Khalani ndi lingaliro loyenera la Chifundo cha Mulungu
DOKOTALAYO anali wokoma mtima ndi wodera nkhaŵa kwambiri. Malinga ndi kupenda kwake kosamalitsa, wodwala wakeyo anafunikira kwambiri kuchitidwa opaleshoni kotero kuti apulumutse moyo wake. Pamene wodwalayo anazengereza kupereka yankho nabutsa nkhani ya kuthiridwa mwazi, dokotalayo anadabwa. Pamene anafotokoza kuti chifukwa cha zifukwa za chipembedzo sangavomereze kuchitidwa opaleshoni imene ikafunikira kuthiridwa mwazi, dokotalayo anadodomadi kwambiri. Iyeyo anayesayesa kuganizaganiza njira yomthandizira. Potsirizira pake, anaganiza kuti wapeza njirayo. Iye anati: “Mukudziŵa nanga, ngati simuvomereza kuthiridwa mwazi, mudzafa. Inu simukufuna zimenezo, kodi sichoncho?”
“Ndithudi ayi,” anatero wodwala wakeyo.
“Koma, mwachionekere, ngati muvomereza, mudzachimwira zikhulupiriro za chipembedzo chanu, zimene zili zofunikanso kwa inu. Chabwino, nali lingaliro langa. Bwanji osangovomereza kuthiridwa mwazi kuti mupulumutse moyo wanu. Ndiyeno nkuulula kwa Mulungu kuti mwachimwa, ndi kulapa. Mwanjira imeneyo, mudzabwezeretsedwanso m’chipembedzo chanu.”
Dokotala wokhala ndi cholinga chabwino ameneyu analingalira kuti anapeza yankho labwino kwambiri. Iye anazindikira kuti wodwala wakeyo anakhulupirira mwa Mulungu wachifundo. Ndithudi, imeneyi inali nthaŵi yoyenera kugwiritsira ntchito chifundo cha Mulungu! Koma kodi lingaliro lakelo linali labwino monga momwe linamvekeramo?
Kodi Timalingalira Motere Nthaŵi Zina?
Nthaŵi zina tingapeze kuti tikulingalira monga momwe dokotalayo anachitira. Mwinamwake timaopa kuukiridwa kosayembekezereka kusukulu kapena kuntchito. Kapena mwina tingapeze kuti tili mumkhalidwe wochititsa manyazi wotitsendereza kuchita kanthu kena kamene kangakhumudwitse chikumbumtima chathu. Mosadziŵa, tingakhoterere pakutenga njira yosavuta ndi kuchita zimene tikudziŵa kuti nzolakwa, tikumalingalira za kupempha chikhululukiro pambuyo pake.
Kapena anthu alionse paokha angayesedwe ndi zikhoterero zawo zolakwa. Mwachitsanzo, mnyamata angakhale mumkhalidwe umene umuyesa kwambiri kuchita chisembwere. Mmalo mwa kulimbana ndi chikhumbo choipa chimenecho, iye angachilolere molakwa, akumalingalira kudzalungamitsa nkhaniyo ndi Mulungu pambuyo pake. Ena afikira ngakhale pakuchita tchimo lalikulu mosasamala kanthu kuti akudziŵa kuti angachotsedwe mumpingo Wachikristu. Mwachionekere iwo alingalira kuti, ‘Ndidzalola kuti papite nthaŵi yaifupi. Ndiyeno ndidzalapa ndi kubwezeretsedwa.’
Mikhalidwe yonseyi ili ndi zinthu ziŵiri zofanana. Choyamba, anthuwo amalolera molakwa mmalo mwa kumenya nkhondo ya kuchita chimene chili chabwino. Chachiŵiri, iwo amalingalira kuti atachita cholakwacho, Mulungu adzangowakhululukira mosavuta ngati atangopempha chikhululukiro.
Kodi Lingaliro Labwino Nliti?
Kodi zimenezi zimasonyeza chiyamikiro choyenera kaamba ka chifundo cha Mulungu? Eya, taganizirani za chifundo chimenecho kwakanthaŵi. Yesu anati: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Mtumwi Yohane anafotokoza mmene chifundo chimenecho chimagwirira ntchito pamene anati: “Izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama.” (1 Yohane 2:1) Chifukwa chake, ngati tigwera muuchimo chifukwa cha kupanda ungwiro, tikhoza kufikira Mulungu m’pemphero ndi kumpempha chikhululukiro pamaziko a nsembe ya Yesu.
Komabe, kodi zimenezi zimatanthauza kuti zilibe kanthu kuti tachimwa kapena ayi, chinthu chachikulu nchakuti tipemphe chikhululukiro pambuyo pake? Kutalitali. Kumbukirani mawu oyamba a mawu ogwidwawo: “Izi ndikulemberani, kuti musachimwe.” Mawu enanso a Yohane m’vesili akusonyeza za kakonzedwe kachikondi ka Yehova pochita ndi kupanda ungwiro kwathu. Komabe, tiyenera kuyesayesa kwambiri kuti tipeŵe kuchimwa. Apo phuluzi, tingasonyeze kupanda ulemu kochititsa chisoni kaamba ka chikondi cha Mulungu, mofanana ndi anthu amene amatchulidwa ndi Yuda amene anagwiritsira ntchito kukoma mtima kwa Mulungu kukhala chodzikhululukira pakhalidwe losadziletsa.—Yuda 4.
Kuona chifundo cha Mulungu monga chinthu chotipulumutsa pamene tilakwa mosasamala kanthu ndi zimene timachita kumanyozetsa chifundo cha Mulungu ndi kukupangitsa kuonekera ngati kuti tchimolo siliri loipa kwambiri. Zimenezi sizowona. Mtumwi Paulo anauza Tito kuti: “Pakuti chaonekera chisomo cha Mulungu cha kupulumutsa anthu onse, ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m’dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza.”—Tito 2:11, 12.
Paulo anasonyeza kuyamikira kwake chifundo cha Mulungu m’njira imene analimbanira ndi kupanda ungwiro kwake. Iye anati: “Ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.” (1 Akorinto 9:27) Paulo sanaone zinthu mwawamba chifukwa chakuti akanachimwa mobwerezabwereza. Kodi ife tiyenera kutero?
Lingaliro la Yesu
Panthaŵi ina, Yesu anasonyeza mmene anaonera lingaliro la kulolera molakwa ndi kutenga njira yosavuta kotero kuti tipeŵe mavuto. Pamene anayamba kuuza ophunzira ake za imfa yake yansembe imene inalinkudza, Petro anayesa kumletsa kuti sizichitika, akumati: “Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa inu ayi.” Kodi Yesu anachita motani? “Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.”—Mateyu 16:22, 23.
Chidzudzulo champhamvu cha Yesu kwa Petro chinasonyeza mwamphamvu kuti Yesu anakana kutenga njira yosavuta imene inaloŵetsamo kutsutsana ndi chifuniro cha Mulungu. Cholembedwacho chimasonyeza kuti iye anatsatira njira yabwino mosandenguma, akumavutitsidwa ndi Satana. Potsirizira pake anasekedwa, kumenyedwa kwambiri, ndipo anafa imfa yaululu. Komabe, iye sanalolere molakwa, ndipo chifukwa cha zimenezi anali wokhoza kupereka moyo wake monga dipo lathu. Ndithudi iye sanapirire zonsezi kotero kuti ‘tidzichitire chifundo’ pamene zovuta kapena mayesero abuka!
Ponena za Yesu kwanenedwa kuti: “Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa.” (Ahebri 1:9) Kaŵirikaŵiri kutenga njira yosavuta kumaphatikizapo kuchita chisalungamo. Chifukwa chake, ngati timadadi chimenechi—monga momwe Yesu anachitira—nthaŵi zonse tidzakana kulolera molakwa. M’buku la Miyambo, Yehova amati: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) Chilungamo cha Yesu chachikatikati komanso chosalolera molakwa chinadzetsa chikondwerero mumtima mwa Yehova. Nafenso tingakondweretse Yehova mofananamo ngati titsatira njira ya Yesu ya umphumphu.—1 Petro 2:23.
Kuphunzitsidwa Mwakupirira
Mtumwi Petro analemba kuti: “Mmenemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthaŵi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu, kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo amtengo wake woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pavumbulutso la Yesu Kristu.” (1 Petro 1:6, 7) Chifukwa chakuti ndife opanda ungwiro ndipo tikukhala m’dziko la Satana, tidzayang’anizanabe mosalekeza ndi mayeso ndi mayesero. Monga momwe Petro akusonyezera, ameneŵa angakwaniritse chifuno chabwino. Amayesa chikhulupiriro chathu, kuchisonyeza kaya ngati chili chofooka kapena champhamvu.
Amatithandizanso kuphunzira zinthu. Yesu “anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo.” (Ahebri 5:8) Nafenso tingaphunzire kumvera, ndiponso kudalira Yehova, ngati tipirira m’chiyeso. Ndipo njira imeneyi yophunzirira zinthu idzapitirizabe kufikira itatha, monga momwe Petro ananenera kuti: “Mulungu . . . adzafikitsa inu opanda chirema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.”—1 Petro 5:10.
Komabe, ngati tilolera molakwa poyesedwa, timadzisonyeza kukhala amantha kapena ofooka, opanda chikondi champhamvu pa Yehova ndi pachilungamo kapena osadziletsa. Kufooka kulikonse kotero kumaopseza kwambiri unansi wathu ndi Mulungu. Ndithudi, chenjezo la Paulo lingakhaledi lowona kwa ife: “Tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziŵitso cha chowonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo.” (Ahebri 10:26) Nkwabwino chotani nanga kuti tisachimwe poyambirira pomwe mmalo mwa kugonjera pamkhalidwe wofooka ndi kudziika pangozi ya kutayikiridwa ndi ziyembekezo zonse za moyo!
Umphumphu Wosadalira Pakanthu Kena
M’masiku a mneneri Danieli, Ahebri atatu anawopsezedwa ndi imfa ya moto ngati akakana kulambira fano. Kodi iwo anayankha motani? “Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m’ng’anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m’dzanja lanu, mfumu. Koma akapanda kutero, dziŵani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolidi mudaliimikalo.”—Danieli 3:17, 18.
Iwo anatenga kaimidwe kameneko chifukwa chakuti anafuna kuchita chimene chinali choyenera. Ngati kaimidwe kameneka kakanawatengera kuimfa, anali ololera kutero. Chidaliro chawo chinali pachiukiriro. Komabe, ngati Mulungu akanawapulumutsa, zimenezo zikanakhala zabwino kwambiri. Komatu kaimidwe kawo kolimbako sikanadalire pakanthu kena. Motero ndimo mmene ziyenera kukhalira ndi atumiki a Mulungu nthaŵi zonse.
M’tsiku lathu lino ena amene akana kulolera molakwa amangidwa, kuzunzidwa, ngakhale kuphedwa. Ena adzimana zinthu zakuthupi, akumasankha kukhala osauka koposa kupeza chuma mwakunyalanyaza malamulo a mkhalidwe abwino. Kodi nchiyani nanga chimene chinachitika kwa mkazi Wachikristu wotchulidwa pachiyambi pa nkhaniyi? Iye anayamikira chisonkhezero choperekedwa mokoma mtima komabe chosokera cha dokotalayo, koma sanalolere molakwa chikhulupiriro chake. Mmalomwake, kulemekeza kwake lamulo la Yehova kunamchititsa kukana opaleshoniyo. Mwachimwemwe, iye anachira napitiriza kutumikira Yehova mokangalika. Komabe, pamene ananena molimba mtima za mkhalidwe wakewo, sanadziŵe chimene chikatsatira, koma anali wokonzekera kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova.
Kodi nchiyani chimene chinamthandiza kukhala wolimba kwambiri pansi pa chitsenderezocho? Iye sanayese kudzidalira, ndipo mtumiki aliyense wa Mulungu sayenera kutero. Kumbukirani, “Mulungu ndiye pothaŵirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso.” (Salmo 46:1) Kuli bwino kwambiri chotani nanga kutembenukira kwa Mulungu kaamba ka chithandizo pamene tiyesedwa koposa kuchimwa ndiyeno kutembenukira kwa iye kuti tichitiridwe chifundo!
Inde, tiyenitu tisapeputse chifundo chachikulu cha Mulungu. Mmalomwake, tiyeni tikulitse chikhumbo chowona cha kuchita zabwino, ngakhale pamikhalidwe yovuta. Zimenezi zidzakulitsa unansi wathu ndi Yehova, zidzatipatsa maphunziro amene tikufuna kaamba ka moyo wosatha, ndi kulemekeza moyenera chifundo cha Mulungu. Khalidwe lotero la nzeru lidzakondweretsa mtima wa Atate wathu wakumwamba.
[Chithunzi patsamba 24]
Kudalira pachiukiriro kotheratu kunathandiza Ahebri atatu kusunga umphumphu