Mutu 2
Bukitsani Kuti Yehova Ndiye Mulungu Woona Yekha
BAIBULO limati ngakhale kuti ilipo yambiri imene imaonedwa monga milungu, “koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate.” (1 Akorinto 8:5, 6) “Mulungu mmodzi” ameneyo ndi Yehova, Mlengi wa zinthu zonse. (Deuteronomo 6:4; Chivumbulutso 4:11) Yesu anatcha Mulungu ameneyo kuti “Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.” (Yohane 20:17) Anavomerezana ndi Mose yemwe kalelo anali atanena kuti: “Yehova ndiye Mulungu [woona, NW]; palibe wina wopanda iye.” (Deuteronomo 4:35) Yehova amaposa kwambiri zinthu zina zilizonse zimene zimalambiridwa, monga ngati mafano, anthu, kayanso mdani wake Satana Mdyerekezi, yemwe ndi “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano.” (2 Akorinto 4:3, 4) Mosiyana ndi zinthu zonsezi, Yehova ndiye ‘Mulungu woona yekha,’ monga ananenera Yesu.—Yohane 17:3.
2 Anthu oyamikira amene amaphunzira makhalidwe osangalatsa a Mulungu, ndiponso zimene watichitira ndi zimene adzatichitira, amayamba kum’konda. Pamene chikondi chawo pa Yehova chikukula, amaona kuti akuyenera kubukitsa za iye. Motani? Njira imodzi ndiyo kuuza ena za iye. “Ndi m’kamwa [munthu] avomereza kutengapo chipulumutso,” amatero Aroma 10:10. Njira ina ndiyo kumutsanzira m’mawu athu ndi zochita zathu. “Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa,” amatero Aefeso 5:1. Kuti tichite zimenezi bwinobwino, tifunika kudziŵa kuti Yehova ndi ndani.
3 M’Baibulo lonse, muli mawu ambiri amene amafotokoza makhalidwe apadera a Mulungu. Makhalidwe ake akuluakulu anayi ndiwo nzeru, chilungamo, mphamvu, ndi chikondi. ‘Kwa Iye kuli nzeru.’ (Yobu 12:13) ‘Njira zake zonse ndi chiweruzo,’ kapena kuti n’zachilungamo. (Deuteronomo 32:4) ‘Ali wolimba mphamvu.’ (Yesaya 40:26) ‘Mulungu ndiye chikondi.’ (1 Yohane 4:8) Komabe, pa makhalidwe akuluakulu anayiŵa a Mulungu, kodi ndi khalidwe liti limene n’lapadera kwambiri, khalidwe lomwe limasonyeza mmene Mulungu alili kuposa khalidwe lina lililonse?
“Mulungu Ndiye Chikondi”
4 Talingalirani chomwe chinachititsa Yehova kulenga kumwamba ndi dziko lapansi komanso mizimu yanzeru ndi anthu anzeru. Kodi zinali nzeru zake kapena mphamvu zake? Ayi, chifukwa ngakhale kuti Mulungu anagwiritsa ntchito nzeru zake ndi mphamvu zake, zimenezi sindizo zinamuchititsa kufuna kuyamba kulenga zinthu. Ndiponso sanafunike kupatsa moyo zinthu zina kuti akwaniritse chilungamo chake. M’malo mwake, chikondi chachikulu cha Mulungu ndicho chinamulimbikitsa kupatsa ena moyo kuti azisangalala pokhala zolengedwa zanzeru. Chikondi chinamulimbikitsa kukhala ndi cholinga chakuti anthu omvera akhale ndi moyo kosatha m’Paradaiso. (Genesis 1:28; 2:15) Chikondi chinamuchititsa kukonza zochotsa chilango chimene Adamu anapatsira anthu chifukwa cha kuchimwa kwake.
5 Motero mwa makhalidwe onse a Mulungu, khalidwe lake lapadera kwambiri ndi chikondi. Ndicho chikhalidwe chake. Ngakhale kuti nzeru zake, chilungamo chake, ndiponso mphamvu zake n’zofunika kwambiri, Baibulo silinena kuti Yehova ndiye khalidwe lililonse la ameneŵa. Koma limanena kuti iye ndiye chikondi. Inde, ngati tingalingalire chikondi kukhala munthu, Yehova yekha ndiye angakhale munthu ameneyo. Chimenechitu ndi chikondi chosachita zinthu mongotengeka maganizo, koma ndi chikondi chozikika pa kutsatira mfundo za makhalidwe abwino. Mulungu amasonyeza chikondi chake potsatira mfundo za choonadi ndi zachilungamo. Chimenechi n’chikondi chapamwamba kwambiri, chomwe chitsanzo chake timachiona mwa Yehova Mulungu iye mwini. Chikondi chotere chilibe dyera ngakhale pang’ono ndipo nthaŵi zonse chimayendera limodzi ndi zochitika zimene zimapereka umboni wooneka wa chikondichi.
6 Chikondi chapamwamba chimenechi n’chomwe chimatithandiza kutsanzira Mulungu ameneyu. Tingaganize kuti sitingathe kuchita zimenezi bwinobwino popeza ndife anthu wamba opanda ungwiro, ndipo timachimwa nthaŵi ndi nthaŵi. Komatu nachi chitsanzo china cha chikondi chachikulu cha Yehova: Amadziŵa zimene sitingakwanitse ndipo safuna kuti tizichita zinthu monga angwiro. Amadziŵa kuti pakali pano ndife opanda ungwiro. (Salmo 51:5) Ndicho chifukwa chake Salmo 130:3, 4 limati: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye? Koma kwa Inu kuli chikhululukiro.” Inde, Yehova ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka.” (Eksodo 34:6) “Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira.” (Salmo 86:5) Zimenezitu n’zolimbikitsa zedi. Ndipo n’zosangalatsadi kwambiri kutumikira Mulungu wochititsa chidwi ameneyu n’kumaona akutisamalira mwachikondi ndi mwachifundo.
7 Tingathenso kuona chikondi cha Yehova m’zimene analenga. Taganizirani zinthu zabwino zambirimbiri zimene Yehova watipatsa kuti tizisangalala nazo, monga mapiri okongola, nkhalango, ndi nyanja. Watipatsa chakudya cha mitundumitundu chokoma komanso chotithandiza kukhala ndi moyo. Yehova watipatsanso maluŵa okongola ndi onunkhira bwino osiyanasiyana, limodzinso ndi nyama zochititsa chidwi. Analenga zinthu zosangalatsa anthu, ngakhale kuti analibe mangawa opanga zinthu zimenezo. Zoonadi, popeza tikukhala m’dziko loipali ndipo ndife opanda ungwiro, sitingathe kusangalala ndi zonse zimene analenga. (Aroma 8:22) Koma tangoganizirani zimene Yehova adzatichitira m’Paradaiso! Wamasalmo anatitsimikizira kuti: “Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo [chabwino].”—Salmo 145:16.
8 Kodi njira yopambana kwambiri imene Yehova anaonetsera chikondi pa anthu ndi iti? Baibulo limafotokoza kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Kodi Yehova anachita izi chifukwa chakuti anthu anali kuchita zabwino? Aroma 5:8 amayankha kuti: “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.” Inde, Mulungu anatumiza padziko lapansi Mwana wake wangwiro kuti adzapereke moyo wake nsembe ya dipo yotiwombolera ku chilango cha uchimo ndi imfa. (Mateyu 20:28) Zimenezi zinatsegula njira yoti anthu okonda Mulungu apeze moyo wosatha. Ubwino wake n’ngwakuti Mulungu amakonda aliyense amene amafuna kuchita chifuniro chake, pakuti Baibulo limatiuza kuti: “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”—Machitidwe 10:34, 35.
9 Kodi mfundo yakuti Yehova wapereka Mwana wake kukhala dipo lathu ndi kutitsegulira njira ya ku moyo wosatha, iyenera kukhudza motani moyo wathu pakalipano? Iyenera kukulitsa chikondi chathu pa Mulungu woona, Yehova. Ndiponso, iyenera kutichititsa kufuna kumvera Yesu, amene amaimira Mulungu. “[Yesu] adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa Iye amene adawafera iwo.” (2 Akorinto 5:15) Kutsatira mapazi a Yesu n’kosangalatsa kwambiri, chifukwa iye anali chitsanzo chabwino zedi pa kutsanzira chikondi ndi chifundo cha Yehova. Tikuona zimenezi m’mawu aŵa amene Yesu ananena kwa anthu odzichepetsa: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.”—Mateyu 11:28-30.
Kusonyeza Chikondi kwa Ena
10 Kodi tingasonyeze motani kuti timakonda Akristu anzathu monga mmene Yehova ndi Yesu amatikondera? Taonani njira zambirimbiri izi zochitira zimenezi: “Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziŵa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa; sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi; chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse. Chikondi sichitha nthaŵi zonse.”—1 Akorinto 13:4-8; 1 Yohane 3:14-18; 4:7-12.
11 Ndaninso ena amene tiyenera kuwasonyeza chikondi, ndipo tingawakonde motani? Yesu anati: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Izi zimaphatikizapo kufotokozera anthu amene pakalipano si Akristu anzathu uthenga wabwino wa dziko latsopano la paradaiso la Mulungu lomwe likubwera. Yesu ananena mosapita m’mbali kuti sitiyenera kukonda anthu okha amene amakhulupirira zomwe ifenso timakhulupirira. Iye anati: “Ngati muwakonda akukondana ndi inu [okha] mphoto yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho? Ndipo ngati mulankhula abale anu okhaokha, muchitanji choposa ena? Kodi angakhale anthu akunja sachita chomwecho?”—Mateyu 5:46, 47; 24:14; Agalatiya 6:10.
‘Yendani M’dzina la Yehova’
12 Mbali ina yofunika pa kubukitsa za Mulungu woona ndiyo kudziŵa dzina lake lapadera, lakuti Yehova, kuligwiritsa ntchito, ndi kuliphunzitsa kwa ena. Wamasalmo ananena zimene anali kukhumba mu mtima mwake kuti: “Kuti adziŵe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi.” (Salmo 83:18) Dzina lakuti Yehova limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Iye ndiye Wamkulu pokwaniritsa zolinga, moti nthaŵi zonse amakwaniritsa bwinobwino zolinga zake. Ndipo amene angayenerere kukhala ndi dzina limenelo ndi Mulungu woona yekha, chifukwa anthu sangakhale otsimikiza kuti zochita zawo zidzayenda bwino. (Yakobo 4:13, 14) Ndi Yehova yekha amene anganene kuti mawu ake “adzakula” monga anawatumizira. (Yesaya 55:11) Ambiri amasangalala zedi pamene kwa nthaŵi yoyamba aona dzina la Mulungu m’mabaibulo awo ndi kuphunzira zimene limatanthauza. (Eksodo 6:3) Koma kudziŵa zimenezi kudzawapindulitsa pokhapokha ‘atayenda m’dzina la Yehova kwamuyaya.’—Mika 4:5.
13 Salmo 9:10 limanena za dzina la Mulungu kuti: “Iwo akudziŵa dzina lanu adzakhulupirira Inu.” Zimenezi sizikutanthauza kungodziŵa dzinalo lakuti Yehova, chifukwa munthu akangodziŵa dzina lakelo sindiye kuti wamukhulupirira. Kudziŵa dzina la Mulungu kumatanthauza kumvetsetsa kuti Yehova ndi Mulungu wotani, kulemekeza ulamuliro wake, kumvera malamulo ake, ndi kumudalira m’zinthu zonse. (Miyambo 3:5, 6) Mofananamo, kuyenda m’dzina la Yehova kumatanthauza kudzipatulira kwa iye ndi kumamuimira monga wolambira wake; kugwiritsadi ntchito moyo wathu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. (Luka 10:27) Kodi inu mukuchita zimenezi?
14 Kuti titumikire Yehova mpaka muyaya, sitiyenera kumutumikira chabe chifukwa chakuti tili naye mangawa ayi. Mtumwi Paulo analangiza Timoteo, yemwe anali atatumikira Yehova zaka zambiri, kuti: “Khala ukudziphunzitsa uli ndi cholinga chokhala wodzipereka kwa Mulungu.” (1 Timoteo 4:7, NW) Munthu amakhala wodzipereka kwa wina chifukwa chakuti mumtima mwake amayamikira kwambiri munthu winayo. ‘Kudzipereka kwa Mulungu’ kumasonyeza kuti munthu amalemekeza Yehova kwambiri. Kumaonetsa kuti munthuyo wadziphatika kwa Yehova posonkhezereka ndi chikondi chifukwa chomulemekeza kwambiri Yehovayo ndi njira zake. Kumatichititsa kufuna kuti aliyense azichitira ulemu dzina lake. Tikhale odzipereka kwa Mulungu pa moyo wathu kuti tithe kuyenda m’dzina la Yehova, Mulungu woona yekha, mpaka muyaya.—Salmo 37:4; 2 Petro 3:11.
15 Kuti titumikire Mulungu movomerezeka, kulambira kwathu kusakhale kogaŵanika, chifukwa iye ndi “Mulungu wansanje.” (Eksodo 20:5) Sitingakonde Mulungu panthaŵi yofananayo n’kumakondanso dziko loipali lomwe Satana ndiye mulungu wake. (Yakobo 4:4; 1 Yohane 2:15-17) Yehova amadziŵa bwino zedi kuti aliyense wa ife akufuna kukhala munthu wotani. (Yeremiya 17:10) Ngati timakondadi chilungamo, iye amaona zimenezi ndipo adzatithandiza kupirira ziyeso za tsiku ndi tsiku. Mwa kutipatsa mzimu wake woyera wamphamvu zedi, adzatithandiza kupambana zoipa zimene zili ponseponse m’dzikoli. (2 Akorinto 4:7) Adzatithandizanso kukhalabe ndi chiyembekezo cholimba cha moyo wosatha padziko lapansi la paradiso. Chimenechitu n’chiyembekezo chapamwamba kwabasi! Tiyeni tichiyamikire kwambiri ndipo titumikire Mulungu woona, Yehova, mwakufuna kwathu pakuti moyo wosathawu udzatheka chifukwa cha iye.
16 Anthu mamiliyoni ochuluka padziko lonse avomereza ndi mtima wonse zimene ananena wamasalmo pamene analemba kuti: “Bukitsani pamodzi ndine ukulu wa Yehova, ndipo tikweze dzina lake pamodzi.” (Salmo 34:3) Yehova akukupemphani kuti mukhale mmodzi wa anthu ochuluka a m’mitundu yonse omwe akuchita zimenezi.
Bwerezani Zimene Mwakambirana
• Kodi Yehova ali ndi umunthu wotani? Kodi timapindula motani tikamvetsetsa makhalidwe ake?
• Kodi ena tingawasonyeze chikondi motani?
• Kodi kudziŵa dzina la Yehova ndiponso kuyenda m’dzina lake kumatanthauzanji?
[Mafunso]
1. Kodi Mulungu woona yekha ndani?
2. Pamene tikuphunzira za Mulungu, kodi moyo wathu uyenera kukhudzidwa motani?
3. Kodi makhalidwe akuluakulu a Mulungu ndi ati?
4. Kodi ndi khalidwe liti la Mulungu limene linamuchititsa kulenga kumwamba ndi dziko lapansi komanso zamoyo zonse?
5. Malinga n’kunena kwa Baibulo, ndi khalidwe liti limene titalilingalira kukhala munthu, ndi Yehova yekha amene angakhale munthu ameneyo, ndipo n’chifukwa chiyani?
6. Kodi n’chifukwa chiyani timatha kutsanzira Mulungu, ngakhale kuti iye amatiposa?
7. Kodi chikondi cha Yehova tingachione motani m’zimene analenga?
8. Kodi njira yopambana kwambiri imene Yehova anaonetsera chikondi pa ife ndi iti?
9. Kodi mfundo yakuti Yehova wapereka Mwana wake kukhala dipo lathu iyenera kutikhudza motani?
10. Kodi ndi njira zina ziti zimene tingasonyezere chikondi kwa Akristu anzathu?
11. Ndaninso ena amene tiyenera kuwasonyeza chikondi, ndipo tingawakonde motani?
12. N’chifukwa chiyani dzina la Mulungu lili loyenera iye yekha basi?
13. Kodi kudziŵa dzina la Yehova ndiponso kuyenda m’dzina lake kumatanthauzanji?
14. Kuti titumikire Yehova mpaka muyaya, kodi chofunika n’chiyani kuwonjezera pa kukhala kwathu ndi mangawa?
15. Kodi tingatani kuti tizilambira Mulungu yekhayo basi?
16. Kodi mufunika kuchitanji pamodzi ndi anthu ena mamiliyoni ochuluka?
[Zithunzi patsamba 14]
Yehova, mwa chikondi chake chachikulu, ‘adzaolowetsa dzanja lake n’kukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo’