Kukonda Osoŵa
AKRISTU ali ndi udindo komanso mwaŵi wa kukonda abale awo ndi alongo awo osoŵa. (1 Yohane 3:17, 18) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pabanja lachikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10) Mbale amene watumikira Yehova kwa zaka pafupifupi makumi anayi posachedwapa anaona chikondi cha ubale wachikristu pamene mkazi wake ankadwala ndiponso pamene anamwalira. Iye akulemba motere:
“Popeza kuti ndinkadwazika mkazi wanga, ndinalephera kupita kuntchito pafupifupi kwa miyezi iŵiri. Ndinatonthozedwa chotani nanga pamene mabwenzi a mumpingo anatithandiza mofunitsitsa! Tinapatsidwa ndalama zochuluka—‘zogulira zosoŵa zina,’ monga momwe makhadi otumizidwa pamodzi ndi ndalamazo ankanenera—tinazigwiritsira ntchito kulipirira lendi, magetsi ndi madzi, ndi zofunika zina.
“Milungu iŵiri mkazi wanga asanamwalire, woyang’anira dera wathu anadzatichezera ndi kudzatilimbikitsa. Inde anationetsanso mafilimu amene ankayembekezera kukaonetsa kumpingo kumapeto kwa mlungu umenewo. Tinamvetsera misonkhanoyo patelefoni—kuphatikizapo kukumana kwa utumiki wakumunda kotsogozedwa ndi woyang’anira derayo. Tsiku lina atakumana chonchi, iye anauza onse amene anasonkhana kuti apite mu utumiki wakumunda kunenera pamodzi kuti ‘muli bwanji,’ kwa mkazi wanga. Choncho, ngakhale kuti anali kwayekha mwakuthupi, sanadzimve kukhala yekha.
“Patangotha ola limodzi iye atamwalira, pafupifupi akulu onse anafika kunyumba kwanga. Abale ndi alongo oposa zana limodzi anafika tsiku limenelo lokha. Chakudya chokwanira onse amene analipo chinaonekera pathebulo ‘mozizwitsa.’ Sindingathe kutchula mphatso zonse, mawu osonyeza chisoni, mawu otonthoza, ndi mapemphero amene anaperekedwa chifukwa cha ine. Zinali zolimbikitsa chotani nanga! Pomaliza ndinachita kuwapempha abalewo kuti asiye kubweretsa chakudya ndi kusamala m’nyumba!
“Tingachipezenso kuti chifundo, kuganizirana ndi chikondi chotere kuposa m’gulu la Yehova lokha? Anthu ambiri lerolino ali ndi mabwenzi enieni ochepa kwambiri. Yehova watidalitsatu potipatsa banja lalikulu la abale ndi alongo auzimu!”—Marko 10:29, 30.