Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 11/1 tsamba 9-14
  • Kodi Mumawakonda Motani Mawu a Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumawakonda Motani Mawu a Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Kulitsani Chilakolako” cha Mawu a Mulungu
  • Wamasalmo Amene Ankakonda Mawu a Mulungu
  • Kalonga Amene Sanaope Kukhala Wosiyana ndi Ena
  • Mawu a Mulungu Analimbitsa Yesu
  • Otsanzira Ena a Kristu
  • Khulupirirani Mawu a Yehova
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Lolani Kuti Mawu a Mulungu Aunike Njira Yanu
    Nsanja ya Olonda—2005
  • “Anapitiriza Kumamatira Yehova”
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kuŵerenga Baibulo—N’kopindulitsa ndi Kosangalatsa
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 11/1 tsamba 9-14

Kodi Mumawakonda Motani Mawu a Mulungu?

“Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiliramo ine tsiku lonse.”​—SALMO 119:97.

1. Kodi njira imodzi imene anthu oopa Mulungu amasonyezera chikondi chawo pa Mawu a Mulungu ndi yotani?

AMUNA ndi akazi mamiliyoni mazana ambiri ali ndi Baibulo. Koma kukhala ndi Baibulo n’kosiyana ndi kukonda Mawu a Mulungu. Kodi munthu anganenedi kuti amakonda Mawu a Mulungu ngati amangowaŵerenga mwa apa ndi apo? Ndithudi ayi! Komanso ena amene kale sanali kulikonda Baibulo tsopano amaliŵerenga masiku onse. Aphunzira kukonda Mawu a Mulungu, ndipo monga wamasalmo, iwo tsopano amalingalira Mawu a Mulungu “tsiku lonse.”​—Salmo 119:97.

2. Kodi chikhulupiriro cha mmodzi wa Mboni za Yehova chinalimbitsidwa motani pamavuto?

2 Munthu wina amene anakonda Mawu a Mulungu ndi Nasho Dori. Pamodzi ndi okhulupirira anzake, anatumikira Yehova mopirira kwa zaka zambiri, m’dziko lakwawo la Albania. Kwazaka zambiri m’nthaŵi imeneyo, Mboni za Yehova zinali zoletsedwa, ndipo Akristu okhulupirika ameneŵa sanali kulandira zofalitsa zofotokoza Baibulo zambiri. Koma chikhulupiriro cha Mbale Dori chinakhalabe cholimba. Motani? “Cholinga changa,” iye anatero, chinali “kuŵerenga Baibulo kwa ola limodzi tsiku lililonse, zimene ndinachita kwa zaka ngati 60 maso anga asanachite khungu.” Mpaka chaposachedwapa, kunalibe Baibulo lonse lathunthu m’chinenero cha Chialubaniya, koma Mbale Dori anaphunzira Chigiriki adakali mwana, choncho ankaŵerenga Baibulo m’chinenero chimenecho. Kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse kunalimbitsa Mbale Dori pamayesero osiyanasiyana, ndipo ifenso kungatilimbitse.

“Kulitsani Chilakolako” cha Mawu a Mulungu

3. Kodi Akristu ayenera kukulitsa mzimu wotani ponena za Mawu a Mulungu?

3 “Monga makanda obadwa chatsopano,” analemba motero mtumwi Petro, “kulitsani chilakolako cha mkaka wosasukuluka wa mawu.” (1 Petro 2:2, NW) Monga momwe khanda limalirira mkaka wa amake, Akristu amene akudziŵa chosoŵa chawo chauzimu amasangalala kwambiri kuŵerenga Mawu a Mulungu. Kodi inuyo mumamva motero? Ngati ayi, musade nkhaŵa. Inunso mungakulitse chilakolako cha Mawu a Mulungu.

4. Kodi muyenera kuchita chiyani kuti mupange kuŵerenga Baibulo kukhala chizoloŵezi cha tsiku ndi tsiku?

4 Kuti muchite zimenezo, choyamba dziphunzitseni kupanga kuŵerenga Baibulo kukhala chizoloŵezi cha nthaŵi zonse, cha masiku onse ngati n’kotheka. (Machitidwe 17:11) Mwina simungakwanitse kuthera ola limodzi tsiku lililonse pa kuŵerenga Baibulo monga momwe Nasho Dori anachitira, koma muyenera kuti tsiku lililonse mungathe kupatula nthaŵi inayake yoŵerenga Mawu a Mulungu. Akristu ambiri amadzuka mwamsanga kuti akhale ndi mphindi zingapo zosinkhasinkha pa ndime inayake ya m’Baibulo. Kodi pangakhalenso njira yabwinopo yoyambira tsiku? Ena amasankha kumaliza tsiku mwa kuŵerenga Baibulo asanagone. Komanso ena amaŵerenga Baibulo panthaŵi inayake yabwino. Chofunika ndicho kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse. Kenako, sinkhasinkhani kwa mphindi zingapo pazimene mwaŵerenga. Tiyeni tikambirane zitsanzo zina za anthu amene anapindula ndi kuŵerenga ndi kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu.

Wamasalmo Amene Ankakonda Mawu a Mulungu

5, 6. Ngakhale kuti sitikudziŵa dzina lake, kodi tingaphunzirenji ponena za amene analemba Salmo la 119 mwa kuŵerenga ndi kusinkhasinkha zimene analemba?

5 Amene analemba Salmo la 119 ankayamikiradi Mawu a Mulungu. Kodi ndani analemba salmo limenelo? Wolemba wake sakutchulidwa m’Baibulo. Komabe, malinga ndi nkhani yake, tikuphunzirapo zinthu zina ponena za iye, ndipo tikudziŵa kuti moyo wake sunali wopanda mavuto. Anzake ena amene anayenera kukhala olambira Yehova sanali kukonda mapulinsipulo a m’Baibulo monga iye. Komabe, wamasalmoyo sanalole maganizo awo kum’letsa kuchita zabwino. (Salmo 119:23) Ngati mumakhala kapena kugwira ntchito ndi munthu amene salemekeza miyezo ya Baibulo, mungaone kufanana pakati pa mkhalidwe wa wamasalmoyo ndi wanu.

6 Ngakhale kuti anali munthu woopa Mulungu, wamasalmo sanali kudziona ngati wosalakwa. Mosapita m’mbali anavomereza za zophophonya zake. (Salmo 119:5, 6, 67) Komabe, sanalole uchimo kum’lamulira. Iye anafunsa kuti: “Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji?” Yankho lake linali lakuti: “Akawasamalira monga mwa mawu anu.” (Salmo 119:9) Ndiyeno, pogogomezera kuti Mawu a Mulungu ndiwo mphamvu yaikulu yotisonkhezera kuchita zabwino, wamasalmoyo anapitiriza kuti: “Ndinawabisa mawu anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.” (Salmo 119:11) Mphamvu imene ingatithandize kupeŵa kuchimwira Mulungu ndi yaikuludi!

7. N’chifukwa chiyani achinyamata makamaka ayenera kuzindikira kufunika kwa kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku?

7 Achinyamata achikristu amachita bwino kuganizira mawu a wamasalmo. Akristu achinyamata akuukiridwa lerolino. Mdyerekezi amafunitsitsa kuipitsa maganizo a olambira Yehova ochepa msinkhuŵa. Cholinga cha Satana ndicho kunyengerera Akristu achinyamata kuti atsatire zilakolako zathupi ndi kuswa malamulo a Mulungu. Mafilimu ndi mapologalamu a pa wailesi yakanema nthaŵi zambiri amasonyeza maganizo a Mdyerekezi. Ngwazi za m’mapologalamu amenewo zimaoneka ngati anthu abwino ndi okondeka; chisembwere chimene amachita pakati pawo chimaonetsedwa ngati chinthu chabwinobwino. Uthenga wake? ‘Palibe cholakwa ngati anthu osakwatirana agonana malinga ngati amakondanadi.’ N’zomvetsa chisoni kuti chaka chilichonse Akristu achinyamata angapo amanyengedwa ndi maganizo amenewo. Ena amataya chikhulupiriro chawo. Chotero palidi nkhondo! Koma kodi nkhondo yake ndi yaikulu moti achinyamatanu simungathe kupirira? Kutalitali! Yehova wapereka njira imene Akristu achinyamata angagonjetsere zilakolako zoipa. Angalimbane ndi chida chilichonse chimene Mdyerekezi angapange mwa ‘kusamala monga mwa Mawu a Mulungu, kubisa zonena za Mulungu mumtima mwawo.’ Kodi mumathera nthaŵi yaitali motani pa kuŵerenga Baibulo kwaumwini ndi kusinkhasinkha kwa nthaŵi zonse?

8. Kodi zitsanzo zolongosoledwa m’ndimeyi zingakuthandizeni motani kukulitsa kuyamikira kwanu Chilamulo cha Mose?

8 Wolemba Salmo la 119 anafuula kuti: “Ha! Ndikondadi chilamulo chanu.” (Salmo 119:97) Kodi anali kunena chilamulo chiti? Anali kunena mawu ovumbulidwa a Yehova, kuphatikizapo mawu a m’Chilamulo cha Mose. Ena poyamba anganene kuti mawu a m’Chilamulo ameneŵa ndi achikale komanso angakayikire zoti munthu angawakonde. Komabe, pamene tisinkhasinkha pa mbali zosiyanasiyana za Chilamulo cha Mose, monga momwe anachitira wamasalmo, tingazindikire nzeru ya Chilamulo chimenecho. Kusiyapo mbali zaulosi zambirimbiri za Chilamulo, palinso malangizo okhudza ukhondo ndi madyedwe, amene anachirikiza chiyero ndi thanzi labwino. (Levitiko 7:23, 24, 26; 11:2-8) Chilamulo chinalimbikitsa kuona mtima pazamalonda ndipo chinalimbikitsa Aisrayeli kusonyeza chifundo kwa olambira anzawo osoŵa. (Eksodo 22:26, 27; 23:6; Levitiko 19:35, 36; Deuteronomo 24:17-21) Ziweruzo za milandu zinkayenera kupangidwa mosakondera. (Deuteronomo 16:19; 19:15) Pamene wolemba Salmo 119 anadziŵa zambiri m’moyo, mosakayikira anaona mmene zinthu zinayendera bwino kwa awo amene anatsatira Chilamulo cha Mulungu, ndipo chikondi chake pa Chilamulocho chinakula. Mofananamo lerolino, pamene Akristu atsatira mapulinsipulo a Baibulo mwachipambano, chikondi chawo ndi kuyamikira kwawo Mawu a Mulungu zimakula.

Kalonga Amene Sanaope Kukhala Wosiyana ndi Ena

9. Kodi Mfumu Hezekiya anakulitsa mzimu wotani ponena za Mawu a Mulungu?

9 Nkhani ya m’Salmo 119 ikugwirizana bwino lomwe ndi zimene timadziŵa ponena za Hezekiya pamene anali kalonga wachinyamata. Akatswiri ena a Baibulo amanena kuti Hezekiya ndiye analemba salmolo. Pamene kuli kwakuti sitingatsimikizire zimenezi, tikudziŵa kuti Hezekiya ankawalemekeza kwambiri Mawu a Mulungu. Mwa moyo wake, anasonyeza kuti anali kugwirizana kwambiri ndi mawu a pa Salmo 119:97. Ponena za Hezekiya, Baibulo limati: “Anaumirira Yehova osapambuka pambuyo pake, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.”​—2 Mafumu 18:6.

10. Kodi chitsanzo cha Hezekiya n’cholimbikitsa motani kwa Akristu amene sanaleredwe ndi makolo oopa Mulungu?

10 Nkhani zonse zimasonyeza kuti Hezekiya sanakulire m’banja laumulungu. Atate wake, Mfumu Ahazi, anali munthu wopanda chikhulupiriro ndiponso wolambira mafano amene anaotchapo mmodzi mwa ana ake aamuna​—mbale wake weniweni wa Hezekiya​—monga nsembe ya mulungu wonyenga! (2 Mafumu 16:3) Mosasamala kanthu za chitsanzo choipa chimenechi, Hezekiya anakwanitsa ‘kuyeretsa mayendedwe ake’ kupeŵa zisonkhezero zachikunja mwa kuphunzira Mawu a Mulungu.​—2 Mbiri 29:2.

11. Hezekiya akuonerera, kodi zinthu zinawayendera bwanji atate wake osakhulupirikawo?

11 Pamene Hezekiya anali kukula, anaona ndi maso ake mmene atate wake wolambira mafanowo anasamalilira nkhani za Bomalo. Yuda anazingidwa ndi adani. Panali Rezini, mfumu ya Aramu, amene anagwirizana ndi Peka mfumu ya Israyeli pozinga Yerusalemu. (2 Mafumu 16:5, 6) Panali Aedomu ndi Afilisti, amene anakantha Yuda nthaŵi zingapo nalandanso midzi ina ya Yuda. (2 Mbiri 28:16-19) Kodi Ahazi anatani nawo mavutoŵa? M’malo mochonderera Yehova kuti am’thandize kulimbana ndi Aramu, Ahazi anapita kwa mfumu ya Asuri, kuipatsa chiphuphu cha golidi ndi siliva, kuphatikizapo zochokera m’chipinda chosungiramo chuma cha m’kachisi. Koma zimenezi sizinadzetse mtendere wokhalitsa kwa Yuda.​—2 Mafumu 16:6, 8.

12. Kodi Hezekiya anali kudzapeŵa kubwereza zolakwa za atate wake mwa kuchita chiyani?

12 M’kupita kwa nthaŵi, Ahazi anamwalira ndipo Hezekiya anakhala mfumu ali ndi zaka 25 zakubadwa. (2 Mbiri 29:1) Anali wamng’onopo inde, koma zimenezo sizinam’letse kukhala mfumu yabwino. M’malo motsanzira khalidwe la atate wake osakhulupirikawo, iye anamamatira ku Chilamulo cha Yehova. Chimenechi chinaphatikizapo lamulo lapadera kwa mafumu lakuti: “Pakukhala [mfumu] pa mpando wachifumu wa ufumu wake, adzilemberere chofanana cha chilamulo ichi m’buku, achitenge pa ichi chili pamaso pa ansembe Alevi; ndipo azikhala nacho, naŵerengemo masiku onse a moyo wake; kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake, kusunga mawu onse a chilamulo ichi.” (Deuteronomo 17:18, 19) Mwa kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku, Hezekiya anali kudzaphunzira kuopa Yehova ndi kupeŵa kubwereza zolakwa za atate wake osaopa Mulunguwo.

13. Kodi Mkristu angakhale motani wotsimikiza kuti m’lingaliro lauzimu, zonse zimene azichita adzapindula nazo?

13 Si mafumu a Israyeli okha amene analimbikitsidwa kumalingalira Mawu a Mulungu nthaŵi zonse koma Aisrayeli onse oopa Mulungu anayenera kutero. Salmo loyambirira limati munthu wachimwemwedi ndi amene “m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.” (Salmo 1:1, 2) Ponena za munthu wotero, wamasalmo anati: “Zonse azichita apindula nazo.” (Salmo 1:3) Koma ponena za munthu wopanda chikhulupiriro mwa Yehova Mulungu, Baibulo limati: “[Ndi] munthu wa mitima iŵiri [amene] akhala wosinkhasinkha [“wosatsimikiza,” NW] panjira zake zonse.” (Yakobo 1:8) Tonsefe tikufuna kukhala achimwemwe ndi achipambano. Kuŵerenga Baibulo kwatanthauzo nthaŵi zonse kungatithandize kukhala achimwemwe.

Mawu a Mulungu Analimbitsa Yesu

14. Kodi Yesu anasonyeza motani chikondi pa Mawu a Mulungu?

14 Panthaŵi ina, makolo a Yesu anam’peza atakhala pakati pa aphunzitsi m’kachisi ku Yerusalemu. Mmenetu akadaulo a Chilamulo cha Mulungu ameneŵa “[anadabwira] ndi chidziŵitso chake, ndi mayankho ake”! (Luka 2:46, 47) Nthaŵi imeneyo n’kuti Yesu ali ndi zaka 12 zakubadwa. Inde, ngakhale pamene anali wachichepere, zinali zoonekeratu kuti anali kukonda Mawu a Mulungu. Pambuyo pake, Yesu anagwiritsa ntchito Malemba kudzudzula Mdyerekezi, nati: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:3-10) Posapita nthaŵi, Yesu analalikira kwa anthu a m’mudzi wakwawo wa Nazarete, mwa kugwiritsa ntchito Malemba.​—Luka 4:16-21.

15. Kodi Yesu anapereka motani chitsanzo polalikira kwa ena?

15 Nthaŵi zambiri Yesu anali kutchula mawu a m’Mawu a Mulungu kuti achirikize ziphunzitso zake. Omvetsera ake “anazizwa ndi chiphunzitso chake.” (Mateyu 7:28) Ndipo n’zosadabwitsa chifukwa ziphunzitso zake zinachokera kwa Yehova Mulungu iyemwini! Yesu anati: “Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine. Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwiniyekha. Iye wakufuna ulemu wa Iye amene anam’tuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.”​—Yohane 7:16, 18.

16. Kodi Yesu anasonyeza chikondi chake pa Mawu a Mulungu kufikira pati?

16 Mosiyana ndi wolemba Salmo 119, ‘munalibe chosalungama’ mwa Yesu. Analibe uchimo, Mwana wa Mulungu, amene “anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa.” (Afilipi 2:8; Ahebri 7:26) Koma, ngakhale kuti anali wangwiro chotero, Yesu ankaphunzira ndi kumvera Chilamulo cha Mulungu. Ndicho chinthu chachikulu chimene chinam’pangitsa kukhalabe wokhulupirika. Pamene Petro anagwiritsa ntchito lupanga poyesa kuteteza Ambuye wake kuti asagwidwe, Yesu anadzudzula mtumwiyo ndi kum’funsa kuti: “Uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi awiri? Koma pakutero, malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho?” (Mateyu 26:53, 54) Inde, kukwaniritsidwa kwa Malemba ndiko kunali kofunika kwambiri kwa Yesu kuposa kuthaŵa imfa yankhanza ndi yotonzetsa. Kumenekotu n’kuwakonda zedi Mawu a Mulungu!

Otsanzira Ena a Kristu

17. Kodi Mawu a Mulungu anali ofunika motani kwa mtumwi Paulo?

17 Mtumwi Paulo analembera Akristu anzake kuti: “Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Kristu.” (1 Akorinto 11:1) Monga Ambuye wake, Paulo anakhala ndi chikondi cha pa Malemba. Anavomereza kuti: “Mumtima mwanga ndimachikonda zedi Chilamulo cha Mulungu.” (Aroma 7:22, The Jerusalem Bible) Nthaŵi zambiri Paulo anali kugwira mawu a m’Mawu a Mulungu. (Machitidwe 13:32-41; 17:2, 3; 28:23) Pamene anapereka malangizo omalizira kwa Timoteo, mtumiki mnzake wokondedwa, Paulo anagogomezera mbali yofunika imene Mawu a Mulungu ayenera kuchita m’moyo watsiku ndi tsiku wa aliyense amene ali “munthu wa Mulungu.”​—2 Timoteo 3:15-17.

18. Tchulani chitsanzo cha munthu amene, m’nthaŵi zamakono, anasonyeza chikondi pa Mawu a Mulungu.

18 Atumiki ambiri okhulupirika a Yehova m’nthaŵi zamakono nawonso atsanzira chikondi cha Yesu pa Mawu a Mulungu. Cha kuchiyambi kwa zaka za zana lino, mnyamata wina analandira Baibulo kuchokera kwa bwenzi lake. Anafotokoza chotsatirapo cha mphatso yamtengo wapatali imeneyi kwa iye nati: “Ndinatsimikiza mtima kuti ndiyenera kuŵerenga chigawo chinachake m’Baibulo tsiku lina lililonse.” Mnyamata ameneyo anali Frederick Franz, ndipo chikondi chake pa Baibulo chinam’pangitsa kukhala ndi moyo wautali ndiponso wachipambano muutumiki wa Yehova. Amakumbukiridwa kwambiri chifukwa cha luso lake lokhoza kutchula mawu a m’machaputala athunthu a m’Baibulo mosapenyera m’Baibulomo.

19. Kodi ena amasanja motani kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu kwa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase?

19 Mboni za Yehova zimaona kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse kukhala chinthu chofunika kwambiri. Mlungu uliwonse, pokonzekera umodzi mwa misonkhano yawo yachikristu, Sukulu ya Utumiki Wateokalase, amaŵerenga machaputala angapo m’Baibulo. Mfundo zazikulu za kuŵerenga Baibulo kwa mlunguwo zimakalongosoledwa pamsonkhanowo. Mboni zina zimaona kuti n’kothandiza kugaŵa kuŵerenga Baibulo kwa mlunguwo m’zigawo zisanu ndi ziŵiri zazing’ono ndi kumaŵerenga chigawo chimodzi patsiku. Poŵerengapo, amasinkhasinkha mfundo zake. Ngati n’kotheka, amafufuza mfundo zowonjezeka mothandizidwa ndi zofalitsa zofotokoza Baibulo.

20. Kodi n’chiyani chofunika kuti mudzikhala ndi nthaŵi yoŵerenga Baibulo nthaŵi zonse?

20 Mungafunikire ‘kuchita machaŵi’ pazochita zina kuti mudzipeza nthaŵi yoŵerenga Baibulo nthaŵi zonse. (Aefeso 5:16) Komabe, mapindu ake adzaposa kutali zilizonse zomwe mwadzimana. Pamene mukulitsa chizoloŵezi choŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, chikondi chanu pa Mawu a Mulungu chidzakula. Posapita nthaŵi, mudzasonkhezereka kunena pamodzi ndi wamasalmo kuti: “Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiliramo ine tsiku lonse.” (Salmo 119:97) Mzimu umenewo udzadzetsa mapindu aakulu tsopano ndi m’tsogolo, monga momwe nkhani yotsatira idzasonyezera.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi wolemba Salmo 119 anasonyeza motani chikondi chake chachikulu pa Mawu a Mulungu?

◻ Kodi tingaphunzirepo chiyani pa zitsanzo za Yesu ndi Paulo?

◻ Kodi ifeyo patokha tingakulitse motani chikondi chathu pa Mawu a Mulungu?

[Zithunzi patsamba 10]

Mafumu okhulupirika ankafunikira kuŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse. Kodi inuyo mumatero?

[Chithunzi patsamba 12]

Ngakhale pamene anali wachichepere, Yesu anali kukonda Mawu a Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena