Kodi Mukuchita Zoposa?
“NDZACHITA zomwe ndingathe.” Ndikangati nanga pamene mawu ameneŵa amatsatiridwa ndi “koma” ndi zodzikhululukira zambirimbiri za kulephera kuchita zamphamvu kwa munthuyo! Bwanji zakudzipatulira kwathu kwa Yehova? Kodi tikukwaniritsa lonjezo lathu lakumchitira zomwe tingathe?
Kudzipatulira kumatanthauza ‘kudzipereka inumwini kotheratu ku utumiki kapena kulambiridwa kwa Mulungu kapena zochita zopatulika.’ Yesu anachita zambiri kusonyeza chimene kudzipatulira kwa Yehova kumaphatikizapo mwakunena kuti: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge [mtengo wozunzirapo, NW] wake, nanditsate ine.” (Mateyu 16:24) Munthu amene wadzikana ndi kudzipatulira kwa Mulungu amapanga kuchitidwa kwa chifuniro cha Mulungu chinthu chofunika koposa m’moyo wake.
Monga anthu odzipatulira, tiyenera kudzipenda kuwona ngati tikukhala ndi moyo mogwirizana ndi kudzipatulira kwathu. Petro anasonyeza chifukwa chake tiyenera kudzipenda pamene analimbikitsa Akristu odzozedwa kuti: “Onjezani kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita izi, simudzakhumudwa nthaŵi zonse.” (2 Petro 1:10) Inde, ngati tichita zoposa, sitidzakhala olephera mwauzimu.
Zoposa Zathu Zingakulitsidwe
Kunena za onse, atumiki odzipatulira onse a Mulungu akuyembekezeredwa kuchita zoposa, kapena zothekera koposa, kukondweretsa Yehova. Komabe, kuchita kwathu zoposa m’kuchita chifuniro cha Mulungu kungakule. Kwa mnyamata wa zaka zitatu, kutumidwa kukapereka uthenga kungakhale zoposa zimene angachite kuthandiza amake, koma pamene akusinkhuka, adzakhala wokhoza kuchita zowonjezereka. Choteronso ndi kukula kwathu kwauzimu—zimene kale zinali zothekera zathu sizingakhalebe zotero. Timasonkhezeredwa kuchita zowonjezereka kwa Yehova.
Chiyamikiro chathu chowonjezereka kwa Yehova chimasonkhezera kufunitsitsa kwathu kuchita zowonjezereka. Chiyambukiro cha zimene watichitira chimalimbikitsidwa mwa phunziro laumwini la Mawu ake, Baibulo. Mwachitsanzo, pamene tifufuza mosamalitsa ndi kusinkhasinkha mmene Yehova anatumira Mwana wake kudzapereka moyo wake kuwombola anthu kuuchimo, timasonkhezeredwa kutumikira Woyambitsa wa kakonzedwe ka dipo. (Yohane 3:16, 17; 1 Yohane 4:9-11) Pamene mowonjezereka ‘tilaŵa ndi kuwona kuti Yehova ndiye wabwino,’ ndipamenenso mitima yathu imasonkhezeredwa kumtumikira.—Salmo 34:8.
Minisitala wanthaŵi yonse wotchedwa Jetter anazindikira zimenezi. Kuti asanthule mwakuya zimene anali kuphunzira, anapatula chipinda chaching’ono m’nyumba yake kaamba ka chifuno chimenecho. Iye analinganiza kotero kuti akhoze kusumika maganizo posanthula. Iye ali ndi Watch Tower Publications Indexes kuphatikizaponso mavolyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! opezeka pa shelefu ya mabuku. “Pamene ndisanthula chidziŵitso chokondweretsa,” akutero mkaziyu, “mwamsanga ndimakachigaŵana ndi ena.”
Komabe, monga momwe kudya chakudya chaphwando panthaŵi ndi nthaŵi sikumaletsa munthu kufunikira kudya chakudya cha tsiku ndi tsiku, kusanthula kozama kwa apa ndi apo m’Baibulo sikumaletsa kufunika kwa tsiku ndi tsiku kwakudya chakudya chauzimu. Ruth amazindikira kufunikira kumeneku, pakuti kalekale monga momwe angathe kukumbukira, banja lake linaŵerengera Baibulo pamodzi m’mamaŵa ndi madzulo aliwonse pambuyo pa chakudya. Tsopano, pamsinkhu wazaka 81, pokhala atathera zaka zoposa 60 mu utumiki wanthaŵi yonse, amaŵerengabe Baibulo mokhazikika atadzuka pa 6:00 a.m. Atangolandira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, Ruth amapeza nthaŵi yakuwaŵerenga. Amaŵerenga nkhani imodzi katatu kapena kanayi kapena kuposapo asanaiphunzire ku mpingo. “Kuphunzira Mawu a Mulungu nkumene mumafunikira kuti mukhale wolimba m’chikhulupiriro,” iye akutero. Kwamthandizanso kupitirizabe mu utumiki waumishonale kwa zaka zambiri.
Kuchita Zoposa m’Kuthandiza Ena
Mwaphunziro lozama ndi lokhazikika la Mawu a Mulungu, changu chathu chakutumikira Mulungu chimawonjezereka, ndipo kanthu kena mkati mwathu kamatisonkhezera kuchita zowonjezereka. (Yerekezerani ndi Yeremiya 20:9.) Changu chotero chinasonkhezera Hirohisa kuchita uminisitala wake mokwanira. (2 Timoteo 4:5) Iye anali kukhala panyumba ya kholo limodzi ndi abale ndi alongo ake aang’ono anayi. Pamene anali wa zaka za pakati pa 13 ndi 19, Hirohisa anachilikiza banja lake mwakudzuka 3 koloko mbandakucha kukapereka mtokoma wamanyuzipepala. Iye anafuna kuchita zowonjezereka m’kuuza ena za Yehova, chotero Hirohisa anafunsira mwaŵi wautumiki waupainiya, monga momwe minisitala wanthaŵi yonse wa Mboni za Yehova amatchedwera. Ali wachichepere motero, anasangalala kuthandiza ena kugwirizana naye m’kuchita kwawo zoposa kutamanda Yehova.
Kuchita zoposa m’kuthandiza ena kumaphatikizapo kukhala wogwira mtima mu uminisitala wathu. Nthaŵi zina Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti: “Ngati mudziŵa izi, odala inu ngati muzichita.” (Yohane 13:17) Naomi ali chitsanzo chabwino chakugwiritsira ntchito malingaliro operekedwa ndi gulu la Yehova kuwongolera uminisitala wathu. Iye anali ndi vuto kulankhula ndi anthu osadziŵika kunyumba ndi nyumba ndipo kaŵirikaŵiri anali kusoŵa chonena pamene anafika pamakomo. Akulu mumpingo anamlimbikitsa kugwiritsira ntchito malingaliro opezeka m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba, m’chigawo cha “Mawu Oyambirira Ogwiritsira Ntchito mu Uminisitala Wakumunda.”a Iye analoŵeza pamtima mawu oyambirira pamutu wakuti “Banja/Ana” nawayeseza nthaŵi zambiri. Monga chotulukapo, anali wokhoza kuyambitsa makambitsirano ndi mkazi wina wapanyumba amene anali wazaka za m’ma 30. Ngakhale pamene Naomi anali asanapange ulendo wobwereza, mkaziyu anafika pa Nyumba Yaufumu. Phunziro Labaibulo linalinganizidwa. Mkazi wapanyumba ameneyu ndi mwamuna wake tsopano ali Akristu obatizidwa, akusangalala ndi moyo wabanja wachimwemwe limodzi ndi ana awo.
Kuchita Zoposa m’Kusonyeza Chisamaliro Chathu
Tingathenso kutsanzira mtumwi Paulo, amene anati: “Ndichita zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nawo.”—1 Akorinto 9:22, 23.
Hatsumi amasonyeza mkhalidwe wamaganizo umenewu. Pamene Hatsumi anali mu uminisitala wapoyera, mkazi wina analankhula mwaulemu pa intercom kuti anali wotanganitsidwa kwambiri kotero kuti sakakhoza kulankhula naye. Liwu la mwininyumbayo linali lofatsa, chotero Hatsumi anapitirizabe kumchezera. Mwininyumbayo anali kumangoyankhira pa intercom, osatuluka konse kudzawonana ndi Hatsumi. Zimenezi zinapitirizabe kwa zaka ziŵiri ndi theka.
Tsiku lina Hatsumi anasintha nthaŵi yakucheza kwake, akumafika madzulo. Palibe munthu anayankha. Komabe, pamene anali kuchoka, liwu lozoloŵereka kumbuyo kwake linafunsa kuti, “Kodi ndinu yani?” Mkaziyo anali atangobwera kumene kuchokera kokacheza. Atamva dzina la Hatsumi, iye anayankha msanga kuti, “Oo, ndinu amene mwakhala mukundichezera. Zikomo chifukwa cha kundidera nkhaŵa.” Chifukwa chakuti mkaziyo anali ataimitsa phunziro lake Labaibulo ndi Mboni za Yehova kumalo ena, iye ankachita manyazi kwambiri kuti aloŵetse Hatsumi m’nyumba. Phunziro Labaibulo linayambitsidwanso, ndipo mwininyumbayo akupita patsogolo bwino lomwe. Kodi timadera nkhaŵa kwambiri ndi anthu amene tikumana nawo mu uminisitala wakunyumba ndi nyumba?
Chitani Zoposa Zimene Mungathe
Yehova amayamikira kuyesayesa kwathu kuchita zoposa pomtumikira. Iye ali wofanana ndi atate amene ana ake amadza kwa iye ndi mphatso. M’kupita kwa zaka, mphatsoyo ingasiyane modalira ndi msinkhu wa mwana ndi zimene ali nazo. Monga momwedi atate aliri wachimwemwe kulandira mphatso iliyonse yochokera pansi pa mtima imene mwana wake ampatsa, chotero Yehova amavomera moyamikira utumiki wathu wa mtima wonse mogwirizana ndi kukula msinkhu kwathu kwauzimu.
Ndithudi, palibe chifukwa choyerekezera zoposa zathu ndi za ena. Monga momwe Paulo akunenera, tidzakhala ndi chifukwa chakukondwerera mwa ife eni, “sichifukwa cha wina.” (Agalatiya 6:4) Tipitirizetu kulabadira uphungu wa mtumwi Petro wakuti: “Chitani zoposa kuti mupezedwe potsirizira pake opanda banga ndi opanda chilema ndi mu mtendere.”—2 Petro 3:14, NW.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 29]
Kodi mukuchita zoposa m’kugwiritsira ntchito malingaliro a uminisitala wakumunda?