Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 3/15 tsamba 19-24
  • Mmene Mungakumanire ndi Mtendere wa Umulungu Mokwanira Kwambiri?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungakumanire ndi Mtendere wa Umulungu Mokwanira Kwambiri?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Zina za Zinthu Izi Zimafunikira Chisamaliro Chanu?
  • Londolani Mtendere Mopitirira
  • Mtendere wa Umulungu Kaamba ka Awo Ophunzitsidwa ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Lolani “Mtendere wa Mulungu” Uchinjirize Mtima Wanu
    Nsanja ya Olonda—1991
  • ‘Funafunani Mtendere ndi Kuulondola’
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mtendere​—Kodi Mungaupeze Bwanji?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 3/15 tsamba 19-24

Mmene Mungakumanire ndi Mtendere wa Umulungu Mokwanira Kwambiri?

“Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”​—YESAYA 48:18.

1. Kodi nchiyani chomwe chikufunikira ngati tikufuna kukhala ndi mtendere mokwanira monga mmene tingathere?

AWO omwe amagawana mokhazikika mu phunziro la mpingo la Baibulo ndi thandizo la magaziniyi amazindikira mtengo wa mtendere umene Mulungu amapereka, ndipo amafuna mtendere umenewo. Ambiri mosakaikira amasangalala nawo. Koma sionse amene amakumana nawo mokwanira monga mmene angachitire. Nchifukwa ninji ichi chiri tero? Ponena za awo omwe ali ndi mtendere wa umulungu Yehova anati: “Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga! Mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chiiungamo chako monga mafunde a nyanja.”​—Yesaya 48:17, 18.

2. (a) Kodi nchiyani chomwe chikusonyezedwa ndi mawu akuti “pereka chisamaliro”? (b) Kodi ndi ku malamulo angati a Mulungu amene tiyenera kupereka chisamaliro? (1 Yohane 5:3)

2 Mwachiwonekere, aliyense angapindule mwakupezeka pa misonkhano kumene timakambitsirana Baibulo. Koma kokha awo amene amapereka chisamaliro ku malamulo a Yehova, kupanga kugwiritsira ntchito kwa iwo ndi kugonjera ku iwo, mowonadi amasangalala ndi mtendere wa umulungu. Kodi pali mbali zimene mukufuna kuchita ichi mokwanira? (2 Petro 1:2) Sichiri chokwanira kaamba ka ife kulabadira zochepa za zifuno za Mulungu koma kenaka kuika pambali izo zimene ziri zosayenera kapena zovuta. Pamene Mdyerekezi anayesa kunyenga Yesu Kristu kudza ku njira yake yadyera ya kulingalira, Yesu molimbika anayankha: “Kwalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu otuluka m’kamwa mwa Mulungu.’”​—Mateyu 4:4.

3. Kodi ndi mbali ziti za miyoyo yathu zomwe zikafunikira kubweretsedwa m’chigwirizano ndi njira za Yehova ngati ife mowonadi tikayenera kukhala ndi mtendere wochuluka?

3 Malamulo a Mulungu amakhudza mbali iriyonse ya miyoyo yathu. Choyambirira, iwo amakhudza chiyanjo chathu ndi Yehova. Kenaka amakhudza kayang’anidwe kathu kulinga ku gulu lake lowoneka ndi maso ndi uminisitala Wachikristu, njira mu imene timasamalira ziwalo za banja, ndi kuchita kwathu zinthu ndi anthu a ku dziko. Awo amene mofunitsitsa amapereka chisamaliro ku malamulo a Yehova mu mbali zonsezi ali awo amene anadalitsidwa ndi mtendere wochuluka. Tiyeni tilingalire zinthu zochepa zomwe zingatithandize ife kukumanizana ndi chimenecho mwaumwini.

Kodi Zina za Zinthu Izi Zimafunikira Chisamaliro Chanu?

4. (a) Kodi ndi chifukwa ninji phunziro la panyumba la Baibulo kapena kupita ku Nyumba ya Ufumu sikuli chitsimikiziro chakuti tiri pa mtendere ndi Mulungu? (b) Kodi nchiyani chomwe chikuphatikizidwamo mkusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu Kristu? (Yohane 3:36)

4 Kodi inu posachedwapa mwayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova? Kapena kodi inu mwinamwake mwakhala mukuyanjana ndi mpingo wa kumaloko kwa miyezi ingapo kapena ngakhale zaka? Ngati ndi tero, inu mosakaikira mwapeza chimwemwe mkukhala ndi chidziwitso cha zifuno za Mulungu zikufutukulidwa pamaso panu. Koma chenicheni chakuti munthu amasangalala ndi phunziro la Baibulo la panyumba kapena amapeza chisangalalo mkupita ku Nyumba ya Ufumu sichimatsimikizira kuti iye ali pa mtendere ndi Mulungu. Tonse tinabadwira mu uchimo, ndipo mtendere wa Mulungu uli wothekera kaamba ka ife kokha kudzera mwa Yesu Kristu. (Yesaya 53:5; Machitidwe 10:36) Kungokhulupirira chabe mwa Yesu sikumabweretsa mtendere umenewo. Chiri choyenerera kuyamikira mwaumwini kufunika kwathu kaamba ka dipo, kusonyeza chikhulupiriro mu mtengo wa nsembe ya Yesu, ndipo kenaka kusonyeza chitsimikiziro cha chikhulupiriro chimenecho mwakumvera malamulo ake. (Yakobo 2:26) Limodzi la malamulo amene Yesu anapereka pamene anali pa dziko lapansi linali lakuti awo amene adzakhala ophunzira ake ayenera kubatizidwa m’madzi. (Mateyu 28:19, 20) Kodi inu munamizidwa mu chisonyezero cha kudzipereka kwanu kwa Yehova kudzera mwa Yesu Kristu?

5. Kodi ndi chifukwa ninji kudzipereka ndi kubatizidwa kuli kofunika kwambiri ku kukhala kwathu pa mtendere ndi Mulungu?

5 Kodi pali china chake mu moyo wanu chimene sichimakuyeneretsani inu kaamba ka ubatizo? Ngati mukudziwa kuti chiripo, kapena ngati mkati mwa kuphunzira kwanu muphunzira kuti chimenechi ndiye chifukwa, musachedwe kukonza zinthu. Zindikirani kuti kachitidwe kali konse kapena mkhalidwe womwe sumayeneretsa munthu kaamba ka ubatizo chiri chokhumudwitsa ku kukhala kwake pa mtendere ndi Mulungu. Chitani mwachangu pamene nthawi itadakalipo. Monga kwasonyezedwa pa 1 Petro 3:21, awo amene apatsidwa chikumbumtima chabwino ndi Yehova Mulungu choyamba amadzipereka iwo eni kwa iye pa maziko achikhulupiriro mwa nsembe ya Kristu, kubatizidwa mu chisonyezero cha kudzipereka kumeneko, ndi kuchita chifuniro cha Mulungu Kenaka mtendere umene umapita ndi chikumbumtima chabwino chifukwa chakukhala ndi kaimidwe kovomerezeka pamaso pa Yehova umakhala wawo; iwo siuli wothekera m’njira ina iriyonse. Komabe, iwo uli kokha mayambiriro.

6. Kodi ndi chifukwa ninji khalidwe lathu kulinga ku misonkhano ya mpingo liri ndi chotulukapo pa kusangalala kwathu ndi mtendere?

6 Kenaka, lingalirani kukhazikika kwanu mkupezeka pa misonkhano ya mpingo ndi kutenga kwanu mbali mu iyo pamene muli wokhoza. Kodi misonkhano imeneyi iri ndi malo m’moyo wanu kotero kuti simulola kuti itsekerezedwe ndi dziko kapena ndi zochitachita zina zaumwini? Kodi mumakonzekera kaamba ka misonkhano ndi kuwerengera iwo kukhala mwawi wapadera kugawanamo? Zinthu izi nazonso, ziri ndi mawonekedwe achindunji pa kusangalala kwa wina ndi mtendere. Chifukwa ninji? Chifukwa mzimu wa Mulungu uli ndi anthu ake osonkhana, ndipo mtendere uli chipatso chamzimu umenewo. (Agalatiya 5:22)Pali pa misonkhano imeneyi pamene timathandizidwa kumvetsetsa zifuno za Yehova, ndipo timafunikira ichi ndi cholinga chakuchita zomwe ziri zosangalatsa m’maso mwake. Pano, kachiwirinso, tikuphunzira mmene tingapititsire patsogolo mtendere mu mayanjano athu ndi anthu anzathu​—mu mpingo, kunyumba, ku sukulu, ndi ku malo athu antchito. Misonkhano yathu iri imodzi ya njira zofunika zimene timaphunzitsidwira ndi Yehova, ndipo monga mmene Malemba amalozera, ali awo amene amaphunzitsidwa ndi Yehova omwe amasangalala ndi mtendere wochuluka.​—Yesaya 54:13.

7. Kodi ndi kutsatira kotani kumene kuli kofunikira ponena za zinthu zomwe zakambitsiridwa ku misonkhano yathu?

7 Nsonga ina yofanana kwambiri yomwe imafunikira chisamaliro iri kugwiritsira ntchito kopita patsogolo mu miyoyo yathu kwa zimene timaphunzira. Sitikufuna kukhala ngati Aisrayeli omwe Yehova anati ‘imvani inu ndithu koma osazindikira.’ (Yesaya 6:9) Mkuwonjezera kodi sitifuna kukhala ngati awo amene Yehova anawalongosola kwa Ezekieli​—anthu amene anamvetsera kwa aneneri a Yehova koma osachita chimene ananena chifukwa iwo anasankha kukwaniritsa zikhumbo zawo zoipa kapena zakuthupi? (Ezekieli 33:31, 32) Mosiyanako, awo amene amasonkhana pa nyumba ya Yehova m’tsiku lathu ndipo amapeza chivomerezo chake akulongosoledwa motere: “Tiyeni tikwere ku phiri la Yehova ndi ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m’mabande ake.” (Mika 4:2) Ngati ife mowonadi timasamalitsa malangizo amene timalandira pa misonkhano yathu, ngati pa msonkhano uli wonse timapatula chifupifupi nsonga imodzi yomwe ife mwaumwini timaifuna ndipo kenaka kugwirira ntchito pa iyo, tidzatuta zipatso za mtendere. Monga mmene Yesu ananenera pa Luka 11:28:“Odala iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga!”

8. Kodi ndimotani mmene kugawana mu utumiki wa m’munda kumlingo wokulira kwambiri umene mikhalidwe yathu ingalole kuli kopindulitsa kwa ife mwaumwini?

8 Chimodzi cha zinthu zomwe zimagogomezeredwa pa misonkhano yathu kuli kufunika kwa kugawana kotheratu m’kulalikira Ufumu wa Mulungu ndi kuthandiza ena kukhala ophunzira. (Mateyu 24:14; 28:19) Kodi ntchito zimenezi ziri zowonekera motani mu moyo wanu? Ngati ife mowonadi tapereka chisamaliro ku zimene Yehova amanena kwa ife kudzera mu Mawu ake ndi kudzera mu gulu lake, timadziwa kuti iyi iri ntchito yofunika kwambiri yomwe ikuchitidwa pa dziko lapansi lerolino. (Chivumbulutso 14:6, 7) Ndipo chiri chinthu chodziwika bwino lomwe kuti awo amene ali mu utumiki wa nthawi zons​e—limodzinso ndi awo amene, ngakhale sangakhale apainiya, ali mowonadi achangu mu utumiki​—ali awo pakati pa ife omwe mowonekera ali achimwemwe. Mtendere umene iwo amasangalala nawo siuli monga ngati dontho la madzi chabe, koma monga mmene Yehova ananenera iwo umakhala “ngati mtsinje.” (Yesaya 48:18) Kodi chimenecho ndi chimene mukukumanizana nacho? Tonse a ife tingatero.

9. Kodi nchiyani chomwe chingatithandize ife kusunga mtendere wathu wopatsidwa ndi Mulungu angakhale pamene tiyang’anizana ndi mavuto okulira?

9 Kulabadira kwathu chenjezo limeneli, komabe, sikumatipanga ife kukhala otemera kuzitsenderezo za moyo za dongosolo iri la zinthu. Koma mosasamala kanthu kuti ndimovuta chotani mmene mikhalidwe ingakhalire, Mulungu amatitsimikizira ife za thandizo lake la chikondi ngati titembenukira kwa iye. (1 Petro 5: 6, 7) Kodi taphunzira kufuna thandizo la Yehova ndi chitsogozo mu chirichonse chimene timachita, mwaufulu kutembenukira kwa iye mu pemphero ndipo, pambuyo pakuchita zomwe tingathe mu mikhalidwe yovuta, kusenzetsa nkhawa zanthu pa Yehova, mwachidaliro kuzisiya izo ndi iye? (Miyambo 3:5, 6; Masalmo 55: 22) Mwachimwemwe tikulimbikitsidwa pa Afilipi 4:6, 7: “Musadere nkhawa konse, komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero pamodzi ndi chiyamiko zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu; ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” Chiri chopereka chabwino chotani nanga! Kodi mwaphunzira kupindula mokulira kuchokera ku mtendere wa Mulungu umene mwakutero wapangidwa kukhala wothekera?

Londolani Mtendere Mopitirira

10. Pambuyo pa kufunafuna mtendere, kodi nchiyani chimene chikufunikira ku mbali yathu?

10“Pamene takhala ndi mtendere woterewo, sitingakhoze kukhala osasamala ponena za iwo. Kuyesetsa kofunitsitsa kumafunikira ndi cholinga chaku usunga iwo. Mwakutero 1 Petro 3:10, 11 amati: “lye wofuna kukonda moyo ndi kuona masiku abwino, . . . afunefune mtendere ndi kuulondola.” Pokhala titafuna chonulirapo ndi kuchipeza. icho, munthu angakhale wopusa kuchitenga icho mopepuka. Pambuyo pa kufuna ndi kupeza mtendere, tikafunikira kukhala osamalira ndi zinthu zomwe zingasokoneze iwo. Kuwonjezera ku chimenecho, mokangalika tiyenera kufunafuna zinthu zimene zimawonjezera ku mtendere.

11. (a) Kodi ndi khalidwe lotani limene lingaike pangozi unansi wathu ndi Yehova? (b) Ndi liti pamene kwenikweni tiyenera kupempha kaamba kathandizo la Mulungu m’chigwirizemo ndi mayesero? (Mateyu 6:13)

11 Ngati tapeza mtendere ndi Mulungu kudzera mu njira imene iye wapereka, tikafunikira kukhala osamalira kusasokoneza chiyanjo chimenecho mwa kubwerera ku njira zathu zochimwa. Komabe, popeza tonse a ife tiri opanda ungwiro, tonse a ife timachimwa. Koma pali ngozi pamene munthu alungaimitsa mikhalidwe ndi kachitidwe mwa iyemwini imene Mulungu amadana nayo. Sitingakhoze kokha kugwedeza mapewa athu ndi kunena kuti, “Mmenemo ndi mmene ndinapangidwira.” (Aroma 6:16, 17) Tiyenera kulapa ku kachitidwe kolakwa m’malo mwa kukalungamitsa iko, ndipo kenaka tiyenera kupempha Mulungu kaamba ka chikhululukiro pa maziko a chikhulupiriro chathu mu nsembe ya Yesu. Tikafunikiranso kuphunzira kutembenukira kwa Mulungu kaamba kathandizo tisanachite cholakwa. M’malo mwa kuyesa kumenya nkhondoyo tokha, pomalizira ndi kugonja, ndipo kenaka kupempha kaamba ka chikhululukiro. Ndi thandizo la Mulungu, tingapambane mkuvala “umunthu watsopano womwe unalengedwa monga mwa Mulungu m’chilungamo ndi m’chiyero cha chowonadi.”​—Aefeso 4:20-24.

12. (a) Kuti tisangalale ndi mtendere, kodi ndi maunansi ena otani amene amafunikira chisamaliro? (b) Kodi nchiyani chimene chikafunikira kwa ife m’chigwirizanochi?

12 Kusangalala ndi mtendere, angakhale kuli tero, kumaphatikizaponso maunansi ndi ena. Akristu owona amatumikira Mulungu monga mbali ya gulu; iwo ali “gulu la abale.” (1 Petro 2:17, NW) Monga mmene Yesu ananenera kuti chidzakhala chowona ndi otsatira ake, iwo ali owonekera mu chikondi chawo kaamba ka wina ndi mnzake. (Yohane 13:35) Koma palibe aliyense wa iwo amene ali wangwiro: Chifukwa cha kupanda ungwiro kwathu ndi uko kwa ena, tingafunikire kupemphera mofunitsitsa ponena za mikhalidwe ina ndi kugwira ntchito molimbika kuthetsa mavuto. Ahebri 12:14 amatilimbikitsa ife: “Londolani mtendere ndi anthu onse. Ndipo m’mayanjano athu ndi abale Achikristu ndi alongo, pali chifunsiro chapadera m’kupirira m’kulondola mtendere. Mwachindunji, 1 Atesalonika 5:13 amati: “Khalani mu mtendere mwa inu nokha.” Chimenecho sichimatanthauza kokha kungodzipatula ku kubwezera koma kukhala opititsa patsogolo mtendere okangalika, kutenga sitepi yoyambirira kubwezeretsa mtendere ndi kukhala okhumba: kugonjera ku chikondwerero cha mtendere.​—Aefeso 4: 1-3.

13. (a) M’kupititsa patsogolo mtendere ndi osakhulupirira, kodi nchiyani chimene tingachite, koma kodi ndimotani mmene timasonyezera kuti mtendere ndi Mulungu umabwera poyamba? (b) Kodi ndimotani mmene chiriri chothekera kaamba ka ife kukhala ndi mtendere pamene pali phokoso pozungulira ife?

13 Kunja kwa mpingo, ngakhale kuli tero, sionse amene ali okhumba kukhala amtendere. Chotero, motsimikizirika, Aroma 12:18 amapereka uphungu: “Ngati nkotheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.” Koma zoyesayesa zathu za kupititsa patsogolo mtendere sizimaphatikiza kugonjera m’chigwirizano ndi zifuno zolungama za Yehova. Tingakonzenso nthawi kaamba ka kuchita zinthu zina, koma tikudziwa kuti chingakhale chopanda nzeru kusiya kupezekapo pa misonkhano ya mpingo kapena kudzipatula m’kugawana mu utumiki wa m’munda ndi cholinga chofuna kusunga mtendere ndi wokwatirana nawo kapena anansi. Ndipo tikudziwa kuti Yehova sangavomereze kugwirizana kwathu ndi machitachita opanda umulungu ndi ogwira nawo ntchito kapena ndi anzathu a ku sukulu ndi cholinga chofuna kukhala ndi chivomerezo chawo. Timazindikira kuti mtendere weniweni uli kokha kwa awo amene poyamba amasangalala ndi mtendere ndi Mulungu, kwa awo amene amakonda malamulo a Yehova ndi kuyenda mu njira zake. Uli mtendere umenewo umene timauwona kukhala wa mtengo wapatali kuposa china chirichonse. (Masalmo 119:165) Zowonadi, pozungulira ife pangakhale pali phokoso, anthu osakhulupirira angamakangane ndi kumenyana wina ndi mnzake, iwo mwinamwake angaunjike chitonzo pa ife chifukwa cha chikhulupiriro chathu. Koma timadziwa kuti ndimotani mmene Mawu a Mulungu atiphunzitsira ife kudzisamalira ife eni. Mwakupitiriza kufunafuna njira yomwe iri yogwirizana ndi njira za chilungamo cha Yehova, ife sitikumanidwa mtendere umene uli wofunika koposa.​—Yerekezani ndi Masalmo 46:1, 2.

14. Angakhale kuti ife mwaumwini timakumanizana ndi chisautso, kodi nchiyani chimene chimachipangitsa icho kukhala chothekera kaamba ka ife kupitirizabe kusunga uchete wa mkatikati ndi kawonekedwe kowala?

14 Pa usiku womaliza asanafe, Yesu anauza atumwi ake okhulupirika: “Ndalankhula ndi inu zinthu izi kuti mwa ine mukhale nawo mtendere. M’dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima! Ndalilaka dziko lapansi ine.” (Yohane 16:33) Inde, timakumana nacho chivuto. Monga Akristu, timapita pansi pa chizunzo cha mitundu yosiyanasiyana. Tingakumanizane ndi kupanda chilungamo, ndipo ena amavutika ndi kusautsidwa koopsya. Koma mtendere wa umulungu umalimbikitsa ife tonse kupyola mu izi. Chifukwa chakuti taphunzitsidwa ndi Yehova, timadziwa ndi chifukwa ninji Akristu amasautsidwa. Sitiri okaikira ponena za nchifukwa ninji kulibe chilungamo ndipo ndi chifukwa ninji timavutitsidwa. Timadziwanso zimene mtsogolo muli namo. Timadziwa kuti monga chotulukapo cha njira ya moyo yokhulupirika ya Yesu ndi imfa yake ya nsembe, chipulumutso chiri chotsimikizirika. Kuwonjezerapo, timadziwa kuti mosasamala kanthu za mavuto omwe tingayang’anizane nawo tsopano, tingatembenukire kwa Mulungu m’pemphero ndi chidaliro kuti iye mwachikondi amasamalira kaamba ka ife ndi kuti iye adzatithandiza ife mwanjira ya mzimu wake.​—Aroma 8:38, 39.

15. Kodi chiri chowona motani kuti mtendere umene Kristu amaupangitsa kukhala wothekera siuli wofanana ndi umene dziko limapereka?

15 Moyenerera, Yesu ananena pa Yohane 14: 27: “Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani. Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.” Icho motsimikizirika chiri chowona​—-dziko liribe chirichonse chofanana ndi mtendere umene Mulungu amapereka kudzera mwa Yesu Kristu. Iwo umatitheketsa ife kukhala amphamvu m’kuyang’anizana ndi mikhalidwe yomwe ingapangitse ena kutaya chiyembekezo chonse.

16. (a) Kodi ndi chiyembekezo chotani chimene chiri kutsogolo kwa awo amene tsopano mowonadi amawona monga chuma mtendere umene Mulungu amapereka? (b) Kodi ndimotani mmene tingasonyezere kuti timawona mtendere umenewu kukhala chinthu cha mtengo wapatali?

16 Ndi mtsogolo mozizwitsa motani nanga mmene muli kutsogolo kwa awo omwe tsopano amakupatira mtendere womwe umabwera kuchokera kwa Mulungu ndi yemwe amaupatsa iwo kuwonekera kumene umafunikira mu miyoyo yawo! Posachedwapa dziko limene liri pa udani ndi Mulungu lidzapita. Zolengedwa zonse m’kupita kwa nthawi zidzakhala zogwirizana mu mtendere mwa zifuniro zolungama za ulamuliro wa dziko lonse. Lolani chiyamikiro chathu kaamba ka ziyembekezo zazikulu zimenezi chititsogoze ife ku kugwira ntchito mokulira m’chigwirizano ndi icho tsopano. Tiyeni tonse a ife timvetsere mosamalitsa ku malangizo a Yehova ndikulola malamulo ake kuzikidwa mokhazikika m’mitima mwathu kotero kuti mowonadi tizikonde njira zake ndi kuchita zomwe amafuna. Monga mmene Miyambo 3:1, 2 amanenera: “Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga, pakuti adzakuwonjezera masiku ambiri ndi zaka za moyo ndi mtendere.”

Mafunso a Kapendedwe

◻ Malingandi Yesaya 48:18, nchiyani chimene chimafunikira kuti tikhale ndi mtendere wochuluka?

◻ Ndi mwakuchita zinthu ziti mmene tingakumanire ndi mtendere wa umulungu mokwanira?

◻ Kodi nchiyani chimene chikuyembekezeredwa kwa ife kotero kuti tisunge mtendere ndi abale athu ndi alongo?

◻ Kodi ndimotani mmene tingasungire mtendere ngakhale pamene tazingidwa ndi anthu osakhulupirira?

[Chithunzi patsamba 20]

Ubatizo

[Chithunzi patsamba 21]

Kupezeka pa misonkhano Mokhazikika

Kugwiritsira ntchito zimene timaphunzira

[Chithunzi patsamba 22]

Kugawana kotheratu mu utumiki wa m’munda

Kusenzetsa nkhawa zathu pa Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena