Chigawo 5
Mphatso Yabwino Kwambiri ya Ufulu Wakudzisankhira
1, 2. Kodi ndi mphatso yabwino kwambiri iti imene ili mbali yampangidwe wathu?
KUZINDIKIRA chifukwa chake Mulungu walola kuvutika ndi zimene adzachita nako, tifunikira kuzindikira mmene anatipangira. Iye anachita zowonjezereka kuposa kutilenga chabe tili ndi thupi ndi ubongo. Iye anatilenganso tili ndi mikhalidwe yapadera ya maganizo ndi malingaliro.
2 Mbali yaikulu ya mpangidwe wa maganizo ndi malingaliro athu ndiyo ufulu wakudzisankhira. Inde, Mulungu anaika mwa ife mkhalidwe wa ufulu wakusankha. Inalidi mphatso yabwino kwambiri yochokera kwa iye.
Mmene Tapangidwira
3-5. Kodi n’chifukwa ninji timayamikira ufulu wakudzisankhira?
3 Tiyeni tipende mmene ufulu wakudzisankhira ukuphatikizidwira m’kuloleza kwa Mulungu kuvutika. Choyamba, talingalirani izi: Kodi mumayamikira kukhala ndi ufulu wakusankha zimene mudzachita ndi kunena, zimene mudzadya ndi kuvala, ntchito imene mudzachita, ndi kumene mudzakhala ndi mmene mudzakhalira? Kapena kodi mukanakonda kuti munthu wina azikuuzani mawu alionse amene muyenera kunena ndi chochita pamphindi iliyonse ya moyo wanu?
4 Palibe munthu wa maganizo olama amene angafune kulandidwa moyo wake kotheratu motero. Nkulekeranji? Chifukwa cha mmene Mulungu anatipangira. Baibulo limatiuza kuti Mulungu adalenga munthu ‘m’chifanizo ndi m’chifanefane chake,’ ndipo umodzi wa mikhalidwe imene Mulungu mwiniyo ali nayo ndiwo ufulu wakusankha. (Genesis 1:26; Deuteronomo 7:6) Pamene analenga anthu, iye anawapatsa mkhalidwe wabwino kwambiri umodzimodziwo—mphatso ya ufulu wakudzisankhira. Ndicho chifukwa chake timakupeza kukhala kogwiritsa mwala kukhala muukapolo kwa olamulira otsendereza.
5 Chotero chikhumbo cha ufulu sichinadze chokha, pakuti Mulungu ali Mulungu wa ufulu. Baibulo limati: “Pamene pali mzimu wa Ambuye pali ufulu.” (2 Akorinto 3:17) Chifukwa chake, Mulungu anatipatsa ufulu wakudzisankhira monga mbali ya mpangidwe wathu weniweniwo. Popeza kuti anadziŵa mmene maganizo athu ndi malingaliro akagwirira ntchito, iye anadziŵa kuti tikakhala achimwemwe kopambana ngati tili ndi ufulu wakudzisankhira.
6. Kodi ndi motani mmene Mulungu analengera ubongo wathu kuti ugwire ntchito mogwirizana ndi ufulu wakudzisankhira?
6 Limodzi ndi ufulu wakudzisankhira, Mulungu anatipatsanso mphamvu yakuganiza, kupenda zinthu, kupanga zosankha, ndi kudziŵa chabwino ndi choipa. (Ahebri 5:14) Chotero, ufulu wakudzisankhira unayenera kuzikidwa pachosankha chaluntha. Sitinapangidwe mofanana ndi maloboti osaganiza opanda chosankha cha iwo eni. Ndiponso sitinalengedwe kuti tichite zinthu mwachibadwa monga momwe zinyama zilili. Mmalomwake, ubongo wathu wodabwitsawo unalinganizidwira kugwira ntchito mogwirizana ndi ufulu wathu wakusankha.
Chiyambi Chabwino Koposa
7, 8. Kodi ndi chiyambi chabwino kwambiri chotani chimene Mulungu anapatsa makolo athu oyambirira?
7 Kusonyeza mmene Mulungu analiri wosamala, limodzi ndi mphatso ya ufulu wakudzisankhira, makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, anapatsidwa chilichonse chimene munthu aliyense mwanzeru akanafuna. Iwo anaikidwa m’paradaiso wamkulu wonga paki. Iwo anali ndi moyo wa mwana alirenji. Iwo anali ndi maganizo ndi matupi angwiro, kotero kuti sakafunikira kukalamba kapena kudwala, kapena kufa—iwo akanakhala ndi moyo kosatha. Iwo akanabala ana amenenso akanakhala ndi mtsogolo mwachimwemwe mosatha. Ndipo chiŵerengero chomawonjezerekacho cha anthu chikanakhala ndi ntchito yokhutiritsa imene potsilizira pake ikanasanduliza dziko lonse lapansi kukhala paradaiso.—Genesis 1:26-30; 2:15.
8 Ponena za zimene zinagawiridwa, Baibulo limasimba kuti: “Ndipo anaziwona Mulungu zonse zimene anazipanga, ndipo, tawonani, zinali zabwino ndithu.” (Genesis 1:31) Baibulo limanenanso za Mulungu kuti: “Ntchito yake ndi yangwiro.” (Deuteronomo 32:4) Inde, Mlengi anapatsa banja laumunthu chiyambi changwiro. Sikukanakhala bwino kuposa apa. Iye anatsimikizira kukhala Mulungu wosamala chotani nanga!
Ufulu Mkati mwa Malire
9, 10. Kodi n’chifukwa ninji ufulu wakusankha uyenera kulamulidwa bwino lomwe?
9 Komabe, kodi Mulungu analinganiza kuti ufulu wakudzisankhira ukhale wopanda malire? Tayerekezerani mzinda wodzala magalimoto koma wopanda malamulo alionse a pamsewu, kumene munthu aliyense akayendetsa galimoto kumbali iliyonse paliŵiro lililonse. Kodi mukanafuna kuyendetsa galimoto mumikhalidwe imeneyo? Ayi, mkhalidwewo ukanakhala chipolowe cha pamsewu ndipo ukanachititsadi ngozi zambiri.
10 Choteronso mphatso ya Mulungu ya ufulu wakudzisankhira. Ufulu wopanda malire ukatanthauza chipolowe m’chitaganya cha anthu. Pakafunikira malamulo otsogoza zochitika za anthu. Mawu a Mulungu amati: “Dzisungireni monga anthu a ufulu, ndipo musagwiritsire ntchito konse ufulu wanu monga chodzikhululukira nacho kukuchita zoipa.” (1 Petro 2:16, JB) Mulungu amafuna kuti ufulu wakudzisankhira ulamuliridwe kaamba ka ubwino wa onse. Iye sanatilinganizire kukhala ndi ufulu wopanda malire koma ufulu wokhala ndi polekezera, wolamulidwa ndi lamulo.
Malamulo Ayani?
11. Kodi ndi malamulo ayani amene tinalinganizidwira kumvera?
11 Kodi ndi malamulo ayani amene ife tinalinganizidwira kumvera? Mbali ina ya lembalo pa 1 Petro 2:16 (JB) imati: “Simuli akapolo a munthu wina koma a Mulungu.” Izi sizitanthauza ukapolo wotsendereza, koma, mmalomwake, zikutanthauza kuti ife tinalinganizidwa kukhala achimwemwe koposa pamene tili ogonjera kumalamulo a Mulungu. (Mateyu 22:35-40) Malamulo ake, koposa malamulo ena aliwonse opangidwa ndi anthu, amapereka chitsogozo chabwino koposa. “Ine ndine Yehova, Mulungu wako amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.”—Yesaya 48:17.
12. Kodi ndi ufulu wakusankha uti umene tili nawo mkati mwa malamulo a Mulungu?
12 Panthaŵi imodzimodziyo, malamulo a Mulungu amapereka ufulu waukulu wakusankha mkati mwa malire ake. Izi zimachititsa kusiyanasiyana ndipo zimapangitsa banja laumunthu kukhala lokondweretsa. Talingalirani mitundu yosiyanasiyana ya chakudya, zovala, nyimbo, maluso, ndi nyumba padziko lonse lapansi. Ndithudi ife timakonda kupanga chosankha chathu m’nkhani zotero mmalo mwakuti munthu wina atisankhire.
13. Kodi ndi malamulo akuthupi ati amene tiyenera kumvera kaamba ka ubwino wathu?
13 Chotero tinalengedwa kukhala achimwemwe koposa pamene tigonjera kumalamulo a Mulungu amakhalidwe aumunthu. Nkofanana ndi kugonjera kumalamulo a Mulungu akuthupi. Mwachitsanzo, ngati tinyalanyaza lamulo la mphamvu yakukoka ndi kudumpha kuchoka pamalo aatali, tidzavulala kapena kufa. Ngati tinyalanyaza malamulo a mkati mwa thupi lathu ndi kuleka kudya, kumwa madzi, kapena kupuma mpweya, tidzafa.
14. Kodi timadziŵa bwanji kuti anthu sanapangidwe kukhala osadalira pa Mulungu?
14 Monga momwedi tinalengedwera ndi kufunikira kugonjera kumalamulo a Mulungu akuthupi, tinalengedwa tili ofunikira kugonjera malamulo a Mulungu a makhalidwe ndi achitaganya cha anthu. (Mateyu 4:4) Anthu sanalengedwere kukhala osadalira pa Mpangi wawo ndi kupeza chipambano. Mneneri wake amati: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake. Yehova, mundilangize.” (Yeremiya 10:23, 24) Chotero m’njira iliyonse anthu analengedwa kukhala ndi moyo pansi pa ulamuliro wa Mulungu, osati iwo wokha.
15. Kodi malamulo a Mulungu akanakhala olemetsa kwa Adamu ndi Hava?
15 Kumvera malamulo a Mulungu sikukanakhala kolemetsa kwa makolo athu oyamba. Mmalomwake, kukanawayendetsera bwino zinthu zawo ndi zabanja lonse laumunthu. Ngati aŵiri oyambirirawo akanakhala mkati mwa malire a malamulo a Mulungu, zonse zikanayenda bwinobwino. Kunena zowona, ife tsopano tikanakhala tili m’paradaiso wabwino kwambiri wachisangalalo monga banja laumunthu lachikondi, ndi logwirizana! Sipakanakhala kuipa, kuvutika, ndi imfa.
[Chithunzi patsamba 11]
Mlengiyo anapatsa anthu chiyambi changwiro
[Chithunzi patsamba 12]
Kodi mukafuna kuyendetsa galimoto pakati pa magalimoto ochuluka ngati panalibe malamulo a pamsewu?