Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 5/15 tsamba 16-20
  • Mtundu wa Chikhulupiriro Chanu Ukuyesedwa Tsopano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtundu wa Chikhulupiriro Chanu Ukuyesedwa Tsopano
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Inu Mungayesedwe Motani?
  • Kupindula ndi Chikhulupiriro Choyesedwa
  • Chikhulupiriro Chachikristu Chidzayesedwa
    Nsanja ya Olonda—1998
  • ‘Ndiyeseni, Yehova’
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Mayesero Tiziwaona Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2002
  • “Ndithandizeni M’mene Ndisoŵa Chikhulupiriro!”
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 5/15 tsamba 16-20

Mtundu wa Chikhulupiriro Chanu Ukuyesedwa Tsopano

“Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, mmene mukugwa m’mayesero a mitundu mitundu; pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.”​—YAKOBO 1:2, 3.

1. Nchifukwa chiyani Akristu ayenera kuyembekezera ziyeso pa chikhulupiriro chawo?

AKRISTU oona samakhumba kuvutika ayi, ndipo samasangalala nako kupwetekedwa ndi kunyozedwa. Komabe, amakumbukira mawu ali pamwambawa olembedwa ndi Yakobo, mbale wake wa Yesu mwa atate ena. Kristu anauza ophunzira ake momvekera bwino kuti anayenera kuyembekezera chizunzo ndi zovuta zina chifukwa chotsata njira za Mulungu. (Mateyu 10:34; 24:9-13; Yohane 16:33) Komabe, ziyeso zoterozo zingatipatse chimwemwe. Motani?

2. (a) Ndi motani mmene ziyeso za chikhulupiriro chathu zingatipatsire chimwemwe? (b) Kodi chipiriro chingachite motani ntchito yake kwa ife?

2 Chifukwa chachikulu chimene timapezera chimwemwe pokumana ndi mayesero kapena ziyeso pa chikhulupiriro chathu nchakuti izo zitha kubala zipatso zabwino. Monga momwe ananenera Yakobo, kuchirimika polimbana ndi ziyeso kapena zovuta ‘kumachita chipiriro.’ Tikhoza kupindula mwa kukulitsa mkhalidwe wachikristu umenewo. Yakobo analemba kuti: “Chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chirema, osasoŵa kanthu konse.” (Yakobo 1:4) Chipiriro chili ndi “ntchito” yoichita. Ntchito yake ndiyo kutikwaniritsa m’mbali zonse, kutithandiza kukhala Akristu okwana bwinobwino. Choncho, polola mayesero kuchita ntchito yake, ndi kusayesa kugwiritsira ntchito njira zosemphana ndi Malemba zowathetsera msanga, chikhulupiriro chathu chimayesedwa ndi kuyengedwa. Ngati takhala tikusoŵa kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kapena chikondi pochita ndi mikhalidwe ina kapena ndi anthu anzathu, chipiriro chingatithandize. Inde, dongosolo lake ndi ili: Ziyeso zimabala chipiriro; chipiriro chimakulitsa mikhalidwe yachikristu; zimenezi zimapatsa chimwemwe.​—1 Petro 4:14; 2 Petro 1:5-8.

3. Nchifukwa chiyani sitiyenera kuopa mayesero a chikhulupiriro chathu?

3 Mtumwi Petro anagogomezeranso chifukwa chake sitiyenera kuchita mantha kapena kuopa ziyeso za chikhulupiriro chathu. Iye analemba kuti: “Mmenemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthaŵi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu, kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo amtengo wake woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Kristu.” (1 Petro 1:6, 7) Mawu ameneŵa ali olimbikitsa kwambiri makamaka tsopano chifukwa “chisautso chachikulu”​—nthaŵi ya chitamando, ulemerero, ulemu, ndi chipulumutso​—chayandikira kwambiri kuposa mmene ena akuganizira komanso chili pafupi kuposa pamene tinakhala okhulupirira.​—Mateyu 24:21; Aroma 13:11, 12.

4. Kodi mbale wina anaziona bwanji ziyeso zimene iye ndi Akristu odzozedwa ena anakumana nazo?

4 M’nkhani yapitayo, tinakambitsirana ziyeso zimene otsalira odzozedwa anakumana nazo kuchokera mu 1914 kumka mtsogolo. Kodi zimenezo zinawapatsa chimwemwe? A. H. Macmillan anapereka maganizo ake pa zimene anaona kumbuyoko nati: “Ndaona mayesero ambiri oopsa omwe anafika pa gululi ndi ziyeso pa chikhulupiriro cha anthu ali mmenemo. Mwa chithandizo cha mzimu wa Mulungu gululi linapulumuka ndipo likupitabe patsogolo. Ndaona nzeru ya kuyembekezera Yehova moleza mtima kuti aunike kamvedwe kathu pazinthu za m’Malemba m’malo mokhumudwa ndi lingaliro latsopano. . . . Zilibe kanthu kaya tingapange masinthidwe otani nthaŵi ndi nthaŵi malinga ndi maganizo athu, zimenezo sizingasinthe makonzedwe a dipo ndi lonjezo la Mulungu la moyo wosatha. Choncho sitiyenera kulola chikhulupiriro chathu kufooka chifukwa cha ziyembekezo zosakwaniritsidwa kapena masinthidwe pamalingaliro ena.”​—Nsanja ya Olonda yachingelezi ya August 15, 1966, tsamba 504.

5. (a) Ndi mapindu otani amene anapezeka pamene otsalira anapirira ziyeso? (b) Nchifukwa chiyani ife tsopano tikufuna kudziŵa bwino za nkhani ya kuyesedwa imeneyi?

5 Akristu odzozedwa omwe anapirira nyengo yakuyesedwa ya 1914​—19 anamasulidwa pachisonkhezero champhamvu cha dziko ndi pa miyambo yambirimbiri ya chipembedzo yachibabulo. Otsalira anapita patsogolo monga anthu oyeretsedwa ndi oyengedwa, akumapereka nsembe mwaufulu zotamanda Mulungu nakhala ndi chitsimikizo chakuti anali anthu ovomerezedwa kwa iye. (Yesaya 52:11; 2 Akorinto 6:14-18) Chiweruzo chinali chitayambira panyumba ya Mulungu, koma sichinathere panthaŵi imeneyo. Kuyesa ndi kuyenga anthu a Mulungu kudakapitirizabe. Aja oyembekezera kupulumuka “chisautso chachikulu” monga a “khamu lalikulu” chikhulupiriro chawo chikuyesedwanso. (Chivumbulutso 7:9, 14) Zimenezi zikuchitika m’njira zofanana ndi zimene otsalira odzozedwa anakumana nazo ndi mwanjira zinanso.

Kodi Inu Mungayesedwe Motani?

6. Kodi ambiri akumana ndi chiyeso choopsa chotani?

6 Akristu ambiri alingalira za vuto lakulimbana ndi ziyeso za kuukiridwa mwachindunji. Iwo amakumbukira lipoti ili: “[Atsogoleri achiyuda] mmene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula. Pamenepo ndipo anapita kuchokera ku bwalo la akulu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo.” (Machitidwe 5:40, 41) Ndipo mbiri yamakono ya anthu a Mulungu, makamaka mkati mwa nkhondo zapadziko lonse, imasonyeza bwino lomwe kuti Mboni za Yehova zambiri zinakwapulidwa koipitsitsa ndi ozunza.

7. Kodi Akristu ena amakono aonetsa chikhulupiriro chawo mpaka pamlingo wotani?

7 Ponena za kuzunzidwa kwa Akristu, dziko silisiyanitsa pakati pa otsalira odzozedwa ndi khamu lalikulu la “nkhosa zina.” (Yohane 10:16) Pazaka zonsezi, a m’magulu onse aŵiriwo ayesedwa koopsa mwa kuponyedwa m’ndende ndipo ngakhale kunyongedwa chifukwa cha kukonda kwawo Mulungu ndi kumkhulupirira. Magulu onsewo afunikira mzimu wa Mulungu, mosasamala kanthu za chiyembekezo chawo. (Yerekezerani ndi Nsanja ya Olonda ya June 15, 1996, tsamba 31.) M’ma 1930 ndi ma 1940 m’Germany wa Nazi, atumiki a Yehova ambiri, kuphatikizapo ana, anaonetsa chikhulupiriro chodabwitsa, ndipo ambiri anayesedwa kotheratu. M’zaka zaposachedwa, anthu a Yehova akumana ndi chiyeso cha kuzunzidwa m’maiko onga Burundi, Eritrea, Ethiopia, Malaŵi, Mozambique, Rwanda, Singapore, ndi Zaire. Ndipo ziyeso zonga zimenezi zikupitirizabe.

8. Kodi mawu a mbale wina wa mu Afirika akusonyeza motani kuti chikhulupiriro chathu chimayesedwa m’zambiri osati chabe kupirira chizunzo cha kumenyedwa?

8 Komabe, monga taonera kale, chikhulupiriro chathu chikuyesedwanso m’njira zina zamachenjera. Ziyeso zina si zachindunji ndipo nzosazindikirika msanga. Taganizirani mmene mungachitire pazotsatirazi. Mbale wina ku Angola yemwe anali ndi ana khumi anali mumpingo umene kwa nthaŵi yaitali ndithu unalibe njira yolankhulirana ndi abale audindo. Pambuyo pake kunakhala kotheka kuchezera mpingowo. Iye anafunsidwa za mmene anakwanitsira kudyetsa banja lake. Zinali zovuta kuti ayankhe, anangoti zinali zovuta. Kodi anakhoza kudyetsa ana ake ngakhale kamodzi kokha patsiku? Poyankha iye anati: “Komatu movutikira. Taphunzira kupulumukira pa kamene tili nako.” Kenako ndi liwu lodzaza chidaliro, anati: “Nanga sizimene tiyenera kuyembekezera zimenezi m’masiku otsiriza ano?” Chikhulupiriro choterocho nchodabwitsa m’dzikoli, koma sichachilendo pakati pa Akristu okhulupirika, amene ali ndi chidaliro chonse chakuti malonjezo a Ufumu adzakwaniritsidwa.

9. Kodi tikuyesedwa motani mogwirizana ndi 1 Akorinto 11:3?

9 Akhamu lalikulu akuyesedwanso m’kachitidwe ka zinthu ka teokrase. Mpingo wachikristu wa dziko lonse ukutsogozedwa motsata mapulinsipulo aumulungu ndi malamulo ateokrase. Zimenezi zimafuna choyamba kuzindikira Yesu monga Mtsogoleri, amene wasankhidwa monga Mutu wa mpingo. (1 Akorinto 11:3) Mtima wogonjera kwa iye ndi Atate wake timauonetsa mwa kukhulupirira oikidwawo ndi zigamulo zimene zimapangidwa zotigwirizanitsa pamodzi pochita chifuniro cha Yehova. Ndiponso, mumpingo uliwonse, muli amuna oikidwa monga atsogoleri. Iwo ndi anthu opanda ungwiro amene tikhoza kuona zofooka zawo mosavuta; komabe tikulangizidwa kuti oyang’anirawo tiwalemekeze ndi kuwagonjera. (Ahebri 13:7, 17) Kodi nthaŵi zina kumakuvutani kuchita zimenezo? Kodi chimenechi chilidi chiyeso kwa inu? Ngati zili choncho, kodi mukupindula ndi chiyeso chimenechi pa chikhulupiriro chanu?

10. Kodi timakumana ndi chiyeso chotani ponena za utumiki wakumunda?

10 Timayesedwanso pa mwayi wathu ndi udindo wathu woloŵa nawo mu utumiki wakumunda mokhazikika. Kuti tipambane chiyeso chimenechi, tiyenera kuzindikira kuti kutenga mbali mokwanira mu utumiki kumalira zambiri, osati chabe kulalikira kwa patalipatali. Kumbukirani mawu a Yesu othokoza mkazi wamasiye waumphaŵi uja amene anapereka zake zonse. (Marko 12:41-44) Tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndikudzipereka kwathunthu pautumiki wakumunda?’ Tonsefe tiyenera kukhala Mboni za Yehova tsiku lonse lathunthu, tikumakhala okonzekera kuŵalitsa kuunika kwathu pampata uliwonse.​—Mateyu 5:16.

11. Kodi kusintha m’kamvedwe ka mfundo zina kapena uphungu wa khalidwe ungakhale chiyeso motani?

11 Chiyeso china chimene tingakumane nacho chikukhudzana ndi mlingo wa chiyamikiro chathu pakuunika kowonjezereka kwa choonadi cha Baibulo ndi mauphungu operekedwa ndi kagulu kakapolo wokhulupirika. (Mateyu 24:45) Nthaŵi zina zimenezi zimafuna kusintha khalidwe lathu laumwini, monga nthaŵi ina pamene kunaunikidwa bwino kuti onse osuta fodya akayenera kusiya ngati anafuna kukhalabe mumpingo.a (2 Akorinto 7:1) Kapena chiyeso chingakhale pakusiya nyimbo zina zimene timakonda kapena mitundu ina ya zosangulutsab Kodi tidzakayikira nzeru yake ya uphungu woperekedwawo? Kapena kodi tidzalola mzimu wa Mulungu kuumba kalingaliridwe kathu ndi kutithandiza kuvala umunthu wachikristu?​—Aefeso 4:20-24; 5:3-5.

12. Kodi chofunika nchiyani kuti munthu alimbitse chikhulupiriro chake pambuyo paubatizo?

12 Kwa zaka makumi ambiri, chiŵerengero cha khamu lalikulu chakhala chikuwonjezeka, ndipo pambuyo pobatizidwa amapitiriza kulimbitsa unansi wawo ndi Yehova. Zimenezi zimaphatikizapo zambiri, osati chabe kufika pamsonkhano wachikristu, pamisonkhano ina pa Nyumba ya Ufumu, kapena kuloŵa nawo mu utumiki wakumunda mwa kamodzikamodzi ayi. Tifanizire motere: Munthu angakhale kunja kwa Babulo Wamkulu mwakuthupi, ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, koma kodi iye wachokamodi ndi mtima wake wonse? Kodi adakaumirirabe pazinthu zosonyeza mzimu wa Babulo Wamkulu​—mzimu wonyalanyaza makhalidwe olungama a Mulungu? Kodi kudzisungira ndi kukhulupirika pabanja amakutenga mopepuka? Kodi amakonda kwambiri zinthu zakuthupi kuposa zauzimu? Inde, kodi iye wakhaladi wopanda banga la dzikoli?​—Yakobo 1:27.

Kupindula ndi Chikhulupiriro Choyesedwa

13, 14. Kodi ena achitanji atayamba kale kuyenda m’njira ya kulambira koona?

13 Ngati tathaŵadi kuchoka ku Babulo Wamkulu ndi kuchokanso ku dziko, tisayang’ane pazinthu zakumbuyo. Mogwirizana ndi mfundo ya pa Luka 9:62, kuti wina aliyense mwa ife ayang’ane kumbuyo kukatanthauza kulephera kukhala nzika ya Ufumu wa Mulungu. Yesu anati: “Palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang’ana za kumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu.”

14 Koma ena amene anakhala Akristu kumbuyoku alola kufanizidwa ndi dongosolo la zinthu lilipoli. Iwo sanakanize mzimu wa dzikoli. (2 Petro 2:20-22) Zocheukitsa za dziko zawakopa iwo ndi kuwalanda nthaŵi, moti zatsamwitsa kupita kwawo patsogolo. M’malo mosumika maganizo ndi mitima yawo pa Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake, akumaziika patsogolo m’moyo wawo, iwo apambuka panjira nayamba kutsatira zolinga zakuthupi. Iwo afunikira kuzindikira chikhulupiriro chawo chofookacho ndi kufunda kwawoko kuti asinthe njira yawo mwa kufuna uphungu waumulungu, apo phuluzi, ali pangozi yotaya unansi wamtengo wapatali umene ali nawo ndi Yehova limodzi ndi gulu lake.​—Chivumbulutso 3:15-19.

15. Kodi kumaliranji kukhalabe wovomerezeka pamaso pa Mulungu?

15 Kuti tidzapezedwe oyanjidwa ndi oyenera chipulumutso pa chisautso chachikulu chofika mofulumiracho kudzadalira pakusunga kwathu chiyero, ‘kuyeretsa zovala zathu m’mwazi wa Mwanawankhosa.’ (Chivumbulutso 7:9-14; 1 Akorinto 6:11) Ngati sitikhala ndi kaimidwe koyera, ndi kolungama pamaso pa Mulungu, utumiki wathu wopatulika sudzalandiridwa. Ndithudi, aliyense wa ife ayenera kuzindikira kuti kuyesedwa kwa chikhulupiriro chathu kudzatithandiza kupirira ndi kupeŵa mkwiyo wa Mulungu.

16. Kodi mabodza angakhale motani chiyeso pachikhulupiriro chathu?

16 Nthaŵi zina, ofalitsa nkhani ndi akuluakulu ena amanena zonama ponena za anthu a Mulungu, akumaipitsa mbiri ya ziphunzitso zathu zachikristu ndi moyo wathu. Zimenezitu zisatidabwitse ayi, chifukwa Yesu akunena momvekera bwino kuti ‘dziko litida chifukwa sitili a dziko.’ (Yohane 17:14) Kodi tidzalola aja amene Satana akuwakhalitsa akhungu kuti atiopseze ndi kutifooketsa kuti tichite manyazi ndi uthenga wabwino? Kodi tidzalola mabodza ounjikidwa pachoonadi kutibweza m’mbuyo pakusonkhana mokhazikika ndi pantchito yathu yolalikira? Kapena kodi tidzachirimika komanso kukhala olimbika ndi otsimikiza mtima kuposa ndi kalelonse popitiriza kubukitsa choonadi cha Yehova ndi Ufumu wake?

17. Kodi ndi chitsimikizo chotani chimene chingatisonkhezere kusaleka kuonetsa chikhulupiriro chathu?

17 Malinga ndi kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo, tsopano tikukhala mkati mwenimweni mwa nthaŵi yamapeto. Ziyembekezo zathu zozikidwa pa Baibulo za dziko latsopano lachilungamo zili zotsimikizirika kuti zidzakwaniritsidwa mosangalatsa. Mpaka kufika kwa tsikulo, tiyeni tonsefe tisonyeze chikhulupiriro chosagwedera pa Mawu a Mulungu ndi kutsimikizira za chikhulupiriro chathu mwa kusaleka kulalikira padziko lonse uthenga wabwino wa Ufumu. Talingalirani za zikwizikwi za ophunzira atsopano omwe akubatizidwa mlungu ndi mlungu. Kodi chimenecho sichifukwa chabwino chokhalira oyamikira kuti kuleza mtima kwa Yehova ponena za kupereka chiweruzo chake kungapatse anthu ambiri mwayi wopulumuka? Sitili osangalala kodi poona kuti Mulungu walola ntchito yopulumutsa moyo yolalikira Ufumu kuti ipitirize? Ndipo sitili okondwa kodi, poona kuti mamiliyoni alandira choonadi komanso akuonetsa chikhulupiriro chawo?

18. Kodi muli wotsimikiza mtima chotani ponena za kutumikira Yehova?

18 Sitikudziŵa kuti kuyesedwa kwa chikhulupiriro chathu kumeneku kupitiriza mpaka liti. Koma za ichi chokha tili otsimikiza: Kuti Yehova ali ndi tsiku loikika lakuweruza miyamba yoipa ilipoyi ndi dziko lake. Padakali pano, tiyeni tikhale otsimikiza mtima kutsanzira chikhulupiriro chenicheni choyesedwa chimene anaonetsa Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu, Yesu. Ndipo tiyeni titengere chitsanzo cha otsalira odzozedwa okalambawo ndi cha enanso pakati pathu omwe akutumikira molimbika mtima.

19. Kodi nchiyani chimene muli otsimikiza za icho kuti chidzalaka dzikoli?

19 Tiyenera kutsimikiza mtima kumalengeza mosalekeza uthenga wabwino ku mtundu uliwonse, fuko, manenedwe, ndi anthu mogwirizana ndi mngelo wakuuluka mumlengalenga. Lolani kuti amve chilengezo cha mngelo chakuti: “Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake.” (Chivumbulutso 14:6, 7) Chiweruzocho chitaperekedwa, kodi chidzatsatirapo nchiyani ponena za chikhulupiriro chathu choyesedwa? Kodi sichidzakhala chilakiko chaulemerero​—kulanditsidwa ku dongosolo la zinthu lilipoli ndi kuloŵa m’dziko latsopano lolungama la Mulungu? Mwa kupirira ziyeso za chikhulupiriro chathu, tidzanenadi mmene ananenera mtumwi Yohane kuti: “Ichi ndi chilako tililaka nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu.”​—1 Yohane 5:4.

[Mawu a M’munsi]

a Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya June 1, 1973, masamba 336-43, ndi July 1, 1973, masamba 409-11.

b Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya July 15, 1983, masamba 27-31.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi ndi motani mmene ziyeso za chikhulupiriro chathu zingatipatsire chimwemwe?

◻ Kodi ndi ziyeso zina ziti za chikhulupiriro chathu zimene kungakhale kovuta kuzizindikira?

◻ Kodi ndi motani mmene tingapezere mapindu osatha ngati tilaka ziyeso za chikhulupiriro chathu?

[Zithunzi patsamba 17]

A. H. Macmillan (patsogolo chakumanzere) pafupifupi nthaŵi imene iye ndi akuluakulu ena a Watch Tower Society anaponyedwa m’ndende kosayenera

Iye anali nthumwi pamsonkhano wa ku Detroit, ku Michigan, mu 1928

M’zaka zake zomalizira, Mbale Macmillan anaonetsabe chikhulupiriro chake

[Chithunzi patsamba 18]

Mofanana ndi banjali, Akristu ambiri mu Afirika aonetsa chikhulupiriro choyesedwa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena