Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 4/15 tsamba 13-19
  • Funafunani Mtendere Weniweni ndi Kuulondola!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Funafunani Mtendere Weniweni ndi Kuulondola!
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu Atha Kukhala Amtendere
  • Awo Amene Akulondola Mtendere
  • Kusintha Kwakukulu Kwambiri
  • Ulamuliro wa Kalonga wa Mtendere
  • Kodi Adzatsogolera Anthu ku Mtendere Ndani?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Mtendere Weniweni—Kodi Udzachokera Kuti?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Mtendere wa Umulungu Kaamba ka Awo Ophunzitsidwa ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Mmene Mungakumanire ndi Mtendere wa Umulungu Mokwanira Kwambiri?
    Nsanja ya Olonda—1987
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 4/15 tsamba 13-19

Funafunani Mtendere Weniweni ndi Kuulondola!

“Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, . . . apatuke pachoipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuulondola.” ​—1 PETRO 3:10, 11.

1. Kodi ndi mawu odziŵika ati a Yesaya amene mosakayikira adzakwaniritsidwa ndithu?

“ADZASULA malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” (Yesaya 2:4) Ngakhale kuti lemba lotchukali analiika pafupi ndi malikulu a dziko lonse a United Nations ku New York City, bungwe la padziko lonse limenelo lalephera kotheratu kulikwaniritsa. Komabe, pokhala mbali ya mawu otsimikizika a Yehova Mulungu, chilengezo chimenecho chidzachitikadi.​—Yesaya 55:10, 11.

2. Kodi “padzakhala” chiyani “masiku otsiriza,” malinga ndi Yesaya 2:2, 3?

2 Kwenikweni, mawu opezeka pa Yesaya 2:4 ali mbali ya ulosi wina wochititsa chidwi, ulosi wonena za mtendere weniweni​—ndipo ukukwaniritsidwa m’nthaŵi yathu yomwe ino. Ulosiwo usanalengeze ziyembekezo zosangalatsa kwambirizo zakuti nkhondo ndi zida zankhondo sizidzakhalakonso, uwo umati: “Padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pansonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. Ndipo anthu ambiri adzamka, nati, Tiyeni tikwere kumka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake; chifukwa m’Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mawu a Yehova kuchokera m’Yerusalemu.”​—Yesaya 2:2, 3.

Anthu Atha Kukhala Amtendere

3. Kodi munthu angasinthe motani kuchoka pa kukhala wankhondo kukhala wamtendere?

3 Onanitu kuti anthu ayenera kulangizidwa njira za Yehova asanalondole njira ya mtendere. Kutsatira chiphunzitso cha Yehova kungasinthe kaganizidwe ka munthu ndi zochita zake, kotero kuti amene anali wankhondo amakhala wamtendere. Kodi kusandulika kumeneku kumatheka bwanji? Aroma 12:2 amati: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” Timakonzanso mtima wathu, kapena kuusonkhezera pazinthu zosiyana ndi zoyamba, mwa kuudzaza ndi mapulinsipulo ndi malamulo a m’Mawu a Mulungu. Phunziro la Baibulo lokhazikika limatithandiza pakusintha kumeneku ndipo limatitheketsa kuzindikira chimene chili chifuniro cha Yehova kwa ife, kuti tione bwino lomwe kumene tiyenera kupita.​—Salmo 119:105.

4. Kodi munthu amavala motani umunthu watsopano wa mtendere?

4 Choonadi cha Baibulo sichimangosanduliza kaganizidwe kathu komanso zochita zathu ndi umunthu wathu. Chimatithandiza kuchita zimene mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuchita: “Muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; koma . . . mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.” (Aefeso 4:22-24) Mzimu wa mtima umenewu ndi wamkati. Umasandulika ndi kukhala wamphamvu pamene chikondi chathu cha Yehova ndi malamulo ake chikula, ndipo umatichititsa kukhala anthu auzimu ndi amtendere.

5. Kodi “lamulo latsopano” limene Yesu anapatsa ophunzira ake limachititsa motani mtendere pakati pawo?

5 Timaona kufunika kwa kusandulika kumeneku pamalangizo amene Yesu anapatsa ophunzira ake kutangotsala maola angapo kuti asakhalenso nawo: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34, 35) Chikondi chonga cha Kristu chimenechi chopanda dyera chimamangirira ophunzira pamodzi mu umodzi wangwiro. (Akolose 3:14) Okhawo ofunitsitsa kulandira ndi kutsatira “lamulo latsopano” limeneli ndiwo adzasangalala ndi mtendere umene Mulungu akulonjeza. Kodi pali anthu alionse amene akuchita zimenezi lerolino?

6. Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zili pamtendere, mosiyana ndi anthu akudziko?

6 Mboni za Yehova zimayesayesa kusonyeza chikondi mu ubale wawo wapadziko lonse. Ngakhale kuti zachokera m’mitundu yonse ya m’dziko, sizimaloŵa m’mikangano yadziko, ngakhale zitakakamizidwa kwambiri ndi ndale kapena zipembedzo zina. Monga anthu ogwirizana, iwo akuphunzitsidwa ndi Yehova, ndipo ali pamtendere. (Yesaya 54:13) Iwo amasunga uchete pamikangano yandale, ndipo saloŵa m’nkhondo. Ena amene kale anali achiwawa ausiya moyo umenewo. Iwo akhala Akristu okonda mtendere, otsanzira chitsanzo cha Kristu Yesu. Ndipo ndi mtima wonse amamvera uphungu wa Petro wakuti: “Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choipa, ndi milomo yake isalankhule chinyengo; ndipo apatuke pachoipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuulondola.”​—1 Petro 3:10, 11; Aefeso 4:3.

Awo Amene Akulondola Mtendere

7, 8. Tchulani zitsanzo za anthu amene anasiya nkhondo ndi kukhala ofunafuna mtendere weniweni. (Simbani za ena amene mudziŵa.)

7 Mwachitsanzo, pali Rami Oved, yemwe kale anali mkulu wa gulu la akatswiri olimbana ndi zigaŵenga. Iye anaphunzitsidwa kupha adani ake. Anakonda kwambiri dziko lake la Israel kufikira tsiku lina pamene anadziŵa kuti arabi sanafune kuti iye akwatire mkazi amene anakonda chifukwa chabe chakuti anali Mmwenye, Wakunja. Anayamba kufunafuna choonadi m’Baibulo. Kenako anakumana ndi Mboni za Yehova. Kuphunzira kwake Baibulo ndi Mboni kunamkhutiritsa maganizo kuti sayenera kukhalanso wodzipereka pa utundu. Chikondi chachikristu chinatanthauza kusiya nkhondo ndi zida ndiyeno kuphunzira kukonda anthu a mitundu yonse. Mmene anadabwira nanga pamene analandira kalata yosonyeza kukoma mtima imene inayamba ndi mawu akuti, “Mbale wanga Rami”! Kodi panali chiyani chachilendo pamenepo? Amene anailemba anali Mboni ina yachipalestina. “Kwa ineyo zinali zosatheka zimenezo,” akutero Rami, “popeza kuti Apalestina anali adani anga, ndipo pano mmodzi wa iwo anali kunditcha ‘Mbale Wanga.’” Rami ndi mkazi wake tsopano akulondola mtendere weniweni m’njira ya Mulungu.

8 Chitsanzo china ndi chija cha Georg Reuter, amene anali m’gulu la nkhondo la German limene linaloŵa m’Russia m’Nkhondo Yadziko II. Posapita nthaŵi anagwiritsidwa mwala ndi zolinga zopanda pake za Hitler za kulamulira dziko lonse. Atabwerako kunkhondo, anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Analemba kuti: “Potsirizira pake, zinthu zinayamba kumveka kwa ine. Ndinazindikira kuti Mulungu sindiye anali ndi mlandu wa kukhetsa mwazi konseko . . . Ndinaphunzira kuti chifuno chake nchakuti akhazikitse paradaiso wa padziko lonse lapansi ndi kupatsa anthu omvera madalitso osatha. . . . Hitler anadzitama ndi ‘Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi’ koma anangolamulira [zaka] 12​—ndipo zotulukapo zake zinali zoopsa! Ndi Kristu osati Hitler . . . amene angakhazikitse ulamuliro wa zaka chikwi padziko lapansi ndipo adzaterodi.” Kwa zaka ngati 50 tsopano, Georg wakhala akutumikira monga nthumwi ya mtendere weniweni mu utumiki wa nthaŵi zonse.

9. Kodi chokumana nacho cha Mboni za Yehova ku Nazi Germany chimasonyeza motani kuti ndi zolimba mtima komabe zamtendere?

9 Umphumphu ndi uchete wa Mboni za Yehova ku Germany panthaŵi ya ulamuliro wa Nazi ukupitirizabe kupereka umboni wa chikondi chawo cha Mulungu ndi mtendere ngakhale tsopano, zaka zoposa 50 pambuyo pake. Kabuku kofalitsidwa ndi Holocaust Memorial Museum ku Washington, D.C. ku United States, kamati: “Mboni za Yehova zinapirira chizunzo choopsa mu ulamuliro wa Nazi. . . . Kulimba mtima kumene ambiri anasonyeza pokana [kusiya chipembedzo chawo], mosasamala kanthu za kuzunzidwa, kuvutitsidwa m’misasa yachibalo, ndipo nthaŵi zina kuphedwa, kunachititsa anzawo ambiri kuwalemekeza.” Ndiyeno kakuwonjezera kuti: “Pachimasuko cha misasayo, Mboni za Yehova zinapitirizabe ndi ntchito yawo, zikumapita uku ndi uku pakati pa opulumukawo, kuwatembenuza.”

Kusintha Kwakukulu Kwambiri

10. (a) Kodi ndi kusintha kwakukulu kotani kumene kukufunika kuti mtendere weniweni udze? (b) Kodi buku la Danieli linazisonyeza motani zimenezi?

10 Kodi zimenezi zikutanthuza kuti Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti zingadzetse mtendere padziko lonse mwa kutembenuza anthu ochuluka kuti akhulupirire uchete wachikristu? Iyayi! Kuti padziko lapansi pakhalenso mtendere, pafunika kukhala kusintha kwakukulu kwambiri. Kotani? Ulamuliro wa anthu wochititsa magaŵano, wopondereza, ndi wachiwawa uyenera kuchoka kuti paloŵe ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, umene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuupempherera. (Mateyu 6:9, 10) Koma kodi zimenezo zidzachitika motani? M’maloto ouziridwa ndi Mulungu, mneneri Danieli anaphunzira kuti m’masiku otsiriza, Ufumu wa Mulungu, monga mwala waukulu ‘wosemedwa popanda manja a munthu,’ udzaphwanya fano lalikulu loimira maulamuliro andale a anthu a dzikoli. Ndiyeno analengeza kuti: “Masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka kunthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.”​—Danieli 2:31-44.

11. Kodi Yehova adzakudzetsa motani kusintha kofunikaku kuti pakhale mtendere?

11 Kodi nchifukwa ninji kusintha kwakukulu kumeneku kwa mkhalidwe wa dziko kudzachitika? Chifukwa Yehova walonjeza kuti adzayeretsa dziko lapansi kuchotsapo aja onse amene akuliipitsa ndi kuliwononga. (Chivumbulutso 11:18) Kusintha kumeneku kudzachitika pankhondo yolungama ya Yehova yowononga Satana ndi dziko lake loipa. Timaŵerenga pa Chivumbulutso 16:14, 16 kuti: “Pakuti ali [ndiko kuti, mizimu yonyansa] mizimu ya ziŵanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kumka kwa mafumu [olamulira andale] a dziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse. Ndipo anawasonkhanitsira kumalo otchedwa m’Chihebri Harmagedo.”

12. Kodi Armagedo idzakhala motani?

12 Kodi Armagedo idzakhala motani? Sidzakhala chiwonongeko cha nyukiliya kapena tsoka lina lochititsidwa ndi anthu. Ayi, iyo ndi nkhondo ya Mulungu yothetsa nkhondo zonse za munthu ndi kuwononga onse ochirikiza nkhondo zimenezi. Ndi nkhondo ya Mulungu yodzetsa mtendere weniweni kwa aja amene amakonda mtendere. Inde, Armagedo idzabwera monga Yehova wafunira. Sidzachedwa. Mneneri wake Habakuku anamuuzira kulemba kuti: “Masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.” (Habakuku 2:3) Chifukwa cha maganizo athu aumunthu zingaoneke monga Armagedo yachedwa kwambiri, koma Yehova amasunga nthaŵi yake. Iyo idzaulika paola limene Yehova anaikiratu.

13. Kodi Mulungu adzatani naye maliwongoyo, Satana Mdyerekezi?

13 Chochitika chosapeneka chimenechi chidzatsegulira njira mtendere weniweni! Koma kuti mtendere weniweni ukhazikitsidwe molimba, zina zake ziyenera kuchitidwa​—kuchotsapo uyo amene amachititsa magaŵano, udani ndi ndewu. Ndipo ndi zimenezo kumene, zimene Baibulo limalosera kuti zidzachitika​—kuponyedwa m’mphompho kwa Satana, woyambitsa nkhondo ndi atate wa bodza. Mtumwi Yohane anaona chochitika chimenechi m’masomphenya aulosi, olembedwa pa Chivumbulutso 20:1-3 kuti: “Ndinaona mngelo anatsika Kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha phompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye Mdyerekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi, namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi.”

14. Kodi chipambano cha Yehova pa Satana tingachifotokoze motani?

14 Limeneli si loto ayi; ndi lonjezo la Mulungu​—ndipo Baibulo limati: “Mulungu sakhoza kunama.” (Ahebri 6:18) Ndiye chifukwa chake Yehova anakhoza kunena kwa Yeremiya mneneri wake kuti: “Ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m’dziko lapansi, pakuti mmenemo ndikondwerera, ati Yehova.” (Yeremiya 9:24) Yehova amachita mwachiweruziro ndi chilungamo, ndipo amakondwera ndi mtendere umene adzadzetsa padziko lapansi.

Ulamuliro wa Kalonga wa Mtendere

15, 16. (a) Kodi ndani wasankhidwa ndi Yehova kuti alamulire monga Mfumu? (b) Kodi ulamuliro umenewo wafotokozedwa motani, ndipo ndani adzakhalamo ndi phande?

15 Kutsimikiza kuti mtendere weniweni udzadza kwa onse okhala m’makonzedwe ake a Ufumu, Yehova wapereka ulamuliro kwa Kalonga weniweni wa Mtendere, Yesu Kristu, monga kunaloseredwera pa Yesaya 9:6, 7 kuti: “Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa pheŵa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha . . . Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.” Wamasalmo nayenso analemba mwaulosi za ulamuliro wamtendere wa Mesiya kuti: “Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi.”​—Salmo 72:7.

16 Ndiponso, abale a Kristu 144,000 odzozedwa ndi mzimu adzalamulira limodzi naye kumwamba. Ameneŵa ndiwo oloŵa nyumba anzake a Kristu amene Paulo analemba za iwo kuti: “Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Kristu chikhale ndi inu nonse.” (Aroma 16:20) Inde, ameneŵa adzamenya nkhondo ali kumwamba pamodzi ndi Kristu, ndi kugonjetsa woyambitsa nkhondo, Satana Mdyerekezi!

17. Kodi tiyenera kuchitanji kuti tikapeze mtendere weniweni?

17 Choncho funso tsopano ndi ili, Kodi muyenera kuchitanji kuti mukapeze mtendere weniweni? Mtendere weniweni udzadza m’njira ya Mulungu yokha, ndipo kuti mukaupeze pali zimene muyenera kuchita motsimikiza. Muyenera kulandira Kalonga wa Mtendere ndi kutembenukira kwa iye. Zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kulandira Kristu monga Mombolo ndi Wopereka Dipo la anthu ochimwa. Yesu iye mwini ananena mawu odziŵikawa: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Kodi ndinu wofunitsitsa kusonyeza chikhulupiriro mwa Kristu Yesu monga Nthumwi ya Mulungu yodzetsa mtendere weniweni ndi chipulumutso? Palibe dzina lina pansi pa thambo limene lingadzetse mtendere ndi kuusungitsa. (Afilipi 2:8-11) Chifukwa ninji? Chifukwa Yesu ndiye Wosankhidwa wa Mulungu. Ndiye yekha mthenga wa mtendere wamkulu koposa yemwe anakhalako padziko lapansi. Kodi mudzamvetsera Yesu ndi kutsanzira chitsanzo chake?

18. Kodi tiyenera kuchitanji motsatira mawu a Yesu olembedwa pa Yohane 17:3?

18 “Moyo wosatha ndi uwu,” anatero Yesu, “kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Inoyo ndiyo nthaŵi yoloŵetsera chidziŵitso cholongosoka mwa kupezeka nthaŵi zonse pamisonkhano ya Mboni za Yehova pa Nyumba ya Ufumu. Misonkhano yophunzitsa imeneyi idzakusonkhezerani kuuza ena za chidziŵitso chanu ndi chiyembekezo chanu. Inunso mungakhale nthumwi ya mtendere wa Mulungu. Mungapeze mtendere tsopano mwa kukhulupirira Yehova Mulungu, monga momwe Yesaya 26:3 amanenera malinga ndi New International Version kuti: “Mudzamsunga mumtendere wangwiro iye amene maganizo ake ali okhazikika, chifukwa amakukhulupirirani inu.” Kodi muyenera kukhulupirira yani? “Khulupirirani Yehova nthaŵi zamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.”​—Yesaya 26:4.

19, 20. Kodi nchiyani chikuyembekeza awo amene akufunafuna mtendere ndi kuulondola lerolino?

19 Sankhani tsopano lino moyo wosatha m’dziko latsopano la mtendere la Mulungu. Pa Chivumbulutso 21:3, 4, Mawu a Mulungu akutitsimikiza kuti: “Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.” Kodi imeneyi sindiyo nthaŵi ya mtendere yamtsogolo imene mukulakalaka?

20 Pamenepo kumbukirani zimene Mulungu walonjeza. “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka. Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima! Pakuti kumatsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere.” (Salmo 37:11, 37) Pamene tsiku losangalatsalo lidzafika, tidzanenetu moyamikira kuti, “Mtendere weniweni potsirizira pake! Tithokoza Yehova Mulungu, amene apereka mtendere weniweni!”

Kodi Mungafotokoze?

◻ Kodi nchiyani chingamthandize munthu kusintha maganizo ndi zochita zake?

◻ Kodi Mboni za Yehova, aliyense payekha ndipo monga gulu, zasonyeza motani kukonda kwawo mtendere weniweni?

◻ Kodi Yehova adzatani nawo onse amene akuchirikiza udani ndi nkhondo?

◻ Kodi ulamuliro wa Kalonga wa Mtendere udzawachitiranji anthu?

[Zithunzi patsamba 14]

Mawu a Yesaya akwaniritsidwa, osati ndi UN, koma ndi awo amene akutsatira chiphunzitso cha Yehova

[Zithunzi patsamba 15]

Amuna aŵiriwa anasintha kuti alondole mtendere

Rami Oved

Georg Reuter

[Chithunzi patsamba 16]

Mtendere weniweni udzakhazikika mu ulamuliro wa Kalonga wa Mtendere

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena