Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 2/1 tsamba 9-13
  • “Mulungu Anatikonda Ife Kotero”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mulungu Anatikonda Ife Kotero”
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Mulungu Ndiye Chikondi”
  • Anakonzeranji Dipo?
  • Kodi Mtengowo Unali Waukulu Chotani?
  • Zimene Limatheketsa
  • Dipo la Yesu Ndi Mphatso ya Mulungu Yamtengo Wapatali Kuposa Zonse
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Dipo la Yesu Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali Imene Mulungu Anatipatsa
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Dipo la Kristu Njira ya Mulungu ya Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Cholinga cha Yehova Chidzakwaniritsidwa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 2/1 tsamba 9-13

“Mulungu Anatikonda Ife Kotero”

“Ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.”​—1 YOHANE 4:11.

1. Pa March 23 dzuŵa litaloŵa, nchifukwa ninji anthu mamiliyoni ambiri adzasonkhana m’Nyumba za Ufumu ndi malo ena osonkhanira kuzungulira dziko lonse?

PA Sande, March 23, 1997, dzuŵa litaloŵa, anthu oposa 13,000,000 mosakayikira adzasonkhana m’Nyumba za Ufumu ndi malo ena osonkhanira omwe Mboni za Yehova zimagwiritsira ntchito. Chifukwa? Chifukwa mitima yawo yakhudzika ndi chikondi choposa chimene Mulungu anasonyeza kwa mtundu wa anthu. Yesu Kristu anasonyeza umboni waukulu wa chikondi cha Mulungu chimenecho mwa kunena kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”​—Yohane 3:16.

2. Kodi ndi mafunso ati onena za kulabadira kwathu chikondi cha Mulungu amene angatipindulitse ife tonse titadzifunsa?

2 Pamene tilingalira za chikondi chimene Mulungu wasonyeza, tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimayamikiradi zimene Mulungu wachita? Kodi njira imene ndimakhalira ndi moyo wanga imapereka umboni wakuti ndili ndi chiyamikiro chimenecho?’

“Mulungu Ndiye Chikondi”

3. (a) Kodi nchifukwa ninji si nkhani yachilendo kwa Mulungu kusonyeza chikondi? (b) Kodi mphamvu ndi nzeru zimaonekera motani m’ntchito zake za kulenga?

3 Kwa Mulungu, kusonyeza chikondi si nkhani yachilendo ayi chifukwa “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Chikondi ndicho mkhalidwe wake waukulu. Pamene anali kukonza dziko lapansi kuti anthu akhalemo, kukweza kwake mapiri ndi kusonkhanitsa madzi m’nyanja kunali chionetsero cha mphamvu yake yodabwitsa. (Genesis 1:9, 10) Pamene Mulungu anayambitsa njira ya madzi ndi njira ya oxygen, pamene analenga tizilombo tosaŵerengeka ndi zomera zamitundumitundu zosintha mankhwala a m’dziko lapansi kukhala zinthu zimene anthu angadye kuti akhale ndi moyo, pamene anaika nthaŵi mwa ife zamoyo kuti ilingane ndi utali wa masiku ndi miyezi papulaneti la Dziko Lapansi, anasonyeza nzeru yaikulu. (Salmo 104:24; Yeremiya 10:12) Komabe, umboni wa chikondi cha Mulungu ngwapadera kwambiri m’chilengedwe chooneka.

4. M’chilengedwe chooneka, kodi ndi umboni uti wa chikondi cha Mulungu umene ife tonse tiyenera kuona ndi kuuyamikira?

4 Mphamvu yathu yolaŵa imatiuza za chikondi cha Mulungu titaluma chipatso chakupsa chotsekemera chimenetu iye anapanga osati chabe kuti chitipatse nyonga yokha komanso kutisangalatsa. Maso athu amaona umboni wake wotsimikizika pamene dzuŵa likuloŵa mochititsa kaso, ataona thambo lodzala ndi nyenyezi usiku wopanda mitambo, maluŵa amitundumitundu ndi maonekedwe ake oŵala, tiana ta nyama tikuseŵera, ndi mabwenzi akumwetulira mokondwa. Mphuno zathu zimatidziŵitsa za icho titapuma fungo lokoma la maluŵa a m’ngululu. Makutu athu amachimva pamene timvetsera kulira kwa mathithi, nyimbo za mbalame, ndi mawu a okondedwa athu. Timachimva wokondedwa wathu atatifungata mwachikondi. Nyama zina zili ndi mphamvu yoonera, kumva, kapena kununkhiza zinthu zimene anthu sangathe. Koma mtundu wa anthu, wopangidwa m’chifanizo cha Mulungu, uli ndi mphamvu yozindikira nayo chikondi cha Mulungu mwanjira imene nyama iliyonse singathe.​—Genesis 1:27.

5. Kodi Yehova anasonyeza motani chikondi chochuluka kwa Adamu ndi Hava?

5 Pamene Yehova Mulungu analenga anthu oyamba, Adamu ndi Hava, anaika ponseponse umboni wa chikondi chake. Iye analima munda, paradaiso, ndipo anameretsa mitengo yamtundu uliwonse mmenemo. Anakonza mtsinje woutsirira ndipo anaudzaza ndi mbalame ndi nyama zochititsa kaso. Zonse zimenezi anazipatsa kwa Adamu ndi Hava monga mudzi wawo. (Genesis 2:8-10, 19) Yehova anachita nawo ngati ana ake, a m’banja lake lonse. (Luka 3:38) Atawakonzera Edene monga chitsanzo, Atate wakumwamba wa anthu aŵiri oyamba ameneŵa anawapatsa ntchito yokhutiritsa yofutukula Paradaiso padziko lonse. Dziko lonse lapansi linayenera kudzazidwa ndi mbadwa zawo.​—Genesis 1:28.

6. (a) Kodi muganiza bwanji za njira yachipanduko imene Adamu ndi Hava anaitenga? (b) Kodi nchiyani chingasonyeze kuti taphunzirapo kanthu pa zimene zinachitika m’Edene ndi kuti tapindula nacho chidziŵitsocho?

6 Komabe, Adamu ndi Hava posakhalitsa anakumana ndi chiyeso cha kumvera, chiyeso cha kukhulupirika. Anayamba ndi mmodzi kulephera kuyamikira chikondi chimene iwo anasonyezedwa ndiyeno panatsatira mnzake. Zimene anachita zinali zonyansa. Zosakhululukika! Chotero, anataya unansi wawo ndi Mulungu, kuchotsedwa m’banja lake, napitikitsidwa m’Edene. Ife lero tikali kuvutika ndi zotsatira zake za uchimo wawo. (Genesis 2:16, 17; 3:1-6, 16-19, 24; Aroma 5:12) Koma kodi taphunzirapo kanthu pazimene zinachitika? Kodi ife tikuchilabadira motani chikondi cha Mulungu? Kodi zosankha zathu zatsiku ndi tsiku zimasonyeza kuti tikuyamikira chikondi chake?​—1 Yohane 5:3.

7. Mosasamala kanthu za zimene Adamu ndi Hava anachita, kodi Yehova anachisonyeza motani chikondi kwa mbadwa zawo?

7 Ngakhale kuti makolo athu aumunthu oyamba sanayamikire konse zinthu zonse zimene Mulungu anawachitira, zimenezo sizinaletse chikondi chake cha Mulungu. Chifukwa cha chifundo chake pa anthu osabadwa panthaŵiyo​—kuphatikizapo ife amoyo lero​—Mulungu analola Adamu ndi Hava kukhala ndi banja asanafe. (Genesis 5:1-5; Mateyu 5:44, 45) Akadapanda kutero, palibe ndi mmodzi yense wa ife akadabadwa. Mwa kuvumbula chifuniro chake pang’onopang’ono, Yehova anayalanso maziko a chiyembekezo kwa awo onse a mbadwa za Adamu amene adzasonyeza chikhulupiriro. (Genesis 3:15; 22:18; Yesaya 9:6, 7) Makonzedwe ake anaphatikizapo njira imene anthu a mitundu yonse angapezerenso chimene Adamu anataya, ndiko kuti, moyo wangwiro monga oyanjidwa a m’banja lonse la Mulungu. Anachita zimenezo mwa kukonza dipo.

Anakonzeranji Dipo?

8. Kodi nchifukwa ninji Mulungu sakanangolamula kuti ngakhale kuti Adamu ndi Hava anayenera kufa, mbadwa zawo zomvera sizidzafa?

8 Kodi mtengo wake wa dipo la moyo wa munthu unafunikiradi kulipiridwa? Kodi Mulungu sakanangolamula kuti ngakhale kuti Adamu ndi Hava anayenera kufa chifukwa cha kupanduka kwawo, mbadwa zawo zonse zimene zidzamvera Mulungu zikakhale ndi moyo kosatha? Malinga ndi nzeru zopereŵera za munthu, zimenezo zingamveke zanzeru. Komabe, Yehova ndiye “wakukonda chilungamo ndi chiweruzo.” (Salmo 33:5) Adamu ndi Hava anabala ana atachimwa; choncho palibe ndi mmodzi yense wa anawo anabadwa wangwiro. (Salmo 51:5) Onse anali ndi choloŵa cha uchimo, ndipo chilango cha uchimo ndi imfa. Ngati Yehova akananyalanyaza zimenezi, kodi akanapereka chitsanzo chotani kwa a m’banja lake lonse? Sananyalanyaze miyezo yake yolungama. Analemekeza zofuna za chilungamo. Kulibe aliyense amene moyenerera angapeze chifukwa ndi njira imene Mulungu anasamalira nkhani zobukapo.​—Aroma 3:21-23.

9. Malinga ndi muyezo wa Mulungu wa chilungamo, kodi ndi dipo lotani limene linafunikira?

9 Nanga kodi maziko oyenera opulumutsa awo a mbadwa za Adamu amene adzamvera Yehova mwachikondi akanakonzedwa motani? Ngati munthu wangwiro akanafa monga nsembe, chilungamo chikanalola kuti moyo wangwiro umenewo ukhale chophimba machimo a awo amene akanavomereza dipo mwachikhulupiriro. Popeza kuti uchimo wa munthu mmodzi, Adamu, ndiwo unachititsa banja lonse la anthu kukhala lochimwa, mwazi wokhetsedwa wa munthu winanso wangwiro, wolingana mtengo wake, ukanakhutiritsa chilungamo. (1 Timoteo 2:5, 6, NW) Koma kodi munthu wotero akanapezeka kuti?

Kodi Mtengowo Unali Waukulu Chotani?

10. Kodi nchifukwa ninji mbadwa za Adamu sizinathe kupereka dipo lofunikira?

10 Pambadwa za Adamu wochimwayo, panalibe ndi mmodzi yemwe amene akanapereka zofunika kuti agule moyo wamtsogolo umene Adamu anataya. “Kuombola mbale sangadzamuombole, kapena kumperekera dipo kwa Mulungu: (popeza chiombolo cha moyo wawo nchamtengo wake wapatali, ndipo chilekeke nthaŵi zonse:) kuti akhale ndi moyo osafa, osaona chivundi.” (Salmo 49:7-9) M’malo mosiya mtundu wa anthu wopanda populumukira, Yehova mwiniyo mwachifundo anapanga makonzedwe.

11. Kodi ndi motani mmene Yehova anakonzera moyo wa munthu wangwiro wofunikira kaamba ka dipo loyenera?

11 Yehova sanatumize mngelo padziko lapansi kuti adzanamizire kufa mwa kupereka thupi losanduka pamene ali wamoyo monga mzimu. M’malo mwake, mwa kuchita chozizwitsa chomwe Mulungu yekha, Mlengi, akanalingalira, anasamutsira mphamvu ya moyo ndi umunthu wa mwana wake wakumwamba m’mimba mwa mkazi, Mariya mwana wa Heli, wa fuko la Yuda. Mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, mzimu wake woyera, inateteza kakulidwe ka mwanayo m’mimba mwa amake, ndipo anabadwa ali munthu wangwiro. (Luka 1:35; 1 Petro 2:22) Chotero ameneyu anali ndi mtengo wofunika woperekera dipo limene likanakwaniritsiratu zofunika za chilungamo cha Mulungu.​—Ahebri 10:5.

12. (a) Kodi Yesu ali “Mwana wobadwa yekha” wa Mulungu m’lingaliro lotani? (b) Kodi kumtumiza kwake Mulungu iyeyu kuti apereke dipo kunasonyeza motani chikondi Chake pa ife?

12 Kodi ntchito imeneyi Yehova anaipatsa kwa yani pakati pa ana ake akumwamba miyandamiyanda? Kwa iye wofotokozedwa m’Malemba kuti “Mwana [wake] . . . wobadwa yekha.” (1 Yohane 4:9) Mawu ameneŵa amagwiritsiridwa ntchito, osati kufotokozera zimene iye anakhala atabadwa monga munthu, koma zimene iye anali kumwamba zimenezo zisanachitike. Ndi iye yekha amene Yehova anamlenga mwachindunji popanda kuthandizidwa ndi wina aliyense. Ndiye Woyamba Kubadwa wa chilengedwe chonse. Ndi iyeyu amene Mulungu anamgwiritsira ntchito kulenga zolengedwa zina zonse. Angelo ali ana a Mulungu, monga momwe Adamu analili mwana wa Mulungu. Koma Yesu akufotokozedwa kuti ali ndi “ulemerero wonga wa [mwana, NW] wobadwa yekha wa Atate.” Amanenedwa kuti akukhala “pachifuŵa cha Atate.” (Yohane 1:14, 18) Unansi wake ndi Atateyo ngwolimba, wodalirana, wachikondi. Ali ndi chikondi chomwenso Atate wake ali nacho pamtundu wa anthu. Miyambo 8:30, 31 imafotokoza mmene Atate wake amamvera ponena za Mwanayu ndi mmene Mwanayo amamvera ponena za mtundu wa anthu kuti: “Ndinamsekeretsa [Yehova] tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera pamaso pake nthaŵi zonse; . . . ndi [iye Yesu, Mmisiri wa Yehova, nzeru yofotokozedwa ngati munthu] kusekerera ndi ana a anthu.” Anali Mwana wamtengo wapatali ameneyu amene Mulungu anamtumiza padziko lapansi kudzapereka dipo. Chotero, mawuwa a Yesu ali ndi tanthauzo chotani nanga: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha”!​—Yohane 3:16.

13, 14. Kodi mbiri ya Baibulo yakuti Abrahamu anayesa kupereka Isake nsembe iyenera kutithandiza kuzindikira chiyani pazimene Yehova anachita? (1 Yohane 4:10)

13 Kuti tithandizidwe kumvetsa tanthauzo la zimenezo pamlingo wakutiwakuti, Mulungu analangiza Abrahamu kale kwambiri Yesu asanadze padziko lapansi, zaka ngati 3,890 zapitazo, kuti: “Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isake, amene ukondana naye, numuke kudziko la Moriya; numpereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe.” (Genesis 22:1, 2) Mwachikhulupiriro, Abrahamu anamvera. Talingalirani kuti inu munali Abrahamu. Bwanji ngati ameneyo anali mwana wanu, mwana wanu wamwamuna yekha amene mumamkonda kwambiri? Kodi mukanamva motani poŵaza nkhuni za nsembe yopsereza, poyenda ulendo masiku ambiri kupita kudziko la Moriya, ndi kuika mwana wanu paguwa la nsembe?

14 Kodi kholo lachifundo limakhaliranji ndi malingaliro amenewo? Genesis 1:27 amati Mulungu analenga munthu m’chifanizo Chake. Malingaliro athu achikondi ndi chifundo amasonyeza mwanjira yochepa chikondi chake cha Yehova ndi chifundo. Ponena za Abrahamu, Mulungu analoŵererapo kotero kuti Isake sanaperekedwe nsembe ayi. (Genesis 22:12, 13; Ahebri 11:17-19) Koma, ponena za iye mwini, Yehova sanaleke kutatsala pang’ono kuti akonze dipo, ngakhale kuti anachita zimenezo mwa kutayikidwa kwambiri iye mwini ndi Mwana wake yemwe. Zimene zinachitika sizinali chifukwa chakuti Mulungu anali ndi thayo ayi, koma m’malo mwake, anasonyeza chisomo chapadera kwambiri. Kodi timachiyamikira kwambiri?​—Ahebri 2:9.

Zimene Limatheketsa

15. Kodi dipo lakhudza motani moyo ngakhale m’dongosolo lino la zinthu?

15 Makonzedwe achikondi amenewo amene Mulungu anapanga amakhudza kwambiri moyo wa awo amene amawalandira ndi chikhulupiriro. Kale iwo anali kutali ndi Mulungu chifukwa cha uchimo. Malinga ndi zimene Mawu ake amanena, iwo anali ‘adani chifukwa maganizo awo anali pantchito zoipa.’ (Akolose 1:21-23, NW) Koma ‘anayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake.’ (Aroma 5:8-10) Pokhala atasintha moyo wawo ndi kulandira chikhululukiro chimene Mulungu amatheketsa kwa awo osonyeza chikhulupiriro m’nsembe ya Kristu, amakhala ndi chikumbumtima choyera.​—Ahebri 9:14; 1 Petro 3:21.

16. Kodi ndi madalitso otani amene kagulu ka nkhosa kapatsidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo m’dipo?

16 Yehova wayanja mwachisomo oŵerengeka mwa ameneŵa, kagulu ka nkhosa, kuti akagwirizane ndi Mwana wake mu Ufumu wakumwamba, ndi cholinga cha kukwaniritsa chifuno choyamba cha Mulungu cha dziko lapansi. (Luka 12:32) Ameneŵa atengedwa mu ‘mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse, . . . adawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko.’ (Chivumbulutso 5:9, 10) Kwa ameneŵa, mtumwi Paulo analemba kuti: “Munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nawo, kuti, Abba, Atate. Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso oloŵa nyumba; inde oloŵa nyumba ake a Mulungu, ndi oloŵa anzake a Kristu.” (Aroma 8:15-17) Powalandira Mulungu monga ana ake, iwo amapatsidwa unansi wamtengo wapatali umene Adamu anataya; komanso ana ameneŵa adzapatsidwa mathayo owonjezera okatumikira kumwamba​—amene Adamu analibe. Chifukwa chake mtumwi Yohane anati: “Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu”! (1 Yohane 3:1) Kwa oterewa, Mulungu sangosonyeza chikondi cha lamulo (a·gaʹpe) komanso chikondi chochokera mumtima (phi·liʹa), chimene chimakhalapo pakati pa mabwenzi enieni monga chomangira.​—Yohane 16:27.

17. (a) Kodi onse osonyeza chikhulupiriro m’dipo apatsidwa mwaŵi wotani? (b) Kodi “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu” udzatanthauzanji kwa iwo?

17 Enanso​—onse osonyeza chikhulupiriro m’makonzedwe abwino a Mulungu a moyo mwa Yesu Kristu​—Yehova amawatsegulira mwaŵi wopezera unansi wamtengo wapatali umene Adamu anataya. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Chiyembekezetso cha cholengedwa [anthu ochokera mwa Adamu] chilindira vumbulutso la ana a Mulungu [ndiko kuti, akuyembekezera nthaŵi pamene zidzaonekeratu kuti ana a Mulungu oloŵa anzake a Kristu a Ufumu wakumwamba akuchitapo kanthu mwamphamvu m’malo mwa mtundu wa anthu]. Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru [anabadwira mu uchimo oyembekezera kufa, ndipo analibe njira imene akanadzimasula nayo], chosafuna mwini, koma chifukwa cha Iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo [choperekedwa ndi Mulungu] kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:19-21) Kodi ufuluwo udzatanthauzanji? Kuti amasuka ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. Adzakhala angwiro m’maganizo ndi kuthupi, Paradaiso adzakhala mudzi wawo, adzakhala ndi moyo wamuyaya umene adzasangalalamo ndi ungwiro wawo ndipo adzayamikira Yehova, Mulungu yekha woona. Nanga tsopano zonsezi zatheka bwanji? Mwa nsembe ya dipo ya Mwana wa Mulungu wobadwa yekha.

18. Pa March 23 dzuŵa litaloŵa, kodi ife tidzakhala tikuchitanji, ndipo chifukwa ninji?

18 Pa Nisani 14, 33 C.E., m’chipinda chapamwamba m’Yerusalemu, Yesu anayambitsa Chikumbutso cha imfa yake. Phwando lapachaka lokumbukira imfa yake lakhala chochitika chofunika pamoyo wa Akristu onse oona. Yesu mwiniyo analamula kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” (Luka 22:19) Mu 1997 Chikumbutso chidzachitika dzuŵa litaloŵa pa March 23 (pamene Nisani 14 iyamba). Tsiku lomwelo, kulibe chidzakhala chofunika kuposa kupezekapo panthaŵi ya Chikumbutso imeneyi.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi Mulungu wasonyeza motani chikondi chochuluka kwa mtundu wa anthu?

◻ Kodi nchifukwa ninji panafunikira moyo wa munthu wangwiro kuti uombole mbadwa za Adamu?

◻ Kodi Yehova anataya zochuluka motani pokonza dipo?

◻ Kodi dipo limatheketsa chiyani?

[Chithunzi patsamba 10]

Mulungu anapereka Mwana wake wobadwa yekha

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena