-
Kodi “Kukonda Adani Anu” Kumatanthauza Chiyani”?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
‘Muzidalitsa omwe amakutembererani.’ (Luka 6:28) Timadalitsa adani athu polankhula nawo mokoma mtima ndiponso mowaganizira, ngakhale pomwe iwowo akutilankhula mwachipongwe. Baibulo limati: “Osabwezera . . . chipongwe pa chipongwe, koma m’malomwake muzidalitsa.” (1 Petulo 3:9) Malangizo amenewa angatithandize kuthetsa chidani.
-