Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • pe mutu 10 tsamba 90-98
  • Mizimu Yoipa Njamphamvu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mizimu Yoipa Njamphamvu
  • Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KUYEREKEZERA KUKHALA SAMUELI WAKUFA
  • ANGELO AMENE ANAKHALA MIZIMU YOIPA
  • MMENE MIZIMU YOIPA IMASOKERETSERA
  • KUTSUTSA ZIUKIRO ZA MIZIMU YOIPA
  • Mmene Zochita za Angelo Komanso Ziwanda Zimakhudzira Moyo Wathu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Chifukwa Chimene Muyenera Kupeŵera Kukhulupirira Mizimu
    Galamukani!—2000
  • Lolani Kuti Yehova Akuthandizeni Polimbana ndi Mizimu Yoipa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Kodi Pali Mizimu Yoipa?
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
Onani Zambiri
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
pe mutu 10 tsamba 90-98

Mutu 10

Mizimu Yoipa Njamphamvu

1. Kodi nchifukwa ninji anthu ambiri amakhulupirira kuti iwo angalankhule ndi akufa?

KAWIRIKAWIRI ANTHU amati iwo alankhula ndi akufa. Malemu James A. Pike, bishopu wotchuka wa Episikopaliani, ananena kuti analankhula ndi mwana wake wakufa Jim. Malinga ndi kunena kwa Pike, mwana wake anamuuza kuti: “Ndiri ndi maunyinji a anthu ondizinga, ndipo manja akunditukula, kunena kwake nditero . . . ndinali wosakondwa kwambiri kufikira nditakudziwitsani.”

2. (a) Kodi nchifukwa ninji palibe aliyense angalankhule ndi akufa? (b) Motero kodi ndimafunso otani amene akufunsidwa?

2 Popeza kuti zinthu zoterozo nzofala kwambiri, nzachiwonekere kuti anthu ambiri alankhula ndi munthu wina wakudziko lamizimu. Koma iwo sanalankhule ndi wakufa. Baibulo nlomvekera bwino kwambiri pamene limati: “Koma akufa sadziwa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Motero ngati sali akufa amene akulankhula kuchokera kudziko lamizimu, kodi ndani amene akulankhula? Kodi ndani amene akuyerekezera kukhala anthu akufa?

3. (a) Kodi ndani amene amayerekezera kukhala anthu akufa, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi mizimu yoipa kawirikawiri imapereka mawu kwa yani?

3 Ndiwo mizimu yoipa. Mizimu imeneyi, kapena ziwanda, ndiyo angelo amene anagwirizana ndi Satana n’kupandukira Mulungu. Kodi nchifukwa ninji iwo amayerekezera kukhala anthu amene amwalira? Ndiko kuti apititse patsogolo lingaliro lakuti akufa ngamoyobe. Mizimu yoipa yachititsanso ambiri kukhulupirira kuti imfa ndiyo kusinthira ku moyo wina chabe. Kuti ifalitse bodza limeneli, mizimu yoipa imapereka obwebweta, alauli ndi openduza okhala ndi chidziwitso chapadera chimene kokha chimawonekera kukhala ngati chikuchokera kwa anthu amene amwalira.

KUYEREKEZERA KUKHALA SAMUELI WAKUFA

4. (a) Kodi nchifukwa ninji Mfumu Sauli anali wosowa chithandizo? (b) Kodi lamulo la Mulungu linali lotani ponena za obwebweta ndi alauli?

4 M’Baibulo muli chitsanzo cha mzimu woipa umene unayerekezera kukhala mneneri wakufa wa Mulungu, Samueli. Kumeneku kunali m’chaka cha 40 cha kulamulira kwa Mfumu Sauli. Gulu lankhondo lamphamvu la Afilisiti lidadza kulimbana ndi gulu lankhondo Lachiisrayeli la Sauli, ndipo iye anawopa kwambiri. Sauli anadziwa lamulo la Mulungu: “Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nawo.” (Levitiko 19:31) Komabe, m’kupita kwa nthawi, Sauli anapandukira Yehova. Chifukwa cha chimenecho Samueli, amene pa nthawiyo anali wamoyo, anakana kuwonananso ndi Sauli. (1 Samueli 15:35) ndipo tsopano, m’nthawi ino ya vuto, Mfumu Sauli anali wosowa chochita chifukwa chakuti Yehova sanamvere mfuu zake za chithandizo.

5. (a) Kodi nkuti kumene Sauli anapita kaamba ka chithandizo? (b) Kodi nchiyani chimene wobwebwetayo anali wokhoza kuchita?

5 Sauli anali wofunitsitsa kwambiri kudziwa chimene chidzachitika chakuti anapita kwa obwebweta ku Endori. Iye anali wokhoza kutulutsa mpangidwe wa munthu amene iye anatha kuwona. Mwa kufotokoza kwake mpangidwewo, Sauli adamdziwa kukhala “Samueli.” Zitatere munthu wauzimu, woyerekezera kukhala Samueliyo, analankhula: “Wandivutiranji kundikweretsa kuno?” Sauli anayankha: “Ndirikusautsika kwambiri, pakuti Afilisiti aponyana nkhondo ndi ine.” Munthu wauzimuyo anayankha: “Ndipo undifunsiranji ine, popeza Yehova anakuchokera, nasandulika mdani wako?” Munthu wauzimu woipayo, amene anali kuyerekezera kukhala Samueli wakufa, kenako anapitiriza kuuza Sauli kuti iye akaphedwa mu nkhondo ndi Afilisiti.—1 Samueli 28:3-19.

6. Kodi nchifukwa ninji sakanakhala anali Samueli amene analankhula ndi Sauli?

6 Mwachiwonekere, sanalidi Samueli amene wobwebwetayo adalankhula naye. Samueli anafa, ndipo pa imfa munthu “amabwerera kunthaka yake; m’tsiku lomwelo maganizo ake amatha.” (Salmo 146:4, NW) Kuganiza pang’ono pa nkhaniyo kumasonyezanso kuti mawuwo sanali kwenikweni aja a Samueli wakufa. Samueli anali mneneri wa Mulungu. Motero iye anatsutsa obwebweta. Ndipo, monga momwe tawonera, pamene iye anali wamoyo adakana kulankhulanso ndi Sauli wosamverayo. Motero, pamenepa, ngati Samueli akanakhala wamoyobe, kodi akadalola wobwebweta ameneyu kuliganiza kuti iye awonane ndi Sauli? Ganiziraninso: Yehova adakana kupatsa Sauli chidziwitso chirichonse. Kodi wobwebweta akanakakamiza Yehova kupatsa Sauli uthenga kudzera mwa Samueli wakufa? Ndipo ngati amoyo akathadi kulankhula ndi akufa okondedwa, ndithudi Mulungu wa chikondi sakadanena kuti iwo adakhala “odetsedwa” chifukwa cha kutembenukira kwa wobwebweta.

7. Kodi ndi chenjezo lotani limene Mulungu anapereka kutetezera anthu ake ku mizimu yoipa?

7 Chenicheni ndicho chakuti mizimu yoipa njofuna kuvulaza anthu, motero Yehova amapereka machenjezo kutetezera atumiki ake. Werengani chenjezo lotsatirapo kwa mtundu wa Israyeli. Limakupatsani lingaliro la njira zimene ziwanda zimagwiritsira ntchito kusocheza anthu. Baibulo limati: “Asapezeke mwa inu . . . wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.” (Deuteronomo 18:10-12) Tiyenera kufuna kudziwa zimene mizimu yoipa ikuchita kuti ivulaze anthu lerolino ndi mmene tingadzitetezere kwa iyo. Koma tisanaphunzire za zimenezi, tiyeni tilingalire nthawi ndi mmene mizimu yoipa inayambira.

ANGELO AMENE ANAKHALA MIZIMU YOIPA

8. (a) Kodi ndaninso amene Satana anachititsa kupandukira Mulungu? (b) Ataleka ntchito yawo kumwamba, kodi iwo anapita kuti?

8 Mwa kunamiza Hava m’munda wa Edene, cholengedwa china chaungelo chinadzipanga kukhala mzimu woipa Satana Mdyerekezi. Pambuyo pake iye anayesa kuchititsa angelo enanso kupandukira Mulungu. M’kupita kwa nthawi iye anapambana. Angelo ena analeka ntchito imene Mulungu adawapatsa kuti achite kumwamba, ndipo iwo anatsikira kudziko lapansi nadzipangira matupi anyama onga awo a anthu. Wophunzira Wachikristu Yuda analemba ponena za iwo pamene anatchula “angelonso amene sanasunga chikhalidwe chawo choyamba, komatu anasiya pokhala pawopawo.” (Yuda 6) Kodi anadzeranji kudziko lapansi? Kodi ndichikhumbo cholakwa chotani chimene Satana anaika mumtima mwawo kuwachititsa kusiya malo abwino kwambiri amene anali nawo kumwamba?

9. (a) Kodi nchifukwa ninji angelo anadza kudziko lapansi? (b) Kodi ndimotani mmene Baibulo limasonyezera kuti zimene iwo anachita zinali zoipa?

9 Baibulo limatilola kudziwa pamene limati: “Ana aamuna a Mulungu anayang’ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.” (Genesis 6:2) Inde, angelowo anavala matupi anyama, anadza kudziko lapansi kudzagona ndi akazi okongola. Koma kugonana koteroko kunali kolakwa kwa angelo. Kameneka kanali kachitidwe ka kusamvera. Baibulo limsonyeza kuti chimene iwo anachita chinali cholakwa mofanana ndi machitidwe a kugonana kwa ofanana ziwalo kwa anthu a Sodomu ndi Gomora. (Yuda 6, 7) Kodi chinatsatirapo nchiyani?

10, 11. (a) Kodi angelowo anabala ana a mtundu wotani? (b) Kodi nchiyani chimene chinachitikira zimphonazo pamene Chigumula chinadza? (c) Kodi nchiyani chimene chinachitikira angelo pa nthawi ya Chigumula?

10 Eya, ana anabadwa kwa angelo ndi akazi awo amenewa. Koma anawo anali osiyana. Iwo anapitiriza kukhala akulu kufikira iwo anakhala zimphona, inde, zimphona zoipa. Baibulo limawatcha “anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.” Zimphona zimenezi zinayesa kukakamiza aliyense kukhala woipa mofanana ndi iwo. Chifukwa cha chimenecho, Baibulo limanena kuti “kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.” (Genesis 6:4, 5) Chifukwa cha chimenecho Yehova anadzetsa Chigumula. Zimphonazo, kapena “Anefili,” ndi anthu onse oipa anaphedwa ndi madzi. Koma kodi nchiyani chimene chinachitikira angelo amene adadza kudziko lapansi?

11 Iwo sanaphedwe ndi madzi. Iwo anachotsa matupi awo anyama ndi kubwerera kumwamba monga anthu auzimu. Koma iwo sanaloledwe kukhalanso mbali ya gulu la Mulungu la angelo oyera. M’malo mwake, Baibulo limanena kuti “Mulungu sanalekerera angelo adachimwawo, koma anawaponya kundende nawaika ku maenje a mdima, asungike akaweruzidwe.”—2 Petro 2:4.

12. (a) Kodi nchiyani chimene chinachitikira angelo oipa pamene iwo anabwerera kumwamba? (b) Kodi nchifukwa ninji iwo sangavalenso matupi aumunthu? (c) Motero kodi nchiyani chimene iwo tsopano akuchita?

12 Angelo oipa amenewa sanaponyedwe m’malo enieni otchedwa Ndende. M’malo mwake, Ndende, imene yatembenuzidwa molakwa kukhala “helo” m’Mabaibulo ena, imatanthauza mkhalidwe wonyozeka kapena wotsika wa angelo amenewa. Iwo anadulidwa ku kuwunika kwauzimu kwa gulu la Mulungu, ndipo iwo akungoyembekezera kokha chiwonongeko chosatha. (Yakobo 2:19; Yuda 6) Chiyambire nthawi ya Chigumula, Mulungu sanalole angelo oipa amenewa kuvala matupi anyama, motero iwo sangathe kukhutiritsa mwachindinji zikhumbo zawo zoipa zakugonana. Komabe iwo angasonyezebe mphamvu yowopsa pa amuna ndi akazi. Kunena zowona, mothandizidwa ndi ziwanda zimenezi Satana ‘akasokeretsa dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu.’ (Chivumbulutso 12:9) Kuwonjezeka kwakukulu lerolino m’zoipa zakugonana, chiwawa ndi kuchita zoipa kwina kumasonyeza kufunikira kwathu kwa kukhala ochenjerera kusokeretsedwa nawo.

MMENE MIZIMU YOIPA IMASOKERETSERA

13. (a) Kodi ndimotani mmene mizimu yoipa imasokeretsera? (b) Kodi kukhulupirira mizimu nchiyani, ndipo kodi nchiyani chimene Baibulo limanena za iko?

13 Taphunzira poyambirirapo kuti Satana, monga “mulungu wa dongosolo lino la zinthu,” amagwiritsira ntchito maboma adziko ndi chipembedzo chonyenga kuchititsa khungu anthu ku chowonadi Chabaibulo. (2 Akorinto 4:4, NW) Njira ina yaikulu imene mizimu yoipa imasokeretsera amuna ndi akazi ndiyo mwa kukhulupira mizimu. Kodi kukhulupirira mizimu nchiyani? Ndiko kulankhula ndi mizimu yoipa, mwina mwachindunji kapena mwa wobwebweta. Kukhulupirira mizimu kumalowetsa munthu mu ulamuliro wa ziwanda. Baibulo limatichenjeza kuti titalikirane ndi kachitidwe kalikonse kogwirizana ndi kukhulupirira mizimu.—Agalatiya 5:19-21; Chivumbulutso 21:8.

14. (a) Kodi ula nchiyani? (b) Kodi Baibulo limanenanji za uwo?

14 Ula ndiwo mpangidwe wofala kwambiri wa kukhulupirira mizimu. Ndiwo kachitidwe koyesa kudziwa za mtsogolo, kapena kanthu kena kosadziwika, mothandizidwa ndi mizimu yosawoneka. Zimenezi zikusonyezedwa ndi zimene wophunzira Wachikristu Luka analemba: “Anakomana ndi ife namwali wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ake zambiri pakubwebweta pake.” Mtumwi Paulo anali wokhoza kumasula namwaliyo ku mphamvu ya mzimu woipa umenewu, ndipo sanakhozenso kuneneratu mtsogolo.—Matchitidwe 16:16-19.

15. (a) Kodi ndizinthu zina zotani zogwirizana ndi kukhulupirira mizimu? (b) Kodi nchifukwa ninji kukhala ndi phande m’zinthu zoterozo kuli kowopsa?

15 Anthu ambiri ngokondwera ndi kukhulupirira mizimu chifukwa chakuti nkozizwitsa ndi kodabwitsa. Kumawakondweretsa. Motero iwo amakhala odziphatikiza ndi ufiti, using’anga, kugoneka tulo, matsenga, kupenda nyenyezi, matabwa owombezera kapena kanthu kenanso kogwirizana ndi kukhulupirira mizimu. Iwo angawerenge mabukhu onena za zinthu zimenezi, kapena kupita ku akanema, kapena kuwonera maprogramu a televizheni onena za izo. Iwo angapite ngakhale ku msonkhano kumene wobwebweta amafunafuna kulankhula ndi mizimu. Koma zonsezi nzosayenera kwa munthu amene akufuna kutumikira Mulungu wowona. Nkowopsanso. Kungatsogolere ku vuto lenileni tsopano. Ndiponso, Mulungu adzaweruza ndi kutaya otsatira kukhulupirira mizimu onse.—Chivumbulutso 22:15.

16. Kodi ndimotani mmene Baibulo limasonyezera kuti Akristu ali ndi nkhondo yomenyana ndi mizimu yoipa?

16 Ngakhale pamene munthu achita zonse zimene angathe kulekana ndi kukhulupirira mizimu, iye angaukiridwebe ndi mizimu yoipa. Kumbukirani kuti mawu a Mdyerekezi mwiniyo anamvedwa ndi Yesu Kristu, akumamuyesa kuti aswe lamulo la Mulungu. (Mateyu 4:8, 9) Atumiki ena a Mulungu akhala ndi ziukiro zoterozo. Mtumwi Paulo anati: “Tiri ndi nkhondo . . . yomenyana ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.” Zimenezi zikutanthauza kuti mtumiki aliyense wa Mulungu ayenera “kutenga zovala zonse za nkhondo zochokera kwa Mulungu, kuti [iye] akakhale wokhoza kutsutsa.”—Aefeso 6:11-13, NW.

KUTSUTSA ZIUKIRO ZA MIZIMU YOIPA

17. Kodi muyenera kuchitanji ngati “mawu” ochokera kwa mizimu alankhula kwa inu?

17 Kodi muyenera kuchitanji ngati “mawu” ochokera kwa mizimu alankhula nanu? Bwanji ngati “mawuwo” akuyerekezera kukhala wachibale wakufa kapena mzimu wabwiono? Eya, kodi nchiyani chimene Yesu anachita pamene “mfumu ya ziwanda” inalankhula naye? (Mateyu 9:34) Iye anati: “Choka Satana!” (Mateyu 4:10) Mungachitenso zomwezo. Ndiponso, mungapemphe Yehova chithandizo. Pempherani mofuula ndi kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu. Kumbukirani kuti iye ngwamphamvu kwambiri koposa mmene mizimu yoipa iriri. Tsatirani njira yanzeru imeneyi. Musamvetsere mawu oterowo ochokera kwa mizimu. (Miyambo 18:10; Yakobo 4:7) Zimenezi sizitanthauza kuti munthu aliyense amene amava “mawu” alinkulankhulidwa ndi ziwanda. Nthawi zina kumvedwa kwa mawu kungachititsidwe ndi matenda ena akuthupi kapena amaganizo.

18. Kodi ndichitsanzo cha Akristu oyambirira chotani pa Efeso chimene chiri chabwino kutsatira ngati munthu akufuna kuwonjoka m’kukhulupirira mizimu?

18 Mwina mwake nthawi ina inu munachita nawo machitidwe ena a kukhulupirira mizimu ndipo tsopano mukufuna kuleka. Kodi mungachitenji? Eya, lingalirani chitsanzo cha Akrisu oyambirira ku Efenso. Iwo atalandira “mawu a Yehova” olalikidwa ndi mtumwi Paulo, Baibulo limati: “Ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabukhu awo, nawatentha pamaso pa onse.” Ndipo mabukhu amenewa anali okwanira ndalama zasiliva 50,000! (Machitidwe 19:19, 20) Motsanzira awo amene anakhala atsatiri a Kristu ku Efeso, ngati muli ndi zinthu m’manja mwanu zimene ziri zogwirizana mwachindunji ndi kukhulupirira mizimu njira yanzeru ndiyo kuziwononga ziribe kanthu zikhale zamtengo motani.

19. (a) Kodi nchiyani chimene anthu ochuluka amene amakhala ndi phande m’kukhulupirira mizimu samadziwa? (b) Ngati tikufuna kukhala ndi moyo kosatha m’chimwemwe padziko lapansi, kodi tiyenera kuchitanji?

19 Popeza kuti kuli chikondwerero chachikulu lerolino m’zodabwitsa ndi zozizwitsa, anthu owonjezerekawonjezereka akudzilowetsa m’kukhulupirira mizimu. Komabe, ochuluka a anthu amenewa, samadziwa kuti iwo akudzigwirizanitsadi ndi mizimu yoipa. Chimenechi sichiri chokondweretsa chopanda liwongo. Mizimu yoipa iri ndi mphamvu ya kuvulaza ndi kuwononga. Iyo njanjiru. Ndipo, Kristu asanaiike m’ndende m’chiwonongeko kosatha, iyo ikuchita zonse zimene ingathe kulowetsa anthu mu ulamuliro wawo woipa. (Mateyu 8:28, 29) Motero ngati mukufuna kukhala ndi moyo kusatha m’chimwemwe padziko lapansi kuipa konse kutachotsedwa, mufunikira kulekana ndi mphamvu yoipa mwa kusagwirizana ndi mtundu uliwonse wa kukhulupirira mizimu.

[Chithunzi patsamba 91]

Kodi wobwebweta wa ku Endori analankhula ndiyani?

[Zithunzi pamasamba 92, 93]

Ana a Mulungu aungelo anawona ana akazi a anthu

[Chithunzi patsamba 94]

Angelo ovala matupiwo sanafe ndi madzi. Iwo anavula matupi awo anyama ndi kubwerera kumwamba

[Chithunzi patsamba 97]

Baibulo limachenjeza kuti: ‘Lekanani ndi mipangidwe yonse ya kukhulupirira mizimu’

[Chithunzi patsamba 98]

Awo amene anakhala Akristu mu Efeso anatentha mabukhu awo onena za kukhulupirira mizimu—Chitsanzo chabwino kwa ife lerolino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena