Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 6/1 tsamba 5-7
  • Dikirani Moleza Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dikirani Moleza Mtima
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Khalani Tcheru
  • Mulungu Sazengereza
  • Zochita Zathu Nzofunika Kwambiri Kuposa Zolankhula Zathu
  • Kudziŵiratu
  • “Mudzisunge Nokha m’Chikondi cha Mulungu”
  • Kumbukirani Tsiku la Yehova Nthaŵi Zonse
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Tigwiritse Chikhulupiriro Chathu Chamtengo Wapatali!
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kufunika Kokhala Wokhululuka
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kukhululukira Ena
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 6/1 tsamba 5-7

Dikirani Moleza Mtima

MBUSA amene ankakonda kufuula mobwerezabwereza kuti “Mmbulu!” pamene kunalibe ndi mmbulu womwe anasoŵa womthandiza pambuyo pake pamene anafuula kaamba ka thandizo. Mofananamo lerolino, ambiri amanyalanyaza za kuyandikira kwa tsiku la Yehova chifukwa chakuti akhala akumva machenjezo osaŵerengeka ochititsa nthumanzi koma amene anapezeka kuti anali onyenga. Mdani wamkulu wa Mulungu, Satana, wodzionetsa ngati “mngelo wa kuunika,” amapezerapo mwayi pa kulephera kwa anthu ambiri kuzindikira za chenjezo lenileni loti alitsatire.​—2 Akorinto 11:14.

Mzimu wonyalanyaza ungakhale wangozi ngakhale kwa amene atumikira Yehova kwa nthaŵi yaitali. Chifukwa ninji? Talingalirani za chenjezo loperekedwa ndi mtumwi Petro m’zaka za zana loyamba.

Khalani Tcheru

Kalata yachiŵiri youziridwa ya Petro inalembedwa ncholinga chokumbutsa Akristu oyambirira, ndipo ikutikumbutsanso lerolino. “Okondedwa,” iye analemba motero, “uyu ndiye kalata wachiŵiri ndilembera kwa inu tsopano; mwa onse aŵiri nditsitsimutsa mtima wanu woona ndi kukukumbutsani.” (2 Petro 3:1) Kodi nchiyani chimene chinapangitsa Petro kuti akhale ndi nkhaŵa imeneyi? Petro akugogomezera za kufika kwa onyoza amene kunyoza kwawo kumasonyeza kunyalanyaza kufulumira kwa nthaŵi imene atumiki a Mulungu akukhalamo. Ino ndiyo nthaŵi yoyenera kukhala tcheru kuti tisakopeke ndi onyoza. Choncho, Petro akuchenjeza oŵerenga ake kuti ‘akumbukire mawu onenedwa kale ndi aneneri oyera.’ (2 Petro 3:2; Machitidwe 3:22, 23) Kodi aneneriwo ananenanji?

Atumiki okhulupirika a Mulungu nthaŵi zambiri ananena za mmene ziweruzo za Mulungu zinathetsera kuipa. Petro akukumbutsa oŵerenga ake za Chigumula cha m’tsiku la Nowa chimene Mulungu anagwiritsira ntchito monga njira yake yoloŵerererapo pamene dziko lapansi linadzala ndi zoipa. Chigumula chowononga chimenecho chinathetsadi dziko lapansi la panthaŵiyo. Koma Mulungu anapulumutsa Nowa ndi banja lake m’chingalawa pamodzi ndi zolengedwa “zonse zokhala ndi moyo” zosungidwa monga mbewu. Nthano zambiri zamakedzana kuzungulira dziko lonse zimachitira umboni za kulondola kwa nkhani imeneyi ya m’Baibulo.a​—Genesis 6:19; 2 Petro 3:5, 6.

Petro anatcha kuloŵererapo kumeneko kwa Mulungu kuti chinthu chimene anthu ena ‘anaiŵala.’ Ndipo ena anakopeka nakhala onyalanyaza chifukwa cha onyoza a m’tsikulo. Komabe, ife sitiyenera kuiŵala za zimene Yehova wachita kale. Petro akutiuza kuti: “Koma miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mawu omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.” (2 Petro 3:7) Inde, Mulungu adzaloŵereraponso.

Mulungu Sazengereza

Papita kale zaka zikwi zambiri. Kodi nchifukwa ninji Mulungu wayembekezera nthaŵi yaitali chomwechi osathetsa mavuto a anthu? Petro akufotokozanso za chinthu china. Iye akuti: “Koma ichi chimodzi musaiŵale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi.” (2 Petro 3:8) Yehova amaona nthaŵi mosiyana ndi mmene ife timaionera. Kwa Mulungu wamuyaya, nthaŵi yonse kuchokera pa kulengedwa kwa Adamu mpaka lero sikwana ngakhale mlungu umodzi. Koma kaya nthaŵi timaiona motani, zaka chikwi zilizonse ndi tsiku lililonse limene limapita limatiyandikizitsa ku kukwaniritsidwa kwa chifuno cha Yehova.

Mwambi wachingelezi wakuti “Mphika wodikirira suŵira msanga” umatanthauza kuti kumangoyembekezera chinthu chinachake osachitapo kanthu kumapangitsa munthu kuti aone ngati chikuchedwa. Nchifukwa chake Petro akuti tikhale “akuyembekezera ndi kukumbukira nthaŵi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.” (2 Petro 3:12, NW) Kodi tingakhale motani atcheru pamene kuloŵererapo kwa Mulungu kukuyandikira?

Zochita Zathu Nzofunika Kwambiri Kuposa Zolankhula Zathu

Petro akugogomezera za zochita. Iye akunena za “mayendedwe opatulika” ndi “chipembedzo.” (2 Petro 3:11) Kodi zimenezi zimaphatikizapo chiyani?

Mtumiki weniweni wa Mulungu amachita zinthu m’njira imene imasangalatsa Iye. Chikhulupiriro cha wolambira weniweni ameneyo chimasonyezedwa m’zochita zake. Zimenezi zimamsiyanitsa ndi amene amangolankhula ndi pakamwa chabe kuti amakhulupirira Mulungu ndi malonjezo ake. Mwina inu munaona kuti utumiki wapoyera wa Mboni za Yehova umawasiyanitsa ndi ena. Iwo amafika panyumba panu kuti akufotokozereni za malonjezo a Mulungu olembedwa m’Baibulo. Koma iwo amachitiranso umboni ziyembekezo zawo ndi zikhulupiriro zawo kulikonse kumene akumana ndi anthu.

Wa Mboni amene amadzitanganitsa ndi ntchito yolalikira chikhulupiriro chake kwa ena amalimbitsa zikhulupiriro zake. Kulankhula ndi ena kumakulitsa chidwi chathu ndipo panthaŵi imodzimodziyo kumadzetsa chimwemwe cha mumtima ndi chikhutiro. Pamene tilalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, timakondweretsanso Yehova. Timadziŵa kuti iye ‘sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yathu, ndi chikondicho timachionetsera ku dzina lake,’ monga momwe Paulo, mtumwi mnzake wa Petro ananenera.​—Ahebri 6:10; Aroma 10:9, 10.

Kodi nchiyani chimene chili chotsatirapo cha kudzitanganitsa m’ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu m’masiku ano otsiriza a dongosolo loipa lilipoli? Anthu oona mtima zikwi mazana ambiri akuphunzira za mmene angakhalire ndi unansi wathithithi ndi Yehova, kuti apindule ndi chisomo chake ndi kupeza chimwemwe chenicheni m’chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso.

Kudziŵiratu

Ngakhale kuti timadziŵa kuti Yehova Mulungu adzaloŵererapo panthaŵi yake yoikika malinga nkunena kwa Baibulo, tiyenera kumverabe chenjezo lowonjezereka limene Petro akupereka. “Pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osayeruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.”​—2 Petro 3:17.

Ndithudi, Yehova anadziŵiratu kuti ena amene anali ndi chikhulupiriro chosalimba anali kudzagwa mphwayi chifukwa chakuti Mulunguyo anaoneka ngati kuti akuchedwa kuloŵererapo. Iye anadziŵanso kuti chisonkhezero cha anthu osapembedza chinali kudzaipitsa atumiki ake oona, kapena kufooketsa chikhulupiriro chawo choti kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu kwayandikira. Lingakhale tsoka lalikulu chotani nanga kusiya kuchirimika kwathu m’masiku otsiriza ano!

Ino si nthaŵi yokayikira kapena kukhala osatsimikizira kwenikweni za zimene Yehova adzachita. (Ahebri 12:1) M’malo mwake, ino ndiyo nthaŵi yowonjezera chidziŵitso chathu cha zimene kuleza mtima kwa Yehova kwadzetsa​—chiyembekezo cha chipulumutso kwa anthu mamiliyoni ambiri amene anakhala mbali ya khamu lalikulu la padziko lonse ndiponso amene akuyembekezera kudzapulumuka chisautso chachikulu chikudzacho. (Chivumbulutso 7:9, 14) Petro akutilangiza kuti: “Kulani m’chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Kristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthaŵi zonse. Amen.”​—2 Petro 3:18.

“Mudzisunge Nokha m’Chikondi cha Mulungu”

Kutanganitsidwa m’ntchito yolalikira Ufumu ndi kupezeka pamisonkhano yachikristu mokhazikika ncholinga cholambira Mulungu ndi kuphunzira Mawu ake kumatitetezera. Choncho, sitidzakhala ndi nthaŵi yodera nkhaŵa kwambiri mkhalidwe wa dongosolo loipa lamakonoli umene ukuipiraipirabe. Akristu oona safunikira kukhala ndi mantha ndi nkhaŵa zomkitsa m’moyo wawo. (1 Akorinto 15:58) Pamene tikhala otanganitsidwa ndi ntchito yotumikira Yehova, nthaŵi imapita mofulumira.

Yuda, mnzake wa Petro ndiponso amene anali mbale wa Yesu wa atate wina, akutilangiza kuti: “Inu, okondedwa, podzimangirira nokha pa chikhulupiriro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mu Mzimu Woyera, mudzisunge nokha m’chikondi cha Mulungu, ndi kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Kristu, kufikira moyo wosatha.” (Yuda 20, 21) Onani kuti pamafunikira kupemphera mosalekeza kuti tipitirizebe kuyembekezera zabwino. (1 Atesalonika 5:17) Kenaka Yuda akuwonjezera kuti: “Ena osinkhasinkha muwachitire chifundo, koma ena muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto; koma ena muwachitire chifundo ndi mantha, nimudane nawonso malaya ochitidwa maŵanga ndi thupi.” (Yuda 22, 23) Nkofunika chotani nanga kulimbikitsana m’nthaŵi zino zovuta! Ndipo nkofunika chotani nanga kuti tisagwe m’chiyeso, mwakutenga “tsiku la chipulumutso” lalitalili ndi kulisandutsa chifukwa cha “chilakolako chonyansa,” chimene chili chofala kwambiri m’dziko lamakono lamakhalidwe oipa.​—Yuda 4; 2 Akorinto 6:1, 2.

Ngati mutsatira uphungu wa Petro, Paulo, ndi Yuda ndiponso ngati mukhala otanganitsidwa ndiponso okangalika mu utumiki wa Mulungu, mungadikire moleza mtima kuloŵererapo kwa Yehova. Koma kodi mudzaterodi?

Musazengereze kuonana ndi a Mboni a kwanuko kuti akuthandizeni kulimbitsa chikhulupiriro chanu m’malonjezo a Mlengi a moyo wosatha. Phunzirani zimene zimafunikira kuti muyeneretsedwe kuchita nawo ntchito yochitira umboni padziko lonse yomwe sidzabwerezedwanso ndiponso yomwe idzamalizidwa pachisautso chachikulu chomayandikiracho. (Marko 13:10) Mukatero mudzakhala ndi chiyembekezo chokhala m’dziko lapansi latsopano lachilungamo limene Yehova akulonjeza. (2 Petro 3:13) Mverani zikumbutso zake! Dikirani moleza mtima! Khalani otanganika!

[Mawu a M’munsi]

a Onani buku lotchedwa Baibulo​—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, tsamba 116, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 7]

Phunzirani tsopano lino za malonjezo a Mulungu a Paradaiso

[Mawu a Chithunzi patsamba 5]

Mmbulu: Animals/​Jim Harter/​Dover Publications, Inc.; mbusa wachinyamata: Children: A Pictorial Archive from Nineteenth-Century Sources/​Grafton/​Dover Publications, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena