Yang’anani Kupyola pa Zinthu Zimene Mukuona!
MASO akuthupi abwino ndi dalitso. Kwenikweni, anthu ambiri anganene kuti pali zinthu zochepa zimene ali nazo zimene zingakhale zamtengo wapatali motero. Komabe, kwa Akristu pali maso ena onenedwa ndi mtumwi Paulo amene ali a mtengo wapatali kwambiri kuposa ngakhale maso akuthupi abwino. “Sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka,” analemba motero Paulo. (2 Akorinto 4:18) Amenewo ayenera kukhaladi maso apadera amene amachititsa munthu kuona zinthu zosaoneka! Tinganene kuti ndiwo maso abwino koposa auzimu.
Kodi Nchifukwa Ninji Akufunika?
Akristu a m’zaka za zana loyamba anafunikadi kukhala ndi maso auzimuŵa. Anali kuchita utumiki wawo wachikristu pansi pa mavuto ambiri. Paulo anafotokoza motere: “Ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi; olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka.”—2 Akorinto 4:8, 9.
Ngakhale zinthu zinali motero, ophunzira okhulupirika anaima nji. Ndi chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu, ankanena ngati Paulo kuti: “Sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wamkati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.” Komabe, kodi nchiyani chimene chinachititsa kukonzedwa kwa tsiku ndi tsiku kumeneku? Paulo anapitiriza kunena kuti: “Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthaŵi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero; popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthaŵi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.”—2 Akorinto 4:16-18.
Paulo anali kulimbikitsa abale ake auzimu kuti mavuto, zothetsa nzeru, zizunzo—masautso a mtundu uliwonse—zisachititse khungu maso awo kuti angalephere mfupo yaulemerero imene inaikidwa pamaso pawo. Anayenera kuyang’ana kupyola pa mikhalidwe yomwe inalipo, akumasumika maso awo pa mphotho yosangalatsa ya njira yachikristu. Zimenezi ndizo zimene zinawathandiza kukonza chosankha chawo tsiku ndi tsiku cha kumenyabe nkhondo. Akristu lerolino afunikanso kukhala ndi maso auzimu abwino motero.
Onani Masautso Alipowa Monga Akanthaŵi!
Tifune kapena tisakufune tsiku lililonse timaona zinthu zimene sitimafuna kuona. Kuyang’ana m’kalirole mosakayikira kumationetsa zipsera ndi zilema zathupi zosafunika, zizindikiro za kupanda ungwiro kwakuthupi. Pamene tiyang’ana m’kalirole wa Mawu a Mulungu, timaona zipsera ndi zilema zauzimu, mwa ife eni ndi mwa ena omwe. (Yakobo 1:22-25) Ndipo pamene tiŵerenga nyuzipepala tsiku ndi tsiku kapena kupenyerera wailesi yakanema, nkhani za chisalungamo, nkhanza, ndi masoka mwamsanga zimatikhudza mtima ndi kutimvetsa chisoni.
Satana amafuna kutitayitsa chiyembekezo chathu chifukwa cha zinthu zimene timaona kapena kutichotsa panjira ndi kuyamba kukayikakayika pa chikhulupiriro. Kodi zimenezi tingaziletse motani kuti zisachitike? Tiyenera kulondola chitsanzo cha Yesu Kristu, monga mmene mtumwi Petro ananenera pamene anati: “Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Kristu anamva zoŵaŵa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.” (1 Petro 2:21) M’mbali iliyonse ya moyo wachikristu, Yesu anali chitsanzo chabwino koposa.
Ponena za Yesu monga chitsanzo chathu, Petro ananena molunjika kuti Yesu anamva zoŵaŵa. Zoonadi, Yesu anamva zowawa zambiri pamene anali padziko lapansi. Monga “mmisiri” wa Yehova amene analipo pamene munthu anali kulengedwa, iye anadziŵa zenizeni mmene Mulungu anafunira munthu kukhalira. (Miyambo 8:30, 31) Koma tsopano anadzionera mmene uchimo ndi kupanda ungwiro zinawachitira. Tsiku lililonse ankaona ndipo anali kulimbana ndi zophophonya za anthu ndi zifooko zawo. Zimenezo zinalidi zomuyesa.—Mateyu 9:36; Marko 6:34.
Kuwonjezera pa masautso a ena, Yesu anaonanso ake. (Ahebri 5:7, 8) Koma ndi maso angwiro auzimu, anayang’ana kuseri kwake kuti aone mfupo ya kukwezedwa ku moyo wosafa chifukwa cha kusunga kwake umphumphu. Motero monga Mfumu yaumesiya, adzakhala ndi mwaŵi wa kutulutsa anthu ovutika m’mkhalidwe wawo woluluzika kupezanso ungwiro umene Yehova anawafunira poyamba. Kusumikabe maso ake pa ziyembekezo za mtsogolo zimenezi zosaoneka kunamthandiza kukhalabe wachimwemwe mu utumiki waumulungu mosasamala kanthu za masautso amene anakumana nawo tsiku ndi tsiku. Paulo analemba pambuyo pake kuti: “Chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira [mtengo wozunzirapo, NW], nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.”—Ahebri 12:2.
Yesu sanalole konse mavuto ndi mikhalidwe yovuta kumutayitsa chiyembekezo chake, kuchoka panjira, kapena kukayikakayika pa chikhulupiriro chake. Monga ophunzira ake, tiyenera kulondola mosamalitsa chitsanzo chake chabwino koposa.—Mateyu 16:24.
Yang’anitsitsani pa Zinthu Zosaoneka Zosatha!
Ponena za zimene zinachititsa Yesu kupirira, Paulo anatisonyezanso njira pamene analemba kuti: “Tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera [W]oyambira ndi [W]omaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu.” (Ahebri 12:1, 2) Inde, kuti tithamange m’njira yachikristu mwachipambano ndi mwachimwemwe, tiyenera kuyang’ana kupyola pa zinthu zimene zili pamaso pathu. Koma kodi ndi motani mmene ‘tingapenyerere’ Yesu, ndipo kodi zimenezi zidzatichitira chiyani?
Mwachitsanzo, mu 1914, Yesu anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulugu, ndipo amalamulira kuchokera kumwamba. Zoonadi, zonsezi sitimaziona ndi maso athu akuthupi. Komabe, ngati ‘tipenyerera’ Yesu, maso athu auzimu adzatithandiza kuona kuti tsopano ali wokonzeka kuchitapo kanthu kuthetsa dongosolo la zinthu loipa lilipoli ndi kumanga Satana ndi magulu ake a ziŵanda m’ndende kwakuti sadzagwira ntchito. Tikayang’anabe mtsogolo, maso athu auzimu adzatisonyeza dziko latsopano labwino kwambiri limene ‘simudzakhalanso imfa; ndipo simudzakhalanso maliro kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.’—Chivumbulutso 19:11-16; 20:1-3; 21:4.
Motero, m’malo motopetsedwa ndi masautso osakhalitsa amene tingakumane nawo tsiku lililonse, bwanji osasumika maso athu pa zinthu zosatha? Ndi maso achikhulupiriro, bwanji osayang’ana kupyola pa matenda ndi umbombo za dziko lapansili loipitsidwa kuti tione paradaiso wodzala ndi anthu athanzi labwino, achimwemwe, ndi osamala za ena? Bwanji osayang’ana kupyola pa zilema zathu, zakuthupi ndi zauzimu zomwe, ndi kudziona ife eni titamasulidwa ku izo kwamuyaya ndi nsembe ya dipo ya Kristu? Bwanji osayang’ana kupyola pa anthu akufa ndi ovulala pambuyo pa nkhondo, upandu, chiwawa ndi kuona oukitsidwa chatsopano akulangizidwa mumtendere ndi chilungamo cha Yehova?
Ndiponso, ‘kupenyerera’ Yesu kumaphatikizaponso kuyang’anitsitsa ndi maso athu auzimu pa zimene Ufumu, ngakhale kuti ngwosaoneka, wakwaniritsa kale pakati pa anthu a Mulungu padziko lapansi: mgwirizano, mtendere, chikondi, chikondi cha pa abale, ndi kulemera kwauzimu. Mkazi wina wachikristu ku Germany, pambuyo pa kupenyerera vidiyo ya United by Divine Teaching, analemba kuti: “Vidiyo imeneyi idzandithandiza kwambiri kukumbukira kuti abale ndi alongo achikristu ambiri kuzungulira dziko lonse lapansi akutumikira Yehova mokhulupirika panthaŵi inoyi—ndipo akumachita zimenezi ngakhale kuti pali chitsutso cha anthu. Kugwirizana kwathu kwa paubale nkwamtengo wapatalidi m’dziko lachiwawa ndi chidani!”
Kodi ‘mumaona’ Yehova, Yesu, angelo okhulupirikawo, ndi mamiliyoni a Akristu anzanu akukuchirikizani? Ngati zili tero, simudzakhala kwambiri ndi “nkhaŵa za dongosolo lino la zinthu,” [NW] zimene zingakulefuleni ndi kukuimitsani ndiponso kukuchititsani kukhala “wopanda chipatso” mu utumiki wachikristu. (Mateyu 13:22) Motero, ‘penyererani’ Yesu mwa kusumika maso anu auzimu pa Ufumu wa Mulungu wokhazikitsidwa ndi pa madalitso ake, atsopano ndi amtsogolo omwe.
Khalani ndi Moyo Kuti Mukaone Zosaoneka!
Poona kusiyana kwakukulu pakati pa dziko latsopano lamuyaya la Mulungu ndi dziko lino lakale lomanyonyotsoka, tiyenera kusonkhezeredwa kudzisungira kwakuti tidzayesedwe woyenera kukhala ndi moyo kuti tikaonedi zinthu zimene timaona kokha ndi maso auzimu lerolino. Anthu ambiri oukitsidwa sadzakhulupirira konse zimene adzaona atagalamuka ndi kuona dziko lapansi lolungama laparadaiso losiyaniratu ndi dziko limene anaona asanafe. Tangolingalirani za chimwemwe chathu pokhala ndi moyo ndi kuwalandira ndi kuwafotokozera zimene Mulungu wachita!—Yerekezerani ndi Yoweli 2:21-27.
Inde, maso abwino auzimu ngamtengo wapatalidi, ndipo nkofunika kotani nanga kuwasungabe ali akuthwa! Tingachite zimenezi mwa kukhala ndi phunziro laumwini la Baibulo nthaŵi zonse, kupezeka pamisonkhano yachikristu, kulankhula ndi ena za chiyembekezo chathu chozikidwa pa Baibulo, ndipo koposa zonse, kupempherera chitsogozo chaumulungu. Zimenezi zidzasungabe maso athu auzimu ali akuthwa ndi oona patali, akumatikhozetsa kuyang’ana kupyola pa zinthu zimene timaona!