziko lapansi” (Chigiriki, koʹsmos) m’njira zosiyanasiyana. Monga momwe tinafotokozera m’nkhani yoyambayo, nthaŵi zina m’Baibulo “dziko lapansi” limatanthauza anthu onse. Ili ndilo dziko limene Mulungu anakonda ndiponso limene Yesu anafera. Komabe, The Oxford History of Christianity ikuti: “‘Dziko lapansi’ m’Chikristu ali mawu otanthauzanso chinthu cholekanitsidwa ndi Mulungu ndipo chokhala paudani ndi iye.” Kodi zimenezi nzoona motani? Wolemba wachikatolika Roland Minnerath, m’buku lake lakuti Les chrétiens et le monde (Akristu ndi Dziko Lapansi), akufotokoza kuti: “Choncho m’tanthauzo lake lonyoza, dziko lapansi limaonedwa kukhala . . . dziko mmene maulamuliro otsutsana ndi Mulungu akuchita ntchito zawo ndipo dziko limene chifukwa cha kutsutsana kwake ndi ulamuliro wolakika wa Kristu lili ufumu wodana naye wolamuliridwa ndi Satana.” “Dziko lapansi” limeneli ndilo anthu onse olekanitsidwa ndi Mulungu. Akristu oona saali mbali ya dziko lapansi limeneli, ndipo limawada.

3 Chakumapeto kwa zaka za zana loyamba, Yohane anali kunena za dziko limeneli pamene analemba kuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye. Pakuti chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.” (1 Yohane 2:15, 16) Analembanso kuti: “Tidziŵa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Yesu iye mwini anatcha Satana kuti “mkulu wa dziko ili lapansi.”​—Yohane 12:31; 16:11.

Kukula kwa Maulamuliro a Dziko Lonse

4. Kodi maulamuliro a dziko lonse anakhalapo motani?

4 Dziko la anthu limene lilipoli lolekanitsidwa ndi Mulungu linayamba kukula Chigumula cha m’tsiku la Nowa chitangotha, pamene mbadwa zambiri za Nowa zinaleka kulambira Yehova Mulungu. Wotchuka m’masiku oyambirirawo anali Nimrode, womanga mzinda ndipo “mpalu wamphamvu wotsutsana ndi Yehova.” (Genesis 10:8-12, NW) M’zakazo dzikoli kwenikweni linali la mizinda yomwe inali maufumu aang’ono, amene nthaŵi ndi nthaŵi anaphatikana ndi kuthirana nkhondo. (Genesis 14:1-9) Maufumu ena a mizinda analanda ena mphamvu ndi kukhala maulamuliro a chigawocho. Maulamuliro ena a zigawo m’kupita kwa nthaŵi anakula ndi kukhala maulamuliro amphamvu a dziko lonse.

5, 6. (a) Kodi maulamuliro a dziko lonse asanu ndi aŵiri a m’mbiri ya Baibulo ndi ati? (b) Kodi nchiyani chimaphiphiritsira maulamuliro a dziko lonse ameneŵa, ndipo kodi mphamvu yawo imachokera kuti?

5 Potsatira njira ya Nimrode, olamulira m’maulamuliro a dziko lonse sanali kulambira Yehova, zimene zinasonyezedwa ndi zochita zawo zankhanza ndi zachiwawa. Malemba amaphiphiritsira maulamuliro a dziko lonse ameneŵa ndi nyama zakuthengo, ndipo pazaka mazana onsewa, Baibulo latchula asanu ndi umodzi amene anakhudza kwambiri anthu a Yehova. Ameneŵa anali Igupto, Asuri, Babulo, Amedi ndi Aperisi, Grisi, ndi Roma. Ulamuliro wa dziko lonse wachisanu ndi chiŵiri unaloseredwa kuti udzakhalapo Roma atapita. (Danieli 7:3-7; 8:3-7, 20, 21; Chivumbulutso 17:9, 10) Umenewu unadzakhala Ulamuliro wa Dziko Lonse wa Anglo-America, wopangidwa ndi Ufumu wa Britain ndi wogwirizana naye wake United States, amene m’kupita kwa nthaŵi mphamvu zake zinaposa Britain. Ufumu wa Britain unayamba kukula gawo lomaliza la Ufumu wa Roma litatha.a

6 Buku la Chivumbulutso limaphiphiritsira maulamuliro a dziko lonse asanu ndi aŵiri otsatizanawa ndi mitu ya chilombo cha mitu isanu ndi iŵiri chotuluka m’nyanja ya anthu osakhazikika. (Yesaya 17:12, 13; 57:20, 21; Chivumbulutso 13:1) Kodi ndani akupatsa chilombo cholamulira chimenechi mphamvu imene chili nayo? Baibulo likuyankha kuti: “Chinjoka chinampatsa iye mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.” (Chivumbulutso 13:2) Chinjokacho si winanso koma Satana Mdyerekezi.​—Luka 4:5, 6; Chivumbulutso 12:9.

Ulamuliro Ukudzawo wa Ufumu wa Mulungu

7. Kodi Akristu akuyembekezera chiyani, ndipo ndi motani mmene chimenechi chimakhudzira unansi wawo ndi maboma a dziko?

7 Kwa zaka pafupifupi 2,000, Akristu apemphera kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Mboni za Yehova zimadziŵa kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene ungadzetse mtendere weniweni padziko lapansi. Pokhala otsatira bwino kwambiri maulosi a Baibulo, iwo amakhulupirira zedi kuti pemphero limeneli lidzayankhidwa posachedwapa ndi kuti Ufumuwo posachedwapa udzalamulira zinthu za padziko lapansi. (Danieli 2:44) Kumamatira kwawo ku Ufumu umenewu kumawapangitsa kusunga uchete pankhani za maboma a dziko lapansi.

8. Kodi maboma achitanji ndi ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, monga kunaloseredwera mu Salmo 2?

8 Maiko ena amanena kuti akutsata malamulo achipembedzo. Komabe, mwa zochita zawo amanyalanyaza choonadi chakuti Yehova ndiye Mfumu ya Chilengedwe Chonse ndi kuti waika Yesu kukhala Mfumu yakumwamba yolamulira dziko lapansi. (Danieli 4:17; Chivumbulutso 11:15) Salmo laulosi limati: “Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake [Yesu], ndi kuti, Tidule zomangira zawo, titaye nsinga zawo.” (Salmo 2:2, 3) Maboma safuna “zomangira” kapena “nsinga” za Mulungu zimene zingaike malire pa ufulu wa kudzilamulira m’maiko awo. Chotero, Yehova akunena kwa Yesu, Mfumu yake yosankhidwa, kuti: “Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale choloŵa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako. Udzawatyola ndi ndodo yachitsulo; udzawaphwanya monga mbiya ya woumba.” (Salmo 2:8, 9) Komabe, dziko la mtundu wa anthu limene Yesu anafera ‘silidzatyoledwa’ kotheratu.​—Yohane 3:17.

Kupeŵa “Chilembo” cha “Chilombo”

9, 10. (a) Kodi m’buku la Chivumbulutso tikuchenjezedwa za chiyani? (b) Kodi kulandira ‘chilembo cha chilombo’ kumaphiphiritsira chiyani? (c) Ndi zizindikiro ziti zimene atumiki a Mulungu amavomereza?

9 Chivumbulutso chimene mtumwi Yohane analandira chinachenjeza kuti dziko la mtundu wa anthu lolekanitsidwa ndi Mulungu lidzafuna zambiri litatsala pang’ono kutha, kuchita “kuti onse, aang’ono ndi aakulu, achuma ndi osauka, ndi mfulu ndi akapolo, alandire chilembo pa dzanja lawo ndi pamphumi pawo; ndi kuti munthu sangakhoze kugula kapena kugulitsa, koma iye yekha wakukhala nacho chilembo.” (Chivumbulutso 13:16, 17) Kodi zimenezi zimatanthauzanji? Chilembo padzanja lamanja chili chizindikiro choyenerera chosonyeza kuchirikiza mokangalika. Nanga chilembo cha pamphumi chimatanthauzanji? The Expositor’s Greek Testament imati: “Tanthauzo lophiphiritsira kwambiri limeneli linatengedwa pa kachitidwe kolemba asilikali ndi akapolo chizindikiro china choonekera . . . ; kapenanso, makamaka, mwambo wachipembedzo wa kuvala dzina la mulungu monga chithumwa.” Anthu ambiri mwa zochita zawo ndi mawu awo mophiphiritsira amavala chilembo chimenechi, chowadziŵikitsa kuti ndi “akapolo” kapena “asilikali” a “chilombo.” (Chivumbulutso 13:3, 4) Ponena za tsogolo lawo, Theological Dictionary of the New Testament ikuti: “Adani a Mulungu akulola [chizindikiro] cha chilombo, nambala yachinsinsi yokhala ndi dzina la chilombocho, kuti chilembedwe pamphumi pawo ndi padzanja limodzi. Zimenezi zikuwapatsa mwaŵi waukulu wopita patsogolo m’zachuma ndi m’zamalonda, koma zikuwadzetsera mkwiyo wa Mulungu ndipo zikuwachotsa mu ufumu wa zaka chikwi, Chiv. 13:16; 14:9; 20:4.”

10 Kulimbana ndi zikakamizo za kulandira “chilembo” kumafuna kulimbadi mtima ndi chipiriro. (Chivumbulutso 14:9-12) Komabe, atumiki a Mulungu ali nayo nyonga imeneyo ndipo ndiye chifukwa chake nthaŵi zambiri amadedwa ndi kunenezedwa. (Yohane 15:18-20; 17:14, 15) M’malo mokhala ndi chizindikiro cha chilombo, Yesaya ananena kuti iwo adzalemba mophiphiritsira padzanja lawo kuti, “Ndine wa Yehova.” (Yesaya 44:5) Ndiponso, popeza “akuusa moyo ndi kulira” chifukwa cha zonyansa zochitidwa ndi chipembedzo champatuko, iwo akulandira chizindikiro chophiphiritsira pamphumi pawo chowadziŵikitsa kuti sayenera kulangidwa pamene ziweruzo za Yehova ziperekedwa.​—Ezekieli 9:1-7.

11. Ndani amapereka chilolezo choti maboma a anthu alamulire mpaka Ufumu wa Mulungu utadza kudzatenga ulamuliro wa dziko lapansi?

11 Mulungu akulola maboma a anthu kulamulira mpaka nthaŵi yoti Ufumu wa kumwamba wa Kristu utenge ulamuliro wonse wa dziko lapansi. Profesa Oscar Cullmann m’buku lake lakuti The State in the New Testament anatchulapo za kulekereredwa kwa maboma andale ndi Mulungu kumeneku. Analemba kuti: “Lingaliro losamvetsetseka lakuti Boma ndi ‘lapakanthaŵi’ ndilo linachititsa Akristu oyambirira kuti asamayanjane ndi Boma nthaŵi zina, komabe lingalirolo limaoneka monga lotsutsana ndi Boma. Ndigogomezera kuti limaoneka ngati lotero. Tingatchule chabe Aroma 13:1, ‘Munthu aliyense agonjere maulamuliro . . . ’ limodzi ndi Chivumbulutso 13: Boma monga chilombo chotuluka pansi.”

“Chilombo” ndi “Kaisara”

12. Kodi ndi lingaliro loyenerera lotani limene Mboni za Yehova zili nalo ponena za maboma a anthu?

12 Kungakhale kulakwitsa kunena kuti anthu onse m’maulamuliro a maboma ali antchito a Satana. Ambiri adzisonyeza kukhaladi anthu a mapulinsipulo abwino, monga kazembe Sergio Paulo amene m’Baibulo akufotokozedwa kukhala “munthu wanzeru.” (Machitidwe 13:7) Olamulira ena molimba mtima achirikiza zoyenera za anthu osiyana ndi ena, motsogozedwa ndi chikumbumtima chawo chopatsidwa ndi Mulungu ngakhale kuti sanadziŵe Yehova ndi zifuno zake. (Aroma 2:14, 15) Kumbukirani kuti Baibulo limagwiritsira ntchito mawuwo “dziko lapansi” m’njira ziŵiri zosiyana: dziko la anthu, limene Mulungu amakonda ndipo limene tiyenera kulikonda, ndi dziko la anthu olekanitsidwa ndi Yehova, limene Satana ndiye mulungu wake ndipo limene tiyenera kupatukana nalo. (Yohane 1:9, 10; 17:14; 2 Akorinto 4:4; Yakobo 4:4) Choncho, atumiki a Yehova ali ndi lingaliro loyenerera ponena za ulamuliro wa anthu. Timasunga uchete pankhani zandale popeza tikutumikira monga akazembe kapena nthumwi zoimira Ufumu wa Mulungu ndipo tinapatulira miyoyo yathu kwa Mulungu. (2 Akorinto 5:20) Komabe, timagonjera aulamuliro malinga ndi chikumbumtima chathu.

13. (a) Kodi Yehova amawaona motani maboma a anthu? (b) Kodi Mkristu angagonjere maboma a anthu kufikira pati?

13 Lingaliro loyenerera limeneli limasonyeza lingaliro lenileni la Yehova Mulungu. Pamene maulamuliro a dziko, kapena ngakhale Maboma aang’ono kwambiri, agwiritsira ntchito molakwa ulamuliro wawo, kupondereza anthu awo, kapena kuzunza amene amalambira Mulungu, iwo amayenereradi mafotokozedwe aulosi akuti ali zilombo zolusa. (Danieli 7:19-21; Chivumbulutso 11:7) Komabe, pamene maboma a maiko achita chifuno cha Mulungu posungitsa lamulo ndi bata mwachilungamo, amawaona kukhala “atumiki” ake. (Aroma 13:6) Yehova amayembekezera anthu ake kulemekeza maboma a anthu ndi kuwagonjera, koma kugonjera kwawo kuli ndi polekezera. Pamene anthu afuna kwa atumiki a Mulungu zinthu zoletsedwa ndi lamulo la Mulungu kapena pamene aletsa zinthu zimene Mulungu akufuna kuti atumiki ake achite, atumiki akewa amatsatira kaimidwe kamene atumwi anatenga, kakuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”​—Machitidwe 5:29.

14. Kodi kugonjera maboma a anthu kwachikristu kukulongosoledwa motani ndi Yesu? ndi Paulo?

14 Yesu ananena kuti otsatira ake adzakhala ndi mangawa ponse paŵiri kwa maboma ndi kwa Mulungu pamene anati: “Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.” (Mateyu 22:21) Mouziridwa, mtumwi Paulo analemba kuti: “Anthu onse amvere maulamuliro aakulu; . . . Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa. Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale omvera, sichifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbumtima. Pakuti chifukwa cha ichi mupatsanso msonkho.” (Aroma 13:1, 4-6) Chiyambire zaka za zana loyamba C.E. mpaka lero, Akristu amayamba aganiza pamene Boma lafuna chinthu kwa iwo. Amayamba azindikira bwino ngati kutsatira zofunazo kungawasemphanitse ndi kulambira kwawo kapena ngati zofunazo zili zoyenera ndipo zofunika kuzitsatira malinga ndi chikumbumtima chawo.

Nzika Zotsatira Chikumbumtima

15. Kodi Mboni za Yehova motsatira chikumbumtima chawo zimampatsa motani Kasaira zimene zili zake?

15 “Maulamuliro aakulu” andale amakhala “mtumiki” wa Mulungu pamene achita ntchito yawo yovomerezedwa ndi Mulungu, imene imaphatikizapo mphamvu ‘yolanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino.’ (1 Petro 2:13, 14) Motsatira chikumbumtima chawo, atumiki a Yehova amapatsa Kaisara zimene iye amafuna moyenerera pankhani yamisonkho, ndipo amachita zonse zimene chikumbumtima chawo chophunzitsidwa ndi Baibulo chingawalole kukhala omvera kwa ‘akulu, ndi aulamuliro, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino.’ (Tito 3:1) ‘Ntchito yabwino’ imaphatikizapo kuthandiza ena, monga pamene kwagwa tsoka. Ambiri achitira umboni kukoma mtima kumene Mboni za Yehova zasonyeza kwa anthu anzawo m’mikhalidwe imeneyi.​—Agalatiya 6:10.

16. Kodi ndi ntchito zabwino zotani zimene Mboni za Yehova motsatira chikumbumtima chawo zimachitira maboma ndi anthu anzawo?

16 Mboni za Yehova zimakonda anthu anzawo ndipo zimaona kuti ntchito yabwino yopindulitsa kwambiri imene zingawachitire ndiyo kuwathandiza kudziŵa molongosoka za chifuno cha Mulungu chodzetsa “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano” lolungama. (2 Petro 3:13) Mwa kuphunzitsa ndi kutsatira mapulinsipulo apamwamba a khalidwe labwino a Baibulo, iwo ngofunika kwambiri kwa anthu, kupulumutsa ambiri kumakhalidwe osayenera. Atumiki a Yehova amasunga malamulo ndipo amalemekeza nduna za boma, akuluakulu a boma, oweruza, ndi akuluakulu a mizinda, kupereka ulemu kwa “eni ake a ulemu.” (Aroma 13:7) Makolo amene ali Mboni amagwirizana mosangalala ndi aphunzitsi a ana awo kusukulu ndipo amathandiza ana awo kuphunzira bwino, kuti pambuyo pake anawa adzathe kudzipezera okha zofunika m’moyo ndipo asadzakhale chothodwetsa kwa anthu. (1 Atesalonika 4:11, 12) M’mipingo yawo, Mboni zimatsutsa tsankhu laufuko ndi kusankhana malinga ndi chuma chimene munthu ali nacho, ndipo kulimbitsa moyo wa banja amakuona kukhala kofunika kwambiri. (Machitidwe 10:34, 35; Akolose 3:18-21) Chotero, mwa zochita zawo, amasonyeza kuti zinenezo zakuti amatsutsa kukhala ndi banja kapena kuti samathandiza m’chitaganya nzabodza. Choncho, mawu a mtumwi Petro ngoonadi: “Chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa.”​—1 Petro 2:15.

17. Kodi ndi motani mmene Akristu ‘angayendere munzeru ndi iwo akunja’?

17 Choncho, pamene kuli kwakuti otsatira enieni a Kristu “siali a dziko lapansi,” iwo adakali m’dziko lokhalidwa ndi anthu ndipo ayenera kupitirizabe ‘kuyenda munzeru ndi iwo akunja.’ (Yohane 17:16; Akolose 4:5) Malinga ngati Yehova alolabe maulamuliro aakulu kugwira ntchito monga mtumiki wake, ife tidzawachitira ulemu woyenerera. (Aroma 13:1-4) Pamene kuli kwakuti sitidzatengamo mbali m’nkhani zandale, timapempherera “mafumu ndi onse akuchita ulamuliro,” makamaka pamene ameneŵa akukambirana nkhani zimene zingakhudze ufulu wa kulambira. Tidzapitirizabe kuchita zimenezi “kuti m’moyo mwathu tikakhale odikha mtima ndi achete m’kulemekeza Mulungu, ndi m’kulemekeza monse,” kuti ‘anthu onse [“anthu amtundu uliwonse,” NW] adzapulumuke.’​—1 Timoteo 2:1-4.

[Mawu a M’munsi]

a Onani buku lakuti Revelation​—Its Grand Climax At Hand!, mutu 35, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Mafunso Openda

◻ Kodi ndi “dziko lapansi” liti limene Akristu ali mbali yake, koma ndi “dziko lapansi” liti limene sangakhale mbali yake?

◻ Kodi nchiyani chimaphiphiritsiridwa ndi “chilembo” cha “chilombo” padzanja la munthu kapena pamphumi pake, ndipo ndi zizindikiro zotani zimene atumiki okhulupirika a Yehova ali nazo?

◻ Kodi ndi lingaliro loyenerera lotani limene Akristu oona ali nalo ponena za maboma a anthu?

◻ Kodi Mboni za Yehova zimathandizira ubwino wa chitaganya cha anthu m’njira zina ziti?

[Zithunzi patsamba 16]

Baibulo limafotokoza maboma a anthu kukhala mtumiki wa Mulungu ndi chilombo

[Chithunzi patsamba 17]

Chifukwa chosonyeza chisamaliro chachikondi pa ena, Mboni za Yehova nzofunika kwambiri m’zitaganya zawo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena