“Koposa Zonse Mukhale Nacho Chikondano Chenicheni”
“Chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; . . . koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha.”—1 PETRO 4:7, 8.
YESU ankadziŵa kuti maola ake omaliza kukhala limodzi ndi atumwi ake anali amtengo wapatali. Ankadziŵa zimene zidzawachitikire m’tsogolo. Ophunzirawo anali ndi ntchito yaikulu yofunika kuchita, koma Yesu anadziŵa kuti adzadedwa ndi kuzunzidwa monga momwe zinachitikira kwa iye. (Yohane 15:18-20) Usiku womaliza kukhala nawo limodzi umenewo, Yesu anawakumbutsa maulendo angapo kufunika ‘kokondana wina ndi mnzake.’—Yohane 13:34, 35; 15:12, 13, 17.
2 Mtumwi Petro, amene analipo usiku umenewo, anamvetsa mfundo imeneyo. Patapita zaka zingapo, pamene Petro analemba kalata Yerusalemu atatsala pang’ono kuwonongedwa, anagogomezera kufunika kwa chikondi. Analangiza Akristu kuti: “Chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; . . . koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha.” (1 Petro 4:7, 8) Mawu a Petro ali ndi tanthauzo lalikulu kwa anthu amene akukhala mu “masiku otsiriza” a dongosolo la zinthu lilipoli. (2 Timoteo 3:1) Kodi “chikondano chenicheni” n’chiyani? N’chifukwa chiyani tifunika kukhala ndi chikondi choterocho pa ena? Ndipo tingasonyeze bwanji kuti tili nachodi?
Kodi “Chikondano Chenicheni” N’chiyani?
3 Anthu ambiri amaganiza kuti chikondi ndi chinthu chimene chiyenera kungobwera chokha popanda munthu kuchitapo kalikonse. Koma Petro sankanena za chikondi wamba. Ankanena za mtundu wapamwamba kwambiri wa chikondi. Liwu lakuti “chikondano” lopezeka pa 1 Petro 4:8 analimasulira kuchokera ku liwu lachigiriki lakuti a·gaʹpe. Liwu limenelo limatanthauza chikondi chopanda dyera chimene munthu amachisonyeza chifukwa chotsatira, kapena kulamulidwa ndi mfundo zinazake. Buku lina linati: “Chikondi cha agape chimatheka kuchilamulira chifukwa sichitengera kwenikweni mmene munthu akumvera mumtima koma munthu amatha kudziuza kuti achite chinachake.” Chifukwa chakuti tinabadwa ndi chizoloŵezi chodzikonda, timafunikira kutikumbutsa kuti tizikondana, ndi kuti tizichita zimenezi motsatira mfundo za Mulungu.—Genesis 8:21; Aroma 5:12.
4 Zimenezi sizikutanthauza kuti tiyenera kukondana chifukwa chakuti tifunika kutero basi. Sikuti munthu akamasonyeza chikondi cha a·gaʹpe sakhala waubwenzi kapena sasonyeza mmene akumvera. Petro anati ‘tikhale nacho chikondano chenicheni [“chotambasuka,” Kingdom Interlinear] mwa ife tokha.’a Komabe, kukhala ndi chikondi choterocho kumafuna kuchitapo kanthu. Ponena za mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “chenicheni,” katswiri wina anati: “Amapereka chithunzi cha munthu amene akuthamanga amene akutambasula miyendo yake kwambiri kufika pomaliza mphamvu zake zonse pamapeto pa mpikisano.”
5 Choncho chikondi chathu sichiyenera kutichititsa zinthu zosavuta kuchita zokha, ndiponso sitiyenera kuchisonyeza kwa anthu ochepa chabe. Chikondi chachikristu chimafuna kuti ‘titambasule’ mtima wathu, tisonyeze chikondi ngakhale pamene zingakhale zovuta kutero. Mwachionekere, chikondi choterocho tiyenera kuyesetsa kuti tikhale nacho ndiponso kuti tipitirize kukhala nacho, monga momwe munthu wothamanga pa mpikisano amayenera kuphunzira ndiponso kunola luso lake. M’pofunika kwambiri kuti tikhale ndi chikondi choterocho pa wina ndi mnzake. Chifukwa chiyani? Tiyeni tionepo zifukwa zitatu.
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukondana?
6 Choyamba, ‘chifukwa chakuti chikondi n’chochokera kwa Mulungu.’ (1 Yohane 4:7) Yehova, Mwiniwake wa khalidwe losangalatsa limeneli, ndi amene anayamba kutikonda. Mtumwi Yohane anati: “Umo chidaoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anam’tuma Mwana wake wobadwa yekha, aloŵe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye.” (1 Yohane 4:9) Mwana wa Mulungu ‘anatumidwa’ mwa kukhala munthu, kuchita utumiki wake, ndi kufa pa mtengo wozunzirapo, ndipo anachita zonsezo “kuti tikhale ndi moyo.” Kodi tiyenera kuchita chiyani poona kuti Mulungu anatikonda m’njira yodabwitsa yoteroyo? Yohane anati: “Ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.” (1 Yohane 4:11) Taonani kuti Yohane anati, ‘Ngati Mulungu anatikonda ife kotero,’ osati iwe, koma ife. Mfundo yake n’njoonekeratu: Ngati Mulungu amakonda olambira anzathu, ndiye kuti ifenso tiyenera kuwakonda.
7 Chachiŵiri, m’pofunika kwambiri kukondana makamaka masiku ano kuti tizitha kuthandiza abale athu amene akufunika thandizo, chifukwa chakuti “chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi.” (1 Petro 4:7) Tikukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1) Zochitika padziko lapansi, masoka achilengedwe, ndi kutsutsidwa kumatibweretsera mavuto. Pa nthaŵi zovuta, timafunika kuyandikana kwambiri ndi anzathu. Chikondi chenicheni chidzatigwirizanitsa pamodzi ndi kutilimbikitsa ‘kusamalana wina ndi mnzake.’—1 Akorinto 12:25, 26.
8 Chachitatu, tiyenera kukondana chifukwa sitikufuna ‘kupatsa malo Mdyerekezi’ kuti atipezerere. (Aefeso 4:27) Satana sachedwa kugwiritsira ntchito kupanda ungwiro kwa okhulupirira anzathu, monga zofooka zawo ndi zolakwa zawo, kuti atikhumudwitse. Kodi mawu osaganizira bwino amene wokhulupirira mnzathu wanena kapena zochita zake zosaganizira ena zidzatichititsa kudzipatula ku mpingo? (Miyambo 12:18) Sizidzatero ngati tili ndi chikondi chenicheni! Chikondi choterocho chimatithandiza kukhala pamtendere ndi kutumikira Mulungu mogwirizana ndiponso “ndi mtima umodzi.”—Zefaniya 3:9.
Mmene Mungasonyezere Kuti Mumakonda Ena
9 Kukonda ena kuyenera kuyambira panyumba. Yesu ananena kuti otsatira ake oona adzadziŵika chifukwa cha chikondi chimene adzakhale nacho pa wina ndi mnzake. (Yohane 13:34, 35) Chikondi chiyenera kuoneka, osati mu mpingo mokha, komanso m’banja, pakati pa mwamuna ndi mkazi komanso pakati pa makolo ndi ana. Kudziŵa kuti mumakonda anthu a m’banja mwanu sikokwanira, muyenera kusonyeza zimenezi powachitira zinthu zabwino.
10 Kodi anthu okwatirana angasonyezane bwanji chikondi? Mwamuna amene amakondadi mkazi wake amamusonyeza kuti amamusamalira mwa mawu ndi zochita zake, kaya akhale pagulu kapena paokha. Amamulemekeza monga munthu payekha, ndipo amaganizira malingaliro ake ndi mmene akumvera. (1 Petro 3:7) Amaika ubwino wa mkaziyo patsogolo pa ubwino wake, ndipo amachita zonse zimene angathe kuti amupezere zosoŵa pamoyo wake, amusamale mwauzimu, ndiponso amusangalatse. (Aefeso 5:25, 28) Mkazi amene amakondadi mwamuna wake amamupatsa ulemu waukulu, ngakhale ngati nthaŵi zina sachita zinthu zimene mkaziyo amaganiza. (Aefeso 5:22, 33) Amathandiza mwamuna wake ndipo amamugonjera, osati kumuuza kuti azichita zinthu zovuta kukwanitsa, koma amagwirizana naye akamaika zinthu zauzimu pamalo oyamba m’moyo wawo.—Genesis 2:18; Mateyu 6:33.
11 Makolo, kodi ana anu mungawasonyeze bwanji chikondi? Kukhala kwanu ofunitsitsa kugwira ntchito mwakhama kuti muwapezere zofunika pamoyo ndi umboni woti mumawakonda. (1 Timoteo 5:8) Koma ana amafuna zambiri, osati zakudya, zovala, ndi pogona pokha basi. Kuti akadzakula azidzakonda ndi kutumikira Mulungu, amafunika kuwaphunzitsa zinthu zauzimu. (Miyambo 22:6) Zimenezi zimatanthauza kupatula nthaŵi yoti banja lanu liziphunzira Baibulo, kuchita utumiki, ndi kupezeka pa misonkhano yachikristu. (Deuteronomo 6:4-7) Kuchita zimenezi nthaŵi zonse kumafuna kuti mupeŵe zinthu zina zambiri zimene mukanakonda kuchita, makamaka mu nthaŵi zovuta zino. Kudera kwanu nkhaŵa ndi kuchita kwanu khama kuti musamalire ana anu mwauzimu kumasonyeza kuti mumawakonda, chifukwa kumasonyeza kuti mukuganizira za moyo wawo wosatha.—Yohane 17:3.
12 M’pofunikanso kwambiri kuti makolo azisonyeza chikondi chawo pa ana awo mwa kuonetsetsa kuti anawo akusangalala. Ana sachedwa kukhumudwa, ndipo amafunika kuwatsimikizira nthaŵi ndi nthaŵi kuti mumawakonda. Auzeni kuti mumawakonda, ndipo muziwachitira zinthu zosiyanasiyana zosonyeza kuti mumawakonda, chifukwa zimenezi zimawatsimikizira kuti ndi okondedwa ndiponso ndi amtengo wapatali. Muziwayamikira mwachikondi ndiponso kuchokera pansi pamtima, chifukwa zimenezi zimawasonyeza kuti mumaona ntchito zawo zabwino ndipo mumaziyamikira. Muziwalanga mwachikondi, chifukwa chilango choterocho chimawasonyeza kuti muli ndi chidwi ndi khalidwe limene akukula nalo. (Aefeso 6:4) Njira zosonyezera chikondi zabwino zoterozo zimathandiza kuti banja likhale lachimwemwe ndi logwirizana kwambiri ndipo lingathe kulimbana ndi zovuta za m’masiku otsiriza ano.
13 Chikondi chimatithandiza kunyalanyaza zolakwa za ena. Kumbukirani kuti pamene Petro ankalimbikitsa anthu amene anawalembera kalata yake ‘kukhala ndi chikondano chenicheni mwa iwo okha,’ anapereka chifukwa chimene kuchita zimenezi kulili kofunika kwambiri. Iye anati: “Pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo.” (1 Petro 4:8) ‘Kukwirira’ machimo sikutanthauza kubisa machimo aakulu. Machimo oterowo amayenera kukanenedwa kwa anthu a udindo mu mpingo ndipo amachitapo kanthu. (Levitiko 5:1; Miyambo 29:24) Kungakhale kupanda chikondi ndiponso kusemphana ndi Malemba kulola kuti anthu amene akuchita machimo aakulu apitirizebe kupweteka anthu ena osalakwa.—1 Akorinto 5:9-13.
14 Nthaŵi zambiri, zolakwa za okhulupirira anzathu zimakhala zazing’ono. Tonsefe timalakwa m’mawu ndi m’zochita zathu nthaŵi ndi nthaŵi, ndipo timakhumudwitsana kapena kukwiyitsana. (Yakobo 3:2) Kodi tizifulumira kufalitsa zolakwa za ena? Kuchita zimenezo kungangoyambitsa mikangano mu mpingo. (Aefeso 4:1-3) Ngati timachita zinthu mwachikondi, ‘sitidzaneneza’ kapena kuti, kufalitsa, zolakwa za wokhulupirira mnzathu. (Salmo 50:20) Monga momwe pulasitala ndi penti zimabisira kunyansa kwa khoma, chikondi chimabisa zolakwa za ena.—Miyambo 17:9.
15 Chikondi chidzatichititsa kuthandiza anthu amene akufunikiradi thandizo. Pamene zinthu m’masiku otsiriza ano zikuipiraipira, padzakhala nthaŵi zimene okhulupirira anzathu adzafunike kuwathandiza mwa njira ina yake. (1 Yohane 3:17, 18) Mwachitsanzo, kodi munthu wa mu mpingo mwathu wakumana ndi mavuto aakulu azachuma, kapena ntchito yamuthera? Ndiye kuti mwina tingamuthandizeko m’njira inayake, monga momwe tingathere. (Miyambo 3:27, 28; Yakobo 2:14-17) Kodi nyumba ya mkazi wamasiye wachikulire ikufunika kukonza? Mwina tingayambe kuchitapo kanthu kuti tithandize kukonza nyumbayo.—Yakobo 1:27.
16 Sitisonyeza chikondi kwa anthu amene amakhala m’dera lathu okha. Nthaŵi zina tingamve za atumiki a Mulungu m’mayiko ena amene akuvutika chifukwa kwachitika mphepo ya mkuntho, zivomezi, kapena zipoloŵe. Angafunike chakudya, zovala, ndi zinthu zina mwamsanga. Zilibe kanthu kuti angakhale a mtundu kapena fuko lina. ‘Timakonda abale’ athu onse. (1 Petro 2:17) Choncho, mofanana ndi mipingo ya m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, timakhala ofunitsitsa kuthandiza pakakonzedwa zotumizako thandizo. (Machitidwe 11:27-30; Aroma 15:26) Tikamasonyeza chikondi m’njira zonse zoterozo, timalimbitsa m’gwirizano wathu m’masiku otsiriza ano.—Akolose 3:14.
17 Chikondi chimatichititsa kuuza ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Taganizirani chitsanzo cha Yesu. N’chifukwa chiyani ankalalikira ndi kuphunzitsa? ‘Anagwidwa chifundo’ ndi anthuwo chifukwa anali omvetsa chisoni mwauzimu. (Marko 6:34) Anthuwo ananyalanyazidwa ndi kunamizidwa ndi abusa achipembedzo onyenga, amene anayenera kuwaphunzitsa zinthu zauzimu zoona ndi kuwapatsa chiyembekezo. Choncho, chifukwa chakuti anali ndi chikondi chachikulu ndi chifundo pa anthuwo, Yesu anawalimbikitsa ndi “Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu.”—Luka 4:16-21, 43.
18 Masiku anonso anthu ambiri anyalanyazidwa mwauzimu ndi kunamizidwa, ndipo alibe chiyembekezo. Nafenso, mofanana ndi Yesu, ngati tizindikira zosoŵa zauzimu za anthu amene sakumudziŵa Mulungu woona ndi kukhudzidwa nazo, ndiye kuti tidzakhala ndi chikondi ndi chifundo pa anthu oterowo ndipo tidzafuna kuwauza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 6:9, 10; 24:14) Chifukwa chakuti nthaŵi imene yatsala ndi yochepa, m’pofunika kwambiri kuti tsopano tilalikire mwachangu uthenga wopatsa moyo umenewu.—1 Timoteo 4:16.
“Chitsiriziro cha Zinthu Zonse Chili Pafupi”
19 Kumbukirani kuti Petro asanapereke malangizo ake oti tizikondana ananena kuti: “Chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi.” (1 Petro 4:7, 8) Posachedwapa dziko loipali lidzaloŵedwa m’malo ndi dziko latsopano la Mulungu lachilungamo. (2 Petro 3:13) Motero masiku ano, palibenso nthaŵi yochita mphwayi. Yesu anatichenjeza kuti: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha.”—Luka 21:34, 35.
20 Choncho tiyeni tiyesetse ‘kudikira,’ kuzindikira nthaŵi imene tikukhalamo. (Mateyu 24:42) Tiyeni tipeŵe ziyeso zilizonse za Satana zimene zingatidodometse. Tisalole dziko lopanda chikondi lino kutilepheretsa kusonyeza chikondi kwa ena. Koposa zonse, tiyeni tiyandikane kwambiri ndi Mulungu woona, Yehova, amene Ufumu wake Waumesiya udzakwaniritsa zolinga zake zonse zochititsa chidwi zokhudza dziko lapansili.—Chivumbulutso 21:4, 5.
[Mawu a M’munsi]
a Pa 1 Petro 4:8, mabaibulo ena amanena kuti tizikondana “moonadi,” “mwakuya,” kapena “moona mtima.”
MAFUNSO OGWIRITSA NTCHITO POPHUNZIRA
• Kodi Yesu potsanzikana ndi ophunzira ake anawauza malangizo otani, ndipo n’chiyani chikusonyeza kuti Petro anamvetsa malangizo amenewo? (Ndime 1-2)
• Kodi “chikondano chenicheni” n’chiyani? (Ndime 3-5)
• N’chifukwa chiyani tiyenera kukondana? (Ndime 6-8)
• Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakonda ena? (Ndime 9-18)
• N’chifukwa chiyani nthaŵi ino siyochita mphwayi, ndipo tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani? (Ndime 19-20)
[Chithunzi patsamba 29]
Banja logwirizana lingathe kulimbana bwino ndi zovuta za m’masiku otsiriza ano
[Chithunzi patsamba 30]
Chikondi chimatichititsa kuthandiza anthu amene akufunikiradi thandizo
[Chithunzi patsamba 31]
Kuuza ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumasonyeza kuti timawakonda