Kuphunzira Chinsinsi Chopatulika cha Kudzipereka Kwaumulungu
“Pakutinso Kristu anamva zowawa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake [mosamalitsa, “NW”].”—1 PETRO 2:21.
1. Kodi nchiyani chimene chakhala chifuno cha Yehova ponena za ‘chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu’?
“CHINSINSI chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu” uku sichirinso chinsinsi! (1 Timoteo 3:16, NW) Ndi chosiyana motani nanga ndi zinsinsi za chipembedzo chonyenga, monga Utatu wosamveka, zomwe zimakhalabe zinsinsi! Palibe aliyense yemwe angazimvetsetse. M’malomwake, Yehova walinganiza kuti chinsinsi chopatulika chovumbulidwa mwa munthu yemwe ali Yesu Kristu chifalitsidwe ku ukulu wothekera. Yesu iyemwini anakhala chitsanzo chapadera cha mlengezi wachangu wa Ufumu wa Mulungu. Tingaphunzire zochulukira kuchokera ku uthenga wake ndi mkhalidwe wa kulalikira, monga mmene tidzawonera tsopano.
2. Kodi nchifukwa ninji utumiki wa Yesu waikidwa kukhala woyambirira dipo lisadatero? (Mateyu 20:28)
2 Pamenepa, tiyeni tilingalire mowonjezereka ponena za kukhala kwa Yesu “wowonekera m’thupi.” (1 Timoteo 3:16) Pa Mateyu 20:28 timaŵerenga kuti Yesu “sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” Ichi chimaika utumiki wake kukhala woyambirira dipo lisadatero. Kodi nchifukwa ninji ziri tero? Chabwino, kumbuyoko mu Edene Njoka yochenjerayo inali idatsutsa ulamuliro woyenerera wa Yehova pa mtundu wa anthu, ikumatanthauza kuti chilengedwe cha Mulungu chinali cholakwika ndikuti palibe munthu yemwe angasunge umphumphu kwa Wam’mwambamwamba pansi pa chiyeso. (Yerekezani ndi Yobu 1:6-12; 2:1-10.) Utumiki wopanda banga wa Yesu monga munthu wangwiro, “Adamu wotsirizayo,” unasonyeza Satana wotokosayo kukhala wabodza woipa. (1 Akorinto 15:45) Kuwonjezerapo, Yesu anatsimikizira mokwanira ziyeneretso zake za kutumikira monga “Mtsogoleri ndi Mpulumutsi” wa Mulungu ndi “kuweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo,” m’kutamanda ulamuliro wa Yehova.—Machitidwe 5:31; 17:31.
3. Kodi ndimotani mmene Yesu anatsutsira kotheratu chitokoso cha Satana?
3 Yesu anatsutsa kotheratu chitokoso chotonza cha Satana! Mu mbiri yakale yonse, palibe munthu pa dziko lino lapansi yemwe anatumikira Mulungu modzipereka chotero—mosasamala kanthu za kusekedwa, kukwapulidwa, ndi kuzunzidwa kwakuthupi ndi kwamaganizo. Kristu anafunikira kupirira kunyozedwa koipa monga Mwana wa Mulungu. Kupyola zonsezo—ngakhale kufikira imfa yankhanza ndi yomvetsa manyazi—iye anali wolimba, wosasunthika m’chikhulupiriko kwa Atate wake. Pa Afilipi 2:8, 9, Paulo akulemba kuti chifukwa chakuti Yesu anamvera ‘kufikira imfa, inde, imfa ya pa [mtengo wozunzirapo, NW], Mulungu anamkweza iye ndi kumpatsa dzina lokhala pamwamba pa dzina lina lirilonse.’ Yesu anavumbula Satana kukhala wabodza woipitsitsa!
4. Kodi nchifukwa ninji Yesu anauza Pilato kuti anadza ku dziko lapansi kudzachitira umboni chowonadi?
4 Chotero, kumapeto kwa zaka zoŵerengeka zokha za kulalikira kwakukulu, Yesu akakhoza kuchitira umboni molimba mtima kwa Pontiyo Pilato kuti: “Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi chowonadi. Yense wakukhala mwa chowonadi amva mawu anga.” (Yohane 18:37) Yesu adasonyeza kudzipereka kwaumulungu kopambana koposa m’kulengeza chowonadi cha Ufumu wa Mulungu m’Palestina yonse. Iye anaphunzitsa ophunzira ake kukhalanso alengezi achangu. Chitsanzo chake chimatisonkhezera ife chotani nanga lerolino kutsatira mapazi ake!
Kuphunzira Kuchokera kwa Wokhazikitsa Chitsanzo Wathu
5. Kodi nchiyani chimene tingaphunzire ponena za kudzipereka kwaumulungu mwa kupenyetsetsa pa Yesu?
5 Mwa kudzipereka kwathu kwaumulungu m’kuchita chifuniro cha Yehova, nafenso tingatsimikizire Mdyerekezi kukhala wabodza. Ziyeso zirizonse zimene tingavutike nazo, palibe nchimodzi chomwe chimene chidzalingana ndi kuwawa ndi kunyozedwa zimene Yesu anakumana nazo. Pamenepa, lolani kuti tiphunzire kuchokera kwa Wokhazikitsa Chitsanzo wathu. Monga mmene Ahebri 12:1, 2 ikutilimbikitsira, lolani kuti tithamange mwachipiriro makaniwo “ndi kupenyerera woyamba ndi womalizira wa chikhulupiriro chathu, Yesu.” Mosiyana ndi Adamu, amene analephera poyesedwa ponena za kudzipereka kwaumulungu, Yesu anadzakhala munthu yekha pa dziko lapansi yemwe analaka ziyeso zonse mwangwiro. Mpaka imfa, iye anatsimikizira kukhala “woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa.” (Ahebri 7:26) M’chikhulupiriro chopanda banga, iye akakhoza kunena kwa adani ake kuti: “Ndani mwa inu anditsutsa ine za chimo?” Yesu anafooketsa chitokoso cha Satana, akumalengeza kuti: “Mkulu wa dziko lapansi . . . alibe kanthu mwa ine.” Ndipo pomaliza nkhani yake yothera kwa ophunzira ake asanaperekedwe ndi kumangidwa, anawauza iwo kuti: “Limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi ine.”—Yohane 8:46; 14:30; 16:33.
6. (a) Kodi nchifukwa ninji Yesu akudziŵa mtundu wa mpumulo wofunikira ku mtundu wa anthu? (b) Kodi ndi ku ukulu wotani umene Yesu anasonyeza mantha aumulungu?
6 Pamene anali m’thupi pano pa dziko lapansi, Yesu analaŵa chimene chimatanthauza kukhala munthu, “wochepsedwa pang’ono ndi angero.” (Ahebri 2:7) Iye anazoloŵerana ndi zophophonya zaumunthu ndipo chotero ali wokonzekeretsedwa bwino kutumikira monga Mfumu ndi Woweruza wa mtundu wa anthu kwa zaka chikwi. Mwana wa Mulungu ameneyu, yemwe ananena kuti, “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu,” amadziwa mtundu wa kupumulitsa umene umafunikira kwa mtundu wa anthu. (Mateyu 11:28) Ahebri 5:7-9 ikutiwuza kuti: “M’masiku a thupi lake [Kristu, NW] anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu, angakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo; ndipo pamene anakonzeka wamphumphu [m’chimvero] anakhala kwa onse akumvera iye chifukwa cha chipulumutso chosatha.” Yesu sanagwedezeke, ngakhale kuti anafunikira kupirira kumlingo wa kukumana ndi kuwawa kwa imfa yaumunthu m’kulandira ‘chilonda cha kuchitende’ kuchokera kwa Njoka yachidaniyo. (Genesis 3:15) Mofanana ndi Yesu, lolani kuti nthawi zonse tisonyeze mantha aumulungu, kufikiradi ku imfa ngati chiri choyenerera, tikumakhala achidaliro kuti Yehova Mulungu adzamvetsera mapembedzero athu ndi kutipatsa chipulumutso.
‘Kukhala ndi Moyo m’Chilungamo’
7. Mogwirizana ndi 1 Petro 2:21-24, kodi ndi chitsanzo chotani chimene Kristu anatisiyira, ndipo kodi ndimotani mmene njira yake iyenera kutiyambukira?
7 Pamene adali wowonekera m’thupi, Yesu anamasula mokhulupirika chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu. Timaŵerenga pa 1 Petro 2:21-24 kuti: “Pakutinso Kristu anamva zowawa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake; amene sanachita chimo, ndipo m’kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo; amene pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe, pakumva zowawa, sanaopsa, koma anapereka mlandu kwa iye woweruza kolungama; amene anasenza machimo athu mwini yekha m’thupi mwake pa [mtengo wozunzirapo, NW], kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo.” Pamene tisinkhasinkha pa njira ya Yesu, imatilimbikitsa ife chotani nanga kulondola kudzipereka kwaumulungu, kusunga umphumphu, ndi kukhala ndi moyo m’chilungamo monga mmene iye anachitira!
8. Kodi ndimotani mmene tingakhalire ndi moyo m’chilungamo monga mmene Yesu anachitira?
8 Yesu anakhaladi ndi moyo m’chilungamo. Salmo 45:7 inalosera za iye kuti: “Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa.” Pogwiritsira ntchito mawu amenewo kwa Yesu, mtumwi Paulo pa Ahebri 1:9 ananena kuti: “Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa.” M’chiwunikiro cha kumvetsetsa kwathu kwa chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu kumeneku, lolani kuti ife mofanana ndi Yesu nthawi zonse tikonde chilungamo ndi kudana nacho choipa. M’makhalidwe abwino Achikristu, omwe akuwukiridwa mowopsa chotero lerolino ndi dziko la Satana, ndi m’zochita zathu zonse ndi awo okhala mkati ndi kunja kwa gulu la Mulungu, lolani kuti tikhale ogamulapo kukhala ndi moyo m’chilungamo, kulabadira malamulo a makhalidwe abwino a Yehova. Ndipo lolani kuti tidzidya mosalekeza pa Mawu a Mulungu kotero kuti tikhale ndi chidziŵitso chaumulungu chofunika chotero m’kutsutsa Mdyerekezi ndi machenjera ake!
9. Kodi nchiyani chimene chinawonjezera changu cha Yesu mu utumiki, ndipo kodi ichi chinaphatikizapo chiyani m’chigwirizano ndi abusa a chipembedzo chonyenga?
9 Chinachake chowonjezereka chinasonkhezera Yesu kukhala wachangu mu utumiki wake. Kodi chimenecho chinali chiyani? Pa Mateyu 9:36 timaŵerenga kuti: “Powona makamuwo, anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” Chotero Yesu “anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Marko 6:34) Moyenerera, ichi chinaphatikizapo kuvumbula kuipa ndi kusayeruzika kwa abusa achipembedzo chonyenga. Mogwirizana ndi Mateyu 15:7-9, Yesu ananena kwa ena a amenewa kuti: “Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, Anthu awa andilemekeza ine ndi milomo yawo; koma mtima wawo uli kutali ndi ine. Koma andilambira ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.”
Chinsinsi Chomvetsa Chisoni
10. Lerolino, “utumiki wa kusayeruzika kumeneku” umalunjika kwa yani, ndipo kodi iwo ndi aliwongo la chiyani?
10 Monga mmene Yesu analankhula motsutsa atsogoleri achipembedzo, choteronso ife lerolino tikuchitira chisoni chinsinsi chomwe chimaima mosiyana kwenikweni ndi chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu. Pa 2 Atesalonika 2:7, Paulo anachitcha icho kukhala “chinsinsi cha kusayeruzika.” Icho chinali chinsinsi m’zaka za zana loyamba C.E. chifukwa chakuti sichikavumbulidwa kufikira nthaŵi yaitali pambuyo pa imfa ya atumwi. Lerolino, icho chimalunjikitsa pa atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu, omwe ali okondweretsedwa kwenikweni m’ndale zadziko kuposa ndi kulengeza mbiri yabwino ya Ufumu wolungama wa Mulungu. Chinyengo chikuchulukira m’maudindo awo. Alengezi a pa TV a mipatuko ya Chiprotesitanti cha Dziko Lachikristu ali chitsanzo chowonekera: onyenga omwe amadyerera nkhosa zawo, kumanga maufumu a madola mamiliyoni ochulukira, kuyanjana ndi akazi achigololo, kumvera chisoni konamizira pamene iwo eniwo avumbulidwa, ndi kupitirizabe kupemphapempha ndalama, nthaŵi zonse ndalama zochulukira. Vatican ya Chiroma Katolika imapereka chithunzi chonyansa chofananacho, limodzi ndi kugwirizana kwake koipitsitsa ndi ndale zadziko, chinyengo chakunja, ndi machitachita onyenga osunga ndalama.
11. Kodi nchiyani chimene chidzachitika kwa atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu ndi a Babulo Wamkulu yense?
11 N’chosadabwitsa kuti gulu la atsogoleri a chipembedzo a Dziko Lachikristu lingazindikiridwe kukhala “munthu wosayeruzika”! (2 Atesalonika 2:3) Mbali yolamulira imeneyi ya Babulo Wamkulu wonga mkazi wachigololo idzavumbulidwa mokwanira ndi kuwonongedwa, limodzi ndi zipembedzo zina zonse zonyenga. Monga momwe tikuŵerengera pa Chibvumbulutso 18:9-17, andale zadziko ndi amalonda (ndi osunga ndalama awo) kenaka adzachitira chisoni kuti: “Tsoka, tsoka, mudzi waukulu.” Babulo Wamkulu ndi zinsinsi zake adzakhala atavumbulidwa, m’kusiyana kotheratu ndi zonse zomwe zimawunikira chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu.
12. Kodi kukonda chilungamo kwa Yesu kunamtsogolera kuchita chiyani?
12 Chikondi cha Yesu cha chilungamo ndi kudana nako kusayeruzika chinamtsogolera iye kudziikizako iyemwini m’malo mwa alambiri owona popanda chakukhosi. Pa kuchezera kwake koyamba ku Yerusalemu monga Mwana wa Mulungu wodzozedwa, Kristu anapitikitsa amalonda ndi osinthanitsa ndalama kuwatulutsa m’kachisi, akumalengeza kuti: “Chotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda.” (Yohane 2:13-17) Pa kuchezera kwa pambuyo pake ku kachisiko, Yesu anawuza Ayuda otsutsa kuti: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita, iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaima m’chowonadi, pakuti mwa iye mulibe chowonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwiniwake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Ndi kulimba mtima kotani nanga kumene Yesu anasonyeza m’kuwuza achilikizi a zipembedzo amenewo pamaso pawo kuti anali abodza ndi ana a Mdyerekezi!
13. (a) Kodi ndikuti makamaka kumene kuda kusayeruzika kwa Yesu kwalongosoledwa? (b) Kodi nchifukwa ninji atsogoleri achipembedzo osayeruzika akuyenerera chiweruzo chofanana ndi chija cholengezedwa ndi Yesu pa alembi ndi Afarisi?
13 Kuda kwa Yesu kwa kusayeruzika sikunalongosoledwe bwino kwina kulikonse kuposa m’kutsutsa kwake kopyoza kwa alembi onga njoka ndi Afarisi, monga mmene zalembedwera pa Mateyu mutu 23. Pajapo iye akulengeza “tsoka” la mbali zisanu ndi ziŵiri, akumawayerekeza iwo ku ‘manda opakidwa njereza—odzala ndi zonyansa zonse, chinyengo, ndi kusayeruzika.’ Mmene Yesu anakhumbira kupulumutsa anthu otsenderezedwa kuchoka m’kusayeruzika kumeneko! “Ha, Yerusalemu, Yerusalemu,” iye anafuula tero, “ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafuna ayi! Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.” (Mavesi 37, 38) Atsogoleri a chipembedzo osayeruzika a tsiku lathu ali oyenerera chiweruzo chofananacho chifukwa chakuti, m’mawu a 2 Atesalonika 2:12, ‘iwo samakhulupirira chowonadi koma amasangalala ndi chisalungamo.’ Kusayeruzika kwawo kuli kusemphana kwenikweni kwa kudzipereka kwaumulungu kumene Yesu anakusonyeza mokhulupirika chotero pamene anali pano pa dziko lapansi.
Kulengeza Ziweruzo za Mulungu
14. Kodi kuyamikira chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu kuyenera kutisonkhezera kuchita chiyani?
14 Kuyamikira kwathu kaamba ka chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu kuyenera kutitsogoza ife nthaŵi zonse kutsatira mapazi a Yesu mosamalitsa. Mofanana ndi iye, tiyenera kukhala achangu m’kulengeza chimene Yesaya 61:2 akuchilongosola kukhala “chaka chokomera Yehova, ndi tsiku la kubwezera la Mulungu wathu.” Ndipo lolani kuti tichite mbali yathu mwachangu “kutonthoza olira onse.” Mofanana ndi m’nthawi imene Yesu anali padziko lapansi, chimafunikira kulimba mtima kwa ife lerolino kulengeza ziweruzo za Yehova, kuphatikizapo uthenga wamphamvu wofuulidwa m’nkhani za mu Nsanja ya Olonda ndi m’bukhu la Revelation—Its Grand Climax At Hand! Tiyenera kulalikira molimba mtima ndi mochenjera, zokamba zathu zikukhala “zokometseredwa ndi mchere” kotero kuti zikhale zokoma kwa awo okhoterera kulinga ku chilungamo. (Akolose 4:6, NW) Pokhala titaphunzira kuchokera ku chitsanzo cha Yesu cha kudzipereka kwaumulungu, lolani kuti tikhale okhoza kuchitira ripoti pa nthaŵi yake kuti tatsiriza ntchito imene Yehova anatipatsa ife kuichita.—Mateyu 24:14; Yohane 17:4.
15. Ponena za chinsinsi chopatulika cha Mulungu, kodi nchiyani chimene chachitika chiyambire 1914?
15 Pamene anawonekera m’thupi, ndi Chitsanzo chabwino kwambiri chotani nanga chimene Yesu anali! Ndi momvekera chotani nanga mmene chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu chinakwaniritsidwira mwa iye! Ndi molimba mtima chotani nanga mmene iye analemekezera dzina la Yehova! Ndipo ndi modabwitsa chotani nanga mmene Atate wa Yesu anamfupira iye kaamba ka njira yake yosunga umphumphu! Komabe padakali zowonjezereka ku chinsinsi chopatulika cha Mulungu. Chiyambire 1914, takhala tikukhala ndi moyo “m’tsiku la Ambuye.” (Chibvumbulutso 1:10) Monga mmene Chibvumbulutso 10:7 chikulongosolera, iri nthaŵi kaamba ka ‘chinsinsi chopatulika cha Mulungu mogwirizana ndi mbiri yabwino yoyenera kubweretsedwa ku mathedwe.’ Mawu a kumwamba tsopano alengeza akuti: “Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, [Yehova] ndi wa Kristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthaŵi za nthaŵi.” (Chibvumbulutso 11:15) Yehova wakhazikitsa Mfumu Yaumesiya, Yesu Kristu, pa mpando wake wachifumu waulemerero kukhala wolamulira mnzake ndi Iye!
16. Kodi ndimotani mmene Mfumu yoikidwa chatsopano, Yesu Kristu, anasonyezera mofulumira kulingalira kwake kaamba ka umulungu m’mwamba?
16 Monga wolamulira mnzake wa Mulungu mu Ufumu wobadwa chatsopano, Yesu akutchedwanso Mikaele (lotanthauza, “Alingana ndi Mulungu Ndani?”). Palibe woukira amene angapambane nkomwe kukhala wofanana ndi Mulungu, ndipo Mfumu yoikidwa chatsopanoyo inasonyeza chimenechi mofulumira mwa kuponya Njoka yakaleyo, Satana, ndi angelo ake pa dziko lapansi. (Chibvumbulutso 12:7-9) Inde, Yesu amasamalira umulungu m’mwamba, mongadi mmene iye anasonyezera kudzipereka kwaumulungu pamene adali padziko lapansi. Yesu Kristu wolemekezeka sadzapuma kufikira atachotseratu chipembedzo chonyenga ndi kuwonongeratu gulu la Satana, lowoneka ndi losawoneka.
17. Chiyambire 1914, kodi nchiyani chimene chakhala chikuchitika m’kukwaniritsa Mateyu 25:31-33?
17 Chiyambire 1914 kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu pa Mateyu 25:31-33 kwawunikira chinsinsi chopatulika cha Mulungu mowonekera. Panopa Yesu akulengeza kuti: “Pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake; ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa ku dzanja lake lamanja, koma mbuzi ku lamanzere.” Kuchokera pa malo ake owonera zinthu kumwamba, Mfumu yaulemerero imeneyi, Woweruza, ndi Wochilikiza kudzipereka kwaumlungu idzabwezera, choyamba pa munthu wosayeruzika ndi mbali zina za Babulo Wamkulu, ndipo kenaka pa mbali zonse zotsalira ndi achirikizi onga mbuzi a gulu loipa la padziko lapansi la Satana. Pamenepo Satana adzaikidwa ku phompho. (Chibvumbulutso 20:1-3) Koma “olungama” onga nkhosa adzaloŵa m’moyo wosatha. (Mateyu 25:46) Lolani kuti kulondola kwanu kwa kudzipereka kwaumulungu kukuikeni inu m’gulu lolungama limenelo!
18. Kodi ndi mwaŵi wosangalatsa wotani umene tiri nawo m’chigwirizano ndi chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu?
18 Chibvumbulutso 19:10 chimatilimbikitsa ife “kulambira Mulungu.” Ndipo kodi nchifukwa ninji? Lembalo likupitiriza kuti: “Pakuti umboni wa Yesu ndiwo mzimu wa chinenero.” Chotero ochulukira a maulosi owuziridwa a nthaŵi zakale anachitira umboni za Yesu! Ndipo pamene maulosi amenewa akwaniritsidwa, chinsinsi chopatulika cha Mulungu chakhala chowonekera kotheratu. Chotero, timasangalala kudziŵa kuti chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu kumeneku chinadzazindikiridwa mwa Yesu. Tiri ndi mwaŵi wosaneneka kutsatira m’mapazi ake monga atumiki odzichepetsa a Ufumu wa Mulungu. Inde, ndife olemekezedwa kugaŵana m’kumvetsetsa ndi kulengeza chinsinsi chopatulika chonse cha Mulungu mogwirizana ndi mbiri yabwino!
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Kodi nchiyani chimene tingaphunzire m’chitsanzo cha Yesu cha kudzipereka kwaumulungu?
◻ Kodi ndimotani mmene tingakhalire ndi moyo m’chilungamo monga mmene Kristu anachitira?
◻ Kodi ndi chinsinsi chomvetsa chisoni chotani chimene chikusiyana kwenikweni ndi chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu?
◻ Kodi chiyamikiro chathu cha chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu chiyenera kutisonkhezera kuchita chiyani?
[Chithunzi patsamba 16]
Monga m’chilikizi wa kudzipereka kwaumulungu ndi mlengezi wachangu wa Ufumu, Yesu anauza Pilato kuti: “Ndinadzera ichi ine padziko lapansi, kuti ndichitire umboni chowonadi”
[Chithunzi patsamba 18]
Kudzipereka kwaumulungu kwa Yesu kunasonyezedwa pamene anatsutsa alembi ndi Afarisi