Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Yehova Ndi Wotani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 3. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amatikonda?

      Khalidwe lalikulu kwambiri la Yehova ndi chikondi. Ndipo Baibulo limanena kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Timaona umboni wakuti Yehova amatikonda tikamawerenga Baibulo komanso tikamaona zimene analenga. (Werengani Machitidwe 14:17.) Chitsanzo ndi mmene anatilengera. Mwachitsanzo, anatilenga kuti tizitha kuona kukongola kwa mitundu yosiyanasiyana ya zinthu, kumva nyimbo zabwino, ndiponso kumva kukoma kwa chakudya. Zimenezi zikusonyeza kuti amafuna kuti tizisangalala ndi moyo.

  • Zipembedzo Zonyenga Zimaphunzitsa Zabodza Zokhudza Mulungu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 2. Kodi zimene zipembedzo zonyenga zimachita zimachititsa bwanji anthu kukhulupirira zabodza zokhudza Mulungu?

      Zipembedzo zonyenga zimachitira anthu zinthu zoipa zambiri pomwe Yehova sachita zimenezi. Baibulo limanena kuti “machimo ake [azipembedzo zonyenga] aunjikana mpaka kumwamba.” (Chivumbulutso 18:5) Kwa zaka zambiri, zipembedzo zakhala zikuchita nawo ndale, kulimbikitsa nkhondo ndiponso kuchititsa kapena kuvomereza kuti anthu ambirimbiri aphedwe. Atsogoleri azipembedzo ena amafuna kulemera kwambiri ndipo amauza anthu a m’zipembedzo zawo kuti aziwapatsa ndalama. Zimene amachitazi ndi umboni wakuti Mulungu samudziwa ngakhale pang’ono choncho alibe ufulu wonena kuti ndi atumiki ake.​​​—Werengani 1 Yohane 4:8.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena