Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Ganizirani Mozama za Munthu Amene Anapirira”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
    • “Mutsatire Mapazi Ake Mosamala Kwambiri”

      20, 21. Pa nkhani ya kupirira, kodi Yehova amayembekezera kuti tizitani, nanga tiyenera kutsimikiza kuchita chiyani?

      20 Yesu ankadziwa kuti si zophweka kuti munthu akhale wotsatira wake chifukwa munthuyo amafunika kupirira. (Yohane 15:20) Pa nkhani yopirira, iye anapereka chitsanzo chabwino kwambiri ndipo ankadziwa kuti chitsanzo chakecho chingalimbikitse anthu ena. (Yohane 16:33) N’zoona kuti iye anakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa anali wangwiro, koma ifeyo si ife angwiro. Ndiyeno kodi Yehova amayembekezera kuti ifeyo tizichita chiyani? Petulo anafotokoza kuti: “Khristu anavutika chifukwa cha inu, ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.” (1 Petulo 2:21) Tikaganizira zimene anachita popirira mayesero, timaona kuti Yesu anatisiyira “chitsanzo” chabwino choti tizitsanzira.a Zinthu zonse zimene Yesu anachita posonyeza kuti ndi wopirira kwambiri tingaziyerekezere ndi “mapazi,” kapena kuti zidindo za mapazi. N’zosatheka kuti titsatire ndendende mapazi a wina, n’kumaponda mosalakwitsa malo amene mapazi ake adinda. Koma n’zotheka kutsatira mapaziwo “mosamala kwambiri.”

  • “Ganizirani Mozama za Munthu Amene Anapirira”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
    • a Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “chitsanzo,” kwenikweni amatanthauza “pepala lokhala ndi zilembo limene linkaikidwa pansi pa pepala lina limene ankafuna kulembapo.” Pa anthu onse amene anauziridwa kulemba Malemba a Chigiriki, mtumwi Petulo yekha ndi amene anagwiritsa ntchito mawu amenewa ndipo anthu ena amanena kuti mawuwa amatanthauza “‘pepala lokhala ndi zilembo’ limene mwana amene akuphunzira kulemba ankaika pansi pa pepala lina kuti azilemba motsatira zilembozo ndipo amayesetsa kuti zifanane ndendende.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena