Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 9/1 tsamba 4-7
  • Mapindu a Kulemekeza Makolo Okalamba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mapindu a Kulemekeza Makolo Okalamba
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupatsa Mwakuthupi
  • Kupatsa Mwamaganizo
  • Kupatsa Mwauzimu
  • Mayendedwe Okoma Amayandikizitsa Anthu kwa Mulungu
  • Kodi Nchifukwa Ninji Agogo Ŵathu Anadzakhala Nafe?
    Galamukani!—1992
  • Kulemekeza Makolo Athu Okalamba
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kudziŵana ndi Agogo Anga?
    Galamukani!—2001
  • Kodi Nditani Kuti Ubale Wanga ndi Agogo Ulimbe?
    Galamukani!—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 9/1 tsamba 4-7

Mapindu a Kulemekeza Makolo Okalamba

OLAMBIRA oona a Mulungu amalemekeza ndi kuthandiza makolo awo okalamba chifukwa chakuti amawakonda. Ndi mbali ya kulambira kwawo. Baibulo limati: ‘Ayambe aphunzire iwo [ana kapena adzukulu] kuchitira ulemu a m’banja lawo [“kuchita kudzipereka kwaumulungu m’banja lawo,” NW], ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.’ (1 Timoteo 5:4) Kaya ndife achinyamata kapena achikulire, nkoyenera “kubwezera” makolo athu ndi agogo athu. Mwa njira imeneyi timasonyeza chiyamikiro chathu kaamba ka chikondi chawo, kugwira ntchito kwawo modzipereka, ndi kutisamalira kwawo kwa zaka zambiri. Inde, tili ndi mangawa a moyo wathu weniweniwo kwa makolo athu!

Onani kuti kubwezera makolo ndi agogo ‘nkolandirika pamaso pa Mulungu.’ Nkogwirizana ndi “kudzipereka [kwathu] kwaumulungu.” Choncho, mwa kutsatira uphungu umenewu, timapindula, pozindikira kuti tikuchita chimene chimasangalatsa Mulungu. Zimenezo zimatipatsa chimwemwe.

Muli chimwemwe m’kupatsa, makamaka pamene tipatsa amene anatipatsa moolowa manja. (Machitidwe 20:35) Ndiyetu pali phindu lotani nanga potsatira uphungu uwu wa Baibulo: “Patsa amako ndi atate wako chifukwa chokondwerera, amako wakukubala asekere”!​—Miyambo 23:25, The New English Bible.

Kodi tingabwezere motani makolo athu ndi agogo athu? M’njira zitatu: mwakuthupi, mwamaganizo, ndi mwauzimu. Chilichonse chimadzetsa mapindu ake.

Kupatsa Mwakuthupi

Amene amatumikira Mulungu amadziŵa kuti kuthandiza mwakuthupi a m’banja lawo nkofunika. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.”​—1 Timoteo 5:8.

Tunji ndi Joy amakhala ku West Africa. Ngakhale ngosauka, iwo anaitana makolo okalamba a Joy kuti azikakhala nawo. Abambowo anali odwala ndipo m’kupita kwa nthaŵi anamwalira. Tunji akunena kuti: “Pamene Bambo anamwalira, Mayi anakupatira mkazi wanga ndi kunena kuti: ‘Unayesetsa ndithu mmene ungathere. Usadziimbe konse mlandu wa imfa ya Bambo wako.’ Ngakhale kuti Bambowo timawakumbukira kwambiri, tikudziŵa kuti tinawagulira mankhwala abwino koposa ndipo nthaŵi zonse tinayesetsa kuwachititsa kudzimva kukhala wofunika; tinayesetsa kukwaniritsa udindo wathu wopatsidwa ndi Mulungu. Chikhutiro chimenecho tili nacho.”

Nzoona kuti si aliyense amene angathe kuthandiza ena mwakuthupi. Mwamuna wina amene amakhala ku Nigeria anati: “Ngati munthu sangathe kudzipezera zosoŵa, angathe bwanji kupeza zosoŵa za munthu wina?” M’maiko ambiri mkhalidwewu ungadzafike poipa kwambiri m’zaka zikudzazi. Malinga ndi kupenda zamtsogolo kwa bungwe la United Nations, posachedwapa, theka la anthu okhala kumunsi kwa Sahara ku Afirika adzakhala mu umphaŵi wadzaoneni.

Ngati muli m’mavuto a zachuma, mungatonthozedwe ndi nkhani yoona ya mkazi wina wamasiye waumphaŵi. Pamene Yesu anali padziko lapansi, anaona mkazi wina wamasiye akuika chopereka chochepa mosungiramo ndalama za m’kachisi. Iye anapereka “timakobiri tiŵiri” tokha. Komabe, pokhala atadziŵa mkhalidwe wake, Yesu anati: “Zoonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphaŵi anaikamo koposa onse; pakuti onse ameneŵa anaika mwa unyinji wawo pa zoperekazo; koma iye mwa kusoŵa kwake anaikamo za moyo wake, zonse anali nazo.”​—Luka 21:1-4.

Mofananamo, ngati tiyesetsa kusamalira makolo athu kapena agogo athu mwakuthupi, ngakhale zingakhale zochepa, Yehova amaona ndipo amayamikira. Iye safuna kuti tichite zimene sitingathe kuchita. Mwinamwake makolo athu kapena agogo athu adzaonanso chimodzimodzi.

Kupatsa Mwamaganizo

Kuthandiza makolo athu ndi agogo athu sikumangofuna kuwasamalira mwakuthupi chabe. Tonsefe tili ndi zosoŵa zamaganizo. Aliyense, kuphatikizapo okalamba, amafuna kukondedwa, kudzimva kukhala wofunika, ndiponso kukhala woŵerengeredwa m’banja.

Mary, amene amakhala ku Kenya, wasamalira apongozi ake okalamba kwa zaka zitatu. Mary akuti: “Kuwonjezera pa kuwasamalira mwakuthupi, nthaŵi zonse timacheza nawo. Mayiwa sangathe kuchita zambiri pakhomo, koma timacheza ndipo takhala mabwenzi athithithi. Nthaŵi zina timakambitsirana za Mulungu, nthaŵi zina za anthu a kumudzi kwathu. Ngakhale kuti ali ndi zaka zoposa 90, amakumbukira bwino lomwe. Amakumbukira ndi kukamba za mmene ankakhalira kale akali mtsikana wamng’ono, m’masikuwo 1914 isanafike.”

Mary akupitiriza kuti: “Kusamalira munthu wokalamba nkovuta, koma kukhala nawo kwatipatsa mapindu ochuluka. Tili ndi mtendere ndi chiyanjano m’banja. Chifukwa chakuti ndimawapatsa, ena m’banja atengera khalidweli. Mwamuna wanga amandilemekeza kwambiri tsopano. Ndipo Mayi atamva wina akulankhula mwaukali kwa ine, iwo mwamsanga amandikhalira kumbuyo. Palibe amene anganene mawu oipa kwa ine iwo ali pomwepo!”

Kupatsa Mwauzimu

Monga momwe kupatsa mwakuthupi ndi mwamaganizo kumabweretsera mapindu kwa wopatsayo, zilinso chimodzimodzi ndi zinthu zauzimu. Mtumwi Paulo analembera mpingo wachikristu wa ku Roma motere: “Ndilakalaka kuonana ndi inu, kuti ndikagaŵire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike; ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse aŵiri, chanu ndi changa.”​—Aroma 1:11, 12.

Mofananamo, ponena za kupatsa mwauzimu okalamba amene amatumikira Mulungu, chilimbikitso kaŵirikaŵiri chimachokera kumbali zonse ziŵiri. Osondu, amene amakhala ku Nigeria, akufotokoza kuti: “Chimene agogo anga amandisangalatsira nchakuti iwo amandipatsa mwaŵi woti ndidziŵeko zakale. Agogo anga aamuna, modzazidwa nchimwemwe, amafotokoza za dera limene ankagwiriramo ntchito monga mtumiki wanthaŵi zonse m’zaka za m’ma 1950 ndi m’ma 1960. Amayerekezera kalinganizidwe ka mpingo wamakono ndi mmene zinalili iwo atangokhala Mboni. Zinthu zimenezi zimandithandiza mu utumiki wanga monga mpainiya.”

Mumpingo wachikristu ena angathandizirenso kupatsa anthu okalamba. Tunji, wotchulidwa poyambirira, anafotokoza zimene zinachitika mumpingo wake motere: “Mbale wina wachinyamata mpainiya amene anapemphedwa kukamba nkhani yapoyera anabweretsa autilaini yake kwa Bambo kuti amthandize kukonzekera. Wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda anabwera kwa Bambo ndi kuwauza kuti: ‘Muli ndi chidziŵitso. Mungandiuze zotani kuti ndiwongokere.’ Mkulu ameneyo anapatsidwa uphungu wothandiza ndi Bambo. Abale anatchula dzina la Bambo kangapo m’mapemphero a mumpingo. Zonsezi zinawapangitsa kudzimva kukhala wofunika.”

Mayendedwe Okoma Amayandikizitsa Anthu kwa Mulungu

Nthaŵi zina, pamene tilemekeza ndi kukonda makolo athu ndi agogo athu, timapangitsa anthu kuyandikira kwa Mulungu. Mtumwi Petro analemba kuti: “Ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, mmene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino.”​—1 Petro 2:12.

Andrew, mkulu wachikristu ku West Africa, ankayenda ulendo wamakilomita 95 kaŵiri pamlungu kukasamalira abambo ake odwala, amene anali wosakhulupirira. Iye akusimba kuti: “Pamene ndinangokhala mmodzi wa Mboni za Yehova, abambo anga sanagwirizane nazo mpang’ono pomwe. Koma ataona mmene ndinali kuwasamalirira pamene anali kudwala, anayamba kuuza abale ndi alongo anga aang’ono kuti, ‘Muloŵe chipembedzo cha mbale wanuchi!’ Zimenezo zinawasonkhezera, ndipo tsopano ana onse asanu ndi anayi a abambo anga ndi Mboni za Yehova.”

Kulemekeza ndi kusamalira makolo athu okalamba kungakhale kovuta, makamaka pamene tili m’mavuto a zachuma. Koma pamene Akristu ayesetsa kuchita zimenezi, amapeza mapindu ochuluka. Koposa zonse, iwo amapeza chimwemwe m’kupatsa, pamodzi ndi chikhutiro chakuti akusangalatsa Yehova Mulungu, amene ndiye “Atate wa onse.”​—Aefeso 4:6.

[Bokosi patsamba 6]

Uphungu Waumulungu kwa Amene Amalandira Chisamaliro ndi kwa Amene Amachipereka

Khalani Wolimbikitsa: “Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.”​—Aroma 15:2.

Khalani Wokhazikika: “Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti panyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.”​—Agalatiya 6:9.

Khalani Wodzichepetsa: “Musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini.”​—Afilipi 2:3.

Khalani Wochita Zabwino: “Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.”​—1 Akorinto 10:24.

Khalani Wofatsa: “Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse.”​—Afilipi 4:5.

Khalani Wachifundo: “Mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha.”​—Aefeso 4:32.

[Chithunzi patsamba 7]

Akulu achinyamata angapindule ndi chidziŵitso cha akulu okalamba

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena